Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusonyezana Chikondi Panthaŵi ya Mavuto

Kusonyezana Chikondi Panthaŵi ya Mavuto

Kusonyezana Chikondi Panthaŵi ya Mavuto

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU NIGERIA

KU Nigeria, mu mzinda wa Lagos, anatcha tsiku la January 27, 2002, kukhala Lamlungu Loopsa. Mabomba amene anaphulika kumalo apansi pa nthaka osungirako zida za nkhondo anagwedeza mzinda wonsewo ndipo kumwamba kunaŵala ngakhale kuti unali usiku. Mabombawo anaphulika kwa maola ambiri ndipo zidutswa zake ndi mabomba ena zinakagwera kumalo ozungulira pamene panaphulikapo, pamtunda wa makilomita atatu, ndipo mu mzinda wonsewo munali chisokonezo chokhachokha.

Mphekesera zokokomeza zinangowonjezera mantha amene anthu anali nawo. Chikhamu cha anthu, mitima ili m’mwamba, chinathaŵira m’misewu ndipo onsewo sanadziŵe chimene anali kuthaŵa kapena kumene anali kuthaŵira. Chifukwa chakuti unali usiku ndipo kunali mdima, anthu mazanamazana, kuphatikizapo ana ambiri atasokonezeka, pothaŵa anakagwera mu mtsinje wa madzi akuda ndi kumira. Nyumba, sukulu, ndi masitolo zinawonongekeratu kapena kugumuka modetsa nkhaŵa, ndipo anthu ambiri anasoŵa pokhala ndi ntchito. Pangozi imeneyi akuti panafa anthu pafupifupi 1,000. Koma chiŵerengero chimene chimabwera m’mbuyo mwake chinali chokwera kwambiri.

Mabomba amene anali asanaphulike okwana pafupifupi 1,350, komanso mabomba ouluka, ndi mabomba ochita kuponya ndi manja anakawapeza kumidzi yozungulira pamalo a asilikaliwo. Mwamuna wina anapeza chitsulo m’nyumba yake m’chipinda chochezera. Iyeyo, posadziŵa kuti ndi bomba, anachitenga, kuchiika kumbuyo kwa galimoto lake n’kupita nacho kupolisi.

Mbiri ya mabomba amene anaphulikawo itangomveka ku ofesi ya nthambi ya Nigeria ya Mboni za Yehova, anatumiza uthenga kwa mkulu wina ku Lagos ndi kuuza oyang’anira oyendayenda 16 kuti afufuze ndi kuona mmene vutolo lakhudzira Mboni zokwanira 36,000 za mu mzindawo. Anatumizanso ndalama zokwana 1,000,000 naira (pafupifupi madola 10,000 a ku United States), komanso malangizo akuti akonze komiti yopereka chithandizo.

Pakati pa Mboni, panavulala mwamuna mmodzi modetsa nkhaŵa chifukwa cha tizidutswa ta zitsulo. N’zomvetsa chisoni kuti atsikananso aŵiri anataya miyoyo yawo, ndipo Nyumba za Ufumu ziŵiri ndi nyumba za mabanja okwanira 45 zinawonongeka.

Patadutsa masiku asanu ndi limodzi chiphulikireni mabombawo, pa February 2, 2002, kunabuka chipolowe kumbali ina ya mzindawo pakati pa anthu osiyana mafuko. Malinga ndi a bungwe la Red Cross, akuti pachipolowechi panafa anthu 100, ovulala analipo 430, ndipo 3,000 anathaŵa kwawo, ndiponso panali nyumba 50 zimene zinatenthedwa. Mwamsanga, komiti yopereka chithandizo imene inali kuthandiza anthu “Lamlungu Loopsa” lija inafunafuna abale awo achikristu m’dera limeneli.

Nthaŵi imeneyi palibe wa Mboni amene anataya moyo wake, chifukwa ambiri anali kumsonkhano wadera pamene chipolowecho chinayamba. Komabe, ambiri m’mipingo yonse isanu ya m’dera limeneli sanazipeze nyumba zawo mmene amachoka ku msonkhano. Ngakhale zinali tero, abale awo achikristu anawasunga m’nyumba zawo mwaufulu. Dokotala wina amene ndi wa Mboni anasunga anthu 27 osoŵa pokhala.

Mboni za ku Lagos zimene sizinakhudzidwe ndi mabombawo ndi kumenyana kwa anthu osiyana mafuko zinapereka chakudya, zovala, ndi katundu wa m’nyumba mwaufulu. Mboni yoyang’anira mzinda inati: “Zimene abale a ku Lagos akupereka zachuluka kwambiri kuposa zimene anthu oonekedwa mavutoŵa akufuna.” Choncho, ofesi ya nthambi sinachitire mwina koma kulembera mipingo kuipempha kuti isaperekenso zina. Zimene zinatsala zokwana magalimoto atatu anakazisunga ku ofesi ya nthambi.

Pavuto limeneli, akulu a mpingo anayendera anthu ambiri ndi mabanja ofedwa. Cholinga chawo chinali chakuti awatonthoze mitima anthuwo ndi Malemba. Komiti yopereka chithandizo inaonetsetsa kuti nyumba zonse zimene zinawonongeka zakonzedwa. Inapatsa anthu oonekedwa masoka aŵiriwo katundu wa m’nyumba, zovala, ndi zakudya, ndiponso inathandiza amene analibe pokhala kupezanso nyumba. Komiti imeneyi inathandiza mabanja 90 komanso anthu ena osiyanasiyana.

Ambiri amene anaonekedwa mavutowo anakhudzidwa mtima poona thandizo limene analandira. Wa Mboni wina anauza komiti yopereka chithandizo molimba mtima kuti: “Malinga ndili moyo, Yehova adzakhalabe ‘pothaŵirapo panga ndi mphamvu yanga’!”—Salmo 46:1, 2.

Anthu amene si Mboni anaona mmene Mboni za Yehova zinasamalirana nthaŵi yovuta imeneyi. Amalume a wa Mboni amene anamwalira anauza akulu a mpingo umene mlongoyo anali kusonkhana kuti: “Ndidzafikanso kudzakuthokozani bwino komanso kudzaphunzira zambiri.” Ndipo anauza banja lake kuti: “Ndinaona zodabwitsa ku Lagos. Zimene anthuŵa anachita ngakhale achibale sanazichitepo.”

[Chithunzi patsamba 13]

Galimoto yodzaza ndi katundu wa chithandizo

[Chithunzi patsamba 13]

Ena amene anathandizidwa

[Chithunzi patsamba 14]

Banja ili linasunga anthu 27 osoŵa pokhala

[Chithunzi patsamba 14]

Mboni zikukonza nyumba yowonongeka

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

Pamwamba: Sam Olusegun-The Guardian