Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pali Tchimo Limene Silingakhululukidwe?

Kodi Pali Tchimo Limene Silingakhululukidwe?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Pali Tchimo Limene Silingakhululukidwe?

KODI pali chilango china chilichonse choipa kuposa imfayi? Inde, n’chilango cha imfa yopanda chiyembekezo chodzaukitsidwa chifukwa chochita tchimo loti silingakhululukidwe. Yesu ananena kuti pali tchimo linalake lomwe ‘silingakhululukidwe.’—Mateyu 12:31.

Inde, Baibulo limanena kuti Mulungu amakhululukira. Ngakhale kuti anthu amakonda kusungirana zifukwa, n’kumakhala osakhululukirana, Mulungu ‘amakhululukira koposa.’ (Yesaya 55:7-9) Ndipotu, sizinali zamaseŵera kuti Mulungu atumize Mwana wake wokondedwa padziko lapansi kudzakhala nsembe ya chiwombolo, yamtengo wapatali kwambiri yoti ifafanize machimo.—Yohane 3:16, 17; Machitidwe 3:19; 1 Yohane 2:1, 2.

Nthaŵi yake ikadzakwana, Mulungu adzaukitsa anthu ambiri omwe anachita machimo oopsa koma amene sadzawaimbanso mlandu chifukwa cha zochita zawo zakale. (Machitidwe 24:15; Aroma 6:23) Ndipo Yesu ananena kuti, kusiyapo tchimo lomwe silingakhululukidwelo, “machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa.” (Mateyu 12:31) Ndiye mungafunse kuti, ‘Kodi ndi tchimo loopsa motani limene Mulungu sangakhululukire?’

Kufika Poti Munthu Sangalapenso

Chenjezo la Yesu ndi lonena za ‘kuchitira mwano Mzimu Woyera’ mwadala. Tchimo la mtunduwu n’loti silingakhululukidwe n’komwe, kaya “nthaŵi ino kapena ilinkudzayo,” anatero Yesu. (Mateyu 12:31, 32) Anthu omwe anachita machimo otereŵa sadzaukitsidwa.

Kodi kuchitira mwano mzimu n’kutani? Ndi kuchita mwadala zinthu zoipa mtima. Tchimoli limaipiraipira munthu akamatsutsana ndi mzimu woyera wa Mulungu mochita kuchalira. Mwachitsanzo, malamulo a m’mayiko ena amati pali mitundu iŵiri ya milandu yopha munthu malinga ndi mmene munthuyo waphedwera, motero munthu yekhayo amene wapha mnzake mochita kuchalira ndiye ayenera kuphedwa.

Poyamba mtumwi Paulo anali munthu wamwano, koma kenaka iye anati: “Anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira.” (1 Timoteo 1:13) Kuchimwira mzimu woyera ndiko kutsutsana nawo mwadala. Ndiye kuti munthuyo wafika poti sangasinthenso.

Zikuoneka kuti Paulo ankatchula za tchimo la mtunduwu pamene analemba kuti: “Sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthaŵi yake, nalaŵa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera, nalaŵa mawu okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthaŵi ilinkudza, koma anagwa m’chisokero.” (Ahebri 6:4-6) Mtumwiyu ananenanso kuti: “Tikachimwa ife eni ake [mwadala], titatha kulandira chidziŵitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo.”—Ahebri 10:26.

Khalidwe la atsogoleri ena a chipembedzo a m’nthaŵi yake ndi lomwe linachititsa Yesu kuchenjeza za tchimo limene silingakhululukidwe. Koma atsogoleriwo sanamumvere, m’malomwake anakonza zoti aphedwe. Kenako anamva nkhani yoti sakanaitsutsa ngakhale pang’ono yakuti mzimu woyera wachita zozizwitsa. Anauzidwa kuti Yesu waukitsidwa kwa akufa! Zinali zodziŵikiratu kuti Yesu analidi Kristu! Komabe, iwo anaulakwira kwambiri mzimu woyera powagula ankhondo achiroma kuti azinama za kuuka kwa Yesu.—Mateyu 28:11-15.

Chenjezo kwa Akristu Oona

N’chifukwa chiyani Akristu oona amamvera chenjezo lonena za tchimo limene silingakhululukidwe? N’chifukwa chakuti n’zotheka kukhala ndi mtima woipa ngakhale titam’dziŵa Mulungu molondola ndiponso zinthu zomwe mzimu woyera umachita. (Ahebri 3:12) Tisamale kuti tisamalingalire kuti zimenezi sizingatichitikire. Taganizirani za Yudasi Isikariote. Panthaŵi inayake iye anali wotsatira wa Yesu wokhulupirika. Anasankhidwa kukhala nawo m’gulu la atumwi khumi ndi aŵiri, motero ayenera kuti anali wamakhalidwe abwino. Koma penapake anayamba kuganiza zoipa ndipo kenako zimenezi zinazika mizu. Ankadzionera yekha zozizwitsa zikuluzikulu zomwe Yesu ankachita koma panthaŵi yomweyo ankabanso ndalama. Kenako, pofuna ndalama, anapereka mwadala Mwana wa Mulungu.

Anthu ena amene m’mbuyomu anali Akristu okhulupirika achoka dala m’manja mwa Mulungu, mwina chifukwa cha kudzimbuka, kunyada, kapena dyera, ndipo tsopano ndi anthu ampatuko olimbana ndi mzimu wa Mulungu. Mwadala, iwo amalimbana ndi zinthu zimene zili zoonekeratu kuti zikuchitika ndi mzimu. Kodi tingati anthu ameneŵa achita tchimo limene silingakhululukidwe? Yehova ndiye adzaweruze zonse.—Aroma 14:12.

M’malo molimbana ndi kuweruza ena, ndi bwino kuti tisamale ndi machimo am’tseri omwe angaumitse mitima yathu pang’ono ndi pang’ono. (Aefeso 4:30) Ndipo mtima wathu umakhala m’malo podziŵa kuti tikalapa, Yehova angatikhululukire ndithu, ngakhale titachimwa kwambiri.—Yesaya 1:18, 19.

[Chithunzi pamasamba 18, 19]

Afarisi ena anachita tchimo limene silingakhululukidwe