Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ufulu Wathu Wosankha Tiziugwiritsa Ntchito Bwanji?

Kodi Ufulu Wathu Wosankha Tiziugwiritsa Ntchito Bwanji?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Ufulu Wathu Wosankha Tiziugwiritsa Ntchito Bwanji?

MULUNGU anapatsa anthu oyamba, Adamu ndi Hava, nzeru zoti azitha kusankha okha zinthu. Anauza Adamu kuti ayang’anire munda wa Edene. Ina mwa ntchito za Adamu inali kutcha nyama mayina. (Genesis 2:15, 19) Chofunika kwambiri, Adamu ndi Hava akanatha kusankha kumvera kapena kusamvera Mulungu.—Genesis 2:17, 18.

Chiyambireni nthaŵi imeneyo, anthu apanga zosankha zambirimbiri. Zosankha zambiri zakhala zabwino, zina zolakwika ndipo zina zoipiratu. Zina mwa zolakwikazo zabweretsa mavuto aakulu. Komabe, Mulungu sanaloŵererepo pa ufulu wathu wosankha. Monga Atate wachikondi, Mulungu amatithandiza kuti tisankhe mwanzeru kudzera m’Baibulo. Amatichenjezanso za ngozi zimene tingakumane nazo ngati tisankha molakwika. Baibulo limati tidzatuta zimene timafesa.—Agalatiya 6:7.

Zosankha pa Nkhani Zokhudza Munthu Payekha

Pankhani zina Mulungu amafotokoza bwinobwino zofuna zake ndipo amatipatsa malangizo okhudza nkhani zimenezo. Koma pankhani zotikhudza ifeyo patokha, nthaŵi zambiri Baibulo silikhazikitsa malamulo oti tiwatsatire. M’malo mwake, limapereka malangizo oti tingawagwiritse ntchito pa zinthu zambiri, amene amathandiza anthu ngakhale kuti amakonda zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya zosangalatsa.

Malemba amati Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Mawu ake amatchula za “mphindi yakuseka” ndi “mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:1, 4) Baibulo limatiuzanso kuti Mfumu Davide anaimba nyimbo kuti asangalatse ena. (1 Samueli 16:16-18, 23) Yesu anakapezeka pa phwando la chikwati, ndipo anathandizapo posandutsa madzi kukhala vinyo.—Yohane 2:1-10.

Komabe, Baibulo moyenerera limachenjeza kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) “Kulankhula zopanda pake” ndiponso khalidwe lachiwerewere zimakwiyitsa Mulungu ndipo zingasokoneze ubwenzi wathu ndi iye. (Aefeso 5:3-5) Ngati paphwando pali mowa wambiri popanda anthu ouyang’anira bwinobwino, pangabuke mavuto aakulu. (Miyambo 23:29-35; Yesaya 5:11, 12) Yehova Mulungu amadananso ndi chiwawa.—Salmo 11:5; Miyambo 3:31.

Mavesi a m’Baibulo ameneŵa akutithandiza kuona zosangalatsa mmene Mulungu amazionera. Akristu akamapanga zosankha, amafuna kuti zigwirizane ndi Baibulo. Mulimonsemo, tonsefe tidzatuta zabwino kapena zoipa malinga ndi zimene timasankha.—Agalatiya 6:7-10.

Akristu amalimbikitsidwanso kusankha mwanzeru mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo pankhani ngati kavalidwe, kusankha wokwatirana naye, kukhala ndi ana, ndi zamalonda. Nkhani zina n’zoti Malemba satchula mwachindunji, koma mfundo zake zimawathandiza kusankha mogwirizana ndi chikumbumtima. (Aroma 2:14, 15) Mkristu aliyense payekha ayenera kugwiritsa ntchito mfundo yotsatirayi pa zosankha zake: “Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.

Pankhani imeneyi ya zosankha, Akristu angachitenso bwino kuganizira mfundo ‘yosamala ntchito yakeyake.’ (1 Atesalonika 4:11, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Akristu nthaŵi zambiri amatha kukhala ndi zosankha zingapo zosasemphana ndi chifuniro cha Mulungu. N’chifukwa chake, zimene Mkristu wina angakonde zingasiyane ndi zimene winanso angakonde. Mulungu sangasangalale kuona atumiki ake akuweruzana. (Yakobo 4:11, 12) Mwanzeru Baibulo limalangiza kuti: “Asamve zowawa wina wa inu . . . ngati wodudukira.”—1 Petro 4:15.

Kusankha Kutumikira Mulungu

Baibulo limasonyeza kuti kumvera Mulungu kuli ndi phindu lake. Koma Mulungu sakakamiza anthu kuti amulambire. M’malo mwake amachita kupempha anthu kuti azimulambira. Mwachitsanzo, Baibulo limati: “Tiyeni, tipembedze tiŵerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga.”—Salmo 95:6.

Pamenepa anali kupempha Aisrayeli kuti amulambire. Zaka zoposa 3,500 zapitazo, mtundu wa Israyeli unaimirira m’munsi mwa phiri la Sinai, ndipo Mulungu anasonyeza anthu miyandamiyandawo kapembedzedwe koona kamene anakalemba m’Chilamulo cha Mose. Tsopano anafunikira kusankha: Kodi atumikire Mulungu kapena asam’tumikire? Kodi anati chiyani? Onse pamodzi anati: ‘Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.’ (Eksodo 24:7) Anasankha okha kulambira Yehova.

M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, Yesu anayambitsa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:17; 24:14) Sanaumirize munthu wina aliyense kuti ayambe nawo ntchito imeneyi. Koma, iye mokoma mtima anapempha anthu kuti: ‘Idzani kuno, munditsate Ine.’ (Marko 2:14; 10:21) Anthu ambiri anamtsatira ndipo anayamba kulalikira naye limodzi. (Luka 10:1-9) Koma patapita nthaŵi, ena anasankha kum’siya Yesu. Yudasi anam’pereka Yesu. (Yohane 6:66; Machitidwe 1:25) Pambuyo pake, motsogozedwa ndi atumwi, anthu ambiri anakhala ophunzira, osati moopsezedwa, koma chifukwa cha kufuna kwawo. Anali ofunitsitsa ndipo anakhala ‘okhulupirira.’ (Machitidwe 13:48; 17:34) Masiku anonso, Akristu oona mwa kufuna kwawo amamvera Mawu a Mulungu ndipo amatsatira chiphunzitso cha Yesu.

Choncho, n’zachionekere kuti Mulungu amafuna kuti tizigwiritsa ntchito nzeru zathu posankha. Kudzera m’Baibulo amaperekanso mfundo zotithandiza kuti tisankhe mwanzeru. (Salmo 25:12 ) Popanga zosankha pa nkhani zokhudza munthu payekha, Mkristu aliyense ayenera kuganizira mfundo za Mulungu asanapange zosankhazo. Tikatero, m’pamene tingachite ‘utumiki wopatulika ndi mphamvu yathu ya kulingalira.’—Aroma 12:1, NW.