Ubwino wa Kumwetulira
Ubwino wa Kumwetulira
NGAKHALE kuti chinthu chimenechi chimachitika kwa nthaŵi yochepa, munthu angathe kuchikumbukira moyo wake wonse. N’chinthu chamtengo wapatali kwambiri, koma palibe munthu amene ali wosauka kwambiri moti sangachikwanitse kapena amene ali wolemera kwambiri moti sachifuna. Kodi tikunena za chiyani? Tikunena za kumwetulira.
Kuti munthu amwetulire chimachitika n’chakuti milomo imakokeka n’kumanyevukira m’mwamba ndipo zimenezi zimakhudzanso maso ake. Munthuyo amatero akasangalala ndi chinachake. Khanda limayamba kumwetulira pakatha milungu ingapo litabadwa, ndipotu zimenezi makolo ake amasangalala nazo. Uku sikukhala kumwetulira kochita kufuna. Akatswiri amanena kuti kumwetulira kotere kumakonda kuchitika khanda likamalota ndipo mwina n’chifukwa cha zimene zimachitika m’maganizo ndiponso mu ubongo wake. Ndipo ngakhale tikakula, timathabe kumwetulira motere tikamaphwetsa mkhuto kapena tikamamvetsera nyimbo.
Komano kamwana kakatha mwezi umodzi ndi theka, kamamwetulira chifukwa choti kaona munthu kapena kamva mawu enaake. Inde, ana ndi akulu omwe amamva bwino akamamwetulirana mochita kufuna. Akuti kumwetulira kotere kumathandiza kuti tikhale athanzi. Mirtha Manno ndi Rubén Delauro, madokotala othandiza anthu ovutika kuyankhula, amenenso ali ndi chipatala chophunzitsirapo anthu za phindu la kumwetulira chotchedwa Smiling and Health, anati kumwetulira pakokha kumachititsa thupi kutulutsa madzi enaake opita ku ubongo ndipo zikatere ifeyo timamva bwino.
Kumwetulira n’kofunikanso chifukwa ena amapindulanso nako. Tikamwetulira mochokadi pansi pamtima, kaya pokumana ndi munthu, posonyeza kumvera mnzathu chifundo, kapenanso polimbikitsa ena, anthu amatha kuona mmene tikumvera ngakhale titapanda kunena chilichonse. Nthaŵi zina, kungoona chithunzi cha mwana akumwetulira mochititsa kaso kungachititse kuti ifenso timwetulire.
Tingathe kukhala omasuka, mtima wathu ungazizire komanso tingapirire zovuta zinazake munthu winawake akangotiyang’ana n’kumamwetulira. Baibulo limati: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.” (Miyambo 3:27) Inde, kumwetulira komweku, tingapindule nako ndiponso tingapindulitse nako ena. Bwanji osayesetsa kugwiritsira ntchito bwino mphatso yamtengo wapatali kwambiri imeneyi ya kumwetulira mochoka pansi pamtima?