Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungatetezere Ana Anu

Mmene Mungatetezere Ana Anu

Mmene Mungatetezere Ana Anu

“Makolo ndiwo makamaka angateteze ana ku vutoli. Ayenera kuwapatsa chitsanzo chabwino ndiponso kuwalangiza.”—ANATERO A DONNA SHALALA, NDUNA YA ZAUMOYO NDI ZOTHANDIZA ANTHU KU UNITED STATES.

CHONCHO inuyo makolo ndinu amene makamaka mungateteze ana anu ku vuto limeneli. Tsoka ilo, si makolo onse amene amadziŵa kufunika kwawo polimbana ndi vutoli. Mnyamata wina wa ku Brazil dzina lake Ireneu anati: “Bambo anga ankangotanganidwa ndi zinthu zina. Ankangoyankhula nafe kwa nthaŵi yochepa basi. Sankatilangiza chilichonse pa nkhani ya mankhwala osokoneza bongo.”

Komano tayerekezerani nkhaniyi ndi ya mnyamata winanso wa ku Brazil komweko, dzina lake Alecxandros. Iye anati: “Pa TV akamasonyeza za anthu amene ali ndi vutoli, bambo ankandiitana pamodzi ndi azing’ono anga onse kuti tidzaonere. Ndiye ankatiuza kuti tidzionere tokha mmene anthuwo akuvutikira chifukwa cha khalidwe lawolo. Nthaŵi zina apa ankapezerapo mwayi wotifunsa ngati tikudziŵapo ana alionse kusukulu kwathu a khalidwe lotere. Umu ndi mmene ankatichenjezera za kuopsa kwa khalidweli.”

Kodi munayamba mwakambiranako ndi ana anu za kuopsa kwa mankhwala otere? Choyamba m’pofunika kuti inuyo panokha mudziŵe kaye kuopsa kwake. Makolo achikristu angathandize ana awo kuzindikira kuti mankhwala otere amawasokoneza mwauzimu. Baibulo limatilangiza kuti thupi lathu lizikhala loyera m’njira iliyonse ngakhalenso mwauzimu. (2 Akorinto 7:1) Chizoloŵezi chophunzira Baibulo ndi ana anu chingawateteze kwambiri. *

Khalani Bwenzi Lokhulupirika

Ndibwino kuti muzikhulupirirana ndi ana anu. Yehova, ana ake a padziko lapansi amam’khulupirira. (Yeremiya 3:4) Kodi mwana wanu amakukhulupirirani? Kodi mumamvetseradi zimene mwana wanu akunena? Kodi mwana wanu amamasuka kukuuzani mavuto ake? Kodi mumaona kuti n’kwapafupi kum’kalipira kusiyana n’kum’yamikira? M’dziŵeni bwinobwino mwana wanuyo. Kodi ali ndi anzake ocheza nawo? Nanga anzakewo ndani? Pajatu Baibulo limatichenjeza kuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Musamaope kukhwimitsa malamulo ena ndi ena kapena kum’langiza mwachikondi. Baibulo limati: “Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako.”—Miyambo 29:17.

Komanso mukakhala, musamaganize kuti mwana wanu sangagwe m’vuto limeneli. Makolo ena amadzinamiza kuti poti ana awo anakulira m’banja laulemu wake, ndiye kuti sangagwe m’vuto lotere ayi. Koma Dr. José Henrique Silveira anati: “Anthu ogulitsa mankhwala otere amakonda kugwirizana ndi ana a anthu odziŵika chifukwa amadziŵa kuti malonda awo ayenda bwino.” Ndiyeno ana ena akaona kuti wachinyamata waulemu wake watengeka n’zimenezi, nawonso amangotsata zomwezo.

Motero khalani maso. Dziŵani zizindikiro zina zodziŵira munthu amene wayamba mankhwala otere. Mwachitsanzo kodi mwana wanu wangosintha mwadzidzidzi n’kuyamba kusachezeka, kumangokhala ndwii, kulunda, kapena kusamvera? Kodi wasiya kucheza ndi anzake kapena azibale ake popanda chifukwa chooneka bwino? Ngati n’choncho ndiye kuti kalipokalipo.

Osanama, makolo ena amayesetsa, koma n’zachisoni kuti ana ena amatengerabe za anzawo n’kuyamba mankhwalaŵa. Kodi mwana wanu akatero mungatani?

Mwana Akayamba Khalidweli

Ireneu anati: “Pamene makolo anga ankadziŵa kuti mng’ono wanga wayamba zimenezi n’kuti patatha miyezi ingapo iye akutero. Atadziŵa zimenezi, poyamba maganizo awo anangoti balala chifukwa sankaganizirapo n’komwe kuti mwana wobereka iwowo angadzagwe m’vuto lotereli. Panthaŵiyi bambo anga ankangoona kuti njira yabwino n’kumuthidzimula zolimba mng’ono wangayo.”

Inde, makolo akadziŵa kuti mwana wawo ali ndi vutoli, poyamba mwina amakalipa, kukhumudwa, ndiponso kumaona ngati zawakanika kulera mwanayo. Koma chikalata chimene Unduna wa Zamaphunziro ku United States unatulutsa chinati: “Ugwireni mtima! Ndipo musadziimbe mlandu. Zikatere m’pongofunika kukhazika mtima pansi n’kuyamba mwadziŵa kaye kuti vutoli lafika potani makamaka. . . . Munthu angathe kupeŵa khalidweli ndipo anthu a khalidweli angathe kulandira chithandizo kuti alisiye.”

Inde, kuti zinthu zisaipireipire m’pofunika kuchita zinthu momvetsa ndiponso mosalekerera. Mukakalipa kwambiri kapena kudzimbuka mwana wanuyo sangasiye msanga khalidweli. Komanso cholinga chanu n’chakuti mum’thandize kuti akadzakula adzakhale munthu wochita zinthu zolongosoka, woganiza zakupsa. Choncho kambiranani naye moti amvetse ubwino wosachita nawo khalidweli. Yesetsani kufufuza zimene zili mumtima mwa mwana woloŵererayo ndipo mvetserani bwinobwino zomwe akunenazo.—Miyambo 20:5.

Ireneu ananenanso kuti: “Kenaka makolo anga anasintha maganizo om’thidzimula aja n’kuyamba kum’langiza, kum’letsa kupita kwina ndi kwina ndi kumam’sinthasintha makalasi kuti asamakumanekumane ndi anzake omuwononga aja. Anayamba kum’letsa kuyenda ndi anzake ena ndi ena ndiponso kuonetsetsa zochita zake ngakhalenso za ana enafe.”

Onani njira zina zothandiza zimene makolo enanso anachita atazindikira kuti ana awo ayamba mankhwala osokoneza bongo.

Njira Zothandiza

Bambo wina dzina lake Marcelo yemwe akukhala mumzinda wa São Paulo, ku Brazil anati: “Sitinakumanepo ndi vuto losautsa ngati limeneli. Pa zochita zonse za ana athu aŵiri aamuna, palibe chilichonse chimene ineyo ndi mkazi wanga tinadabwa nacho. Nthaŵi zambiri ankakadya kumalesitilanti pamodzi ndi kagulu ka achinyamata ena amene ifeyo tinkangoti timawadziŵa bwino. Mnzathu atatiuza kuti ana athuwo amasuta chamba tinasokonezeka maganizo kwambiri. Ndiye titawafunsa anawo, sanalimbelimbe n’komwe, anangovomereza kuti zinali zoona.”

Kodi Marcelo anatani nawo ana akeŵa? Iye anavomereza kuti: “Ine ndi mkazi wanga sitinabise kuti zimenezi zatikhumudwitsa. Tinawauza kuti ifeyo chikutinyansa si iwowo ayi koma khalidwe lawolo. Tinagwirizana zakuti kuyambira pamenepo tiyesetsa kuwathandiza anawo kuti asiye mankhwalaŵa. Sitinawabisire maganizo athu, ndipo onse pauŵiri wawo anavomera kutsatira zimene tinawauzazo. Tinawauza kuti apitiriza sukulu komanso azigwira nane ntchito imene ndimagwira. Koma tinawauza kuti sadzapitanso kukasangalala ali okha. Tsiku lililonse tinkachita zinthu zosonyeza kuti timawakonda, osati pokhapokha pakachitika chinachake ayi. Poti ineyo ndimagwira ntchito ya zomangamanga, nthaŵi zambiri ndinkapita nawo kuntchito. Tinayamba kusangalala, n’kumakhala nthaŵi yaitali tikukambirana za m’tsogolo ndiponso za kufunika kokhala ndi zolinga zaphindu.” Umu ndi mmene Marcelo ndi mkazi wake anathandizira ana awo kusiya khalidwe loipali.

Taonaninso nkhani iyi ya bambo winanso wa ku Brazil konko. Mwana wawo Roberto anati: “Bambo anga atadziŵa kuti mng’ono wanga ali ndi vutoli, mmalo mom’kalipira kapena kum’thidzimula, iwo anayamba kum’tenga ngati mnzawo moti mpaka iye anayambanso kuwakhulupirira. Bambowo anayamba kudziŵa anzake onse ndi malo amene ankakonda kupitako ndipo anayamba kum’thandiza maganizo mng’ono wangayo pomuuza kuti mankhwala ndiponso anzake oterowo sanali ofunikira kwa iyeyo. Anamuuzanso kuti sakufuna zomachezera usiku wonse kufunafuna iyeyo.” Poyesa kum’thandiza maganizo mwana woloŵererayo, mayi ake om’peza anayesetsa kwambiri kuthandizana nawo amuna awo. Iwo anagwirizana zochitapo kanthu mwamsanga ndipo anaganiza kuti azim’thandizira kunyumba konko.—Onani bokosi lakuti “Kupeza Chithandizo.”

Musagwe Mphwayi!

Kulera ana “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino kumatopetsa komanso kumasautsa nthaŵi zina. (2 Timoteo 3:1) Komabe, musamaiwale mavuto anu komanso kusamalira moyo wanu wauzimu. (Mateyu 5:3) Pa Miyambo 24:10 sananame kuti: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Mukamacheza ndi Akristu oona amakulimbikitsani kwambiri. Mungalimbikitsidwe ndi kuthandizidwa kwambiri ku misonkhano ya ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.—Ahebri 10:24, 25.

Ndithu, kuphunzitsa ana anu kukhulupirira Mulungu ndiko kungakuthandizeni kwambiri polimbana ndi vutoli. Inde, Mulungu sakakamiza achinyamata kuchita zinthu zimene eniakewo sakufuna. Koma amapereka malangizo othandiza kwambiri. Pa Salmo 32:8; Mulungu amati: “Ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” Mulungu ndi Tate wathu wachikondi wokhala kumwamba ndipo amafuna kuteteza ana kuti pasapezeke chinthu chowasokoneza maganizo, kuwavulaza, ndi kuwaiwalitsa zauzimu. (Miyambo 2:10-12) Dziŵani kuti Mulungu amathandizanso makolo amene amayesetsa kuti ana awo akulire “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.

Komabe, mmene zinthu zilili masiku ano kulera ana kumasoŵetsa mtendere kwambiri nthaŵi zina. Kodi pali chilichonse chimene chingatilimbitse mtima?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mboni za Yehova zafalitsapo nkhani zimene zingathandize makolo pokambirana ndi ana awo za mankhwala osokoneza bongo. Mwachitsanzo, onani mutu 33 ndi 34 m’buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

“Munthu angathe kupeŵa khalidweli ndipo anthu a khalidweli angathe kulandira chithandizo kuti alisiye.”—CHINATERO CHIKALATA CHA UNDUNA WA ZAMAPHUNZIRO KU UNITED STATES

[Bokosi patsamba 6]

Kupeza Chithandizo

Makolo ena amaona kuti ngati mwana wawo ali ndi vutoli ndibwino kuti akathandizidwe kuchipatala. Makolo ayenera kusankha okha chithandizo chimene akufuna. Koma ndibwino kuti azifufuza bwinobwino chifukwa zipatala zimasiyana pa nkhani ya chithandizo. Arthur Guerra de Andrade, yemwe ndi katswiri wa matenda okhudza maganizo, yemwenso ndi pulofesa wa ku yunivesite ya São Paulo ku Brazil, anati ndi anthu 30 okha pa anthu 100 alionse a vutoli omwe amachira akapita kuchipatala. Motero makolo ayenera kuonetsetsa kuti mwana wawo akuthandizidwa m’njira yabwinodi, ngakhale atakhala kuti akuonana ndi madokotala odziŵa bwino ntchito yawo.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]

Mfundo Zothandiza Amene Akuyesetsa Kusiya Khalidweli

Kodi ndinu wachinyamata ndipo mukuyesetsa kuti musiye kugwiritsira ntchito mankhwala otere? Ngati n’choncho dziŵani kuti kuŵerenga Baibulo ndiponso kuchitadi zimene mukuŵerengazo kungakuthandizeni kuti musiye. N’kutheka kuti buku la Masalmo ndilo makamaka lingakuthandizeni kwambiri chifukwa chakuti lili ndi nkhani zambiri zosautsa zangati zimene zili m’maganizo mwanu panopo. Kupemphera kwa Mulungu mochoka pansi pamtima n’kothandizanso. (Afilipi 4:6, 7) Mukatero mumayamba kuona kuti Mulungu amakusamaliranidi ndiponso kuti amafuna kuti zinthu zikuyendereni bwino. Koma chifukwa chakuti Mulungu sakakamiza munthu aliyense kuti achite zinthu zimene iye sakufuna, ndibwino kuti inuyo panokha mutsimikizedi kusiya khalidwe limeneli. Wamasalmo Davide, yemwenso anathandizidwa ndi Mulungu nthaŵi zambiri anati: “Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kupfuula kwanga. Ndipo anandikweza kunditulutsa m’dzenje la chitayiko, ndi m’thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.” (Salmo 40:1, 2) Masiku anonso Mulungu amawathandiza chimodzimodzi anthu amene akufunitsitsa kusiya makhalidwe oipa kuti amutumikire.

[Chithunzi patsamba 5]

“Bambo anga ankatichenjeza za kuopsa kwa mankhwala otere”—Anatero Alecxandros

[Chithunzi patsamba 8]

Yesetsani kuwachenjeza ana anu za mmene mankhwalaŵa amamuwonongera munthu ngakhalenso mwauzimu

[Chithunzi patsamba 8]

Dziŵani anthu omwe mwana wanu amacheza nawo

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Kuchita zinthu mosapupuluma kumathandiza kuti zinthu zisaipireipire