Nyerere Zalusa!
Nyerere Zalusa!
“Timakhala pamudzi wina wa m’dziko la Belize, womwe anthu ayamba kumene kumangapo ndipo kudakali tchire labasi. Tsiku lina m’maŵa cha m’ma 9 koloko, nyerere zinavuta panyumba pathu. Zina zinkaloŵa m’nyumba kudzera pansi pa chitseko ndipo zina zinkaloŵera pena paliponse pamene panali mng’alu pofunafuna chakudya. Sitikanachitira mwina koposa kungoyamba taithaŵa kaye nyumbayo kwakanthaŵi ndithu n’kuzisiyira nyererezo. Titabwerera, tinapeza kuti zatulukamo ndipo zinali zitadya tizilombo tina tonse timene tinali m’nyumbamo.”
KWA ANTHU AMBIRI amene amakhala m’mayiko otentha ngati ku Belize, zimenezi sizachilendo ndipo sizodetsa nkhaŵa kwenikweni. Iwo amaona kuti nyererezo zimawathandiza kuchotsa tizilombo ndi tinyama tina n’tina tosafunikira m’nyumba monga mphemvu ndi nsikidzi. Ndipo zikamachoka zimasiya zitaseseratu m’nyumba monsemo.
Nyerere zimene tikukamba pano zimaoneka ngati mphembedzu ndipo zimachita zinthu ngati asilikali. * M’malo mokonza mafunkha awoawo, nyererezi sizikhala malo amodzi ndipo zimayenda chigulu, koma zimangoumbirirana penapake n’kupiringidzana miyendo kuti zitchingire manthu wawo ndi tiana take. Nyerere zolusa zija zimachokera pamenepo mondandalikana zitatumidwa kukafunafuna phoso lawo, lomwe ndi tizilombo ndi tinyama ting’onoting’ono monga abuluzi. Atsogoleri a nyerere zolusazi amayendanso uku ndi uku, akuoneka kuti ali chire kwambiri kuti agwire ndiwo yawo. Zimenezi zimachitika ngati sizikumva kununkhira kwa ndiwo yawoyo, ndipo zikatere nyerere zotsogolerazo zimachita jenkha n’kuima kaye. Koma zotsatira pambuyo pawo zimangodutsa basi, ndipo zikafika kutsogolo zimakakhala m’magulu oloŵera kosiyanasiyana zitatcheratchera.
Nyererezi zimakhala zikuyenda uku ndi uku kwa masiku pafupifupi 16 kenaka n’kupuma kaye kwa masiku ena okwana 20, ndipo panthaŵi imeneyi mpamene manthu uja amaikira mazira. Pakatha masiku ameneŵa, nyererezo zimamva njala, choncho zimayambiranso ulendo wawo uja, womwe zimayenda zitalusa pokafuna zakudya. Kuchokera ku tsidya limodzi kukafika ku tsidya lina la nyerere zolusazi, mtunda wake umakhala wokwana mamita 10, ndipo m’mbali mwake mumakhala muli akangaude, zinkhanira, akafadala, achule ndi abuluzi ali balalabalala kuthaŵa. Mbalame zimakhala zikungolondola nyererezo kuti zidye tizilombo tothaŵato osati nyererezo.
Nyerere, zimene m’Baibulo pa Miyambo 30:24, 25 amazifotokoza kuti “zipambana kukhala zanzeru,” zili m’gulu la zinthu zimene zinalengedwa modabwitsa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Nkhaniyi ikukamba makamaka za mtundu wa nyerere zimene zimapezeka kuchigawo cha ku Central ndi South America.
[Chithunzi patsamba 29]
Nyerere yangati mphembedzu
[Mawu a Chithunzi]
© Frederick D. Atwood
[Chithunzi patsamba 29]
Zikupanga podutsa popiringidzana miyendo
[Mawu a Chithunzi]
© Tim Brown/www.infiniteworld.org