Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndinakhaliranji Mwana wa Makolo Amene Sanandibereke?

Kodi Ndinakhaliranji Mwana wa Makolo Amene Sanandibereke?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndinakhaliranji Mwana wa Makolo Amene Sanandibereke?

“Zimangokhala ngati ndili ndi chilema. Zimandipweteka kwambiri.”—Anatero Robert.

MKULU ameneyu anangoti atabadwa makolo ena anam’tenga kukhala mwana wawo ndipo apa ankafotokoza mmene zimakhalira kwa iye. Iye anapitiriza kunena kuti: “Tsiku lililonse umangokhalira kuvutika ndi mafunso onga akuti, Kodi makolo anga enieni ndani? Kodi amakhala kuti? N’chifukwa chiyani anandikana?”

Mtsikana wina dzina lake Chantial, yemwe bambo wake analeredwa ndi makolo osakhala owabereka, amadandaula kuti sadziŵa n’komwe azigogo ake enieni. Iye anati: “Zimandiwawa chifukwa chosakhalako ndi amalume, azakhali, ndi asuwani anga enieni.” Si ana onse ongotengedwa kukhala ana a makolo ena amene amakhala ndi maganizo otere. Koma ena amakhala nawo. N’chiyani chimawapangitsa kutero?

Zimakwiyitsa

Mwana akadziŵa kuti anachotsedwa m’manja mwa achibale ake enieni, amatha kuvutika kwambiri ndi maganizo. Catrina, yemwe makolo ena anam’tenga kukhala mwana wawo adakali wamng’ono kwambiri, anati: “Vuto limene ndinali nalo n’lakuti ndinkakwiya kwambiri chifukwa chosamvetsa kuti amayi anga analoleranji zimenezo. Ndinkangoti amayiwo sankandifuna chifukwa chakuti ndinali wonyansa moti sangandikonde ayi. Akanangondisiya kuti ndizikhalabe nawo, ndikhulupirira kuti bwenzi nditayesetsa kuti azinyadira nane. Ndinkakwiya kwambiri ndikangoganizira za amayi angawo.”

Komanso, Catrina sankakhalitsana bwino ndi makolo amene anam’tengawo. Iye anati: “Ndinkangoti iwoŵa ndiwo anachita kundichotsa m’manja mwa amayi anga. Choncho ndinkathera ukali wanga wonsewo pa iwowo.” Inde, nthaŵi zina n’zimene zimachitika kuti makolo ena akatenga mwana kukhala wawo, mwanayo amakwiya.

Nthaŵi zina kukwiya koteroko kumakhala kodzetsa mavuto. Nkhani ya Catrina ikusonyeza kuti nthaŵi zina mukhoza kukwiya mosayenerera kapenanso kukwiyira anthu osalakwa. Baibulo limalangiza kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo.” (Salmo 37:8) Kodi zimenezo zingatheke bwanji? Pajatu Mawu a Mulungu amanenanso kuti: “Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.” (Miyambo 19:11) Kulingalira, kapena kumvetsa mmene zinakhalira kwa inuyo kungakuthandizeni kuti musakwiye kwambiri. Zingatheke bwanji?

Musamaganize Molakwika

Kulingalira kungakuthandizeni kuonanso bwino maganizo amene akukupangitsani kukwiya. Mwachitsanzo, ngati anthu ena anakutengani kukhala mwana wawo, kodi mukuganiza kuti makolo anu anakuperekani chifukwa chakuti sankasangalatsidwa nanu? Zimenezo n’zimene Catrina ankaganiza. Koma kodi zimakhaladi choncho nthaŵi zonse? Mwina simungathe kudziŵa chimene chinachititsa makolo anu kuti atero, koma ndibwino kupeŵa kuganiza molakwika choncho. Ndipo kodi n’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri makolo amapereka ana kwa anthu ena kuti akhale awo? Nthaŵi zambiri makolowo amakhala ataona kuti sangachitirenso mwina ayi.

Taganizirani chitsanzo cha Mose. Nkhani ya m’Baibulo imene ili m’buku la Eksodo chaputala 2 imatiuza kuti Farao wa ku Igupto atalamula kuti makanda onse aamuna a Israyeli aphedwe, amayi ake a Mose, a Yokobedi anakhala akubisa khandalo kwa miyezi itatu. Kenaka anayamba kusoŵa pom’bisa, komabe sakanatha kupirira kuona mwana wawo akuphedwa. Choncho “pamene sanathe kum’bisanso, anam’tengera kabokosi ka gumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m’mbali mwa nyanja.”—Eksodo 2:3.

Sitikukayikira kuti kusiya mwana wawoyo m’njira yotereyi kunali kowavuta kwambiri. Koma nanga akanatani? Pom’konda mwanayo, anachita zimene anaona kuti zingam’thandize. N’zochititsa chidwi kuti mwana wawo wina wamkazi anangoima poteropo n’kumayang’anira khandalo mpaka pamene anaona kuti kamchimwene kakeko katoledwa bwinobwino. N’kutheka kuti amayi akewo omwe analibenso pogwira ndiwo amene anamuuza kuti adikirire pompo.

Apatu sitikunena kuti anthu onse amene anatengedwa kukhala ana amakolo ena anaperekedwa pazifukwa zochita kuonekeratu ngati mmene taonera mu nkhaniyi ayi, koma nthaŵi zambiri cholinga chochitira zimenezo chimakhala chofanana. Robert anati: “Ine, ndine mwana wa pathengo. Ndiye mayi anga akanavutika kwambiri kundilera chifukwa chakuti pakhomopo panalinso ana ena. N’kutheka kuti mayi angawo anangoganiza kuti zinthu zingandikhalire bwino ngati anthu ena atanditenga.”

Zifukwa zoti makolo angopereka ana kwa anthu ena kuti awalere zilipodi zambiri ndithu. Koma zitsanzozi zikusonyeza kuti makamaka sichikhala chifukwa chakuti amayi akudana ndi khanda lawolo kapenanso kuti aona chilema pa mwanayo. Nthaŵi zambiri, mayiyo amakhala akukhulupirira ndi mtima wonse kuti mwanayo angakule bwino ataleredwa ndi anthu ena.

Kukondedwa N’kofunika

Kukhala munthu wolingalira bwino kungakuthandizeninso mukayamba kuganizira chifukwa chimene makolo ena anakutengerani. Taganiziraninso chitsanzo cha Mose uja. Patapita kanthaŵi, “anam’tola mwana wamkazi wa Farao, nam’lera akhale mwana wake.” (Machitidwe 7:21) N’chiyani chinam’chititsa mwana wa Farao kuti mpaka afike poteteza mwana wa Ahebri yemwe ankachita kudziŵiratu kuti anali woyenera kuphedwa? Baibulo limati: ‘Khandalo linkalira. Ndipo anamva naye chifundo.’ (Eksodo 2:6) Mwaonatu, Mose anakaleredwa ndi anthu ena chifukwa chom’konda, osati kudana naye kapena kusam’funa ayi.

Ana ambiri amene amakhala a anthu amene sanawabereke amadzazindikira kuti makolo awo sanangowataya basi, ngakhale kuti zimenezo n’zimene zikuchitika kaŵirikaŵiri masiku anoŵa, koma kuti anawasiya m’manja mwa mabungwe ena oona zosamalira ana. Ndipo anthu ena anawatenga chifukwa chowakonda kwambiri kuti awasamalire. Kodi sizingatheke kuti ndi mmene zinakhaliranso ndi inuyo? Simungamavutikenso maganizo kwambiri mukamaganizira kuti wina anakutengani chifukwa cha chikondi ndiponso mukamayamikira zimene anachitazo.

Komanso anthu ena osangoti amene akukuleraniwo angathe kumakukondaninso. Ngati muli mumpingo wa Chikristu, mukhoza kukhala ndi madalitso okhala ndi azimayi, azibambo, azichemwali, ndi azichimwene auzimu amene amakukondani. (Marko 10:29-30) Akulu Achikristu ‘angakhale monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.’ (Yesaya 32:2) Musaope kupeza Akristu anzanu achikulire n’kuwauza zakukhosi kwanu. Musawabisire zimene mukuganiza ndi mmene mukumvera.

Robert amaona kuti ndibwino kwambiri kumakondana ndi anthu a mumpingo wanu wa Chikristu. Iye anavomereza kuti: “Ndimadandaulabe chifukwa ndilibe abale anga enieni a kubere lathu. Komabe chikondi cha abale anga auzimu chimandithandiza kuiwalako zimenezo.”

Zinthu Zingakuyendereni Bwino

Choncho musamaganizire zinthu molakwika, monga kuganizira kuti poti ndinu mwana wa makolo amene sanakuberekeni ndiye kuti zinthu sizingakuyendereni bwino. Maganizo otereŵa angakulefuleni kwambiri! (Miyambo 24:10) Komanso choti mudziŵe n’chakuti zimenezo n’zongoganizira basi.

Musaiwale kuti Mose anagwiritsira ntchito mwayi umene anali nawo. Baibulo limati: “Mose anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto; nali wamphamvu m’mawu ake ndi m’ntchito zake.” (Machitidwe 7:22) Chofunika kwambiri n’chakuti Mose anamvetsa kwambiri malangizo auzimu, moti mpaka sanakayike n’komwe kuti Atate wake wakumwamba, Yehova, alikodi. (Ahebri 11:27) Kodi zinthu zinam’yendera m’moyo wake?

Ndithudi, Mose anadzakhala mtsogoleri wa anthu ambiri kwabasi, mwina okwanira 3 miliyoni kapena kuposa pamenepo. Anadzakhala mneneri, woweruza, mkulu wa asilikali, wolemba mbiri yakale, mkhala pakati wa pangano la Chilamulo, ndiponso analemba mabuku asanu oyambirira a m’Baibulo. Komanso anthu ambiri amakhulupirira kuti ndiye analemba mabuku a Yobu ndi Salmo 90. Zoonadi, zinthu zinam’yendera bwino kwambiri Mose. Zinthu zimawayenderanso bwino ana ambiri a makolo amene sanawabereke, ndipo inunso zingakuyendereni.

Robert anakwanitsa bwinobwino kulera ana ake aŵiri ndipo panopa ndi mkulu mumpingo wa Chikristu. Poganizira zakale ali m’manja mwa makolo amene sanam’bereke, iye anati: “Ndaphunzira kuti madzi akatayika sawoleka, choncho ndi bwino kuti ndizingoyamikira madalitso amene ndili nawo.”

Ngati panopa mukuleredwa ndi anthu ena kapena ngati munatengedwa kukhala mwana wa makolo ena, sizingalephereke kuti nthaŵi zina muzikhala ndi maganizo olakwika. Koma muziyesetsa kuiwala zimenezo n’kumaganiza zina zabwino. Afilipi 4:8, 9 amalonjeza kuti “Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu” ngati ‘mutamalingalira’ zinthu zimene zimakondweretsa Mulungu. Ndiye kodi njira zina zothandiza zimene mungachite kuti zinthu zikuyendereni bwino mukamakhala ndi makolo amene sanakuberekeni n’zotani? Funso limeneli lidzayankhidwa mtsogolomu m’nkhani ina yotere.

[Zithunzi patsamba 32]

Makolo amene sanakuberekeni akamakulerani ndi umboni wakuti anakukondani kwambiri mwakuti analolera kukutengani n’kumakusamalirani