Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Umodzi wa Akristu Umalira Kuchita Chilichonse Mofanana?

Kodi Umodzi wa Akristu Umalira Kuchita Chilichonse Mofanana?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Umodzi wa Akristu Umalira Kuchita Chilichonse Mofanana?

MASIKU ano zikuoneka ngati m’zipembedzo mulibe umodzi. Ngakhale anthu atchalitchi chimodzi akumatha kukhulupirira zinthu zosiyana ndi anzawo pankhani ya chiphunzitso ndiponso ya makhalidwe abwino. Munthu wina wolemba nkhani anafotokoza zimenezi motere: “Zafika mpaka povuta kupeza anthu aŵiri amene amakhulupirira Mulungu mmodzi yemweyo. Masiku ano, zikungokhala ngati munthu aliyense ali ndi njira yake yodziŵira za Mulungu.”

Mosiyana kwambiri ndi zimenezi, mtumwi Paulo anadandaulira Akristu a ku Korinto m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino kuti ‘anene chimodzimodzi’ ndi kuti ‘azimvana ndi mtima umodzi ndiponso kukhala n’cholinga chimodzi.’ (1 Akorinto 1:10) Anthu ena masiku ano amatsutsa zimene Paulo ananenazi. Iwo amati, ‘Anthu ndi osiyana, ndipo n’kulakwa kulimbikira kuti Akristu onse aziganiza kapena kuchita zinthu mofanana.’ Koma kodi tinene kuti Paulo ankanena kuti Akristu azimvera chilichonse popanda kuganizapo n’komwe? Kodi Baibulo limalola kuti munthu akhale ndi ufulu wake payekha?

Umodzi, Osati Kuchita Zilizonse Mofanana

M’kalata yake ina, Paulo analimbikitsa Akristu kuti potumikira Mulungu aziganizapo mozama. (Aroma 12:1) Ndiye n’zoonekeratu apa kuti iye sanali kuyesa kuchititsa Akristu a mumpingo wa ku Korinto kuti azingotsatira zilizonse mosaganiza n’komwe. Koma n’chifukwa chiyani anawauza kuti ‘azimvana kwenikweni ndi mtima umodzi ndiponso ndi cholinga chimodzi’? Paulo anawalangiza kutero chifukwa chakuti mpingo wa ku Korinto unali ndi mavuto aakulu. Anthu anayamba kusankhana, moti ena ankam’tenga Apolo ngati mtsogoleri wawo pamene ena ankakonda Paulo kapena Petro kapenanso Kristu basi. Kusagwirizana kumeneku siinali nkhani yoyenera kuitenga mwachibwanabwana, chifukwatu mpingowo sunalinso pamtendere.

Paulo ankafuna Akorinto kuti akhale ndi ‘mzimu wa umodzi pokhala mwamtendere,’ monga mmene anadzalimbikitsira Akristu a ku Efeso. (Aefeso 4:3) Iye ankalimbikitsa abalewo kuti azitsatira Yesu Kristu mogwirizana, osati kuti agaŵanike n’kukhala magulu osagwirizana, kapena kukhala anthu ampatuko. Motero akanakhala pamtendere ali ogwirizana pazochita zawo. (Yohane 17:22) Choncho malangizo amene Paulo anauza Akorinto anawathandiza kuti asinthe mmene amaganizira n’kuwalimbikitsa kuti akhale ogwirizana, osati azichita zilizonse mofanana.—2 Akorinto 13:9, 11.

Umodzi ndi wofunikanso pankhani ya chiphunzitso. Otsatira a Yesu amazindikira kuti palidi “chikhulupiriro chimodzi,” mongadi kulili chabe “Mulungu mmodzi ndi Atate.” (Aefeso 4:1-6 ) Motero Akristu amaonetsetsa kuti zimene amakhulupirira n’zogwirizana ndi choonadi chimene Mulungu wachisonyeza poyera m’Mawu ake, chokhudza iyeyo ndi cholinga chake. Chikhulupiriro chawo n’chimodzi pa nkhani yakuti Mulungu ndani ndi kuti amafuna kuti tizichita zotani. Amachitanso zinthu mogwirizana ndi makhalidwe abwino kwambiri amene analembedwa m’Mawu a Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Pochita zimenezi Akristu amakhalabe ogwirizana, kaya pa chiphunzitso kapenanso pa makhalidwe awo.

Pakakhala Makonda Osiyanasiyana

Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti Mkristu aliyense amachita kuuzidwa mmene ayenera kumaganizira kapena zimene ayenera kuchita m’moyo wake wonse. Nkhani zambiri zimakhala za kadziŵamwini. Taonani chitsanzo ichi. Akristu ambiri a ku Korinto m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino sankafuna kudya nyama imene ankaikayikira kuti mwina yachokera ku kachisi wamafano. Ena ankakhulupirira kuti kudya nyama yoteroyo kunali kofanana ndi kulambira konyenga, ndipo ena ankaona kuti zilibe ntchito kuti nyamayo yachokera kuti. Pothetsa nkhani yovutayi, Paulo sanaike lamulo louza Akristu chochita. Koma iye ankazindikira kuti anthu akhoza kusankha mosiyana pankhaniyi. *1 Akorinto 8:4-13.

N’kutheka kuti masiku ano Akristu angaganize mosiyana ndi Akristu anzawo pankhani ya ntchito, mankhwala, zosangalatsa, kapena zinthu zina zimene munthu angathe kusankha payekha. Zinthu zoterezi zikhoza kuwasokoneza ena. Angamadabwe ngati kukonda zinthu zosiyanasiyana kungachititse kuti mumpingo mukhale mikangano kapena magaŵano. Komabe, zimenezi sikuti n’zosapeŵeka ayi. Nachi chitsanzo: Oimba nyimbo amakhala ndi nsambo zoŵerengeka pa gitala lawo limene amaimbira nyimbo, koma angathe kuimba nyimbo zosaŵerengeka ndi nsambo zoŵerengekazo. N’chimodzimodzinso ndi Akristu. Nawonso amasankha zochita zosiyanasiyana koma zosasemphana ndi mfundo za Mulungu. Koma ufulu wochita zinthu paokha amakhala nawo ndithu.

Kodi zimatheka bwanji kuti Akristu akhalebe ogwirizana kwinaku osaloŵerera zimene Mkristu mnzawo wasankha payekha? Chachikulu n’chikondi basi. Kukonda Mulungu kumatichititsa kuti tikhale ofunitsitsa kumvera malamulo ake. (1 Yohane 5:3) Kukonda anzathu kumatichititsa kuti tisanyoze ufulu wawo wochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chawo. (Aroma 14:3, 4; Agalatiya 5:13) Paulo anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi pomvera malangizo a bungwe lolamulira la m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino pankhani yokhudza chiphunzitso. (Mateyu 24:45-47; Machitidwe 15:1, 2) Panthaŵi yomweyo, iye analimbikitsa aliyense kusanyoza chikumbumtima cha Mkristu mnzake pankhani zoti munthu angadziŵe yekha zochita.—1 Akorinto 10:25-33.

N’zoonekeratu apa kuti munthu aliyense sayenera kunyozedwa chifukwa chochita zinthu mogwirizana ndi chikumbumtima chake ngati sizikusemphana ndi mfundo za m’Baibulo. (Yakobo 4:12) Komabe ufulu umenewu suyenera kuchititsa Akristu okhulupirika kuti aziumirira kuchita zinthu zoti zingawononge chikumbumtima cha ena kapena zimene zingasokoneze umodzi wa mpingo. Kapenanso kuchita chinachake chomwe chikuchita kuonekeratu kuti n’choletsedwa ndi Mawu a Mulungu n’kumati ali ndi ufulu wochita zimene akufuna. (Aroma 15:1; 2 Petro 2:1, 19) Kukonda Mulungu kuyenera kutilimbikitsa kusintha chikumbumtima chathu kuti chigwirizane ndi maganizo a Mulungu. Tikatero, padzakhala umodzi pakati pa ifeyo ndi okhulupirira anzathu.—Ahebri 5:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mwachitsanzo, n’zotheka kuti ena amene ankalambira mafano asanakhale Akristu sankatha kusiyanitsa kudya nyama ndi kuchita zinthu zokhudzana n’kulambira. Chifukwa china chomveka n’chakuti Akristu osakhwima chikhulupiriro akanatha kuiona nkhaniyi molakwika n’kukhumudwa.