Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Msamuko Waukulu Wochititsa Chidwi

Msamuko Waukulu Wochititsa Chidwi

Msamuko Waukulu Wochititsa Chidwi

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU KENYA

NTHAKA ikugwedezeka ndi mdidi wa ziboda mamiliyoni ambiri. Chigulu cha nyama chagundika nalo liŵiro, kumbuyo kwakeku chikusiya chifumbi chofiira chimene changoti koboo! Nyamazo zalikumba liŵiro ndi miyendo yawo yaitali ndi yowonda kumatsikira ku zigwa kenako kumakwezeka zitunda. Zikudutsa madambo komanso kuwoloka mitsinje ndi mifuleni. Mmene zikudutsamo zikusiya chimpita, udzu wonse utathyokathyoka mpaka pansi. Ulendo umenewu wa chigulu cha nyama zimene zikuphokosera ndi kuthamanga ndi chimodzi mwa zinthu zochititsa chidwi koposa padziko lapansi pa nyama zakutchire. Umenewu ndi msamuko waukulu wochititsa chidwi wa nyumbu.

Munda wa Edene wa M’Africa

Dera la Serengeti ndi kutchire kwenikweni. Lili ku Tanzania ndi Kenya ndipo ndi dambo lalikulu kwambiri la zigwa ndi zikweza. N’lalikulu masikweya kilomita pafupifupi 30,000. Nthaka yake ili ndi dothi lachonde lochokera m’mapiri ophulika, ndipo zimenezi zimathandiza kuti udzu wake uzikhala wobiriŵira mochititsa kaso. Kuli madera a mitengo ya kesha ndi yaminga imene njovu zimapezako chakudya. Nyamalikiti zikamayenda pang’onopang’ono kudutsa madambo, zimasangalatsa mmene zimaponyera miyendo yake yaitali. Zimangoti zochizochi!

Kumbali zina za derali kuli madambo ndi matanthwe aakulu oimirira komanso osalala chifukwa cha mvula ndi mphepo. Matanthwewo ndi malo abwino kukhalapo mikango ndi akambuku chifukwa amakhala ngati nsanja yawo. M’mitsinje yothamanga komanso yokhotakhota imene imadutsa dzikoli muli mvuu ndi ng’ona zambirimbiri. M’madambo mungaonemo gulu la nyumbu, ngondo, ndi agwape osiyanasiyana akudya udzu. Mbidzi zaludzu zimazungulira maiŵe, muja umaonekera mkanda woyera ndi wakuda m’khosi. Mphoyo ndi nswala zimadumphadumpha pothamanga zikamadutsa m’madambo ndipo sizivutika zikamatere. Njati za nyanga zake zopindika ndi matupi ake amphamvu zimadya udzu pang’onopang’ono, ndipo zimachita kuzula chiputu chonse ndi milomo yake yaikulu.

Ku Serengeti kuli mikango yambirimbiri. Masana kukatentha, imangogona m’mithunzi ya mitengo ndi zitsamba, poyembekeza kuti usiku kukazizira izikasaka nyama. Akambuku si kwapafupi kuwaona kuti agona pati, chifukwa amakhala ali phe m’mitengo pamwamba, atabisika m’masamba. Koma akakwiyo amakonda m’madambo chifukwa muli malo otakasuka bwino kwambiri oyenera nyama imeneyi yaliŵiro. Akamathamangitsa nyama m’madambo, thupi lake laling’onolo sutha kuliona bwinobwino.

Inde, Serengeti ndi malo a nyama okongola ndi ochititsa kaso. Koma pa zinthu zachilengedwe zonse, nyumbu ndi zina mwa nyama zimene zili zozizwitsa koposa.

Nyama Yoseketsa ya M’madambo

Akuti ku Serengeti kuli nyumbu pafupifupi 1,500,000. Nyama yooneka mwachilendo imeneyi ili ndi mutu wautali ndi maso onyezimira komanso otalikirana pamwamba pa mutu. Nyanga zake zonga za ng’ombe n’zopindika pang’ono kupita chapansi, ndiyeno n’kupindikira m’mbali kenako n’kuloza m’mwamba. N’njaifupi kumbuyo ndipo kumbuyoko kumaoneka kofooka, ndiponso n’kwakung’ono poyerekeza ndi mapewa ake ndi khosi lake. Miyendo yake yaitaliyo komanso yowonda imanyamula thupi lake lonse lolemera kwambirilo. Chifukwa cha ndevu zake zazitali zoyerera, manyenje ake akuda, ndi mchira wake wofanana ndi wa kavalo, nyumbu imaoneka ngati nyama zingapo zosiyanasiyana.

Nthaŵi zambiri zochitika zake n’zoseketsa komanso zosangalatsa. Zikakhala pachigulu zimaphokosera ndipo zimamveka ngati kuti achule ambirimbiri akuimba. Zikaimirira m’dambo, nkhope zake zimaoneka ngati zikudabwa chinachake zikamayang’ana uku ndi uku.

Nthaŵi zina, nyumbu yamphongo imagundika nalo liŵiro m’dambo, kujidima cham’mbali ndi kuthamanga mozungulira. Ikamatero imaponya mutu wake uku ndi uku ndipo imadumphadumpha kwinaku italimbitsa miyendo yake. Potero imakhala ikumenyetsa miyendo yakeyo pansi ndi kunyamula fumbi, ndipo zimenezi n’zoseketsa kuziona. Ena amati nyamayi imatero pofuna kukopa zazikazi kapena kuchenjeza mphongo zina pozionetsa mphamvu yake. Koma nthaŵi zina, mphongoyo imakhala ngati ikungoseŵera basi.

Zobadwira M’dziko Loopsa

Nthaŵi ikakwana, nyumbu zimayamba kuswana. Nyama zimenezi n’zodabwitsa chifukwa chakuti zimayamba kuswana nthaŵi imodzi, ndipo pafupifupi ana awo onse amabadwa m’kati mwa milungu itatu. Nthaŵi imeneyi gulu la nyamali limakula chifukwa chokhala ndi ana ambirimbiri ndipo paliponse pamamveka kulira kwa anawo. Ikangobereka, iliyonse imafunika idziŵane bwinobwino ndi mwana wakeyo chifukwa nyamazo zikayamba kuthaŵa, mayi ndi mwana akhoza kutayana mosavuta m’chisokonezo chimene chimakhalapo, ndipo mwina mwanayo sangapulumuke payekha.

Anawo amabadwira m’dziko loopsa lodzaza ndi nyama zatcheru zodya zinzawo. Pobereka, imayamba yaonetsetsa kuti palibe choopsa chilichonse. Koma chodabwitsa n’chakuti ngati nyama ina yolusa yaidzidzimutsa ikuswa mwana, imatha kusiya kaye n’kuthaŵa. Ndiye nthaŵi ina ngati kulibe choopsa chilichonse, imamalizitsa ntchito yoswa mwanayo.

Mwanayo chibadwa chake amakhala ngati akudziŵa kale kuti ali m’dziko loopsa ndipo amati akabadwa, amaimirira patangopita mphindi zochepa chabe. Pakapita mlungu umodzi, amatha kukhuphuthuka m’madambo, liŵirotu limenelo, mpaka mtunda wa makilomita 50 pa ola limodzi.

Nthaŵi Yosamuka

Nyumbu zikamasamuka ku Serengeti, zimayenda m’chigulu. Zonse zimasamuka pofuna mvula. Mvulayo imayendera nyengo imene imasinthasintha pachaka. Nthaŵi zambiri mvula imakhala ikugwa kwinakwake chaka chonse m’dambo lalikulu limeneli.

Nyumbu zimafuna madzi ndi msipu masiku onse. Ngati madzi ndi chakudya zilipo, nyamazi zimakhazikika malo amodzi. Koma chilimwe chikamafika, udzu m’dambolo umayamba kuuma ndipo madzi amaphwa. Nyumbu sizitha kudikira kuti mvula izipeze. M’malo mwake zimalondola mvulayo.

Kulikonse kumene kwagwa mvula, madambo ouma amasintha kamodzi n’kamodzi. Pakapita masiku ochepa chabe, udzu umamera, ndipo paliponse pamakhala mmera wobiriŵira. Udzu wanthete umenewu umakhala ndi chakudya ndi madzi ambiri ndipo zimenezi n’zimene zimakopa nyumbuzi.

Nyama zimenezi zili ndi luso lozindikira kumene kwagwa mvula, ngakhale kutalike bwanji. Palibe amene anganene kuti zimadziŵa bwanji kuti mbali ina ya Serengeti kukugwa mvula—kaya zimaona mtambo waukulu wa mvula kutali kapena zimamva kununkhira kwa madzi mphepo ikamawomba, sitingadziŵe. Mulimonsemo, nyamazi zimafunika kusamuka basi kuti zisafe. Ndipo zimasamukadi!

Ulendo Woopsa

Poyamba nyamazi zimachoka pang’onopang’ono. Nyumbu ndi nyama zokonda kucheza. Zimati imodzi ikayamba kupita kwina, zinazo zimasiya kaye kudya n’kukhala ngati zikuilondola. Basi kenako umangoona kuti chigulu chonsecho chakhamuka, kuchiyamba chiulendo. Chifukwa cha ludzu ndi njala, zimangopitabe. Nthaŵi zina zimathamanga. Nthaŵi zina zimayenda pang’onopang’ono chondondozana, ndipo mmene zimadutsamo mumakumbika kwambiri.

Ulendo wawo umakhala woopsa. Nyama zolusa zimatsata gulu la nyumbuzi, ndipo maso awo amakhala pa nyumbu imene ikuyenda pang’onopang’ono, yolemala, kapena yodwala. Nyumbu zikamayenda pa ulendo wawowu, zimadutsa madera a mikango, imene imakhala itazibisalira. Mikangoyo imavumbuluka kuchoka mu udzu wautali umene yabisalamo n’kuthamanga kukaloŵa pa nyama zimene zikudya udzuzo, ndiye nyamazo zimangoti balala! kumwazikana chifukwa cha mantha. Akambuku, akakwiyo, nkhandwe, ndi afisi amapezerapo mwayi wogwira nyama zimene zatsalira kapena zimene zachoka pagulupo kusiyana ndi zinzake. Akapha nyamayo, miimba imatulukira. Phokoso lili m’kati kwinaku ikulimbirana nyamayo, miimba imadya zonse n’kusiya mafupa okhaokha amene amayera mbuu! chifukwa cha kutentha kwa dzuŵa la ku Africa kuno.

Nyamazi zimavutika kuti ziwoloke zikafika pa mitsinje yothamanga, koma zimafunika kuwoloka basi. Zikamawoloka zimachititsa chidwi kwambiri chifukwa pamakhala chinamtindi cha nyama zimene zimachita kudziponya polumphira m’madzi kuchokera kumtunda. Zambiri zimawoloka bwinobwino mpaka tsidya lina. Koma zina zimakokoloka ndi madzi kapena kugwidwa ndi ng’ona zimene zimabisala m’madzimo. Ulendo woopsa umenewu umachitika chaka ndi chaka. Zikamaliza ulendowu, zimakhala zitayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 3,000.

Munthu Ndiye Mdani Wawo Wamkulu

Kwa zaka zikwi zambiri, anthu sanali kusokoneza msamuko wa nyumbu. Koma tsopano akuusokoneza kwambiri msamuko wochititsa chidwi umenewu. M’zaka za posachedwapa, boma la Tanzania ndi la Kenya layesetsa kuteteza nyama za mu Serengeti. Koma ngakhale kuti msamuko wa nyumbu umachitikira makamaka m’malo otetezeka a nyama za kutchire, nyama zikwi zambiri zimagwidwa m’misampha ndi kuphedwa ndi anthu osaka nyama mosemphana ndi malamulo a boma. Anthuwo atatenga misampha ya mawaya, mivi yopaka ulembe, ndi mfuti, amasaka nyamazo kuti apezeko ndiwo ndiponso zopachika pakhoma zokagulitsa kwa anthu ena amene akuzifuna kwambiri. Gulu la oyang’anira nkhalango za boma limalondera malo oletsedwawo, koma Serengeti ndi malo aakulu kwambiri moti n’zosatheka kuwateteza onsewo bwinobwino. Chifukwa chakuti anthu achuluka, akukakamizika kulanda nyamazi malo achondewo. Kuika padera malo aakulu kuti muzikhala nyama, ndi nkhani yovuta kwambiri ndipo mkangano wake sutha.

Kale ku North America kunali njati mamiliyoni ambiri. Koma tsopano kulibe. Ena akuda nkhaŵa kuti mwina izi n’zimene zichitikirenso magulu aakulu otsala a nyumbu ku East Africa. Ngati zinthu zachilengedwe zochititsa chidwi zimenezi zingadzazimiririke tsiku lina, zidzakhala zinthu zomvetsa chisoni kwambiri. Koma tikulakalaka nthaŵi imene munthu ndi nyama adzatha kukhalira limodzi bwinobwino ndiponso mwamtendere mu ulamuliro wolungama wa Mulungu. (Yesaya 11:6-9) Pakali pano, tipitirizabe kudabwa ndi msamuko waukulu wochititsa chidwi wa nyumbuwu.

[Chithunzi patsamba 18]

Nyamazi zimafunika kuwoloka mitsinje yothamanga