Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Vutoli Litha Posachedwapa!

Vutoli Litha Posachedwapa!

Vutoli Litha Posachedwapa!

MAWU oyamba a m’Pangano la Ufulu Wachibadwidwe wa Mwana amati: “M’chikalata cha mfundo za ufulu wachibadwidwe, bungwe la United Nations linanena kuti mwana amafunika kusamalidwa ndiponso kuthandizidwa bwino.” Ponenapo za kufunika kwa banja, panganolo linapitiriza kuti: “Kuti mwana akule bwino, amafunika kukulira m’banja momwe muli mtendere, chikondi ndi kumvetsetsana.” Komatu, zimenezi sizikuchitika n’komwe.

Kungoyankhula chabe zakuti ana azikhala bwino sikokwanira. Anthu ambiri alibe khalidwe, ndipo amaona kuti ndi momwe ziyenera kukhalira. Malamulo osiyasiyana sangachepetse makhalidwe oipa ndiponso umbombo omwe wafala kwambiri. Nawonso makolo, m’malo moti azikonda ndi kuteteza ana awo, nthaŵi zambiri amawalimbikitsa kuchita makhalidwe oipaŵa. Ndiyeno, kodi pali chiyembekezo chilichonse choti uhule wa ana udzatha?

Ngakhale kuti dziko loipali lalephera kuonetsetsa kuti ana onse akukondedwa m’nyumba zawo ndiponso ali ndi tsogolo labwino, Mlengi wathu posachedwapa adzathetseratu kuipa kulikonse ndiponso zachiwerewere zonse, kuphatikizapo uhule wa ana. Posachedwapa, Yehova Mulungu adzaloŵerera pa zochita za anthu pogwiritsira ntchito Ufumu wake, anthu a m’dzikoli asakuyembekezera. Anthu omwe akuipitsa makhalidwe ndiponso odyera anzawo masuku pamutu sadzasiyidwa pa chiweruzo cha Mulungu. Anthu okhawo omwe amakonda anzawo ndiwo adzapulumuke n’kukhala m’dziko latsopano la Mulungu. “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:21, 22.

Ana ndi akulu omwe azidzakhala popanda khalidwe loipa ndiponso logwirira ena. Koma ndiye zinthu zidzakhala zosangalatsa bwanji! Sipadzakhalanso kuvutika kulikonse chifukwa cha kudyeredwa masuku pamutu ndiponso chiwawa. Anthu omwe anachitidwapo chipongwe adzatha kukhala bwinobwino osavutikanso ndi maganizo. “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.”—Yesaya 65:17.

Nthaŵi imeneyo, sipadzakhalanso ana ozunzidwa kapena kugwiriridwa. Chimwemwe, chikondi, ndiponso kumvetsetsana sizidzakhalanso nkhambakamwa chabe. Yesaya 11:9 amanena kuti anthu odzakhala m’dziko latsopano la Mulungu, ‘sadzaipitsa, sadzasakaza.’

Inde, zidzakhala zosangalatsa kwambiri umphaŵi, mankhwala ozunguza bongo, mabanja osoŵa mtendere, ndiponso kuipa kwa makhalidwe kukadzatha! Padzakhala mtendere, chilungamo, ndiponso chitetezo. “Anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.”—Yesaya 32:18.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]

Chisamaliro cha Makolo Chingapangitse Kuti Ana Asaloŵerere

● “Makolo anga ankandilimbikitsa kuti ndisamachite zibwana kusukulu ndiponso kuti ndiphunzire ntchito inayake. Sankandikakamiza kutsatira zofuna zawo, koma anandithandiza kusankha sukulu zophunzitsa ntchito zomwe zingandithandizedi.”​—⁠Anatero Tais.

● “Ine ndi mng’ono wanga tikamapita kokagula zinthu zathu, mayinso ankapita nawo. Ankatithandiza kuti tisawononge ndalama, komanso kuti tisagule zovala zocheukitsa anthu kapena zosambula.”​—⁠Anatero Bianca.

● “Nthaŵi zonse tikakhala ndi phwando, makolo anga ankandifunsa za anthu omwe akakhalepo, nyimbo za paphwandopo, komanso nthaŵi yomwe phwandolo likayambire ndiponso kutha. Kumapwando ambiri tinkapita tonse m’banja mwathu.”​—⁠Anatero Priscila.

● “Ndili wamng’ono komanso nditasinkhukirapo, ine ndi makolo anga tinkayankhulana momasuka kwambiri. Mtsikana wina amene ndinkaphunzira naye sukulu imodzi ankadziŵa zimenezi ndipo anati: ‘Ndimasirira kwambiri chifukwa umayankhulana ndi makolo ako momasuka pa nkhani iliyonse. Ineyo ndimavutika kuti ndiyankhule ndi mayi anga enieniŵa ndipo nthaŵi zambiri ndikafuna kudziŵa chinachake ndimachita kufunsa kwa anthu ena.’ ”​—⁠Anatero Samara.

● “Ndidakali kamtsikana ndinali munthu womasuka kwambiri ndi anthu. Sindinkaganizako zoti munthu aliyense angandichite chipongwe ndipo ndinkangosekerera zilizonse. Ndinkamasuka tikamacheza ndi azinzanga ndiponso tinkakambirana nkhani zambiri zoseketsa. Makolo anga ankadziŵa kuti ndi mmene ndilili, ndipo sanayese kundipangitsa kuti ndisinthe khalidwe langali. Koma anandithandiza bwinobwino kumvetsa kuti ndiyenera kuopa amuna.”​—⁠Anatero Tais.

● “Monga momwe zimakhalira ndi atsikana ambiri, ndinayamba kuganizira za amuna. Bambo anga anandiuza kuti ndisaganizire za amuna pokhapokha n’takwanitsa zaka mwakutimwakuti. Zimenezi sizinandikhumudwitse, koma ndinadziŵa kuti makolo anga akundifunira zabwino ndipo akufuna kuti ndisadzavutike m’tsogolo.”​—⁠Anatero Bianca.

● “Ndinkaona kuti ukwati ndi wabwino kwambiri, makamaka chifukwa cha chitsanzo cha makolo anga. Nthaŵi zonse ankagwirizana ndiponso ankayankhulana momasuka. Ndikukumbukira kuti ndili pachibwenzi, amayi ankandilangiza zimene ndingamachite pakachitika zinazake, n’kundifotokozera momwe zimenezo zidzathandizire mu ukwati wanga.”​—⁠Anatero Priscila.

[Chithunzi patsamba 10]

M’dziko latsopano la Mulungu, palibe mwana amene adzazunzidwe