Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndizionera Matepi a Nyimbo?

Kodi Ndizionera Matepi a Nyimbo?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndizionera Matepi a Nyimbo?

“Matepi a vidiyo a nyimbo ndi osangalatsa. Ena amakhala ngati timafilimu. Amafotokoza nkhani, ndipo ndimakonda mmene amavinira mwaluso.”—Anatero Casey.

“Ndi njira ina yabwino yodziŵira nyimbo zatsopano. Amaonetsa nyimbo zina zimene sizituluka pa gulu la nyimbo 40 zotchuka. Komanso matepi avidiyo a nyimbo angakuthandize kuti usamasoŵe nkhani pamene ukucheza ndi ena.”—Anatero Josh.

“Zimene zimapezeka m’matepiŵa n’zofunika kwa ine chifukwa ndimaona munthu amene akuimba, zimene wavala, ndi mmene akuvinira. Zonsezi zimandithandiza kumvetsa tanthauzo la mawu a nyimboyo.”—Anatero Kimberly.

“Ndimakonda kuona zimene gulu loimba limene ndimalikonda likuchita. Ndimakondanso kuona mmene zithunzi zikuonekera. Ndipo matepi ena ndi oseketsa. Koma pamafunika kusamala.”—Anatero Sam.

MWINA inunso mumakonda kuonera matepi a nyimbo. Pamene ankayamba kuwaonetsa pa TV, anali otsika mtengo. Koma ataona kuti anthu ayamba kuwakonda ndiponso kuti angapititse patsogolo malonda a nyimbo, anayamba kupanga matepi avidiyo a nyimbo otsogola kwambiri makamaka pa luso lake ndi kapangidwe kake. Masiku ano, ndi amene akutchukitsa oimba ndipo achinyamata amawakonda kwambiri. Mmayiko ena muli matchanelo a TV amene amangoonetsa matepi a nyimbo okhaokha basi.

Koma n’chifukwa chiyani achinyamata ngati Sam, amene ananena mawu amene ali pamwambawo, akunena kuti m’pofunika kusamala? Kodi matepi avidiyo a nyimbo angakusokonezeni maganizo ndi khalidwe lanu komanso kuwononga ubwenzi wanu ndi Mlengi wanu? Mwina funso ngati limeneli n’lodabwitsa. Koma taganizirani izi, Kodi mukanakhala kuti mukupita kokasambira ku nyanja ndiye mwaona chikwangwani chosonyeza kuti malo amene mukufuna kusambirawo ndi oopsa, kodi kungakhale kwanzeru kunyalanyaza chenjezolo? Simungayerekeze dala! Choncho mungachitenso bwino kuona zina mwa ngozi zokhudza matepi avidiyo a nyimbo.

Ndi Oopsa

Muyenera kuvomereza kuti zimene mumaonera ndi kumva zimakukhudzani! Baibulo limatiuza kuti mfumu yoyamba ya Israyeli, Sauli, inagwiritsa ntchito nyimbo kuti zimukhazike mtima pansi. (1 Samueli 16:14-23) Kodi nyimbo zingakhalenso zoipa? Buku lakuti Rock and Roll—Its History and Stylistic Development limati: “Sizingatheke kuzionera popanda kusokonezeka nazo. Ngati tikuvomereza kuti nyimbo za rock zathandiza anthu (monga zachitiramu), tiyeneranso kuvomereza kuti zasokoneza anthu (monga zachitiramu). Munthu amene anganene modzitama kuti, ‘Aa, ine ndimamvetsera nyimbo koma sizindikhudza’ ndi chidzete kapena mbuli.”

Mobwerezabwereza Baibulo limafotokoza mmene zinthu zimene timaona zimakhudzira maganizo anthu komanso mmene timamvera. (Miyambo 27:20; 1 Yohane 2:16) Choncho, mwa kuwonjezerapo zithunzi pa mawu a nyimbo, opanga mavidiyo amawonjezeranso mphamvu ya nyimbozi pa omvetsera. Kodi ndi zithunzi zotani zimene amagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri?

Kafukufuku wina anati pafupifupi 57 peresenti ya matepi avidiyo a nyimbo za rock amakhala ndi zachiwawa. Pafupifupi 76 peresenti ya matepiwa amaonetsa zachiwerewere. Pakafukufuku wina anapeza kuti 75 peresenti ya matepi ofotokoza nkhani amakhalanso ndi zachiwerewere, ndipo opitirira theka amakhala ndi zachiwawa, makamaka chokhudza azimayi. Kodi kuonera matepi amenewo kungakuonongeni? Magazini ina inati “pakafukufuku wosiyanasiyana anapeza kuti kuonera matepi a nyimbo kumachititsa achinyamata kumaganiza ndi kuchita zachiwerewere ali ang’ono.” Ndipo sitingatsutse kuti pamene oimba akuyesetsa kukhala otsogola, matepi awo a nyimbo akumaonetsa zinthu zolaula kwambiri kuposa kale.

Katswiri wina wa zamaphunziro anati: “Anthu ambiri amatsutsa kuti zimene amamva ndi kuonera pa matepi avidiyo a nyimbo n’zosasiyana ndi nyimbo zakale . . . Koma zikuoneka kuti oimba amasiku ano amagwiritsa ntchito mawu otukwana ndi olaula, mopanda ndi manyazi omwe, kuti agulitse nyimbo zawo.” Pokambapo za amene amaonera matepi a nyimbo pa tchanelo china, magazini ya Chicago inati: “Amakhalira kuonera zachiwerewere ndi zolaula zambirimbiri.”

Magazini ya Chicago yomweyi inafotokozanso za tepi ina ya nyimbo imene imaonetsa “mnyamata wina atakhala pa mpando kukauntala mu resitilanti. Kenako akupendeketsa mutu wake chakumbuyo. Mwadzidzidzi akutemedwa pakhosi ndipo pakutuluka magazi ambiri, mutu wake n’kugwera pansi.” Tepi ina yoopsa inasonyeza mwamuna akuvula zovala zake zonse n’kukhala mbulanda kuti asangalatse anthu ndipo kenako anadzisenda khungu ndi kuzomola mnofu wake, n’kusiya magazi ali chuchuchu. Ndipo anaonetsanso zinthu zina zoumitsa thupi zoti sitingazitchule pano.

Koma ena angatsutse zimenezi, ponena kuti matepi amene atchulidwa panoŵa ndi okokomeza ndiponso kuti ambiri si oipa chotero. Ndipo ena anganene kuti iwowo saona kuti matepi avidiyo a nyimbo ndi oumitsa thupi kwenikweni kapena olakwika. Koma kodi zimenezi sizikungosonyeza kuti anthu ameneŵa mitima yawo yauma chifukwa choonera matepiŵa kwa nthaŵi yaitali? Casey, wachinyamata amene ananena mawu amene ali koyambirira kwa nkhani ino, anavomereza kuti: “Ngati suika malire pa zimene umaonera, zinthu zimene kale zimaoneka ngati zolaula zimayamba kuoneka ngati zabwinobwino. Ndiye iweyo mosazindikira, umayamba kuonera zolaula kwambiri kuposa zoyamba zija.”

Kodi chingachitike n’chiyani? Mungayambe kusokonezeka maganizo n’kumalephera kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa chakuti maganizo athu angapotozedwe mosavuta, Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira.” (Miyambo 3:21; 5:2) Chinanso chimene chingachitike n’chakuti ubwenzi wanu ndi Yehova Mulungu ukhoza kuwonongeka. Kodi pa zonse zimene muli nazo, ubwenzi umenewu sindiwo chinthu chamtengo wapatali kwambiri? Choncho, mufunika kuuteteza mwa kupeŵa zosangalatsa zosayenera. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Kudziteteza

Poyamba, muyenera kukhulupirira kuti n’kulakwa kuonera zinthu zimene zikutsutsana ndi zimene Baibulo limanena. (Salmo 11:5; Agalatiya 5:19-21; Chivumbulutso 21:8) Ngati tepi ikuonetsa zinthu zimene ‘n’zosayenera oyera mtima,’ muzisiya kuionera. (Aefeso 5:3, 4) N’zoona kuti kungakhale kovuta kusintha tchanelo kapena kuzimitsa TV pamene akuonetsa tepi yosangalatsa. Koma mufunika kupemphera monga mmene anachitira wamasalmo amene analemba kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe.”—Salmo 119:37.

N’zachidziŵikire kuti munganyansidwe ndi matepi oumitsa thupi ngati amene tatchula pamwamba aja. Komatu, matepi ena angaoneke ngati abwinobwino chifukwa cha mmene anawapangira. Angaonetse zithunzi zachiwerewere kwa kanthaŵi kochepa chabe. Mawu ndi zithunzi angaziphatikize mwaluso kwambiri kuti alimbikitse mfundo zachikunja popanda kutchuliratu kapena kuonetseratu zolakwazo. Ngati chikumbumtima chanu chikukuvutitsani, ngakhale pang’ono chabe, mukatha kuonera tepi inayake, ndiye kuti tepi imeneyo ndi yoipa komanso yosafunika kuti Mkristu aionere. Nanga mungadziŵe bwanji matepi amene muyenera kuonera ndi amene muyenera kupeŵa ngati sizikuonekeratu kuti ndi abwino kapena oipa?

Kaya muzionera kapena simuzionera matepi a nyimbo zili ndi inu komanso makolo anu, amene ali ndi udindo wokusankhirani zimene mungaonere ndi zimene simungaonere. (Aefeso 6:1, 2) Koma ngati makolo anu amakulolani kuonera matepi a nyimbo, musamangoonera zilizonse zimene inuyo mukuona ngati n’zoyenera. Lemba la Ahebri 5:14 limatilimbikitsa kuti ‘tizoloweretse zizindikiritso zathu kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ Timakhala anthu ozindikira mwa kuphunzira mfundo za m’Baibulo, ndipo timatha kusiyanitsa chabwino ndi choipa mogwirizana ndi mmene Yehova amaonera. Mwa kusinkhasinkha pa mfundo za m’Baibulo zimenezi, mudzazindikira zimene zingawononge moyo wanu wauzimu ngakhale patakhala kuti palibe lamulo la m’Baibulo loti likutsogolereni.

Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti kwenikweni zimene zingakuthandizeni pa nkhani imeneyi yosankha matepi a nyimbo oti muonere? Tidzakambirana zimenezi mu nkhani yotsatira.

[Mawu Otsindika patsamba 20]

“Munthu amene anganene modzitama kuti, ‘Aa, ine ndimamvetsera nyimbo koma sizindikhudza’ ndi chidzete kapena mbuli”

[Zithunzi patsamba 21]

Kodi mungaonere zosayenera popanda kusokonezeka?