Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Pagona Vutoli Mpati, Nanga Kuipa Kwake N’kotani?

Kodi Pagona Vutoli Mpati, Nanga Kuipa Kwake N’kotani?

Kodi Pagona Vutoli Mpati, Nanga Kuipa Kwake N’kotani?

“Ndinali ndi njala ndipo munakonza komiti yoti ifufuze za njala yangayo. Ndinalibe pokhala ndipo munalemba lipoti lokhudza vuto langalo. Ndinali kudwala ndipo munachititsa msonkhano woti mukambirane za mavuto a anthu osauka. Munafufuza zonse zokhudzana ndi mavuto anga, koma panopa ndikadali wanjala, wosoŵa pokhala, komanso wodwala.”—Amene analemba sakudziŵika.

NGAKHALE kuti mabungwe osiyanasiyana a padziko lonse ayesera njira zambiri zothetsera matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi, zinthu sizikuyenda monga mmene anali kuyembekezera. Mwa chitsanzo, mu 1996 a bungwe la United Nations la Food and Agriculture Organization (FAO) anachititsa msonkhano wotchedwa World Food Summit. Pamsonkhano umenewu anagwirizana zoti achepetse anthu amene akudwala matenda a kusoŵa zakudya m’thupi ndi theka chikamadzafika chaka cha 2015. Thekalo ndi anthu pafupifupi 400 miliyoni. *

Tiyenera kuyamikira kuti zinthu zina ndi zina zayenda bwino. Koma, tsoka ilo, lipoti laposachedwapa la FAO lotchedwa The State of Food Insecurity in the World 2001 linati: “Zikuoneka kuti ntchito yochepetsa anthu odwala matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi yayamba kubwerera m’mbuyo.” Choncho, zikuoneka ngati zimene anagwirizana pa msonkhano paja sizikutheka. Moti mpaka lipotilo linavomereza kuti “anthu odwala matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi awonjezereka kwambiri m’mayiko ambiri amene akutukuka kumene.”

Kodi n’chifukwa chiyani vuto limeneli likuvuta kwambiri kulithetsa? Kuti tipeze yankho, tiyambe tafotokoza kuti kodi kusoŵa zakudya m’thupi n’chiyani, ndiye kenako tione kuti kuipa kwake n’kotani, ndiponso tione pamene pagona vutoli.

Kodi Chimayambitsa Matendaŵa N’chiyani?

Matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi amayamba ngati maselo a m’thupi sakulandira zakudya zokwanira, ndipo nthaŵi zambiri amayamba pakachitika zinthu ziŵiri izi: (1) kusadya zakudya zokwanira zomanga thupi, zopatsa mphamvu, ndi zoteteza ku matenda, ndiponso (2) kudwaladwala.

Matenda ngati kutsegula m’mimba, chikuku, malungo, ndi matenda a m’chifuŵa amafooketsa thupi kwambiri ndipo amalanda thupi zakudya zofunika. Amam’pangitsa wodwalayo kuti asamamve njala komanso asamadye mokwanira, ndipo zotsatirapo zake n’zakuti amadwala matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi. Komanso, mwana amene akusoŵa zakudya m’thupi amadwaladwala. Umu ndi mmene vuto losathali limayambira, limene limachulukitsa imfa zobwera chifukwa cha matenda a kusoŵa kwa zakudya zomanga thupi ndi zopatsa mphamvu.

Kodi n’chifukwa chiyani ana ndi amene amadwala kwambiri matendaŵa? N’chifukwa chakuti ali pa msinkhu umene munthu amakula kwambiri, ndipo amafunikira zakudya zambiri zopatsa mphamvu ndi zomanga thupi. Pa zifukwa zomwezo, azimayi oyembekezera ndi oyamwitsa nawonso amadwala kwambiri matendaŵa.

Nthaŵi zambiri, vuto la mwanayo limayamba asanabadwe n’komwe. Ngati amayi akupereŵera kapena kusoŵa zakudya m’thupi asanakhale ndi pakati komanso ali oyembekezera, mwana wawo amabadwa wosakwana sikelo. Ndiyeno chifukwa chomuletsa kuyamwa mwamsanga, kusamudyetsa moyenerera, komanso uve, mwanayo angayambe kudwala matendaŵa.

Kusoŵa zakudya zofunikira m’thupi kumamulepheretsa mwanayo kukula moyenerera. Amaliralira ndiponso amadwaladwala. Matendaŵa akamakula, mwanayo amaonda kwambiri, maso ndi liwombo zimaloŵa m’kati, khungu ndi minofu zimakhwinyata, ndipo thupi lake silithanso kutentha kapena kuzizira monga mmene limafunikira.

Nthendayi imabweranso m’njira zina. Zimenezinso zimalepheretsa ana kukula bwinobwino. Mwa chitsanzo, kusadya zakudya zokwanira zokhala ndi maminiro, makamaka ayironi, ayodini, ndi zinki, komanso zakudya zokhala ndi mavitamini, makamaka vitamini A, kungayambitse matendaŵa. Bungwe la United Nations Children’s Fund (UNICEF) linanena kuti ana aang’ono pafupifupi 100 miliyoni padziko lonse lapansi amasoŵa vitamini A ndipo chifukwa cha zimenezi amachita khungu. Kusoŵa vitamini A m’thupi kumafooketsanso chitetezo cha thupi, zimene zimapangitsa kuti mwanayo azingodwaladwala.

Kuipa Kwake

Matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi amaononga zinthu zambiri m’thupi, makamaka thupi la mwana. Angasokoneze ziŵalo ndi ntchito zonse za m’thupi, kuphatikizapo mtima, impso, m’mimba, matumbo, mapapo, ndi ubongo.

Kafukufuku wasonyeza kuti ana okula monyentchera amakhala opereŵera nzeru ndipo sakhoza bwino kusukulu. Lipoti la United Nations linati ameneŵa ndi mavuto amene amabwera chifukwa cha kusoŵa kwa zakudya m’thupi ndipo amakhalapo mpaka kalekale.

Ana amene sanafe ndi matendaŵa akamakula amalimbanabe ndi mavuto ena obwera chifukwa cha matendaŵa. N’chifukwa chake bungwe la UNICEF linadandaula kuti: “Kusakaza kwambiri nzeru za anthu kotereku, chifukwa cha zinthu zimene tikanatha kupeŵa, n’kuwawanya chuma cha m’tsogolo ndiponso ndi nkhaza yosaneneka.” Chotero, mavuto obwera chifukwa cha matendaŵa amene munthu amakumana nawo akakula akudetsa nkhaŵa kwambiri. Kafukufuku wa posachedwapa wasonyeza kuti anthu amene anadwala matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi ali ana amakonda kudwala matenda oopsa ngati a mtima, a shuga, ndi othamanga magazi akakula.

Komabe, si kuti matenda odetsa nkhaŵa a kusoŵa kwa zakudya m’thupi ndi amene ali vuto lalikulu kwambiri, malingana ndi zimene a UNICEF ananena. Iwo anati: ‘Anthu ambiri amene amafa chifukwa cha matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi sikuti amafa chifukwa chakuti amasoŵa zakudya kodetsa nkhaŵa, koma chifukwa chakuti amasoŵa zakudya pang’ono.’ Ana amene akudwala pang’ono matenda a kusoŵa kwa zakudya akakula akhoza kukhala ndi mavuto aakulu a thanzi. Choncho, m’pofunika kuti muziyang’anitsitsa kwambiri kuti muone ngati ana akusoŵa zakudya m’thupi kuti alandire chithandizo choyenera.—Onani bokosi pa tsamba 7.

Pamene Pagona Vutoli

Monga tanenera poyamba paja, matendaŵa amayamba chifukwa cha kusoŵa kwa zakudya. Koma, zinthu zimene zimayambitsa matendaŵa kwambiri n’zokhudzana ndi khalidwe, chuma, miyambo ndi chilengedwe. Pa zonsezi, chachikulu kwambiri ndi umphaŵi, umene ukuvutitsa anthu mamiliyoni ambiri, makamaka m’mayiko amene akutukuka kumene. Umphaŵi umayambitsa matendaŵa, komanso umabwera chifukwa cha matendaŵa, chifukwa kusoŵa zakudya m’thupi kumalepheretsa anthu kugwira ntchito molimbika, ndipo zimenezi zimangowonjezera umphaŵiwo.

Koma palinso zina. Umbuli umachititsa anthu kumadya zakudya zosapatsa thanzi. Matenda ena, monga taona kale, nawonso amawonjezera vutoli. Zina zokhudzana ndi khalidwe komanso miyambo ya anthu, monga kugaŵa chakudya mokondera ndi kuwadyera azimayi masuku pamutu zimayambitsanso vutoli. Azimayi nthaŵi zambiri amadya “pomalizira komanso pang’ono,” kutanthauza kuti amadya azibambo akamaliza, komanso amadya zochepa poyerekezera ndi azibambo. Nthaŵi zambirinso azimayi amamanidwa mwayi wopita ku sukulu kumene akanaphunzirako njira zabwino zosamalira ana awo.

Kuwonjezera apo, zochitika zachilengedwe zimabwezera m’mbuyo ntchito yolima zakudya. Zina mwa izi ndi masoka achilengedwe ndi nkhondo. Malinga ndi lipoti la The State of Food Insecurity in the World 2001, kuyambira mu October 1999 kufika mu June 2001, m’mayiko 22 munali chilala, m’mayiko 17 munachitika mphepo yamkuntho kapena munasefukira madzi, m’mayiko 14 munali nkhondo yapachiŵeniŵeni kapena zipolowe, m’mayiko 3 munazizira koopsa, ndipo m’mayiko 2 munachitika zivomezi.

Kuchiza ndi Kupeŵa

Kodi mwana amene akudwala matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi angachiritsidwe bwanji? Ngati matendaŵa ali odetsa nkhaŵa, mwanayo angafunike kumugoneka m’chipatala kuti alandire mbali yoyamba yachithandizo. Buku limene analemba a World Health Organization kulembera madokotala limati madokotalaŵa ayenera kumuyeza bwinobwino mwanayo, ndi kumupatsa mankhwala a matenda ena alionse amene angakhale nawo, komanso ayenera kumuwonjezera madzi m’thupi ngati atha. Mwanayo angayambe kumudyetsa pang’onopang’ono, ndipo nthaŵi zambiri amadyera mu chubu. Mbali yoyamba imeneyi yothandiza mwanayo ingatenge mlungu umodzi.

Kenako mbali yachiŵiri yomuthandiza mwanayo kuti abwerere mwakale imayamba. Mwanayo amamuyambitsanso kuyamwa, ndipo amamulimbikitsa kudya kwambiri monga momwe angathere. Pa nthaŵi imeneyi mwanayo amafunika kumukonda kwambiri, komanso kukhala naye pafupi. Chisamaliro ndi chikondi zingamuthandize mwanayo kuti achire msanga. Iyi ndi nthaŵi imene mayi wa mwanayo angaphunzitsidwe mmene angasamalire mwana wakeyo pomudyetsa moyenerera ndi kumusamalira mwaukhondo, kuti asakadwalenso. Kenako, mwanayo amatuluka ku chipatalako. N’zofunika kwambiri kuti mwanayo azipita nayebe ku chipatalako nthaŵi ndi nthaŵi kuti azikamuyeza.

Komabe, chofunika kwambiri kuposa zonsezi ndi kupeŵa. Ichi n’chifukwa chake m’mayiko ambiri boma komanso mabungwe osakhala a boma ayambitsa ntchito zogaŵira anthu zakudya zowonjezera pa chakudya chawo chamasiku onse, kapena kuwonjezera mphamvu zina mu zakudya zimene anthu ambiri amadya. Anthu paokha nawonso angadzithandize kupeŵa matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi m’njira zosiyanasiyana. Mwa chitsanzo, iwo angayambitse maphunziro a kadyedwe koyenera, kusamalira pamene amatungapo madzi akumwa, kukumba zimbudzi, kusamala pakhomo, kulimbikitsa ntchito yakatemera, ndi kuthandizana kuyang’anira ana kuti azikula bwino.

Nanga kodi munthu payekha angatani kuti apeŵe matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi? Pa bokosi limene lili pa tsamba 8 pali malangizo othandiza. Kuwonjezera pa zimenezi, dokotala woona za kadyedwe ka ana Georgina Toussaint akulangiza azimayi kuti ayenera kupitanso ku chipatala pakatha masiku seveni atangobereka kumene. Azipitanso ku chipatala mwanayo akatha mwezi umodzi, komanso mwezi uliwonse kuyambira pamenepo. Mayiyo ayeneranso kuthamangira ku chipatala akaona kuti mwana wake watha madzi m’thupi, akutsegula m’mimba kwambiri, kapena akutentha thupi.

Ngakhale kuti malangizo ameneŵa angathandize kuti ana azidya moyenerera, tiyenera kuvomereza kuti vuto la kusoŵa kwa zakudya m’thupi ndi vuto lalikulu kwambiri loti anthu paokha sangalithe. Encyclopædia Britannica inanena kuti: “Kupatsa anthu chakudya chokwanira, komanso kuphunzitsa anthu onse za kadyedwe koyenera kukadali kovuta kwambiri.” Choncho, kodi tingayembekezere kuti tsiku lina “mliri wobisika” umenewu udzatha?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mumve zambiri zokhudza World Food Summit, onani Galamukani! ya August 8, 1997, masamba 12 mpaka 14.

[Bokosi patsamba 7]

KODI MWANA WANU AKUSOŴA ZAKUDYA M’THUPI?

Kodi madokotala amadziŵa bwanji ngati mwana sakudya mokwanira? Pali zizindikiro zosiyanasiyana zimene amayang’ana, ndiponso amafunsa mafunso okhudza mmene mwanayo amadyera komanso amanena kuti mwanayo akapereke zoyesa ku chipatala. Koma nthaŵi zambiri amangomupima mwanayo. Amayeza thupi lake n’kuyerekezera zimene apezazo ndi miyezo imene ali nayo. Izi zimawathandiza kudziŵa zakudya zimene mwanayo akusoŵa komanso kukula kwa matendaŵa.

Miyeso yofunika kwambiri ndiyo kulemera kwa thupi lake, kutalika kwake, ndi kunenepa kwa mkono. Akayerekezera kulemera ndi kutalika kwa mwanayo, amadziŵa kukula kwa matendaŵa. Ngati matendaŵa ali aakulu, mwanayo amakhala wonyentchera ndi woonda kwambiri. Amanena kuti matendaŵa ndi odetsa nkhaŵa ngati sikelo ya mwanayo ndi yotsika ndi 40 peresenti poyerekezera ndi sikelo yoyenerera, koma ngati ndiyotsika ndi 25 mpaka 40 peresenti, amati matendaŵa ndi okulirapo. Ikakhala yotsika ndi 10 mpaka 25 peresenti, amati matendaŵa ndi ochepa. Ngati mwanayo ali wamfupi kwambiri poyerekezera ndi zaka zake, ndiye kuti wakhala akudwala matendaŵa kwa nthaŵi yaitali ndipo anapinimbira.

Matenda oopsa kwambiri amene amabwera chifukwa cha kusoŵa kwa zakudya zomanga thupi ndi zopatsa mphamvu ndi awa: kuonda (marazimasi), kutupa (kwashoko), ndiponso kuonda kophatikizana ndi kutupa. Kuonda kumapezeka makamaka mwa ana oyamwa amiyezi yapakati pa 6 ndi 18. Kumayamba pang’onopang’ono chifukwa chakuti mwanayo wakhala akusoŵa zakudya zopatsa mphamvu ndi zakudya zina zonse zofunika m’thupi kwa nthaŵi yaitali. Vutoli limakula chifukwa chakuti mwanayo sakuyamwa mokwanira kapena akum’mwetsa zakumwa zosungunula kwambiri m’malo momuyamwitsa mkaka wa m’maere. Mwanayo amakhala woonda kwambiri, minofu yake imakhala yopyapyala kwambiri mpaka khungu limamatira ku mafupa ndipo amakula mopinimbira. Amakhalanso ndi “nkhope yangati ya munthu wamkulu,” sachedwa kunyanyuka, ndipo amaliralira.

Liwu lakuti kwashoko, limene linachokera ku chinenero china cha ku Africa kuno, limatanthauza “nthumbidwa.” Izi zimatanthuza kumuletsa mwana kuyamwa asanakule chifukwa chakuti mayi wake waberekanso mwana wina. Nthenda ya kwashoko imabwera mwana akasiya kuyamwa, ndipo ngakhale kuti amasoŵanso zakudya zopatsa mphamvu, kwenikweni imayamba chifukwa cha kusoŵa kwakukulu kwa zakudya zomanga thupi. Nthendayi imachititsa thupi kudzaza ndi madzi, ndipo mwanayo amatupa manja, miyendo ndi mimba. Nthaŵi zina amatupanso nkhope, ndipo imaoneka yozungulira ngati mwezi. Amatuluka zilonda pa khungu pake ndipo tsitsi lake limasintha mtundu komanso limakhala lapepelepepele. Ana odwala matenda ameneŵa amatupa chiŵindi ndipo amaoneka osasangalala ndi omvetsa chisoni. Zimenezi ndi zimene zinamuchitikira Erik, amene tamutchula koyambirira uja, chifukwa mayi ake anangomuyamwitsa mwezi umodzi wokha basi, kenako anayamba kum’mwetsa mkaka wa ng’ombe wosukuluka kwambiri. Atakwanitsa miyezi itatu anayamba kum’mwetsa msuzi wa masamba ndi madzi othira shuga, ndipo anauza amayi ena oyandikana nawo nyumba kuti ndi amene azimusamalira.

Mtundu wachitatu wa matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi ndi kuonda kophatikizana ndi kutupa. Matenda atatu onseŵa amapha ngati munthu sanalandire chithandizo msanga.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

TETEZANI MWANA WANU KU MATENDA A KUSOŴA KWA ZAKUDYA M’THUPI!

▪ M’pofunika kwambiri kuti mayi azidya zakudya zopatsa thanzi. Amayi oyembekezera ndi oyamwitsa amafunika kumadya zakudya zokwanira zopatsa mphamvu ndi zomanga thupi. Zakudya zomanga thupi makamaka zimathandiza kupanga mkaka wa m’maere. Choncho, ngati zakudya zilipo zopereŵera, choyamba mupatse amayi ndi ana aang’ono.

▪ Pafupifupi nthaŵi zonse, chakudya chabwino kwambiri cha mwana ndi mkaka wa m’maere. Izi zili choncho makamaka masiku oyambirira mwana akangobadwa kumene chifukwa mkaka wa m’maere umakhala ndi mankhwala amene amateteza mwanayo ku matenda. Kwa miyezi inayi kapena ingapo yoyambirira mwana akabadwa, mkaka wa m’maere umakhala ndi zakudya zonse zimene mwanayo amafunikira kuti akule bwino.

▪ Kuyambira mwezi wachinayi mpaka wasikisi, mwana akhoza kuyamba kudya zakudya zina, komabe, chakudya chake chachikulu ndi mkaka wa m’maere. Pang’ono ndi pang’ono, yambani kumuphunzitsa kudya zipatso ndi masamba zokanyakanya. Muyambitseni kudya chakudya chatsopano chimodzi basi nthaŵi iliyonse. Pakatha masiku aŵiri kapena atatu, ndipo akachizoloŵera chakudya chimenecho, mpatseni chamtundu wina. N’zoona kuti pamafunika kudekha komanso kuyesetsa kuti mwanayo avomere chakudya chatsopano. Mukamakonza chakudya cha mwana, kumbukirani kuti chilichonse chiyenera kukhala chaukhondo kwabasi! Muyenera kutsuka zakudya ndi ziŵiya zonse bwinobwino!

▪ Kuyambira mwezi wa faifi mpaka wa naini, mwana amafunikira zakudya zambiri zopatsa mphamvu ndi zomanga thupi kuposa zimene angazipeze mu mkaka wa m’maere. Pitirizani ndipo chitani khama kum’phunzitsa kudya zakudya zatsopano. Poyamba mungam’patse phala ndi zakudya za ana za masamba, kenako mungam’patse zakudya za nyama ndi za mkaka. Poyambirira, zakudya za mwanazi muzizisefa, koma kuyambira mwezi wa sikisi, mungayambe kumazidula m’tizidutswa ting’onoting’ono. Sikofunika ndiponso sikoyenera kuthira shuga kapena mchere m’chakudya cha mwana.

▪ Mwana akatha miyezi eyiti, mkaka wa m’maere sukhalanso chakudya chake chachikulu, koma umakhala wongowonjezera chabe pa zakudya zina. Amayamba kudya nawo zakudya zimene anthu ena onse m’banjamo akudya. Chakudyachi chiyenera kukhala cha ukhondo kwambiri ndipo muzichidula m’tizidutswa ting’onoting’ono kuti mwanayo asamavutike potafuna. Kuti azipeza zofunika zonse m’thupi, ayenera kumadya zipatso ndi masamba, phala ndi zakudya za m’gulu la nyemba, komanso zakudya za nyama ndi za mkaka. * Ana amafunika kudya kwambiri zakudya zokhala ndi vitamini A. Zakudya zake ndi monga mkaka wa m’maere, masamba obiriŵira kwambiri, ndiponso zipatso ndi masamba achikasu ngati mango, karoti, ndi mapapaya. Ana osakwana zaka zitatu ayenera kudya kasanu kapena kasanu ndi kamodzi patsiku.

▪ Kuti mwana wanu azipeza zofunika zonse za m’thupi ndipo azitetezedwa ku matenda, ayenera kudya zakudya zakasinthasintha, ndipo muzizisakaniza mosiyanasiyana. Cholinga cha amayi chiyenera kukhala kumpatsa mwanayo zakudya zopatsa thanzi, ndipo sayenera kumukakamiza kudya akakhuta, kapena kumuletsa kudya ngati akuoneka kuti akadali ndi njala.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 43 Mungamve zambiri mu nkhani yakuti “Chakudya Chopatsa Thanzi N’chosasoŵa” imene ili mu Galamukani! ya May 8, 2002.

[Chithunzi]

Akatswiri amavomerezana kuti pafupifupi nthaŵi zonse, mkaka wa m’maere ndiye chakudya chabwino kwambiri cha mwana wakhanda

[Mawu a Chithunzi]

© Caroline Penn/Panos Pictures

[Chithunzi patsamba 7]

Ana akudya mkate wouma wa tirigu ndi masamba ku sukulu ku Bhutan

[Mawu a Chithunzi]

FAO photo/WFP Photo: F. Mattioli

[Chithunzi patsamba 9]

Panokha, pali zimene mungachite kuti mwana wanu azidya moyenera

[Mawu a Chithunzi]

FAO photo