Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Boma Lodzalimbikitsa Mfundo za Mulungu

Boma Lodzalimbikitsa Mfundo za Mulungu

Boma Lodzalimbikitsa Mfundo za Mulungu

INGOYEREKEZERANI kuti dziko lonse lili ndi boma limodzi lokha lolamulira anthu a mafuko ndiponso zinenero zonse. Ingoyerekezerani kuti pali boma lotchuka ndi kuteteza mfundo zabwino kwambiri zoyenera kuzitsatira, boma lotchuka ndi kuthetsa nkhondo, udani, kuswa malamulo, umphaŵi, kuwononga dziko, matenda, ngakhalenso imfa imene!

Mwinatu mukuti ‘n’zabwino ndithu kungoti sizingatheke.’ Ayi, zimenezi n’zotheka ndithu. Ndipotu mulimonsemo, zidzachitika basi. Yesu Kristu analonjeza kuti kukubwera boma lotere. Iye anaphunzitsa om’tsatira kuti azipempherera bomali ponena kuti: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Chifukwa chakuti anthu ambirimbiri padziko lonse amadziŵa kapena anamvako za pempheroli, n’kutheka kuti mawu a m’pempheroli nanunso mukuwadziŵa bwino. Koma kodi munayamba mwaganizapo mozama za tanthauzo lenileni la mawu ameneŵa? Taonani kuti m’pemphero lija Ufumu augwirizanitsa ndi kukwaniritsidwa kwa zofuna za Mulungu. Nangano kodi Ufumu wa Mulunguwo n’chiyani? Ndipo dziko lathuli Mulungu amalifunira zotani?

Tanthauzo la Ufumu wa Mulungu

Akati ufumu amatanthauza boma limene mtsogoleri wake ndi mfumu. Ufumu wa Mulungu ndi umene Yehova Mulungu adzagwiritsire ntchito posonyeza kuti iyeyo ndiye wolamulira wa chilengedwe chonse. Ndi boma lolamulidwa ndi mfumu Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu. Nkhani yakuti Mulungu amalifunira zotani dziko lathuli inafotokozedwa mosapita m’mbali komanso momveka bwino pa Salmo 37:10, 11 pomwe pamati: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”

Choncho musataye mtima ngati kusintha kwa anthu masiku ano kumakufoolani. Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa zinthu ndiponso mfundo zimene anthu akutsatira zisintha kwambiri padziko lonse. Lonjezo lakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uyamba kulamulira padzikoli kuti ulimbikitse anthu kutsatira mfundo za Mulungu siloti n’kulikayikira ngakhale pang’ono.

Tikayamba kukhulupirira malonjezo a Ufumu wa Mulungu sitingamakhale mwamantha. Taganizirani mfundo zina izi za Ufumuwu: “Idzani, penyani ntchito za Yehova, Amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:8, 9) Kodi lonjezo la moyo wamtendere ndiponso wosaopa kanthu lingapose apa?

Polosera za Yesu Kristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, lemba la Salmo 72:12-14 limati: “Adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.”

Mfundo za M’Baibulo

Taganizirani mfundo zina izi zimene Baibulo limalimbikitsa anthu kuzitsatira. Pali mfundo yakuti: “Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wawo Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:3) Ndiye pali inanso yakuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6.

Baibulo limanenanso kuti tonsefe tidzaŵeruzidwa malingana ndi mfundo zimene tikutsatira. Taganizirani lemba la Mlaliki 11:9 lomwe limati: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.” Lemba lomwe linachita kutchula nkhani imeneyi yakuti tidzaŵeruzidwa malingana n’zochita zathu ndi la Miyambo 2:21, 22 lomwe limati: “Owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”

Apatu taona kuti tisataye mtima chifukwa kukubwera boma lolungama. Ndiye bwanji osayamba kum’konda kwambiri Mulungu? Kumakhala ndi anzathu amenenso amafuna Ufumu wa Mulunguwu kungatithandize kuti nafenso tidzakhale mu Ufumu wambambande umenewu n’kumadzasangalala ndi mfundo zake zogwira mtima.

[Chithunzi patsamba 10]

“Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—SALMO 37:11.