Kanachita Kubwera ndi Mphepo
Kanachita Kubwera ndi Mphepo
Mkulu wina akuyenda mu mzinda wa Mumbai ku India, chimphepo chinaulutsira kapepala kenakake chapafupi ndi iyeyo. Kapepalako kanali Uthenga wa Ufumu Na. 36, wakuti “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu ndi Lotani?” Mutuwu unam’chititsa chidwi. Nthaŵi yomweyo anakatola, n’kukaŵerenga mpaka kukamaliza. Kanam’chititsa chidwi kwambiri, ndipo pofuna kuti aimvetse nkhaniyi, anapempha Baibulo ndi mabuku ena.
Kapepalako kanafalitsidwa ndi Mboni za Yehova ndipo kali ndi mfundo zolimbikitsa chikhulupiriro. Kamalongosola momveka bwino kuti mavuto athu onseŵa monga matenda, umphaŵi, ndi nkhondo, amayamba chifukwa cha “umbombo, kusakhulupirirana ndi dyera—mikhalidwe imene siingathetsedwe ndi kafukufuku wa sayansi, luso lopanga zinthu, kapena ndale.” Kapepalako kamanenanso kuti posachedwapa Mulungu adzachotsa kuipa konse padziko pano.
Kodi mungakonde kudziŵa bwino malonjezo a m’Baibulo onena za m’tsogolo? Anthu ambiri amaphunzitsidwa Baibulo m’nyumba zawo ndi Mboni za Yehova pogwiritsira ntchito mabuku ofotokoza Baibulo, monga kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? Kabuku kameneka kamayankha mafunso onga akuti: Kodi Mulungu ndani? Kodi chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi n’chiyani? Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji m’banja?
Ngati mukufuna kuti a Mboni za Yehova afike panyumba panu kuti akuthandizeni kumvetsa zimene Mulungu achite posachedwapa, iwo angakonde kwambiri kutero ndipo adzakuthandizani kumvetsa za Ufumu wa Mulungu. Lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi kuti adzakuthandizeni.
□ Nditumizireni kabuku kakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.