Msonkhano Wofunika Kwambiri Pachaka
Msonkhano Wofunika Kwambiri Pachaka
Ingoyerekezerani kuti mukudwala matenda oopsa kwambiri. Matendawo ndi oti mungachire ndi opaleshoni, koma mtengo wake simungaukwanitse. Ndiye tinene kuti munthu wina wanena kuti akulipirirani opaleshoniyo. Kodi simungayamikire mphatso yake yokupulumutsaniyo?
Baibulo limatiphunzitsa kuti anthu oyambirira, Adamu ndi Hava anapatsira ana awo onse uchimo ndi imfa. Motero tinganene kuti tonsefe tinabadwa ndi matenda osachiritsika, ndipo palibe aliyense amene angakwanitse kutithandiza kuti tichire. (Salmo 49:7-9) Komano Yehova Mulungu anapereka Mwana wake, Yesu Kristu kuti atiwombole potilipirira machimo athu. Chifukwa cha mphatso yotipulumutsa imeneyi, tili ndi mwayi woti tingadzakhale m’Paradaiso kwamuyaya.—Aroma 6:23.
Lachitatu, pa April 16, dzuŵa litaloŵa, Mboni za Yehova zidzakhala zikukumbukira imfa ya Yesu. Chaka chatha panafika anthu oposa 15,000,000, ndipo ambiri sanali Mboni za Yehova. Tikukuitanani kuti chaka chino mudzakhale nafe pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Umenewu ndi msonkhano wofunikadi kwambiri pachaka. Chonde funsani Mboni za Yehova za kwanuko kuti zikuuzeni nthaŵi ndi malo ake enieni.