Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzigona Mokwanira!

Muzigona Mokwanira!

Muzigona Mokwanira!

Kodi ndani angatsutse kuti kugona tulo tabwino n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi thanzi labwino? Mwina palibe angatero. Komabe anthu ambiri amaona kuti kugona kulibe ntchito kwenikweni. “Komatu mumadzavutika maŵa lake” mukapanda kugona bwino, anatero Shawn Currie, dokotala wa matenda okhudza maganizo ndiponso pulofesa wothandizira ku yunivesite ya Calgary, m’dziko la Canada. Kunja sikukucherani bwino ayi.

“Asayansi amati kugona kumapumitsa ubongo, ndiponso kuti munthu amapitirizabe kuphunzira akakhala mtulo,” inatero nyuzipepala ya Calgary Herald. Pulofesa Currie anati: “Usiku m’pamene mumatsendera zinthu zonse zimene zili m’maganizo mwanu ndipo chilichonse chimene mwaphunzira masana chimakhazikika m’mutu mwanu usikuwo. Patapanda nthaŵi yopuma imeneyi simungamaphunzire zinthu bwinobwino.” Komanso anati, “n’kutheka kuti kugona mokwanira kumathandiza kuti maganizo anu azikhazikika.”

Ndiyeno, kodi munthu ayenera kugona nthaŵi yaitali motani? Akatswiri ambiri amanena kuti ndi bwino kumagona maola 8, koma pulofesa Currie anati: “Anthu sagona mofanana.” Motero, iye anati anthu azionetsetsa kuti akugona tulo tofa nato. Koma kodi munthu angakwanitse bwanji zimenezi, makamaka ngati ali ndi vuto losoŵa tulo? Naŵa malangizo ena:

▪ Sambani madzi ofunda bwino musanakagone.

▪ Muzichitako maseŵera olimbitsa thupi kangapo pamlungu; koma osachita kudzitopetsa kwambiri mukatsala pang’ono kukagona.

▪ M’chipinda mwanu muzikhala mopanda phokoso, mwamdima, komanso mozizirirako.

▪ Yesetsani kumadzuka nthaŵi yomweyo m’maŵa uliwonse kuti muzoloŵeze thupi lanu.

Dziganizireni ndipo samalirani kwambiri nkhani ya kugona chifukwa n’zoonekeratu kuti mukamagona bwino mumakhala wathanzi.