Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tangoonani Chimvuucho!

Tangoonani Chimvuucho!

Tangoonani Chimvuucho!

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU KENYA

DZUŴA lapendeka, ndipo chidziŵe chachikulu chomwe chili kumalo osungirako zinyama otchedwa Masai Mara ku Kenya chikuoneka mosangalatsa kwambiri. Dzuŵalo likuzimirira ndipo madziwo akungooneka kuti psuu. Chapatali pang’ono ndi dziŵelo, kukubwera gulu la mbidzi ndi nyumbu zomwe zikungoyenda pang’onopang’ono. Mwadzidzidzi zinyamazo zikututumuka n’kungoima njo, ndipo maso ake angoti dwii kuyang’ana chinachake chomwe chikuoneka ngati chimwala choyandama m’mbali mwa dziŵelo. Chitavundulavundula madziwo mwamphamvu, chinthu changati chimwalacho chikuzimiririka m’madzimo. Kwenikweni zinyamazo zaona chinyama choopsa cha m’madzi, chimvuu.

Mvuu zimapezeka m’maiŵe, mitsinje, ndi m’nyanja za kuno kummaŵa kwa Africa, ndipo njovu zokha ndizo nyama zazikulu kuposa mvuu. Mvuu yaikulu imatha kutalika mamita anayi kuchokera kumutu mpaka kumchira kwake, ndipo ikaimirira imatha kufika msinkhu wa mita imodzi ndi theka. Imatha kulemera pafupifupi matani anayi. N’zosadabwitsa kuti Baibulo limati chinyamachi chili ndi mafupa amene ali ngati “misiwe yamkuwa” ndipo limawayerekezera ndi “zitsulo zamphumphu.”—Yobu 40:15-18.

Mvuu, imangooneka ngati chimgolo ndipo ili ndi chikopa chochindikala, ilibe ubweya, imaoneka yonyansa m’maso ndipo kunena zoona, simungaiike dala pa mpikisano wa ziphadzuŵa. Ili ndi miyendo ifupiifupi, ndipo zimenezi n’zodabwitsa kuti kaya imatha bwanji kunyamula chithunthu chikulukulu chonsecho. Komatu osatiderera timiyendo take tojintchato. Ikakhala pamtunda imathamanga kuposa munthu. Ikakhala m’madzi akuti imathamanga kuposa boti lopalasa mwinanso ngakhale kaboti kainjini kamene.

Mmene Imakhalira Kumadzi

Mvuu zimakonda kukhalira limodzi, ndipo nthaŵi zambiri zimakonda kukhala 10 kapena 15 pagulu n’kumatsogoleredwa ndi yamphongo imodzi. Komanso anthu ena akhala akuzipeza zilipo chigulu mwina mpaka 150. Zimatha kukhala m’madzi kapenanso kumtunda ndipo nthaŵi zambiri kukada mpamene zimatuluka m’madzi, kuti zikadye zomera zosiyanasiyana za m’mbali mwa madzi. Koma kaŵirikaŵiri sizifuna kutalikirana ndi madzi. Komano m’chilimwe, akuti mvuu zina zimatha kuyenda mtunda wokwana makilomita 10 pofunafuna chakudya.

Sizikudziŵika bwinobwino kuti kaya mvuu zimadziŵa bwanji malire a kumene zimakhala. Mvuu zili ndi khalidwe lodabwitsa lomamwaza ndowe zake ndi mchira, ndipo anthu ena amaganiza kuti zimatero pofuna kukopa zazikazi kapena poopseza adani ake. Zikakhala kuti zapanikizidwa ndi chinachake, zimalira mosalekeza ngati mmene hatchi imalirira, koma zikamamenyana zimabangula. Zimamveka kufwenkha kwake ngakhale zili pansi pamadzi. Mvuu yamphongo imene ikutsogolera zinzake imadziŵika chifukwa chomalira kuti MUH-Muh-muh.

Mvuu imakhala tsiku lonse m’madzi, pena kumaonekera pang’ono pena n’kumiriratu, ndipo zimenezi n’zogwirizanadi ndi mmene chithupi chake chiliri. Mvuu siidziŵa kwenikweni kusambira ngati mmene zimachitira zinyama zina zotha kukhala m’madzi ndi kumtunda komwe, koma imatha kukhala pansi pamadzi kwa mphindi mpaka 15! Mvuu ikakhala m’madzi imatha kusiya mfuno, maso, ndiponso makutu ake zikuonekera chifukwa zili chapamwamba. M’madzimu ndi mmene mvuu zimachitiramo zinthu zambiri, ngakhale kumemesa kapenanso kukwerana kumene.

Ikatenga bere, imakhala miyezi pafupifupi isanu ndi itatu n’kuswa kamwana kamodzi pamalo osazama kwambiri. Imatha kuyamwitsira kamwanako pamtunda kapena pamene pali madzi ofika mu akakolomu. Ngakhale kuti mvuu ndi chinyama champhamvu kwabasi, imadziŵa kulera ndi kusamala kamwana kake mogometsa. Ndithudi, kuona mvuu ikuyandama m’madzi kamwana kake kali kumsanaku kumasangalatsa zedi. Kuyesa dala kuchotsa kamwanako kumsana kwa mvuu yooneka ngati yofatsayo, n’kuputa dala mavu pachisa!

Thupi la mvuu ndi loyenereradi kukhala m’madzi. Ikapita kumtunda imaoneka kusintha kwambiri. Chikopa chake chimatulutsa timadzi tonanda tofiirirako ndipo timadziti timakhala tamchere kwambiri. Mukamaonera patali, timadziti timachititsa kuti mvuuyo izioneka ngati ikutuluka thukuta la magazi. Komabe timadzito timateteza chikopacho, m’madzi ndi kumtunda komwe. Anthu akale a kuno ku Africa ankalezaleza chikopa cha mvuu n’kuchiviika m’mafuta. Akatero ankapota tizikopa toleza tija n’kutiumika kuti apangire chikwapu choopsa chimene ankachigwiritsira ntchito pomenyana akamalimbirana malo. * Buku lokamba za zinyama lotchedwa Grzimek’s Animal Life Encyclopedia limafotokoza kuti amati akatha ntchito yokonza bwinobwino chikopa cha mvuu, yomwe imatenga zaka zosachepera zisanu ndi chimodzi, chikopacho “chimafika polimba gwa ngati mwala ndipo chimakhala chochindikala pafupifupi masentimita anayi ndi theka.”

Kuyasamula Kochititsa Chidwi Komanso Koopsa

Osanama, chinthu chochititsa chidwi kwambiri pa mvuu n’kukamwa kwake. Ikakhala kumtunda mvuu imamwetula zomera za kufupi ndi madzi n’kukamwa kwake komwe n’kwakukulu mpaka theka la mita. Komano sikuti kukamwa kwakeko n’kongodyera chabe. Mvuu ikayasamula kwambiri, sikukhala kuyasamula wamba koma imakhalanso ikuopseza kusonyeza kuti yalusa. Pofuna kuteteza malo awo omwe akucheperacheperabe, mvuu zimalolera kuchita ndewu yoopsa ndi adani ake. Ikayasamula, mano ake aakulu akunsi komanso osongoka amaonekera. Mano ameneŵa zimawagwiritsiranso ntchito pandewu ndipo amatha kutalika mpaka masentimita okwana 30.

Kukamwa kwa mvuu n’koopsa kwa mvuu zinzake ngakhalenso kwa anthu. Anthu akhala akuyesa kuti azikhala mosaopana ndi mvuu koma zaoneka kuti n’zosatheka. Ngakhale popanda kuiputa, mvuu imalusira aliyense amene akuyandikira malo amene ili. Siifunanso kuiyandikira makamaka ikakhala ndi chilonda, ndipo motero aliyense amene angafike kufupi nayo akhoza kuona zakuda. Maboti ena asadabuzidwapo ndi mvuu zolusa pogwiritsira ntchito kukamwa kwawo kwamphamvu.

Mvuu imaopsa chimodzimodzi kaya ikhale kumtunda kapena m’madzi. Mwachitsanzo, kukhala cha kumene kuli madzi koma kumtunda kwanu kuli mvuu imene ikudya n’koopsa kwambiri. Indedi, m’madera ena a kuno ku Africa, mvuu zapwetekapo anthu ena akumidzi omwe amangodzikhalira osadziŵa kuti atsekereza njira ya mvuuzo yopitira kumadzi. Nyamayi njoopsa kwa anthu ndi nyama zina za kutchire ndipo ndi yofunika kusamala nayo ndiponso kuipatsa ulemu kwambiri.

Kodi Mvuu Sizidzatha?

Mvuu ikamadya kumtunda ili yokhayokha ikhoza kugwidwa ndi mikango. Komabe, zikuoneka kuti mdani wamkulu woopsa wa mvuu ndi anthu. Buku lotchedwa World Book Encyclopedia limati: “Anthu achepetsa mvuu ndiponso achepetsa malo amene zimakhala. Alenje apha mvuu zambiri, ndipo alimi asandutsa minda malo amene zinkakhala.”

Kunenadi zoona, kuwononga malo okhala mvuu kumene anthu achita kwachititsa kuti mvuuzo zikhale ndi malo ochepa kwambiri, motero mvuuzo zikulephera kuyenda momasuka ndi kuswana bwino. Komabe nkhani yabwino njakuti Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, Mlengi akulonjeza kuti adzachititsa zinthu kuti zibwerere mwakale pakati pa anthu ndi zinyama, kuti pasadzapezeke wopweteka mnzake m’Paradaiso amene akubwerayo.—Yesaya 11:9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 M’Chiswahili mvuu amaitcha kuti kiboko, kutanthauza kuti “chikwapu.”

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Elizabeth DeLaney/Index Stock Photography