Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukapanda Kudyerera Ubwana Wako

Ukapanda Kudyerera Ubwana Wako

Ukapanda Kudyerera Ubwana Wako

“Ufulu wofunika kwambiri kwa ana ndiwo kudyerera ubwana wawo.”—Linatero buku la “The Hurried Child.”

MWINA mungavomereze kuti ana onse amayenera kumasangalala ndi ubwana wawo posakhala ndi nkhaŵa zilizonse ndiponso pochita zinthu zogwirizana ndi msinkhu wawo. Komatu, n’zomvetsa chisoni kuti kwa anyamata ndi atsikana ambiri ang’onoang’ono, zimenezi n’zosatheka. Tangoganizani za zinthu zambiri zimene ana amafuna kudzachita akakula zomwe zimasokonezeka anawo akamavutika ndi nkhondo. Taganizaninso za ana onse omwe sakuumva kukoma moyo chifukwa cha ukapolo kapena chifukwa chochitidwa nkhanza.

Ambirife n’zotivuta kuyerekezera mmene mwana amamvera akakakamizika kukakhala m’misewu poona kuti m’misewumo amakhala wotetezekako kusiyana n’kukhala pakhomo pa makolo ake. Panthaŵi yomwe amafuna kuti azikondedwa kwambiri ndiponso kutetezedwa bwino, ana okhala m’misewuŵa amafunika kuti achangamuke kuti azitha kudziteteza kwa anthu okakala mitima ofuna kuwadyera masuku pamutu. Kaŵirikaŵiri, ana amasokonezedwa ubwana wawo chifukwa cha nthaŵi zathu zovuta zino.

“Ndimalakalaka N’takhalanso Mwana”

Carmen, mayi wa zaka 22, anavutika kwambiri paubwana wake. * Iye ndi mkulu wake anakakamizika kumakakhala m’misewu pofuna kuthaŵa nkhanza za bambo awo komanso chifukwa choti mayi awo sankawasamala. Ngakhale kuti moyo wa m’misewu ngoopsa, atsikanaŵa anakwanitsa kupeŵa mavuto omwe ana ambiri othaŵa kwawo amakumana nawo.

Komabe, Carmen amadandaula kuti sanadyerere ubwana wake, chifukwa choti sakukumbukira n’komwe akuchita zinazake zachimwana. “Kungoyambira ndili khanda mpaka kufika zaka 22 ndakhala ndikuchita zachikulu zokhazokha,” anadandaula motero. Ananenanso kuti, “Ndili pabanja tsopano ndipo ndili ndi mwana, koma ndimalakalaka n’tamachita zinthu zomwe tiatsikana timachita, monga kuseŵeretsa zidole. Ndimafuna kukondedwa ndiponso kukumbatiridwa ndi makolo anga. Ndimalakalaka n’takhalanso mwana.”

Pali ana ambiri amene akuvutika ngati mmene anavutikira Carmen pamodzi ndi mkulu wake. Amakhala m’misewu, zomwe zimachititsa kuti asasangalale ndi ubwana wawo. Ambiri mwa ana ameneŵa amachita zinthu zosayenera kuti adzipezere zinthu zofunika pamoyo. Nkhani komanso malipoti a kufufuza kosiyanasiyana zikusonyeza kuti ana akuyamba kuchita zinthu zosayenera ali ang’onoang’ono kwambiri. Vutoli likukula chifukwa cha vuto linanso lakuti atsikana ambiri akumabereka ana, pamene iwowo adakali ananso.

Vuto Lomwe Anthu Sakulizindikira Msanga

N’zosadabwitsa kuti ana ambiri akusungidwa ndi anthu omwe si makolo awo. Nkhani yolembedwa ndi mkonzi m’nyuzipepala ya Weekend Australian inati: “Kusunga ana a anthu ena kwasanduka vuto lalikulu lomwe layamba mosadziŵika bwinobwino. Ana ambiri ochokera m’mabanja omwe anatha kapena m’mabanja omwe sakuyenda bwino sakusamalidwa bwino.” Nyuzipepalayo inanenso kuti: “Ana ena omwe akusungidwa ndi anthu omwe si makolo awo amakhala miyezi, mwinanso zaka zimene, osakumana ndi anthu oyang’anira mmene anthu owasungawo akuwasamalirira, ndipo ena amangosinthasintha anthu owasunga, osapeza malo okhazikika.”

Lipoti lina linanena za mtsikana wina wa zaka 13 yemwe anayenda m’makomo 97 mwa anthu ongom’sunga m’kati mwa zaka zitatu, ndipo m’makomo ena ankangokhalamo usiku umodzi wokha. Panopo amakumbukira kuti ankavutika maganizo kwambiri chifukwa choona kuti palibe munthu yemwe akufuna kukhala naye komanso kuti alibe chitetezo. Kwa ana ambiri otereŵa, palibe zodyerera ubwana wawo.

Ndiyeno n’zosadabwitsa kuti masiku ano akatswiri a nkhani zimenezi akumanena za vuto lomwe likukula loti ana sakudyerera ubwana wawo. Ngati ndinu kholo, poona zinthu zomvetsa chisonizi mwina mungamanene kuti ndinu wamwayi chifukwa chakuti munapezera ana anu pogona komanso mumawapatsa zinthu zofunika pamoyo wawo. Koma pali vuto linanso. Masiku ano ana sikuti akulephereratu kudyerera ubwana wawo. Nthaŵi zina, ana amangofulumizitsidwa kumachita zachikulu. Kodi zimenezi zikuchitika motani, ndipo kuopsa kwake n’kotani?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Tasintha dzina lake.