Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mliri Wobisikawu” Utha Posachedwa!

“Mliri Wobisikawu” Utha Posachedwa!

“Mliri Wobisikawu” Utha Posachedwa!

“KUYEREKEZERA ndi mmene zinthu zinaliri zaka zochepa zapitazi, masiku ano tikukhala m’dziko la mwanaalirenji. . . . Mogwirizana ndi umboni umene ulipo, . . . pali chakudya choti chikhoza kukwanira munthu aliyense n’kutsalakonso.” Kafukufuku amene linapanga bungwe la World Health Organization (WHO) anasonyeza zimenezi. Ngati zili choncho, kodi n’chiyani makamaka chimene chimayambitsa vuto la kusoŵa kwa zakudya m’thupi?

“Vuto limene lilipo n’lakuti chakudya chikalimidwa sichigaŵidwa mwa chilungamo,” linatero bungwe la WHO. “Nthaŵi zambiri, anthu osauka m’mayiko amene akutukuka kumene amangokhala ndi njala yawo, komanso osoŵa pogwira, kwinaku akuona chakudya chambiri chimene analima chikugulitsidwa kunja. Zotsatira zake n’zakuti anthu ochepa amapindula nthaŵi yomweyo, pamene anthu ambiri amakhala akuvutika kwa nthaŵi yaitali.” Kafukufuku amene a bungwe la Food and Agriculture Organization (FAO) la United Nations anachita posachedwapa akusonyeza kuti ‘pa anthu 100 alionse olemera kwambiri pa dziko lonse, anthu 20 amadya pafupifupi theka la nyama ndi nsomba zonse, pamene nambala yomweyo ya anthu osauka kwambiri padziko lonse amangodyako zochepa chabe.’

Komanso, “kusoŵa kwa maphunziro abwino ndi mfundo zolondola kumayambitsanso matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi,” anatero a United Nations Children’s Fund. Iwo anapitiriza kunena kuti: “Popanda njira zabwino zophunzitsira komanso maphunziro abwino ndi osavuta kuwapeza, sipangakhale anthu ozindikira, aluso, komanso akhalidwe limene limafunika pothana ndi matendaŵa.” Koma kusoŵa kwa zakudya kumawononga thanzi la munthu ndiponso kumamulepheretsa kupeza maphunziro abwino. Zikatere vutoli limangopitirira.

Chilungamo Ndiponso Kukonda Ena

Ngakhale kuti pali zopinga zonsezi, akatswiri ena a nkhani imeneyi akuganiza kuti zinthu ziyenda bwino ndithu. Mwachitsanzo, woyang’anira wamkulu wa bungwe la FAO a Jacques Diouf, ponena za zimene amakhulupirira anati: “Ndikayang’ana kutsogolo ndikuona dziko limene munthu aliyense, wamkazi, wamwamuna, komanso mwana, adzakhale ndi chakudya chokwanira chopatsa thanzi komanso chabwino, tsiku lililonse. M’dziko limeneli kusiyana kwakukulu kumene kulipo pakati pa anthu olemera ndi osauka kudzatha. Mudzakhala kulolerana osati kusankhana, mtendere osati zipolowe, malo otetezeka osati kuwononga zachilengedwe, moyo wotukuka osati moyo wosoŵa pogwira.”

Koma monga momwe taonera, pakufunika zambiri kuti zinthu ngati zimenezi zidzachitikedi. Kulima zakudya zambiri ndi kuzigaŵa bwino kokha si kokwanira ayi. Pa dziko lonse padzafunika pakhale chilungamo ndi kukondana. Koma m’dziko la malondali, makhalidwe osiririka ameneŵa ndi osoŵa.

Kodi zingatheke kuthetsa zopinga zazikulu kwambiri ngati dyera, umphaŵi, zipolowe, ndi kudzikonda, zimene zilipozi kuti matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi athe padziko pano? Kapena kodi n’zosatheka?

Njira Yokhayo Yothetsera Vutoli

Baibulo limanena kuti sitiyenera kudabwa kuti kuli mavuto amene amabweretsa matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi. Ilo limati: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, . . . osakonda abwino, . . . akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”—2 Timoteo 3:1-5.

Kodi anthu angathetse chibadwa choipa chimenechi popanda Mulungu kuwathandiza? N’zovutilapo, kodi si choncho? Mwina munaonapo kuti nthaŵi zina anthu olamulira amatha kufunitsitsa ndithu kuthetsa mavuto amene anthu tili nawo, koma anthu ena odzikonda, okonda ndalama, ndiponso opanda ungwiro, amawalepheretsa komanso kuwawonongera zabwino zonse zimene amati atichitire zija.—Yeremiya 10:23.

Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti mavuto ameneŵa sangathe ayi. Baibulo likulonjeza kuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa vuto la kusoŵa kwa chilungamo komanso mavuto ena onse amene anthu akuvutika nawo masiku ano.

Pa Yesaya 9:6, 7 pali lonjezo lochititsa chidwi ili: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”

Ndi Ufumu umenewu umene anthu amaupempha mu Pemphero la Ambuye, akamamupempha Mulungu kuti, “Ufumu wanu udze.” (Mateyu 6:9, 10) Onani kuti Yesaya anati “changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.” Inde, Yehova Mulungu nthaŵi yonseyi wakhala akufunitsitsa kuthandiza anthu pa zosoŵa zawo. Analenga dzikoli kuti lizitha kubereka zakudya zokwanira anthu onse.

Salmo 65:9-13, ponena za Yehova limati: “Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeza kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nawo madzi: muwameretsera tirigu m’mene munakonzera nthaka. Mukhutitsa nthaka yake yolima; mufafaniza nthumbira zake; muiolowetsa ndi mvumbi; mudalitsa mmera wake. . . . Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu.”

Zoonadi, Mlengi wathu Yehova ndi yekhayo amene angapatse anthu zonse zimene amafunikira. Iye “ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya; pakuti chifundo chake n’chosatha.”—Salmo 136:25.

Tiyeni tikhale ndi chikhulupiriro kuti Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Kristu udzakwaniritsa zosoŵa zonse za anthu. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa,” monga mmene Baibulo limanenera. Komanso, zidzagaŵidwa mofanana kwa aliyense, chifukwa “[Yesu Kristu] adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. . . . Nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi.” (Salmo 72:12, 13, 16) Chotero, musataye mtima! “Mliri wobisika” umenewu watsala pang’ono kutha, ndipo ukadzatha sudzabweranso.

[Mawu otsindika patsamba 11]

“Malinga ndi umboni umene ulipo, tikhoza kuthetsa njala ndi matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi. Zonse zofunika zilipo. Koma vuto lilipo n’lakuti . . . anthu paokha m’dziko lililonse, komanso mayiko onse pamodzi, sakuchita khama kuti athetse vutoli.”—Anatero ndi a World Health Organization

[Chithunzi chachikulu patsamba 10]