Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Baibulo Lingathandizire Odwala Matendaŵa

Mmene Baibulo Lingathandizire Odwala Matendaŵa

Mmene Baibulo Lingathandizire Odwala Matendaŵa

KUTI anthu odwala matendaŵa akhale athanziko ndiponso kuti azipezako bwino, makamaka mpofunika kuti akhale odziletsa ndiponso asamaganizire kwambiri za matendaŵa. Koma kuti odwalawo akhale otero afunika kuwachitira zinthu zothandiza nthaŵi zonse. Choncho si bwino kuti achibale ndiponso anzawo aziwaika dala pachiyeso kuti adye zakudya zosayenderana ndi matenda awo, mwina powanyengerera kuti, ‘Ingodyani pano pokha basi, palibe chichitike.’ Harry, yemwe ali ndi matenda a mtima ndiponso matenda a shuga a mtundu wachiŵiri, anati: “Mkazi wanga amachita zinthu zondithandiza kwambiri. M’nyumba mwathu sasungamo zakudya zimene ineyo sindifunika kudya. Koma ena samvetsa ayi, ndipo sadziŵa kuti kusunga zakudya zimene wodwalayo safunika kudya n’kumuika pachiyeso.”

Ngati nthaŵi zambiri mumakhala ndi munthu amene ali ndi matendaŵa, musaiwale mfundo ziŵiri zotsatirazi zochokera m’Baibulo zomwe n’zothandiza kwabasi. Mfundo zake n’zakuti: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake,” ndiponso “Chikondi . . . sichitsata za mwini yekha.”—1 Akorinto 10:24; 13:4, 5.

Anthu onse amene amaganizira thanzi lawo, kaya ali ndi matendaŵa kapena ayi, ayenera kusamala pa nkhani ya zakudya. Baibulo limatithandiza pankhaniyi chifukwa limasonyeza kuti tonsefe timafunika kukhala odziletsa. Kodi mumalakalaka mutakhala munthu wodziletsa? (Agalatiya 5:22, 23) Chinanso chingatithandize ndi zitsanzo za m’Baibulo monga chitsanzo cha mtumwi wachikristu, Paulo. Munthu wina wodwala matendaŵa anati Paulo “anali ndi munga m’thupi nthaŵi zonse koma ankatumikirabe Mulungu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse. Ndiye ine n’lekerenji?”

Inde, Paulo sanalimbane ndi zinthu zimene sakanatha kuzisintha ndipotu anachita zinthu zambiri m’ntchito ya umishonale. (2 Akorinto 12:7-9) Dustin, ali ndi zaka 18 ndipo anabadwa osaona komanso wakhala akudwala matenda a shuga kuyambira ali ndi zaka 12. Iye analemba kuti: “Ndikudziŵa kuti padziko ponse pano palibe munthu aliyense amene alibe chodandaula chilichonse m’moyo mwake. Ndikungolakalaka dziko latsopano la Mulungu mmene sindidzakhalanso ndi matenda a shuga. Ndimaona kuti matendaŵa sikuti sadzatha. N’zoona kuti ngokhalitsa ndithu powayerekezera ndi chimfine, koma adzatha basi.”

Dustin ananena choncho poganizira zimene Baibulo limalonjeza zakuti anthu adzakhala ndi thanzi m’paradaiso padziko lapansi muulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 21:3, 4) Mawu a Mulungu amalonjeza kuti muulamuliro wa Mulungu umenewu, “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24; Mateyu 6:9, 10) Kodi mungakonde kudziŵa zambiri za lonjezo la m’Baibulo limeneli? Pezani a Mboni za Yehova kwanuko, kapena lemberani kalata ofalitsa magazini ino pogwiritsira ntchito adiresi yoyenerera pa maadiresi amene ali patsamba 5.

[Chithunzi patsamba 12]

Mpofunika kudziletsa ndiponso kusaganizira kwambiri za matendaŵa