Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mliri Woopsa Kwambiri

Mliri Woopsa Kwambiri

Mliri Woopsa Kwambiri

Erik * ali ndi miyezi isanu ndi umodzi. Koma sikelo yake ndi kutalika kwake kungafanane ndi kwa mwana wa mwezi umodzi kapena iŵiri. Ngakhale kuti sikelo yake ndi yotsika kwambiri chonchi, miyendo, mimba ndi nkhope yake n’zotupa. Akuoneka wowezuka, tsitsi lake ndi lapepelepepele, ndipo ali ndi zilonda pakhungu pake, komanso amaliralira. Adokotala akamamuona m’maso, ayenera kusamala kwambiri chifukwa mukhoza kung’ambika mosavuta. Mwachiwonekere, ubongo wa Erik sukukula bwino. Chomvetsa chisoni n’chakuti si Erik yekhayu amene akudwala chonchi, palinso ana ena otere ambiri.

“IMAPHA lopitirira theka la ana onse amene amafa padziko lapansi. Izi zikutanthauza kuti imapha anthu ambiri kuposa matenda ena alionse opatsirana chichitikireni mliri waukulu wa matenda amakoswe. Koma, si nthenda yopatsirana. Pali mamiliyoni ambiri a anthu amene apunduka nayo, ena angosanduka odwaladwala, komanso ena akhala opereŵera nzeru. Imavutitsa azimayi, mabanja, ndipo pamapeto pake, imawonongeratu moyo wa anthu.”—Linatero lipoti la The State of the World’s Children la United Nations Children’s Fund.

Kodi akufotokoza za matenda anji? Matenda a kusoŵa kwa zakudya m’thupi—makamaka kusoŵa zakudya zomanga thupi ndi zopatsa mphamvu kumene a bungwe la World Health Organization (WHO) anakutcha “mliri wobisika.” Kodi mliri umenewu ndi woopsa bwanji? A bungwe la WHO anati matenda ameneŵa “amathandizira nawo kuchititsa imfa zopitirira theka za ana okwanira 10,400,000 amene amafa chaka chilichonse.”

Matenda okhudzana ndi kadyedwe alipo amitundumitundu. Pali kunyentchera, kumene kumabwera chifukwa cha kusoŵa zofunika m’thupi monga mavitamini ndi maminiro, ndiye palinso kunenepa kwambiri, komanso matenda ena aakulu okhudzana ndi kadyedwe. Komabe, kusoŵa zakudya zomanga thupi ndi zopatsa mphamvu “ndi kumene kumapha anthu ambiri,” linatero bungwe la WHO. Amene amafa kwambiri ndi ana osakwana zaka zisanu.

Taganiziraninso za Erik, amene tinamutchula poyambirira uja, komanso za ana mamiliyoni ambiri amene akudwala matenda osoŵa zakudya m’thupi. Palibe chimene analakwa kuti adwale matendaŵa, ndipo palibe chimene angachite kuti awapeŵe. Dokotala woona za kadyedwe ka ana Georgina Toussaint anafotokozera a Galamukani! kuti: “Amene amavutika kwambiri ndi anthu amene sanalakwe chilichonse ndipo amakhudzidwa nawo kwambiri matendaŵa.”

Ena angaganize kuti vutoli n’losapeŵeka chifukwa palibe chakudya chokwanira. Koma kudabwitsa kwake n’kwakuti, malinga ndi kunena kwa bungwe la WHO, “tikukhala m’dziko la mwanaalirenji.” Padziko lapansi pali chakudya chokwanira aliyense, n’kutsalakonso. Chodabwitsa china n’chakuti, matenda osoŵa zakudya m’thupi ndi amene ali osavuta kupeŵa komanso osavuta kuchiza kuposa onse. Kodi zimenezi sizikukupsetsani mtima?

Kodi Amadwala Matendaŵa Ndani?

Si ana okha amene amadwala matendaŵa. Malingana ndi zimene linanena lipoti la WHO la mu July 2001, “kusoŵa zakudya m’thupi ndi vuto lofala, ndipo limakhudza anthu pafupifupi 800 miliyoni—anthu 20 pa anthu 100 alionse okhala m’mayiko amene akutukuka kumene.” Zimenezi zikutanthauza kuti munthu mmodzi pa anthu 8 alionse padziko lapansi pano amadwala matenda ameneŵa.

Kumene kuli anthu ambiri odwala matendaŵa kuposa kwina kulikonse ndi ku Asia, makamaka kuchigawo cha kum’mwera ndi chapakati. Koma tikatenga chiŵerengero cha anthu odwala matendaŵa n’kuchiyerekezera ndi anthu osadwala, ku Africa kuno ndi kumene kuli chiŵerengero chachikulu kwambiri cha anthu odwala matenda osoŵa zakudya m’thupi. Otsatirapo ndi mayiko ena amene akutukuka kumene a ku Latin America ndi ku Caribbean.

Kodi kumayiko otukuka kulibe matenda ameneŵa? Aliko. Mogwirizana ndi lipoti la The State of Food Insecurity in the World 2001, anthu 11 miliyoni amene akukhala m’mayiko otukuka akudwala matenda osoŵa zakudya m’thupi. Enanso amene akudwala matendaŵa ndi anthu okwana 27 miliyoni amene akukhala m’mayiko amene akungotukuka kumene, makamaka mayiko a kum’mawa kwa Ulaya komanso mayiko amene kale anali mu ulamuliro wa Soviet Union.

Kodi n’chifukwa chiyani vuto la kusoŵa kwa zakudya m’thupi lakula kwambiri chonchi? Kodi pali chilichonse chimene chingawathandize anthu amene akudwala matendaŵa pakadali pano? Kodi matendaŵa tsiku lina adzatheratu padziko lapansi pano? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Si dzina lake lenileni.

[Tchati/Chithunzi patsamba 4]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MAYIKO AMENE AKUKHUDZIDWA NDI KUPEREŴERA KWA ZAKUDYA

OKHUDZIDWA KWAMBIRIKO

OKHUDZIDWA KWAMBIRI

OKHUDZIDWA PANG’ONO

OSAKHUDZIDWA KAPENA SIZIKUDZIŴIKA

[Chithunzi patsamba 3]

Akuyembekeza thandizo ku Sudan

[Mawu a Chithunzi]

UN/DPI Photo by Eskinder Debebe