Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Osamangokhulupirira za M’maluŵa

Osamangokhulupirira za M’maluŵa

Osamangokhulupirira za M’maluŵa

Kudziŵa zenizeni pa nkhani zosiyanasiyana n’kovuta kwambiri. Maboma ndiponso makampani akamanena zinthu amaphatikizamo timabodza. Nthaŵi zambiri, ofalitsa nkhani amalonjeza kuti azilemba nkhani zawo mosakondera koma satero. Nthaŵi zina madokotala safotokoza mavuto onse omwe angabuke chifukwa cha mankhwala omwe atipatsa. Kodi pali njira ina iliyonse yodziŵira zinthu zoti n’kuzikhulupirira?

Anthu ambiri anatama kubwera kwa Intaneti n’kumanena kuti ndiyo njira yodalirika yodziŵira zinthu zimene zikuchitika padziko lonse. Inde, zimenezi zingatheke ngati mukudziŵa mmene mungapezere zinthuzo pofufuza pa kompyuta. Nkhani ya mkonzi m’nyuzipepala ya The New York Times, inati: “Ubwino wa Intaneti ndi woti ingaphunzitse anthu ambiri mwamsanga kusiyana ndi njira ina iliyonse yofalitsira nkhani. Ndipo kuipa kwake n’koti ingapinimbitse bongo wa anthu mwamsanga kusiyana ndi njira ina iliyonse yofalitsira nkhani.”

Nkhani ya mkonziyo inanenanso kuti: “Popeza kuti Intaneti ndi yochititsa kaso, anthu osaidziŵa bwino amaikhulupirira kwambiri. Sadziŵa kuti kuipa kwake n’kofanana ndi dzenje la nyansi chifukwa pa Intaneti pamapezeka nkhani zilizonse n’zopanda umboni zomwe.” N’zomvetsa chisoni kuti monga momwe mkonzi wa nkhaniyi analembera, palibe njira iliyonse yochotserapo nkhani zachabechabezo.

Wina aliyense angalembe nkhani iliyonse m’magazini, kapenanso m’buku lopezeka pa Intaneti. Motero tizisamala ndiponso tiphunzire kuti tikamaŵerenga zinthu tisamangokhulupirira zilizonse, ndi za m’maluŵa zomwe. Aliyense amene amafuna kudziŵa zenizeni pa nkhani inayake ayenera kuonetsetsa kuti komwe kwachokera nkhaniyo n’kodalirika. Izi zingatenge nthaŵi ndithu. Koma tikatero ndiponso tikadziŵa zenizeni za nkhaniyo, maganizo athu sangakhale opotoka ndiponso sitingamakayikire pochita zinthu.