Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuonera M’kalasi Kuli ndi Vuto Lanji?

Kodi Kuonera M’kalasi Kuli ndi Vuto Lanji?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Kuonera M’kalasi Kuli ndi Vuto Lanji?

“Aliyense amadziŵa kuti kuonera n’kulakwa, koma kungoti n’kophweka.”—anatero Jimmy, yemwe ali ndi zaka 17.

KODI munayamba mwasuzumirako pa pepala la mnzanu polemba mayeso? Ngati munachitapo zimenezi, dziŵani kuti mulipo ambiri. Jenna, amene ali fomu 4, ananenapo za anzake osachita manyazi n’kuonera mayeso, kuti “amachita kudzitamandira nazo. Ngati iweyo suonera amakuona ngati kuti m’mutu mwako simuli bwino!”

Pa kafukufuku wina ku United States, achinyamata 80 mwa achinyamata 100 alionse amene ankakhoza bwino m’kalasi ananena kuti ankachita kuonera, ndipo pagululi ambiri anali asanagwidwepo n’komwe. Bungwe loona za makhalidwe abwino lotchedwa Josephson Institute of Ethics litachita kafukufuku pakati pa ana oposa 20,000 a m’sukulu za pulayimale ndi sekondale, linapeza kuti: “Zinthu zikuipiraipira pankhani ya kuona mtima.” Akuluakulu a zamaphunziro aima mutu poona mmene khalidwe loonera m’kalasi lafalira! Gary J. Niels, yemwe ndi mkulu wa sukulu inayake, anafika mpaka ponena kuti: “Ndi anthu ochepa chabe amene saonera.”

Makolo ambiri amafuna kuti ana awo azichita zinthu mwachilungamo kusukulu. Tsoka ilo, achinyamata ambiri safuna kuchita chilungamo, koma kuonera. Kodi ndi njira zatsopano ziti zimene akugwiritsira ntchito? Kodi n’chifukwa chiyani achinyamata ena amangoganiza zoonera? Nanga n’chifukwa chiyani khalidweli muyenera kulipeŵa?

Kuonera Pogwiritsira Ntchito Zipangizo Zamakono

Pali njira zosiyanasiyana zimene anthu amagwiritsira ntchito masiku ano poonera. Ndipotu kuonera ntchito yokachitira kunyumba kapena kugwiritsira ntchito likasa si nkhaninso ayi tikakuyerekezera ndi kuonera m’njira zina zamakono. Njira zimenezi ndi monga kulandira mayankho a mayeso pa telefoni yam’manja kuchokera kwa munthu wina amene ali kunja; kugwiritsira ntchito makakyuleta okhala ndi zinthu zina “zowonjezera;” timakamera tobisa m’malaya timene amatumizira mafunso kwa munthu wowauzira amene ali kwinakwake; tizipangizo tinatake totumizira uthenga kwa anthu amene akhala chapafupi; ngakhalenso makompyuta olumikizidwa pa Intaneti amene amatha kukhala ndi mayankho a mayeso onse omaliza!

Akuluakulu a zamaphunziro akuyesetsa kuthetsa khalidwe losautsa loonerali, koma zikuwavuta. China n’chifukwa chakuti, ana ena asukulu ngakhalenso aphunzitsi ena savomerezana chimodzi pankhani ya kuonera. Mwachitsanzo, ana akapatsidwa mayeso ochitira m’magulu, m’povuta kusiyanitsa bwino kukambirana mwachilungamo ndi kubera nzeru za ena. Ndiye palinso ana ena amene amangopezerapo mwayi woti poti n’zapagulu, anzawo ndiwo aziganiza zonse zofunika kuchita. Yuji, amene akuphunzira pa koleji inayake, ananena modandaula kuti: “Ana ena ngaulesi kwambiri, moti palibe chimene amachitapo! Koma mayeso akatuluka, upeza kuti nawonso akhoza bwino. Kwa ineyo, kumenekonso n’kubera!”

N’chifukwa Chiyani Amaonera?

Atafufuza nthaŵi ina, anapeza kuti chifukwa chachikulu chimene chimachititsa ana kuonera n’kusakonzekera. Ena amaona kuti sangachitire mwina, chifukwa chopikisana ndi ena kusukulu kapena chifukwa chakuti makolo awo amavuta akapanda kukhoza bwino kwambiri. Sam, amene ali ndi zaka 13 anati: “Makolo anga amangofuna kuti nthaŵi zonse ndizikhoza bwino basi. Amakonda kundifunsa kuti: ‘Masamu unakhoza bwanji? Nanga Chingelezi bwanji?’ Zimenezi ndimadana nazo kwambiri!”

Kwa ana ena kufunitsitsa kukhoza bwino poopa kusoŵetsedwa mtendere ndi anthu enaake, n’kumene kumawachititsa kuonera. Buku linalake la za achinyamata lotchedwa The Private Life of the American Teenager linati: “Zinthu zimalakwika anthu akasandutsa maphunziro chinthu chosoŵetsa mtendere komanso chosasangalatsa chifukwa chongofuna kukhoza bwino basi.” Ana ambiri amavomereza zimenezi. Chifukwatu palibe munthu amene amafuna kulakwa mayeso, makamaka akakhala otsiriza. Mnyamata wina wa kusekondale, dzina lake Jimmy, anati: “Anthu ena kulakwa kumawachititsa mantha kwambiri. Ngakhale mayesowo atawaphwekera, amaonerabe kuti angokhala otsimikiza.”

Poti anthu ololera kuchita zachinyengo pa mayeso alipo ambiri, khalidweli lingamaoneke ngati labwino. Ndipo nthaŵi zina lingamaoneke ngati njira yabwino kwambiri yom’thandiza munthu. Greg, yemwe ali ndi zaka 17, anati: “Dzulo ndinaona mwana wina akuonera tikulemba mayeso. Lero talandira zotsatira za mayesowo ndipo iyeyo wandiposa.” Ambiri amangotengeka ndi anzawo. Yuji anati: “Ana ena amaganiza kuti ‘ngati ena akuonera, ineyo n’lekerenji?” Koma kodi zimenezi n’nzerudi?

N’chizoloŵezi Choipa

Tatiyeni tiyerekezere khalidwe la kuonera ndi la kuba. Kodi poti anthu ambiri amaba ndiye kuti kuba sikulakwa? Mwina mungayankhe kuti, ‘Ayi, kuba n’kulakwa basi,’ ndipo mungachite kunena motsindika ngati mwaberedwa ndalama zanu! Tikamaonera timatenga nzeru zamwini ngati kuti n’zathu, mwinanso timadyera masuku pamutu anzathu amene akuchita zinthu moona mtimawo. (Aefeso 4:28) Tommy amene wamaliza maphunziro ake a kusekondale posachedwapa anati: “Kuonera n’kulakwa kwabasi. Chifukwa umakhala ukunama kuti ukudziŵa, pamene palibe chimene ukudziŵa. Motero limenelo ndi bodza.” Lemba la Akolose 3:9 limasonyeza bwino mmene Baibulo limaonera nkhaniyi. Lembali limati: “Musamanamizana wina ndi mnzake.”

Kuonera kumatha kuzoloŵereka kwambiri moti munthu angavutike kuti asiye kutero. Jenna anati: “Anthu oonera amazoloŵera kukhoza mayeso popanda kukonzekera. Ndiye amangodalira kuonerako basi. Moti kenaka kuchita zinthu bwinobwino paokha kumadzawavuta kwambiri.”

Mfundo imene ili pa Agalatiya 6:7 njolasa mtima kwambiri. Lembali limati: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” Mapeto a kuonera m’kalasi ngakuti chikumbumtima chingathe kumakupwetekani, anzanu sakudalirani, ndipo mumadzibwezera m’mbuyo chifukwa chozemba kuphunzira. Chinyengo chotere chili ngati matenda a kansa chifukwa chingathe kukhudzanso zochita zanu zina ndipo chingachititse kuti anzanu ofunika kwambiri kwa inuyo asiye kukuyanjani. N’zachidziŵikire kuti Mulungu angasiye kukuyanjani chifukwa amadana n’chinyengo.—Miyambo 11:1.

Anthu amene amadalira kuonera amangodzinamiza. (Miyambo 12:19) Zochita zawozi zimawayika m’gulu la olamulira achinyengo a mumzinda wakale wa Yerusalemu amene anati: “Tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m’zonyenga.” (Yesaya 28:15) Koma zoona n’zakuti munthu sangaonere mobisa kuti Mulungu asadziŵe.—Ahebri 4:13.

Osamaonera!

Nthaŵi zambiri achinyamata amayesetsa kuchita maluso aŵa ndi aŵa kuti aonere m’malo momalimbana n’kuŵerenga kuti akhoze mwachilungamo. Abby, yemwe ali ndi zaka 18 anati: “Akanati azilimbikira kuŵerenga monga mmene amachitira poonera, mwina bwenzi akumakhoza bwino kwambiri.”

N’zoona kuti nthaŵi zina zimavuta kudziletsa kuti musaonere. Koma ndithu, peŵani khalidwe loipali! (Miyambo 2:10-15) Nanga kodi mungalipeŵe bwanji? Choyamba, musaiwale kuti mumapita kusukulu chifukwa chofuna kukaphunzira. N’zoona kuti mwina simungaone phindu lililonse pophunzira zinthu zimene simungadzazigwiritsire ntchito n’komwe. Koma mukamazemba zinthu zotere poonera, mutu wanu sugwira zinthu mwamsanga ndiponso nzeru zimachepa. Munthu sangadziŵe zinthu popanda kuchita khama. Baibulo limati: “Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.” (Miyambo 23:23) Inde, musamachite mphwayi n’kuŵerenga ndiponso kukonzekera. Jimmy anati ndi bwino “kulimbikira kuŵerenga. Chifukwa mukatero mumadzidalira kuti mukhoza.”

N’zoona kuti nthaŵi zina mafunso ena angakuvuteni, motero mwina simungakhoze bwino. Ngakhale zitatero, kusachita zachinyengo kungakuthandizeni kuti muone zimene muyenera kuchita kuti muzikhoza bwino.—Miyambo 21:5.

Yuji, yemwe tam’tchula poyamba paja, ndi wa Mboni za Yehova. Iye analongosola zimene amachita anzake akamam’nyengerera kuti awauzire. Iye anati: “Choyamba ndimawadziŵitsa kuti ndine wa Mboni. Zimenezi zandithandiza kwambiri chifukwa iwowo amadziŵa kuti a Mboni ndi anthu oona mtima. Wina akafuna kuti ndimuuzire pa mayeso, ndimangom’kanira. Kenaka ndimadzam’longosolera chifukwa chake.”

Yuji amagwirizana ndi mawu amene mtumwi Paulo analembera Ahebri, akuti: ‘M’zonse, timafuna kukhala nawo makhalidwe abwino.’ (Ahebri 13:18) Mukakhala oona mtima zingavute bwanji ndiponso mukamadana n’zachinyengo, mukakhoza zimakhaladi zenizeni. Mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene mumakawapatsa makolo anu yochoka kusukulu kwanu ndiyo mbiri ya kukhulupirika kwanu monga Mkristu. (3 Yohane 4) Komanso simuvutika ndi chikumbumtima ndipo mumakhala wosangalala podziŵa kuti mukum’sangalatsa Yehova Mulungu.—Miyambo 27:11.

Choncho peŵani kuonera, ngakhale kutafala motani! Potero, mungamayanjane ndi ena ndiponso mungamayanjane ndi Mulungu wa choonadi Yehova, zomwe n’zofunika kwambiri.—Salmo 11:7; 31:5.

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Anthu ambiri oonera sazindikira kuti kwenikweni kumeneko n’kuba

[Mawu Otsindika patsamba 22]

Nthaŵi zambiri kuonera kumam’phunzitsa munthu kuchita zinthu zina zazikulu zachinyengo

[Mawu Otsindika patsamba 23]

Munthu sangaonere mobisa kuti Mulungu asadziŵe.

[Chithunzi patsamba 23]

Kuŵerenga mokwanira mayeso asanafike kungakulimbitseni mtima