Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Moyo Wanga Unasinthira N’tachita Ngozi

Mmene Moyo Wanga Unasinthira N’tachita Ngozi

Mmene Moyo Wanga Unasinthira N’tachita Ngozi

YOSIMBIDWA NDI STANLEY OMBEVA

M’chaka cha 1982, ndinagundidwa ndi galimoto yomwe inkathamanga kwambiri. Nditalandira chithandizo sindinachedwe kuyambiranso zinthu zomwe ndinkachita masiku onse, ngakhale kuti nthaŵi zina ndinkamva ululu chifukwa cha kusemphana kwa mafupa ena a msana m’munsi pang’ono mwakhosimu. Komano zinthu zinadzafika poipa kwambiri patatha zaka 15.

NGOZIYI isanachitike komanso kwa kanthaŵi ndithu chichitikireni ngoziyo, ndinali munthu wa mphamvu kwabasi. Ndinazoloŵera kumachita zinthu zolimbitsa thupi monga kuthamanga mtunda wa makilomita 10 kapena 13 kumapeto a mlungu uliwonse, kuchita nawo maseŵera enaake ongokhalira jijirijijiri pomamenyetsa kampira kukhoma, ndiponso ndinkagwirako ntchito zolimba ndithu. Ndinathandiza nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova komanso Nyumba ya Msonkhano mu mzinda wa Nairobi, ku Kenya, komwe tikukhala.

Kenaka mu 1997, pamtimapa panayamba kupweteka mosasiyanso ndipo zinali zopitirira muyezo. Atakandiunika kuchipatala anapeza kuti mafupa ena a kumsana anali atasemphana ndipo ankakanikizana. Akuti zimenezi zinachitika chifukwa cha ngozi ija imene ndafotokoza pachiyambi paja.

Ndisanafike povutika chonchi, ndinkagwira ntchito yogulitsa zinthu pakampani inayake. Kampaniyi inapereka mwayi wolipirira aliyense akadwala m’banja mwanga. Kumbali ya ntchito zinthu zinkaoneka kuti zikundiyendera bwino ndithu. Koma chamkatikati mwa chaka cha 1998, kungoyambira cha pamtimapa mpaka kumapazi konseku kunangoti zii, kuferatu. Tsiku lililonse zinthu zinkaipiraipira.

Sipanapite nthaŵi yaitali, anandichotsa ntchito komanso zonse zimene kampani inkandichitira zinathera pompo. Tili ndi ana aŵiri akazi, Sylvia ndi Wilhelmina, ndipo panthaŵiyo Sylvia anali ndi zaka 13 ndipo Wilhelmina anali ndi zaka 10. Popeza kuti sindinalinso pantchito, mwezi ukatha tonsefe tinkangodalira malipiro a mkazi wanga, Joyce. Chifukwa cha kusintha kwa zinthu kumeneku, tinayamba kusagulanso zinthu zina zimene tinaona kuti sizinali zofunika kwenikweni. Tinakwanitsa kumapeza zonse zofunika kwenikweni.

Kusautsika Mtima

Ndisaname ayi, nditaonadi kuti apa zinthu zavuta basi, palibenso chilichonse chimene ndinachiona kuti n’chabwino, sindinkafunanso kumva za wina, ndiponso ndinkangonyanyala msanga. Nthaŵi zina ndinkangokhala wolunda, ndinkatsutsa china chilichonse. Mutu wanga unatsala pang’ono kusokonekera. Aliyense m’banja mwathu zinam’khudza kwambiri. Mkazi wanga ndi ana athu sankadziŵa kuti chikuchitika n’chiyani kwenikweni.

Panthaŵi imeneyo ndinkangoti n’zomveka kuti ndizitero. Ndipo si mmene ndinanenepera pa kanthaŵi kochepa chabe. Ndinkangodziipitsira komanso kukodzedwa. Nthaŵi zambiri zimenezi zinkandichititsa manyazi kwambiri, ndipo ndinkakakhala kwandekhandekha pa kakona kwinaku misozi italengeza m’maso. Nthaŵi zina ndinkangopezeka kuti ndakalipa kwambiri moti zinkaseketsa anthu. Ndinkadziŵa kuti zimene ndinkachitazo sizinali zothandiza malinga ndi vuto langali.

Ndine mkulu mu mpingo wachikristu wa Mboni za Yehova, ndipo ndalangizapo Akristu anzanga kambirimbiri kuti asamaganize kuti Yehova ndiye amene amachititsa anthu kuti azivutika mwa njira iliyonseyo. Komano ine ndemwenso ndinkapezeka kuti ndakhala ndikudzifunsa kangapo konse kuti: ‘Kodi Yehova anafuniranji kuti zimenezi zichitikire ineyo?’ Ngakhale kuti ndinagwiritsirapo ntchito malemba monga 1 Akorinto 10:13 powalimbikitsa ena, maganizo anga anali akuti ululu umene ndikumva ndi wosapiririka!

Ndinavutika Kupeza Dokotala Woyenera

Kuti ndipeze dokotala woyenera, ndinavutika kwambiri. Tsiku limodzi lokha ndinkatha kukumana ndi madokotala osiyanasiyana ochiza matenda okhudzana ndi vuto langali, koma sizinasinthe kwenikweni. Ndinafikira madokotala angapo ndithu, kuphatikizapo woongola mafupa ndi wa opaleshoni ya minyewa ina yopita ku ubongo ndipo onsewo ananena mfundo imodzi. Anati kunali bwino kuti ndichitidwe opaleshoni pofuna kuchepetsa ululu umene ndinkamva komanso kuti achotse timafupa timene tinasemphanato. Popeza ndimakhulupirira zimene Baibulo limanena pankhani yokhudza magazi, ndinawauza madokotalawo momveka bwino kuti asayerekeze n’komwe kundiika magazi zivute zitani.—Machitidwe 15:28, 29.

Dokotala woyamba anandiuza kuti pochita opaleshoniyo adzanding’amba penapake kumsanaku. Ndipo anandiuza kuti opaleshoni yotereyi imakhala yoopsa ndithu. Komano sananditsimikizire kuti ngakhale zitavuta sandiika magazi. Choncho ndinam’siya ameneyu.

Wachiŵiri anandiuza kuti akhoza kundithandiza vutoli mwa kunding’amba pakhosi. Zimenezo zinandiopsa kwambiri. Iyeyu anavomereza kuti sandiika magazi monga ndikufunira mwini wakene, koma ankafuna kuti apange opaleshoniyo nthaŵi yomweyo ndipo sanandifotokozere zonse bwinobwino. Nayenso ndinam’siya.

Kenaka mothandizidwa ndi a Mboni za Yehova amene ali m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala yakwathu kuno, ndinapeza dokotala womvetsa zinthu. Zimene dokotala wachitatuyu ananena zinali zogwirizana ndi za dokotala wachiŵiri uja, zakuti achita opaleshoniyo ponding’amba pakhosi. Iye anafotokoza kuti opaleshoniyo siyodetsa nkhaŵa kwambiri.

Ndinachita mantha kwambiri pondisonyeza mmene adzachitire opaleshoniyo. Makamaka chimene chinandiopsa kwambiri n’kudziŵa kuti pochita opaleshoniyo azidzakhudza ziwalo zofunika kusamala nazo kwambiri monga mtima ndi mapapo. Ndinkangoti: Koma sindingapitirire nayo opaleshoni imeneyi? Maganizo osayeneraŵa anangowonjezera mantha amene ndinali nawo kale.

Pa November 25, 1998, mpamene anandichita opaleshoniyo pa chipatala china chakuno ku Nairobi, ndipo opaleshoniyo inatenga maola anayi. Pa opaleshoniyo, anachotsa kafupa kena m’chiunomu. Kafupako anakakonza mwakuti kanatha bwinobwino kulumikizidwa pamene panali vutopo pokagwirizira ndi kachitsulo kamene anakamangirirapo ndi timanati. Zimenezi zinathandizako, koma sikuti ndinachiriratu. Ndinkamva kupweteka kwambiri poyenda. Mpaka panopa mbali zina za thupili zidakali chifereni.

Kusataya Mtima

Paja ndanena kale kuti nthaŵi zambiri ndinkangokhala ndi maganizo ambirimbiri chifukwa cha vuto langali. Koma kudabwitsa kwake, madokotala ambiri ankati ndine munthu wougwira mtima ndiponso wolimba nazo. N’chifukwa chiyani iwo ankaona choncho? Iwo ankaona kuti ndinkamva ululu kwabasi, koma ndinkawauzabe zimene ndimakhulupirira zokhudza Mulungu.

Ngakhale kuti nthaŵi zina ndinkapsa mtima chifukwa cha vuto langali, sindinasiyebe kudalira Yehova. Iye wakhala akundilimbikitsabe kwambiri m’mavuto anga onseŵa, moti nthaŵi zina ndinkaona kuti penapake sindimam’chitira bwino ayi. Ndinakonza zoti ndionetsetse kuti ndaŵerenga ndi kusinkhasinkha malemba omwe ndinkaona kuti angandilimbikitse pavutoli. Malemba ena ndi aŵa:

Chivumbulutso 21:4: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.” Poganizira lonjezo la m’Baibulo lakuti kudzakhala dziko latsopano limene anthu ake sadzakhala ndi misozi ndiponso zowawa mpaka kalekale, zinandilimbikitsa kwambiri.

Ahebri 6:10: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.” Ngakhale kuti sindinkathanso kuchita zinthu zambiri, ndinkadziŵa kuti Yehova adzaonabe zimene ndimachita pom’tumikira.

Yakobo 1:13: “Munthu poyesedwa, asanena, ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” Ndithu, mawu ameneŵa ndi oona! Ngakhale kuti Yehova analola kuti ndivutike, sikuti iyeyo ndiye anachititsa zimenezi.

Afilipi 4:6, 7: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” Kupemphera kunandithandiza kuti ndikhazike mtima pansi, ndipo zimenezi zinandithandiza kuti vutoli ndilitenge bwino.

Ndinagwiritsirapo ntchito malembaŵa polimbikitsa anthu ena amene ankavutika maganizo, ndipo anawathandizadi! Komano ndinayamba kuzindikira kuti panthaŵiyo ndinali ndisanafike poona kufunika kwake kwenikweni. Kudwala kwangaku n’kumene kunandichititsa kuti ndifike pomvetsa tanthauzo la kudzichepetsa ndiponso kuti ndidziŵe kudalira Yehova ndi mtima wanga wonse.

Zinanso Zimene Zinandilimbikitsa

Anthu ambiri amati ubale wachikristu ndiwo umalimbikitsa kwambiri nthaŵi zamavuto. Komatu n’kosavuta kuyamba kuona abale ndi alongo athu achikristu ngati si ofunika kwenikweni. Sitingakane kuti iwo sangakwanitse kuchita zonse zimene timafuna, koma nthaŵi zonse amakhala okonzeka kuti atithandize. Zimenezi n’zimene ndinaona ine. Nthaŵi zambiri ankabwera kudzandizonda ndili gone kuchipatala, ndipo nthaŵi zina ankachita kulaŵirira kwambiri. Anafika ngakhale podzipereka kuti andithandiza kulipira ndalama za kuchipatalako. Sindidzawaiwala anthu onsewo amene anakhudzidwa ndi vuto langali n’kundithandiza.

Mumpingo wathu, anthu amadziŵa kuti panopa pali zina zimene sindingathenso kuchita. Panopa ndine woyang’anira wotsogolera ndipo ndimagwira ntchito ndi akulu achikristu othandiza kwambiri. Sindinathepo mwezi osalalikira. Ndinathandiza anthu aŵiri kufika mpaka podzipereka kwa Yehova nthaŵi imene vuto langali linali pachimake penipeni. Panopa winayo ndi mtumiki wotumikira mumpingo wina wa Mboni za Yehova kuno ku Nairobi.

Mawu amandisoŵa oti ndim’thokozere mkazi wanga amene wakhala akundithandiza nthaŵi ya kuvutika konseku. Anapirira nane chifukwa chomangokwiyakwiya, kuvuta, ndiponso kumangodandaula ndi zilizonse. Ndikamalira komanso ndikamamva ululu, iye ankandilimbikitsa ndi kundikhazikitsa mtima pansi. Ndimakhalabe wodabwa mpaka pano chifukwa cha kulimba mtima ndi kupirira kwake panthaŵi yosautsayi. Anaonetsadi kuti iye ndi ‘bwenzi lenileni . . . nthaŵi zonse.’—Miyambo 17:17.

Ana athu aphunzira kulimba nalo vuto langali. Amayesetsa kuchita zimene angakwanitse kuti andithandize. Amadziŵa zimene ndikufunikira ndipo amayi awo akachoka, ngati ndikufunika chinachake amandithandiza msangamsanga. Sylvia ndiye wakhala ngati ndodo yanga pomandiyendetsako kuzungulira pakhomo ndikafooka.

Bwanji nanga za chitsirizira chathu, Wilhelmina? Ndikukumbukira nthaŵi inayake yomwe ndinkalephera kudzuka nditagwa m’nyumba. Iye ndiye yekha amene anali pakhomopo nthaŵi imeneyo. Anapeza mphamvu zondidzutsa n’kupita nane pang’onopang’ono m’chipinda chathu. Iye samvetsa kuti kaya anatha bwanji kuchita zimenezo. Sindidzaiwala kulimba mtima kumene anasonyeza nthaŵi imeneyo.

Palibenso china chilichonse chimene chinandisautsapo kwambiri m’moyo wanga wonse kuposa ngoziyo. Panopa ndikuvutikabe chifukwa cha ngozi imeneyo. Moyo ngakhalenso chikhulupiriro changa sichinayesedwepo kufika mpaka pamenepa. Ndaphunzira zinthu zambiri zokhudza kukhala munthu wodzichepetsa, womvetsa, ndi wachifundo. Ndakwanitsa kupirira zonsezi chifukwa cha kudalira ndi kukhulupirira kwambiri Yehova.

Ndaonadi kuti mawu a mtumwi Paulo akuti, “Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife,” ngoona. (2 Akorinto 4:7) Ndimalimbikitsidwa kwambiri ndi lonjezo la Mulungu lakuti kudzakhala “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano.” (2 Petro 3:13) Pemphero langa n’lakuti Yehova apitirize kundilimbitsa pamene ndikuyembekezera dziko latsopano limenelo, pakuti ndidakali wofooka ndipo pandekha sindingathe kuchita zinthu zambiri.

[Zithunzi patsamba 28]

Kuchita zinthu zachikristu pamodzi ndi banja langa kwandithandiza kupirira