“Nkhanza Zosaneneka”
“Nkhanza Zosaneneka”
MARIA * anayamba uhule ali ndi zaka 14. Amayi ake enieni ndiwo anamuumiriza kuyamba khalidwe loipali pomuuza kuti ndi wokongola ndiponso kuti amuna angamukonde kwambiri. Komanso ankamuuza kuti angathe kumapeza ndalama zambiri. Madzulo aliwonse amayi ake ankapita naye kunyumba ina yogona anthu apaulendo komwe ankakakumana ndi amuna, ndipo iwowo ankadikirira chapafupi kuti alandire malipiro ake. Usiku uliwonse, Maria ankagona ndi amuna atatu kapena anayi.
Kufupi ndi kunyumba kwa Maria, mtsikana winanso wa zaka 13, dzina lake Carina, anakakamizidwa kuyamba uhule. Mofanana ndi mabanja ambiri a m’dera lawolo ogwira ntchito m’minda ya nzimbe, makolo a Carina anakonza zoti iye akhale hule pofuna kuti azipeza ndalama zochulukirapo. M’dera linanso, Estela anasiyira sukulu panjira ali mwana kwambiri, asanadziŵe n’komwe kuŵerenga ndi kulemba, n’kuyamba kuyendayenda m’misewu kudikirira amuna. Ndipo Daisy nayenso anali ndi zaka pafupifupi zisanu ndi chimodzi pamene anagwiriridwa ndi mchimwene wake, ndipo ichi chinali chiyambi chabe chochitidwa chipongwe chotere ndi anthu. Ndiyeno anadzakhala hule atakwanitsa zaka 14.
M’madera ambiri padziko lonse, vuto la uhule wa ana likudetsa nkhaŵa kwambiri. Ndipo vutoli likubweretsa zinthu zomvetsa chisoni kwambiri. Nthaŵi zambiri, ana ochita uhule, kaya mwa apo ndi apo kapena mwa nthaŵi zonse, amachitanso zosokoneza ndiponso amagwiritsira ntchito mankhwala ozunguza bongo. Chifukwa choona kuti n’zovuta kapenanso kuti n’zosatheka n’komwe kusiyana nawo moyo woterewu, ambiri amasoŵa mtendere ndiponso amangodziona ngati achabechabe.
Anthu otchuka akudziŵa bwino kuti uhule wa ana ngoipa. Mtsogoleri wakale wa dziko la Brazil, Fernando Henrique Cardoso anati: “Kupangitsa ana uhule ndi nkhanza zosaneneka.” Ponena za uhule wa ana, nyuzipepala ina ya ku Brazil komweko inalemba ndemanga yolasa mtima iyi: “M’mayiko momwe khalidweli n’lofala, n’lovomerezeka, ndiponso lokondedwa chifukwa cha [ndalama] zomwe limabweretsa, anthu amavutika kwambiri tsiku ndi tsiku chifukwa cha mavuto omwe limabweretsa. Phindu lililonse lomwe khalidweli lingabweretse limangothera pa mavuto a munthu wochita uhuleyo, a banja lake, komanso mavuto ena omwe amadza chifukwa cha khalidweli.”
Komabe, vutoli likukula ngakhale kuti anthu omwe akulimbana ndi uhule wa ana sakugona tulo pofuna kuti authetse. Kodi n’chiyani chimapangitsa munthu kuyamba moyo womvetsa chisoniwu? N’chifukwa chiyani anthu ambiri amalola m’chitidwe woipawu kapena mwinanso kuulimbikitsa kumene?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Mayina a m’nkhani zino tawasintha.
[Mawu Otsindika patsamba 3]
“Kupangitsa ana uhule ndi nkhanza zosaneneka.”—ANATERO MTSOGOLERI WAKALE WA DZIKO LA BRAZIL, FERNANDO HENRIQUE CARDOSO
[Mawu Otsindika patsamba 4]
“Zilibe kanthu kuti munthu ndi wa msinkhu wotani, kaya ndi mwamuna kapena mkazi, kaya ndi wa mtundu kapena fuko lotani, kapenanso kuti ndi munthu wotani kwawo, koma kum’tenga ngati hule m’njira ina iliyonse n’kumuchotsera ulemu wake, ndipo kutero n’kumuphwanyira ufulu.”—INATERO MAGAZINI YA UNESCO SOURCES