Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Matenda a Shuga “Amapha Mosadziŵika”

Matenda a Shuga “Amapha Mosadziŵika”

Matenda a Shuga “Amapha Mosadziŵika”

ALI NDI zaka 21, Ken anayamba kumamva ludzu losatherapo komanso lodabwitsa. Ndipo sankati wapita liti kokataya madzi, mpaka anafika pomataya madzi mphindi 20 zilizonse. Posakhalitsa Ken anayamba kulemedwa miyendo ndi manja ake. Ankamva kutopa kwamatenda ndipo anayamba kuona movutikira.

Vuto lake anadzalidziŵa atadwala chimfine. Anapita kuchipatala n’kukamuuza kuti vuto lake si chimfine chokha ayi, koma analinso ndi mtundu woyamba wa matenda a shuga. Matenda ameneŵa amasokoneza thupi kuti lizilephera kugwiritsira ntchito zakudya zinazake zofunika m’thupimu, makamaka shuga. Ken anagonekedwa m’chipatala mwezi umodzi ndi theka asanayambe kupeza bwino.

Tsopano patha zaka zoposa 50 zimenezi zitachitika ndipo kwabwera njira zabwino zothandizira odwala matendaŵa. Koma Ken akudwalabe matenda a shuga, ndipotu si yekhayu ayi. Akuti mwina padziko lonse pali anthu oposa 140 miliyoni odwala matendaŵa, ndipo bungwe loona zaumoyo padziko lonse linati anthuŵa angathe kuchuluka moŵirikiza pofika chaka cha 2025. Mpake kuti akatswiri akuda nkhaŵa ndi kufala kwa matendaŵa. Dr. Robin S. Goland, yemwe anayambitsa nawo chipatala chinachake cha matendaŵa ku United States anati: “Tikaganizira za kuchuluka kwa odwala matenda a shuga tikutha kuona kuti mwina ichi n’chiyambi cha mliri.”

Taonani nkhani zachidule izi za padziko lonse.

AUSTRALIA: Bungwe loona za matenda a shuga padziko lonse la ku Australia, linati “m’zaka za m’ma 2000 zino, matenda a shuga ali m’gulu la matenda ovuta kwambiri kuchiza.”

INDIA: Kuli odwala matendaŵa 30 miliyoni kapena kuposa. Dokotala wina anati: “Pafupifupi zaka 15 m’mbuyomu panalibe munthu aliyense wa zaka zosapitirira 40 wodwala matendaŵa. Koma panopo theka la onse odwala matendaŵa amakhala a zaka zimenezi.”

SINGAPORE: Pafupifupi munthu mmodzi pa anthu atatu aliwonse a zaka 30 mpaka 69 ali ndi matenda a shuga. Ana ambiri ena a zaka 10 zokha apezeka ndi matendaŵa.

UNITED STATES: Kuli odwala matendaŵa pafupifupi 16 miliyoni, ndipo chaka chilichonse anthu pafupifupi 800,000 amawapeza nawo. Anthu ena ambirimbiri ali ndi matendaŵa koma eniake sadziŵa.

Matendaŵa amavuta kuchiza chifukwa chakuti munthu amatha kukhala nawo kwa nthaŵi yaitali asanam’peze nawo. Magazini yotchedwa Asiaweek inati, “nthaŵi zambiri matendaŵa anthu sawazindikira chifukwa chakuti akamayamba kumene sachita kum’pezeketsa wodwalayo ayi.” N’chifukwa chake matenda a shuga amawanena kuti ndi matenda opha mosadziŵika.

Pakuti matendaŵa ngofala ndiponso ngoopsa, nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso aŵa:

● Kodi chimayambitsa matendaŵa n’chiyani?

● Kodi anthu amene ali ndi matendaŵa angapirire nawo bwanji?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 4]

Panachokera Dzinali M’Chingelezi

Dzina la Chingelezi la matenda a shuga limachokera ku liwu la Chigiriki lotanthauza “kupopa” ndiponso ku liwu la Chilatini lotanthauza “kutsekemera ngati uchi.” Mawu ameneŵa ngoyenereradi matendaŵa chifukwa madzi oloŵa m’thupi mwa wodwalayo amangodutsamo ngati kuti winawake akungowapopa kuchokera mkamwa n’kungopitirira mpaka kukawakodza. Chinanso n’chakuti mkodzowo umakhala wotsekemera chifukwa umakhala ndi shuga. Moti kale asanatulukire njira zabwino zamakono, njira ina yodziŵira ngati munthu ali ndi matenda a shuga inali yothira mkodzo wake pafupi ndi chulu cha nyerere. Ndiye nyererezo zikaunjirira mkodzowo ankadziŵa kuti uli ndi shuga.