Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kugona N’kofunikadi Kapena Sikofunika Kwenikweni?

Kodi Kugona N’kofunikadi Kapena Sikofunika Kwenikweni?

Kodi Kugona N’kofunikadi Kapena Sikofunika Kwenikweni?

ANTHU ENA AMAONA KUTI kugona n’kungotaya nthaŵi pachabe. Amaona kuti ndi bwino kukhala otanganidwa ndi ntchito kapena kumangocheza moti sagona pokhapokha atatopa mochita kutheratu. Koma ena amangokhalira kutembenuka usiku wonse mpaka mbandakucha, osapeza tulo ayi moti angalolere kuchita chilichonse kuti apezeko tulo basi.

N’chifukwa chiyani anthu ena amavutika kwambiri kuti apeze tulo pamene ena amachita kufunitsitsa kuti asagone? Kodi kugona tizikuona kuti n’kofunikadi kapena kuti sikofunika kwenikweni? Kuti tiyankhe mafunsoŵa, tiyenera kumvetsa kaye chimene chimachitika tikagona tulo.

Kugona Tulo N’kodabwitsa

Chimene chimachitika kuti munthu afike pogona tulo sichinadziŵikebe bwinobwino. Komano anthu ofufuza apeza kuti nkhani ya kugona njovuta kwambiri kuifotokoza ndipo kuti imayendetsedwa ndi ubongo komanso apeza kuti tsiku lililonse thupi limafunika kuti lizigona ikafika nthaŵi inayake.

Tikamakula, kagonedwe kathu kamasintha. Mwana wakhanda amagona pafupipafupi ndipo patsiku, iye amakhala atagona maola 18. Akatswiri a zakugona amati ngakhale zikuoneka kuti anthu ena aakulu amangofunika kugona maola atatu okha patsiku, palinso ena amene amafunika maola okwana mwina mpaka khumi.

Atafufuza chaposachedwapa apeza kuti achinyamata ena amavutika kudzuka m’maŵa chifukwa thupi limasintha nthaŵi imene likufunika kugona. Zikuoneka kuti munthu akamafika paunyamata thupi limafuna kugona mochedwerapo n’kumadzukanso mochedwerapo. Izi zimachitika kwa achinyamata ambiri aakulu ndipo zimatha zaka zawo zikamayandikira cha m’ma 20.

Thupi lathu limafuna kugona panthaŵi inayake chifukwa cha timadzi tinatake ta m’thupimu ndipo timadzi tambiri totere panopo anatidziŵa. Timadzi tina totere akuti timayambitsa tulo. Timadziti timachokera mu ubongo, ndipo asayansi ena amakhulupirira kuti timadzi totere ndi timene timafooketsa thupi lathu tikatsala pang’ono kugona. Thupi likayamba kutulutsa timadziti limayamba kuzizira, ndipo magazi opita ku ubongo amachepa, kenaka pang’ono ndi pang’ono minofu imayamba kulobodoka n’kufookeratu. Nanga kenaka chimachitika n’chiyani munthu tikam’tenga tulo?

‘N’kopatsa Thanzi Kwambiri’

Tikatha pafupifupi maola aŵiri tili mtulo, maso athu amayamba kuyendayenda. Asayansi ataona zimenezi, anagaŵa tulo m’zigawo ziŵiri zikuluzikulu: Chigawo chimene maso amayendayenda ndi chigawo chimene maso sayendayenda. Chigawo chachiŵirichi amachigaŵanso panayi, kuyambira ndi tulo tochepa kwambiri n’kumapita mtsogolo. Tikagona bwino, nthaŵi zingapo zonse maso amayendayenda ndipo kenaka amasiya.

Nthaŵi zambiri maso athu akamayendayenda m’pamene timalota. Komanso minofu imamasuka kwambiri, motero tikadzuka timamva kuti mphamvu zabwereramo m’thupi mwathu. Ndiponso ofufuza ena amakhulupirira kuti panthaŵiyi ubongo umatsendera zinthu zonse zatsopano kuti tidzathe kuzikumbukira mtsogolo.

Tikagona tulo tofa nato (m’chigawo chachitatu ndi chachinayi chimene maso sayendayenda), mtima umapopa magazi mwapang’onopang’ono, moti zinthu zonse zokhudza kayendedwe ka magazi zimapumako ndithu komanso zimathandiza kuti tisadwale matenda okhudza mtima ndi magazi. Kuphatikizanso apo, thupi limatulutsa timadzi tambiri tokulitsa thupi m’chigawo cha tulo chimene maso sayendayenda kapena kuti chigawo chimene sitilota, moti panthaŵiyi matupi a achinyamata ena amatulutsa timadzi totere mowirikiza ka 50 kuposa mmene timatulukira masana.

Zikuonekanso kuti kudya kumayenderana ndi mmene tagonera. Asayansi atulukira kuti kugona ‘n’kopatsa thanzi kwambiri’ malingana ndi mmene ananenera wolemba maseŵero wotchuka dzina lake Shakespeare. Tikapanda kugona bwino ubongo wathu umaona ngati kuti sitinadye mokwanira. Chimachitika n’chakuti tikamagona thupi lathu limatulutsa timadzi tinatake timene nthaŵi zonse n’tomwe timatidziŵitsa kuti takhuta. Ndiye tikakhala m’maso kwa nthaŵi yaitali kwambiri, thupi lathu limangotulutsa timadzi tochepa chabe totereti, motero timafuna kudya chinachake chokhutitsa. Choncho kusagona mokwanira kungachititse kuti munthu azidya kwabasi mapeto ake n’kunenepa kwambiri.—Onani bokosi lakuti “Kugonako Pang’ono Masana,” patsamba 6.

N’kothandiza Kuti Tisamadwaledwale

Komatu si zokhazo ayi. Kugona kumathandiza kuti thupi lathu lizichotsa zoipa zimene zingachititse kuti tikalambe mwamsanga kapenanso kudwala matenda a kansa. A ku yunivesite ya Chicago anafufuza nkhani ya kugona chaposachedwapa pouza achinyamata 11 athanzi ndithu kuti azigona maola anayi okha kwa masiku asanu ndi limodzi. Masikuŵa atatha, thupi lawo linafooka mofanana ndi thupi la munthu wa zaka 60, ndipo magazi awo anali ofanana ndi munthu wodwala matenda a shuga! Kusagona mokwanira kumachepetsanso mphamvu za thupi motero munthu angadwale mosavuta matenda oyambitsidwa ndi tizilombo ndiponso matenda okhudza mtima.

Ndithu, kugona n’kofunika kuti tikhale athanzi ndiponso oganiza bwino. William Dement, wofufuza yemwe anakhazikitsa bungwe loyamba kufufuza nkhani ya kugona, ku yunivesite ya Stanford, ku America, anaona kuti, “chinthu chofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi moyo wautali zikuoneka kuti n’kugona.” Deborah Suchecki, wofufuza wa bungwe linalake loona za kugona ku São Paulo, m’dziko la Brazil, anati: “Anthu akanadziŵa zimene zimachitika m’thupi tikapanda kugona mokwanira, adakasiyiratu kuganiza kuti kugona n’kutaya nthaŵi chabe kapena kuti ndi ulesi chabe.”—Onani bokosi lili pamwambali.

Koma kodi ndiye kuti nthaŵi zonse tikamagona mphamvu zimabwereramo m’thupi? Nanga bwanji anthu ena amagona usiku wonse koma n’kumadzukabe ali ofooka? Nkhani yotsatirayi ikuthandizani kudziŵa bwino mavuto ena akuluakulu okhudza kugona ndipo ilongosola zimene mungachite kuti muzigona bwino.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 13]

MAVUTO A KUSAGONA MOKWANIRA

OONEKERA MSANGA

▪ Kusinza

▪ Kukhumudwakhumudwa

▪ Kuiwalaiwala

▪ Kulephera kuchita zinthu zakupsa, kulephera kukonzekera zinthu ndiponso kugwira ntchito bwinobwino

▪ Kulephera kuika maganizo pa zinthu

OSAONEKERA MSANGA

▪ Kunenepa kwambiri

▪ Kukalamba msanga

▪ Kumangokhala wotopa kwambiri

▪ Kudwaladwala matenda oyambitsidwa n’tizilombo, matenda a shuga, a mtima, ndiponso a m’mimba

▪ Kudwala matenda oiwala

[Bokosi patsamba 13]

KUGONAKO PANG’ONO MASANA

Kodi tulo tinayamba takusoŵetsaniko mtendere mutangotha kudya masana? Si kuti nthaŵi zonse chimenechi chimakhala chizindikiro chakuti simunagone mokwanira. Masana zimachitika ndithu kuti tifune kugona chifukwa timayamba kumva kutentha. Komanso posachedwapa akatswiri asayansi atulukira kuti ubongo umatulutsa timadzi tinatake tochititsa kuti tizikhala m’maso. Kodi tikadya, chimachitika n’chiyani ndi timadzi timeneti?

Tikamadya, m’thupimu mumatuluka timadzi tamtundu winanso timene timatidziŵitsa kuti takhuta. Komano timadzi timeneti timachititsa kuti timadzi tokhazika munthu m’maso tija tisatuluke. Tingoti timadzi todziŵitsa munthu kuti wakhuta tikachuluka mu ubongo, timadzi tokhazika munthu m’maso timachepa m’thupi ndipo zikatere, munthu amasinza kwambiri. Mwina n’chifukwa chake m’mayiko ena anthu akamagwira ntchito amagonako pang’ono akatha kudya masana.

[Chithunzi patsamba 12]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

ZIGAWO ZA TULO

Chithunzichi n’chachidule chabe

Zigawo za Tulo

Chokhala m’maso

CHOLOTA

CHOSALOTA

Chosachedwa kudzuka 1

2

3

Chatulo tofa nato 4

1 2 3 4 5 6 7 8

Maola Ogona