Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akakufulumizitsa Kumachita Zachikulu

Akakufulumizitsa Kumachita Zachikulu

Akakufulumizitsa Kumachita Zachikulu

KUNJA kunali mitambo. Ndege yaing’ono ya injini imodzi inachita chiphokoso pondondola kuti itenge mphepo, ndipo kenako inauluka kusiya nthaka. Panali atolankhani osiyanasiyana amene ankaulutsa nkhani zimene zimachitikazo, kujambula zithunzi ndiponso kufunsa mafunso osonyeza kugoma ndiponso kutama zinthu zomwe zinali kuchitikazo. Kodi n’chiyani chinakopa chidwi cha anthuŵa mpaka kufika pamenepa? Anthuŵa analibe ntchito ndi munthu wina woyendetsa ndege ndiponso bambo wina omwe anali m’ndegemo. Koma mwana wamkazi wa bamboyo ndiye anakopa anthuwo. Anali mtsikana wa zaka zisanu ndi ziŵiri.

Mtsikanayo ndiye anali woti ayendetse ndegeyo. Iye ankafuna kuti akhale munthu woyamba wa msinkhu wakewo kuchita zimene ena sanachitepo ndiponso anali ndi zinthu zina zambiri zoti achite paulendowu. Ankayembekezera kukakumana ndi atolankhani pamalo pomwe akaime akachoka apa. Choncho, ngakhale kuti kunja kunali mitambo, anthu atatuwo anakwera ndegeyo, mtsikanayo n’kukhala pa mpando pomwe anawonjezera zokhalira zina n’cholinga choti azitha kuona bwino poyendetsera ndegeyo. Komanso anawonjezera zitsulo zina kuti mapazi ake azitha kufikira akamayendetsa ndegeyo.

N’zomvetsa chisoni kuti ulendowu sunafike patali. Kunja kunayamba chimphepo, ndipo mwadzidzidzi ndegeyo inaloza kwina, n’kuzima, ndipo kenako inagwa, anthu onse atatuwo n’kufa. M’malo moti atolankhani aja afalitse nkhani zotama mtsikanayo, anapezeka kuti akufalitsa nkhani yachisoniyi. Atolankhani oŵerengeka komanso akonzi ena a manyuzipepala ananena kuti n’kutheka kuti chinanso chinachititsa ngoziyi ndi anthu ofalitsa nkhaniwo. Anthu ambiri anayamba kunena kuti ana asamayendetse ndege. Motero, ku United States anakhazikitsa malamulo ogwirizana ndi zimenezi. Komabe ngakhale kuti anthu anaikokomeza kwambiri ngoziyi, n’kufulumira kuperekapo njira zothandiza kuti mwina ngozi yotere isadzachitikenso, kwenikweni chinalipo chimene chinatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga.

Ngozi imeneyi inapangitsa anthu ena kuganizira mofatsa za khalidwe lomwe lafala panopo. Masiku ano ana sakudyerera mokwanira ubwana wawo chifukwa akufulumizitsidwa kumachita zachikulu adakali aang’ono. N’zoona kuti nthaŵi zina zotsatirapo za khalidweli sizingochitika mwadzidzidzi ndiponso sizikhala zomvetsa chisoni kwambiri chonchi. Koma zingathe kukhala zodetsa nkhaŵa kwambiri komanso zotenga nthaŵi yaitali. Tatiyeni tioneko zina zomwe zikuchitika kuti ana asamadyerere mokwanira ubwana wawo.

Kuwafulumizitsa pa Maphunziro

Makolo amafunitsitsa kuona kuti ana awo zinthu zikuwayendera, ndipotu mpake kutero. Koma makolowo akamachita kusoŵa nazo tulo zimenezi angathe kuunjikira ana awo ntchito zambiri, n’kuwapanikiza kwambiri anawo adakali aang’ono. Nthaŵi zambiri zimenezi zimayamba ngati zabwino. Mwachitsanzo, m’mayiko ena makolo ambiri ayamba kumalembetsa ana awo aang’ono kuti azichita zinthu zosiyanasiyana akaŵeruka kusukulu, monga maseŵera olimbitsa thupi, maphunziro a zoimbaimba kapenanso zovinavina. Nthaŵi zambiri anawo amakhalanso ndi mphunzitsi wapadera wowathandiza pa maphunziro awo akachoka kusukulu.

Inde, sikulakwa kulimbikitsa luso la mwana. Koma kodi zingatheke kuchita zimenezi monyanyira? Izi n’zosachita kufunsa chifukwa chakuti ana ena akuoneka kuti akupanikizika kwambiri ngati akulu amene. Magazini ya Time inati: “Kale ana ankadyerera ubwana wawo koma tsopano akulimbana n’kuphunzira zintchito; ana amafunika kumasangalala ndi nyonga zawo koma tsopano akungotanganidwa ndi zintchito.”

Makolo ena amayembekezera ana awo aang’ono kuti akhale akatswiri a zothamanga, zoimbaimba, kapena zisudzo. Ana awo asanabadwe, makolo akumakalembetseratu kusukulu zamkaka, n’chiyembekezo choti adzaimbe lokoma m’tsogolo. Komanso, amayi ena apakati akumakalembetsa ku mayunivesite ophunzitsa makanda asanabadwe, komwe amaphunzitsako ana awo zoimbaimba. Cholinga chimakhala kufuna kuti bongo wa makandawo uyambiretu kukhala wochangamuka.

M’mayiko ena ana amaphunzitsidwa luso loŵerenga ndiponso masamu asanakwanitse zaka zisanu ndi chimodzi. Zimenezi zikudetsa nkhaŵa kuti mwina zingathe kuwasokoneza anawo maganizo. Kodi chimachitika n’chiyani, mwachitsanzo, kwa mwana amene amati walephera kumkaka? Mlembi wa buku lonena za ana lakuti The Hurried Child, a David Elkind, ananena kuti sukulu zimathamangira kugaŵa ana m’magulu. Mlembiyu anati, sukulu zimachita zimenezi pofuna kuona mmene aziziyendetsera osati n’cholinga choti ziwaphunzitse bwino anawo.

Kodi kupanikiza ana kuti akhale ngati anthu akuluakulu pamene adakali makanda kuli ndi vuto lililonse? A Elkind akuda nkhaŵa ndi khalidwe losenzetsa ana mavuto a anthu akuluakulu. Iwo anati: “Zikungosonyeza chizoloŵezi chathu chomaona ngati kuti mavuto osatha omwe achinyamata a masiku ano akukumana nawo si mavuto ayi.” Inde, zikuoneka kuti nthaŵi ndi nthaŵi anthu akusintha maganizo awo pankhani ya mmene mwana ayenera kukhalira.

Kuwafulumizitsa Kuti Azipambana

Zikuoneka kuti makolo ambiri sakuona chachilendo chilichonse, mwinanso akumaona kuti ndi bwino kuphunzitsa ana awo kuti kupambana n’kofunika kwambiri, makamaka pa maseŵera. Mendulo zimene anthu amalandira ku maseŵera a Olympic zikudolora mitima ana ambiri masiku ano. Pofuna kupeza ulemelero wa kanthaŵi kochepa womwe munthu amalandira akapambana ndiponso pofuna kuti akadzakula adzakhale ampondamatiki, ana ena saudyerera kwenikweni ubwana wawo kapena mwinanso osaudyerera n’komwe.

Taganizirani za akazi amene amachita maseŵera monga otembenuka munthu ali m’malere. Amayamba ali aang’ono kwambiri kuchita zinthu zolimba mapeto zomwe zimapanikiza kwambiri timatupi tawo. Amatha zaka akukonzekeretsa maganizo ndi matupi kuti adzachite nawo mipikisano ya Olympic. N’zoona kuti pa mipikisanoyo anthu ochepa okha ndiwo amapambana. Kodi olepherawo amaona kuti zotsatira za mipikisanoyo zinali zofunikadi kutherapo nthaŵi yaitali ya ubwana wawo? Pang’ono ndi pang’ono, ajanso amene apambana angayambe kukayikira ngati kupambanako kukugwirizana ndi kukonzekera komwe kunawatengera nthaŵi yaitali ya ubwana wawo.

M’posatheka kuti atsikanaŵa akhale opanda nkhaŵa zilizonse chifukwa chakuti mitima yawo imakhala dyokodyoko kufuna kudzakhala akatswiri a maseŵera olimbitsa thupi. Koma matupi awo angathe kupinimbira ndi zinthu zolimba zomwe amachita pokonzekera mipikisanoyo. Atsikana ena mafupa awo sakula bwino. Amakhala ndi vuto pa nkhani ya kudya. Nthaŵi zinanso, amachedwa kutha msinkhu, mwina ndi zaka zingapo. Komabe, masiku ano atsikana ambiri akukumana ndi vuto losiyana ndi limeneli, akumatha msinkhu adakali aang’ono kwambiri. Onani bokosi lili pamwambali.

Ana Osasoŵa Chilichonse Kupatulapo Ubwana Wawo

Ngati mumakhulupirira zimene amafotokoza m’nkhani zokhudza zosangalatsa, mungathe kuganiza kuti akati kusangalala ndi ubwana amatanthauza kukulira pakhomo losasoŵa kanthu. Makolo ena amagwira ntchito kwambiri n’cholinga chopezera ana awo zinthu zosiyanasiyana zoti azisangalala nazo, monga pogona pabwino, kukhala ndi zosangalatsa zambirimbiri, ndiponso zovala zapamwamba kwambiri.

Komabe, ana ambiri oleredwa mwanjira imeneyi amayamba kumwa mowa, kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, ndiponso sakhala ochezeka ndipo amakhala opanduka. Chifukwa chiyani? Ambiri amawawidwa mitima chifukwa choona kuti akunyalanyazidwa. Ana amafuna makolo achikondi ndiponso owasamalira. Makolo omwe amalephera kuchita zimenezi chifukwa chotanganidwa angathe kumaona ngati kuti akutero pofuna kuti ana awo azikhala mosangalala, koma kwenikweni potero amakhala akuwavutitsa anawo.

Ponena za “makolo olemera amene onse aŵiri amagwira ntchito,” Dr. Judith Paphazy anati iwo nthaŵi zambiri “amalekerera ana awo chifukwa chosadziŵa kuti banja lawo likupwetekeka chifukwa chakuti iwo ngokonda chuma.” Iyeyu amaona kuti, makolo oterowo ‘amangofuna kupeza pozembera udindo wawo waukholo.’

Nthaŵi zambiri anawo amavutika kwambiri. Ngakhale atakhala ndi zinthu zambiri, anawo sakhala ndi mpata wokhala ndi makolo awo kapena kusonyezedwa chikondi chawo zomwe n’zofunika kwambiri kuti mwana asangalale ndi ubwana wake. Adakali aang’ono, anawo mosayembekezera amayamba kulimbana okha ndi nkhani zofunika anthu achikulire chifukwa choti alibe munthu wowalangiza. Amalimbana ndi mafunso monga akuti, ‘Kodi ndiyambe mankhwala osokoneza bongo? Kodi ndiyambe kugona ndi atsikana kapena ndi anyamata? Kodi ndizichita ndewu n’kakalipa?’ N’zotheka kuti angapeze mayankho a mafunsoŵa kuchokera kwa ana anzawo kapena anthu a pa TV mwinanso kwa anthu a m’mafilimu. Nthaŵi zambiri, zotsatira zake zimakhala zongotsekerezeratu ubwana wawowo kapenanso kuwadzetsera mavuto kumene.

Kuona Mwana Ngati Mayi Kapena Bambo

Banja limene lili ndi makolo onse aŵiri likasintha mwadzidzidzi n’kukhala banja la kholo limodzi, kaya chifukwa cha imfa, kunyanyalana, kapena kusudzulana, nthaŵi zambiri maganizo a ana amasokonekera. N’zoona kuti mabanja ambiri a kholo limodzi amayenda bwinobwino. Koma m’mabanja ena, ana amawafulumizitsa kuyamba kumachita zachikulu.

Mpomveka kuti mayi kapena bambo yemwe akulera yekha ana nthaŵi zina angathe kusungulumwa. Komabe, zimenezi zimachititsa makolo ena kuti aziona mwana wawo ngati mayi kapena bambo m’banjamo, ndipo nthaŵi zambiri mwanayo amakhala wamkulu pa onse. Mwina chifukwa chovutika maganizo, makolo otere angathe kumafotokozera mwana wawo wamwamuna kapena wamkazi zakukhosi kwawo, n’kumuunjikira mwanayo mavuto omwe si amsinkhu wake. Makolo ena omwe ali okha amayamba kudalira kwambiri mwana wawoyo kuti aziwathandiza maganizo.

Makolo ena ndiye amangotuliratu pansi udindo wawo wonse waukholo, zomwe zimachititsa mwana kukhala ngati munthu wamkulu m’banjamo. Pamene Carmen ndi mlongo wake, omwe tawatchula poyamba paja ankakayamba kukhala m’misewu, n’kuti zinthu zili choncho kunyumba kwawo. Iwowo anali adakali ana, koma anali ndi udindo woyang’anira azing’ono awo. Inali ntchito yaikulu kwambiri kwa iwo.

Mosakayikira, khalidwe lofulumizitsa ana kumachita zachikulu ndi loopsa kwambiri ndipo n’lofunika kuyesetsa kulipeŵa ngati zingatheke. Koma pali nkhani yabwino: Anthu akuluakulu angachite zinthu zothandiza kuonetsetsa kuti ana awo akudyerera ubwana wawo. Kodi ndi zinthu zotani? Tiyeni tione mayankho omwe akhala akugwira ntchito kwa nthaŵi yaitali.

[Bokosi patsamba 16]

Vuto la Kutha Msinkhu Mwamsanga

Kodi masiku ano atsikana akumatha msinkhu adakali aang’ono? Mayankho a akatswiri a sayansi pafunsoli amatsutsana kwambiri. Ena amanena kuti chamkatikati mwa zaka za m’ma 1800, atsikana ambiri ankatha msinkhu akakwanitsa zaka 17, pamene masiku ano atsikana ambiri akumatha msinkhu asanakwanitse zaka 13. Malinga ndi kufufuza komwe anachita mu 1997 pakati pa atsikana 17,000, anapeza kuti atatu pa atsikana 20 alionse achizungu ndiponso mmodzi pa atsikana aŵiri alionse achikuda m’dziko la United States amasonyeza kuti atsala pang’ono kutha msinkhu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu! Komabe madokotala ena amatsutsa zimenezi ndipo amachenjeza makolo kuti asamangovomereza kuti ‘n’chibadwa’ kuti mtsikana athe msinkhu adakali wamng’ono kwambiri.

Zilibe kanthu kuti pali kusiyana maganizo kumeneku, koma zimenezi zikudzetsa mavuto kwa makolo ndiponso kwa ana. Magazini ya Time inathirirapo ndemanga kuti: “Chodetsa nkhaŵa kwambiri kuposa kuoneka ngati aakulu n’chakuti ana omwe amafunika kuti aziŵerenga nthano, osati kulimbana ndi zidyamakanda, angathe kuwonongeka maganizo chifukwa choti amakhala atafika pakuti angathe kugona ndi amuna. . . . Motero nthaŵi yodyerera ubwana wawo imakhala yaifupi kale.” Nkhaniyo inafunsa funso ili lomwe ndi lovutitsa kwambiri: “Ngati matupi a atsikana ang’onoang’ono amawapangitsa kuti azioneka ngati akuluakulu pamene atsikanawo adakali ana mu mtima ndi m’maganizo, kodi chingasokonezeke kwa moyo wawo wonse n’chiyani?”

Nthaŵi zambiri khalidwe lawo ndilo limasokonezeka chifukwa ana oterowo amaphunzitsidwa zoipa mwa kuwagona. Mayi wina anayankhula mosapsatira mawu kuti: “Atsikana omwe amaoneka okhwima ndithu poyerekeza ndi zaka zawo . . . amadolola anyamata akuluakulu.” Kukakamizika kuchita zachiwerewere munthu udakali wamng’ono n’koopsa kwambiri. Mtsikana angathe kudzichotsa ulemu, sangakhale ndi chikumbumtima chabwino, ndiponso angasokonezeke maganizo komanso angathe kutenga matenda.

[Chithunzi patsamba 15]

Kuunjikira ana ntchito kungathe kuyambitsa mavuto

[Chithunzi patsamba 17]

Kukakamiza ana kuti akhale akatswiri pa maseŵera kungachititse kuti maseŵerawo asamasangalatse

[Chithunzi patsamba 17]

Chuma sichingalere mwana ngati kholo