Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaona Kuti Chinachake Chikusoŵeka Chifukwa Choti Anthu Asintha?

Kodi Mumaona Kuti Chinachake Chikusoŵeka Chifukwa Choti Anthu Asintha?

Kodi Mumaona Kuti Chinachake Chikusoŵeka Chifukwa Choti Anthu Asintha?

“KODI vuto lalikulu kwambiri m’dziko muno n’chiyani?” Anthu ambiri amene anafunsidwa funso limeneli ku United States anasonyeza kuti kwa iwowo mavuto aŵiri aakulu kwambiri ngakuti mabanja olimba komanso makhalidwe abwino ayamba kusoŵa. Anthu ambiri angavomerezane nawo anthuŵa pankhaniyi.

Mwachitsanzo, nyuzipepala ya tsiku n’tsiku ya ku Paris yotchedwa International Herald Tribune inati: “N’zoonekeratu kuti anthu ambiri, makamaka achinyamata, akufunitsitsa kukhala ndi mfundo zabwino zodzathetsera makhalidwe amene afala kwambiri padziko pano, monga umbombo, kusaganizirana komanso kusagwirizana. . . . Chokhacho chakuti anthu ambiri ayamba kuona kuti pakufunika mfundo zinazake zabwino zoti anthu padziko lonse azitsatira chikuonetseratu kuti chinachake chikusoŵa.”

Kodi inuyo mumaona kuti maboma ndi atsogoleri a mayiko, ngakhalenso akuluakulu a zamalonda, amatsatira mfundo zabwino zoti zingadzasinthe dzikoli n’kukhala losangalatsa komanso lopanda zoopsa zambiri? Kodi mukaganizira za mmene anthu asinthira masiku ano, nthaŵi zina mumaona kuti pali chinachake chimene chikusoŵeka?

Mwina chinthu chimene chimakudetsani nkhaŵa kwambiri ndicho nkhani ya chitetezo chanu. Kodi kumene mumakhala mungathe kusiya m’nyumba mosakhoma popanda vuto lililonse? Kodi kwanuko mumatha kuyenda usiku bwinobwino? Mwina muli ndi mwayi wokhala m’dera limene mulibe nkhondo, zipolowe za anthu osankhana mitundu kapenanso za magulu a zigaŵenga. Koma mwina mumaopabe kuti ena angathe kukuchitani zachipongwe, zauchifwambwa, kukuthyolerani nyumba kapena kukuberani. Zimenezi mungalephere kugona nazo tulo n’kumaona kuti mukusoŵekera chinachake.

Pamwamba pa zimenezi, n’kuthekanso kuti mwinamwake munasiya kukhulupirira kwambiri anthu ena. Mwina anthu akuntchito kapena anzanu chabe akhala akukudyerani masuku pamutu, ngakhale pankhani zazing’ono chabe.

M’pofunika Kuti Maboma Azipereka Chitsanzo

Kuyambira kale, anthu amavomereza kuti mfundo zimene anthu amatsatira m’moyo mwawo zimakhala zogwirizana ndi mfundo zimene boma lawo limatsatira. Calvin Coolidge, ananena mawu otsatiraŵa asanakhale mtsogoleri wa dziko la United States: “Anthu amanena kuti munthu aliyense ali ndi ufulu umene analengedwa nawo, koma kodi ndani amene angandisonyeze penapake m’chilengedwemu pamene panalembedwa za ufulu wina uliwonse woti unakhalapo kapena kuperekedwa kwa anthu popanda kukhazikitsa kaye malamulo opereka ufuluwo ndi kuonetsetsa kuti sukuponderezedwa.”

Boma lolamulira basi, ndilo lingapereke kapena kupondereza ufulu wa anthu, zilibe kanthu kuti linapeza bwanji mphamvu zake. Ufulu umenewu ndi monga wofalitsa nkhani, wosonkhana, wopembedza, ndiponso woyankhula zakukhosi pagulu, wosamangidwa kapena kuvutitsidwa popanda mlandu, ndiponso woweruzidwa mwachilungamo.

Abraham Lincoln, ananenanso mawu otsatiraŵa asanakhale mtsogoleri wa dziko la United States: “Cholinga chokhazikitsira boma n’chakuti liziwachitira anthu chilichonse chimene akufunikira, koma chomwe anthuwo sangathe kuchichita kapena kuchikwanitsa bwinobwino paokha.” Maboma akamayesetsa kuchita zinthu zothandiza ngati zimenezi, anthu amakhulupirira atsogoleri amene akuwalamulira.

Koma masiku ano zikuoneka kuti anthu anasiya kukhulupirira olamulirawo. Posachedwapa atafufuza ku United States anapeza kuti anthu 68 pa anthu 100 alionse amene anawafunsa ananena kuti akuluakulu a boma lawo si anthu a mfundo zabwino kwenikweni. M’mayiko ambiri anthu anasiya kukhulupirira akuluakulu a boma chifukwa amatchuka ndi ziphuphu ndiponso katangale. Mpake kuti anthu ambiri ayamba kuona kuti pali chinachake ndithu chimene chikusoŵeka.

Chitsanzo Chabwino cha Mfumu Solomo

Chitsanzo cha munthu wina wakale chimasonyeza kuti anthu olamulira angachititse kuti anthu asinthe kwambiri mfundo zimene amatsatira. Mfumu Solomo inalamulira mafuko 12 a Israyeli kuyambira m’chaka cha 1037 mpaka 998 Nyengo Yathu Ino isanakwane. Bambo ake, Mfumu Davide, anali m’modzi mwa mafumu amene analamulira bwino kwambiri mtundu wa Israyeli. Baibulo limasonyeza kuti Davide anali munthu wokonda choonadi ndi chilungamo komanso makamaka kuti anali munthu wokhulupirira ndi kudalira kwambiri Mulungu wake, Yehova. Davide anam’phunzitsa Solomo kuti nayenso akhale munthu wotero.

Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa Solomo m’maloto, n’kumuuza kuti: “Pempha chomwe ndikupatse.” (2 Mbiri 1:7) M’malo mopempha kuti akhale munthu wachuma chochuluka, waulemerero, kapena wopambana pa zandale, Solomo anasonyeza zimene zinali mumtima mwake popempha kukhala wanzeru, womvetsa zinthu, ndiponso womvera, kuti athe kulamulira bwino mtundu wa Israyeli.

Kodi anthu anasintha motani chifukwa cha ulamuliro wa Solomo? Panthaŵi yonse imene ankatsatira mfundo zonse zothandiza mtundu wa Israyeli pa zinthu zauzimu, Mulungu ankamudalitsa pomupatsa nzeru, ulemerero, ndiponso chuma. Zinthu zamakedzana zimene zapezeka zimatsimikizira kuti muulamuliro wa Solomo mtunduwo unalemeradi. Buku lotchedwa The Archaeology of the Land of Israel limati: “Chuma chochokera kosiyanasiyana chimene chinkapita kunyumba ya mfumu, komanso kuyenda bwino kwa nkhani za malonda . . . kunachititsa kuti dziko lonselo likhale lotukuka.”

Inde, boma labwino la Solomo linachititsa kuti anthu ake azikhala mwamtendere, mosaopa kanthu, ndiponso mosangalala. “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.”—1 Mafumu 4:20, 25.

Chitsanzo Choipa Cha Mfumu Solomo

Koma n’zomvetsa chisoni kuti Solomo anasintha, monga mmenenso amachitira atsogoleri ambiri masiku ano. Baibulo limati: “Ndipo anali nawo akazi mazana asanu ndi aŵiri, ana aakazi a mafumu, ndi akazi achabe mazana atatu; ndipo akazi ake anapambutsa mtima wake. Ndipo kunali, atakalamba Solomo, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.”—1 Mafumu 11:3, 4.

Kodi kusintha kwa Mfumu Solomo kunakhudza bwanji anthu ake? Ngakhale kuti anali munthu wodziŵa kuchita zinthu zambiri komanso wanzeru, chakumapeto kwa ulamuliro wake, Solomo anayamba kulamulira mwankhanza. Boma lake linachititsa kuti dzikolo lisauke pogwiritsira ntchito chuma mosakaza. Anthu ogwira ntchito anasiya kusangalala nazo ntchito zawo. Otsutsa ulamuliro wake analimbana naye ndipo anafuna kum’landa ufumu. Mtunduwo sunkagwirizananso kwenikweni. Komatu Solomo yemweyo, ndiye amene analemba mawu akuti: “Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo.”—Miyambo 29:2.

Pasanapite nthaŵi yaitali Solomo atafa, kusamvana pa zandale ndiponso kusakhulupirirana kunachititsa kuti mtunduwo ugaŵanike n’kuyamba kuvutika kwambiri, kusagwirizana, ndiponso zinthu zinaloŵa pansi kwambiri. Aisrayeli ankaona kuti chinthu chinachake chachikulu chikusoŵeka. Boma lawo linasiya kutsatira mfundo zake zabwino, n’kuwaiwala anthu ake. Vuto lalikulu linali lakuti atsogoleri awo ananyalanyaza Yehova ndiponso malamulo ake. Motero mtundu wonsewo unavutika.

Ambiri Akutaya Chikhulupiriro mwa Atsogoleri

Masiku ano anthu ambiri m’boma, m’zamalonda, ndiponso m’zipembedzo, alibe nazo ntchito kwenikweni zotsatira mfundo zabwino. Motero anthu ayamba kuona kuti chinachake chikusoŵeka. Maboma ndiponso atsogoleri ena, akumalephera kaŵirikaŵiri kuthetsa mavuto odziŵika bwino a m’mayiko mwawo.

Mwachitsanzo akulephera kuthetsa nkhondo kapena kutsitsa mtengo wolipirira zachipatala, kapena kuchepetsa mavuto obwera ndi katangale wa mankhwala osokoneza bongo. Maphunziro nawo sakuyendanso bwino. Komanso pali maboma angapo amene anachita kufika pomathandiza bizinesi za njunga. Nawonso atsogoleri ambiri a zamalonda ndiponso a zachipembedzo akukhumudwitsa kwambiri anthu chifukwa cha katangale ndiponso kusoŵa khalidwe. Motero n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri asiya kukhulupirira anthu amene ankawaona kuti angathe kuwatsogolera.

Kodi n’zotheka kuti boma linalake lingateteze, ngakhalenso kupereka chitsanzo chabwino, pankhani ya kupatsa anthu ufulu wawo wachionekere komanso pankhani ya kutsatira mfundo zabwino? Inde n’zotheka kwabasi. Nkhani yathu yotsirizayi ifotokoza mmene zimenezi zidzachitikire.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

‘Zikuoneka kuti umbombo, kusaganizirana komanso kusagwirizana kwafala kwambiri padziko lonse.’—Inatero INTERNATIONAL HERALD TRIBUNE

[Chithunzi patsamba 8]

Pamene Mfumu Solomo inkamvera malamulo a Mulungu, inkaphunzitsa anthu ake kutsatira mfundo zabwino kwambiri