Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Anthu Akusiya Kutsatira Mfundo Zabwino?

Kodi Anthu Akusiya Kutsatira Mfundo Zabwino?

Kodi Anthu Akusiya Kutsatira Mfundo Zabwino?

ZINA mwa mphatso zikuluzikulu zimene makolo angapatse ana awo ndizo kuwakonda kwambiri ndiponso kuwaphunzitsa kumatsatira mfundo zabwino zomwenso makolowo amatsatira osati zomangoyankhula chabe.

Moyo sungakome n’komwe popanda kutsatira mfundo zabwino. Kutsatira mfundo zabwino kumathandiza kuti moyo ukhale waphindu. Kumathandiza munthu kudziŵa zinthu zimene zili zofunikira kwambiri m’moyo. Ndipo kumathandizanso munthu kukhala ndi khalidwe labwino.

Ngakhale kuti zili choncho, mfundo zabwino zimene anthu akhala akutsatira kuyambira kale zikusintha msangamsanga masiku ano. Mwachitsanzo, Pulofesa Ronald Inglehart ananena kuti “anthu ayamba kutsatira mfundo zolola munthu kuchita chilichonse chomukomera pankhani ya kugonana n’kumatero mogwirizana ndi mmene iyeyo akufunira.” Mu 1997, m’mayiko 16, munachitika kafukufuku wofuna kumva maganizo a anthu pankhani yokhala ndi ana apathengo. Pa kafukufukuyu anapeza kuti: “Kwa anthu a m’madera akumadzulo kwa Ulaya, anthu 90 pa anthu 100 alionse kapenanso kuposa pamenepa amaona kuti khalidwe lafala masiku anoli lilibe vuto, pamene ku Singapore ndi ku India, anthu osakwana 15 pa anthu 100 alionse ndi amene amagwirizana nazo.”

Ena akuyamikira ufulu watsopano umenewu, umene anthu ali nawo pankhani ya kugonana. Komabe, buku lakuti The Rise of Government and the Decline of Morality, lolembedwa ndi James A. Dorn, linanena kuti “kuchuluka kwa ana apathengo” ndiponso “kutha kwa mabanja” ndi “zizindikiro zoonekeratu zosonyeza kuti anthu alibenso khalidwe.”

Mfundo Zina Zimene Zikusiyidwa

Mfundo zinanso zomwe anthu ankaziona kuti n’zabwino kuyambira kale ayamba kuzisiya. Pa kafukufuku wa zachikhalidwe yemwe Pulofesa Inglehart anatsogolera, anapeza kuti m’mayiko olemera “anthu ambiri salemekeza anthu oyenera kupatsidwa ulemu.”

Mfundo inanso imene anthu ankaitsatira kuyambira kale ndiyo kugwira ntchito modzipereka. Komano pali umboni wosonyeza kuti zimenezinso zasintha kwambiri. Ku United States, bungwe lina loona za anthu a bizinesi linafunsa eni ntchito oposa 500,000 za nkhaniyi. “Anthu 31 pa anthu 100 alionse mwa anthuŵa ananena kuti n’kovuta kwambiri kupeza antchito, ndipo anthu 21 pa anthu 100 alionse ananena kuti anthu ambiri sagwira ntchito molongosoka.” Mwini ntchito wina anati: “Masiku ano zikuvuta kwambiri kupeza anthu obwera kuntchito mofulumira komanso ali osaledzera ngakhale kwa masiku aŵiri enieniŵa.”

N’kutheka kuti kayendedwe ka chuma n’kamene kakulimbikitsa vutoli. Eni zintchito angachokoche antchito ena kapena kusiya kuwachitira zinthu zina akaona kuti ndalama zimene amapeza zayamba kuchepa. Magazini ya zachikhalidwe yotchedwa Ethics & Behavior inati: “Nawonso antchito akaona kuti amene anawalemba ntchitowo sakudalirikanso amangoyamba kuwachitira ukamberembere. Sagwiranso ntchito modzipereka chifukwa amadziŵa kuti angathe kuchokochedwa nthaŵi iliyonse.”

Komanso anthu asintha kwambiri pankhani ya khalidwe ndiponso ulemu. Atafufuza ku Australia anapeza kuti: “Pafupifupi antchito 88 pa antchito 100 alionse ananena kuti kusoŵa khalidwe m’maofesi kukuchititsa kuti anthu asamagwire ntchito bwino.” Atafufuza pakati pa anthu ogwira ntchito zamalonda ku United States anapeza kuti, “anthu 80 pa anthu 100 ananena kuti anthu amwano ayamba akuchuluka m’ntchito za malonda.” Malinga ndi zomwe linanena bungwe lofalitsa nkhani la CNN, “masiku ano anthu sakuthandizidwa bwino akaloŵa m’sitolo moti pafupifupi theka la anthu omwe anafunsidwawo ananena kuti chaka chathachi iwo anangotuluka m’sitolo chifukwa cha zimenezi. Theka la anthu ofunsidwawo anati nthaŵi zambiri amaona anthu akuyankhula pa telefoni yam’manja mokuwa kapena mopweteketsa mtima anzawo. Ndipo madalaivala 6 pa madalaivala 10 alionse anati nthaŵi zambiri amaona anthu ena akuyendetsa galimoto mwamisala kapena mwamavuvu.”

Kodi Moyo wa Munthu ndi Wofunika Motani?

Nthaŵi zina, anthu amatha kunena kuti ayamba kutsatira “mfundo zinazake zabwino,” komatu izi zimangokhala nkhambakamwa basi. Mwachitsanzo, bungwe lina lothandiza pa zachikhalidwe linafufuza za mfundo imeneyi kwa anthu a m’mayiko 40. Anthu aŵiri pa anthu asanu alionse anati amaona kuti “kulemekeza moyo” ndi chimodzi mwa zinthu zisanu “zofunika kwambiri.” *

Komano n’chiyani kwenikweni chimene chimachitika? N’zosachita kukayikira kuti mayiko olemera angakwanitse kuthetsa mavuto ambiri amene anthu akukumana nawo. Koma buku la mu 1998 lomwe analemba Carol Bellamy, mkulu wa nthambi ya bungwe la United Nations yoona za ana, linati matenda a kupereŵera zakudya m’thupi “ndi amodzi mwa matenda amene chaka chilichonse akupha theka la ana pafupifupi 12 miliyoni osakwanitsa zaka zisanu a m’mayiko osauka. Ndipo kuchokera pamene mliri wa makoswe [kapena kuti chaola] unasakaza anthu ku Ulaya m’zaka za m’ma 1300 palibenso matenda ena amene anasakazapo motere.” Aliyense amene amaona kuti moyo wa munthu ngofunika kwambiri amasoŵa mtendere ndi malipoti otere. “Komatu, anthu sakutekeseka ndi matenda a kupereŵera zakudya m’thupi omwe avuta padziko lonse, ngakhale kuti pali maumboni ochuluka ochoka kwa asayansi osonyeza kuti vutoli lilipodi. Anthu akuganizira kwambiri za malonda a makampani padziko lonse, osati za mmene matenda opereŵera zakudya m’thupi angasakazire, kapena zakuti wina aliyense ayenera kukhala ndi chakudya cha magulu,” anatero mayi Bellamy.

Zochita za ogwira ntchito m’zipatala zikusonyeza kuti anthu saona moyo ngati chinthu chofunika kwambiri. Cha m’ma 1970 momwemu, mwana akabadwa atatsala mlungu umodzi wokha kuti akwanitse miyezi 6, zoti akhala ndi moyo zinali zokayikitsa kwambiri. Koma masiku ano, mwina ana aŵiri pa ana asanu alionse obadwa masiku asanakwane amatha kupulumuka. Ndiyetu n’zodabwitsa kwambiri kuti padziko lonse azimayi okwana pakati pa 40 ndi 60 miliyoni amachotsa mimba chaka n’chaka! Mimba zambiri zoterezo zimangotsala milungu yochepa chabe kuti zifanane ndi za ana obadwa masiku osakwana aja amene madokotala amayesetsa kuwathandiza kuti akhale ndi moyo! Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti anthu asokonezeka kwambiri pa za makhalidwe?

M’pofunika Mfundo Zabwino Zoyenera Kuzitsatira

Ofufuza ena atafunsa anthu kuti, “Chinthu chosafunika kwambiri m’moyo wawo n’chiyani?” ambiri anayankha kuti chimodzi mwa zinthu ziŵiri zotere ndicho ‘kukhala wokhulupirika ku chipembedzo chawo.’ Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti anthu opita kutchalitchi akucheperachepera. Pulofesa Inglehart anati kutukuka kwa mayiko a azungu “kwachititsa anthu ambiri kuposa kale lonse kuona kuti zinthu zili bwino” ndipo “zimenezi zachititsa kuti anthu asamadalire kwenikweni chipembedzo.”

Kusadalira zipembedzo kukuchititsanso kuti anthu asamakhulupirire Baibulo. Pa kufufuza kwina komwe kunachitika m’mayiko osiyanasiyana, anthu anafunsidwa kuti amadalira ndani kapena chiyani akafuna kudziŵa chinthu chimene chili choyenerera kuchichita. Ambiri anati amadalira nzeru zawo paokha. Ofufuzawo anati, “Mawu a Mulungu anali chinthu chachiŵiri, komabe osati monga chinthu chofunikira kwenikweni.”

Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri akusintha n’kumatsatira mfundo zoipa kwambiri! Kusoŵa mfundo zabwino zoyenera kuzitsatira, kukonda chuma komanso kusaganizirana, kwalimbikitsa anthu kukhala adyera ndiponso osaŵerengera ena. Ndiye chifukwa cha kusintha kumeneku kodi ndi zinthu ziti zomwe sizikupezekanso masiku ano?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Zaka zoposa 50 m’mbuyomu, bungwe la United Nations linayamba kutsatira mfundo za m’Chikalata cha Ufulu Wachibadwidwe. Gawo loyamba la mfundozo limati: “Anthu onse amabadwa omasuka ndipo amayenera kupatsidwa ulemu komanso ufulu wolingana.”

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Anthu ambiri masiku ano sakhala ndi mabanja olimba, sasamala ntchito, ndiponso ngamwano

[Chithunzi patsamba 6]

Azimayi ambirimbiri amachotsa mimba za ana ongotsala milungu yochepa chabe kuti afanane ndi khanda losakwana masikuli