Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Galamukani! Inapulumutsa Moyo Wanga!”

“Galamukani! Inapulumutsa Moyo Wanga!”

“Galamukani! Inapulumutsa Moyo Wanga!”

Ofalitsa Galamukani! analandira kalata yoyamikira kuchokera ku Italy. Mbali ina ya kalatayo inati:

“Ndaŵerenga Galamukani! kwa zaka 40, ndipo ndimachita chidwi ndi mmene imafotokozera nkhani zosiyanasiyana zothandiza kwambiri. Tsiku lina posachedwa pompa, ndinali kuntchito ndipo m’mimba ndi m’chifuwa munayamba kundipweteka kwambiri. Ndinaganiza zopita ku nyumba, koma kupwetekako kutayambiranso, ndinakumbukira zinazake. Ndinakumbukira kuti nkhani ina mu Galamukani! inafotokoza zizindikiro za matenda a mtima. * Choncho, ndinapita kuchipatala. Ndili m’chipinda choyembekezera, mutu wanga unangoti pendekeku kumbali imodzi ndipo ndinakomoka. Ndinauzidwa zimenezi maŵa lake ndili m’chipinda cha odwala mwakayakaya.

“Ndili moyo lero chifukwa adokotala odziŵa bwino ntchito yawo anafulumira kundithandiza. Koma ndithokozenso magazini yanu, imene inandipatsa nzeru zoti ndipite ku chipatala. Galamukani! inapulumutsa moyo wanga!”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani Galamukani! yachingelezi ya December 8, 1996, tsamba 6.