Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Peŵani Mawu Opweteka

Peŵani Mawu Opweteka

Lingaliro la Baibulo

Peŵani Mawu Opweteka

“Mochokera m’kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.”—YAKOBO 3:10.

KUTHA kuyankhula ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimatisiyanitsa ndi zinyama. Koma n’zodandaulitsa kuti anthu ena amagwiritsira ntchito mwayi umenewu molakwika. Mawu okhadzula, otukwana, aphunzo, onyoza za Mulungu ndiponso oseleula ena mwachipongwe amapweteka kwambiri, mwinanso kuposa kupwetekedwa kwenikweni. Baibulo limati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.”—Miyambo 12:18.

Anthu okonda kutukwana akuchuluka. M’sukulu zambiri akuti ana oyankhula zotukwana akuchuluka kwambiri. Ndiye anthu ena amati kuyankhula mopweteka kumathandiza munthu kusonyeza mmene mtima ukuwawira. Munthu wina wamaphunziro a zandale analemba kuti: “Kuyankhula zotukwana kumathandiza panthaŵi imene kuyankhula zabwinobwino sikungasonyeze mmene tikumvera mumtima mwathu.” Kodi moti Akristu aziona nkhani ya mawu opwetekayi mwachibwanabwana chonchi? Kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani imeneyi?

Danani ndi Kuseleula Ena Mwachipongwe

Kutukwana sikunayambe lero. Kodi mungakhulupirire kuti m’nthaŵi ya atumwi, pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, anthu ankatukwana? Mwachitsanzo, zikuoneka kuti ena mumpingo wa ku Kolose ankatukwana akapsa mtima. N’kutheka kuti ankatero pofuna kuti ena ziwapweteke, mwina pobwezera zinazake. Masiku anonso anthu amatukwana akapsa mtima. Motero kalata imene Paulo analembera Akolose ndi yothandizanso masiku ano. Iye analemba kuti: “Tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka mkamwa mwanu.” (Akolose 3:8) N’zoonekeratu apa kuti Akristu akulangizidwa kuti apeŵe kupsa mtima ndi kutukwana ndipo nthaŵi zambiri kutukwanako kumachitika munthu akapsa mtima.

Inde, anthu ambiri amatukwana alibe cholinga chopweteketsa mtima anthu ena. Kaŵirikaŵiri, anthu amatukwana mongoseleulana. Motero anthuwo amangozoloŵera kutukwana akamayankhula. Moti mpaka ena amavutika kuti ayankhule popanda kutukwana. Ndipo nthaŵi zambiri, anthu amatukwana pofuna kuseketsa anzawo. Koma kodi kuseleulana koteroko si kulakwa kwenikweni? Taganizirani izi.

Akati anthu akuseleulana mwachipongwe ndiye kuti zimene akunenazo n’zongofuna kuseketsa ena. Kuseleulana kwa masiku ano nthaŵi zambiri kumakhala kokhudza za kugonana. Ndipo anthu ambiri amene amadziona ngati ndi olemekezeka ndithu amasangalala nazo zimenezi. (Aroma 1:28-32) Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri azisudzo akumakonda kunena nthabwala zokhudza kugonana koyenerera komanso zina zokhudza kugonana kwachilendo. Nkhani zoterezi akumazionetsa m’mafilimu ambiri, komanso kuziulutsa m’ma TV ndi mawailesi.

Sikuti Baibulo silitchulapo zoyenera kuchita pankhaniyi. Mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Efeso kuti: “Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa [kuseleulana mwachipongwe] zimene siziyenera.” (Aefeso 5:3, 4) Apa n’zoonekeratu kuti kutukwana, kaya n’zolinga zotani, n’kulakwirabe Mulungu. Ndithu, n’koipa ndipo kuli m’gulu la mawu opweteka.

Mawu Okhadzula Amene Amaipira Mulungu

Kunena zoona, mawu opweteka si mawu otukwana okha. Mawu okhadzula, antchedzera, oseka ena, ndiponso olalata amapweteka kwambiri. N’zoona kuti tonsefe lilime lathu limatichimwitsa, makamaka pakakhala anthu okonda ntchedzera ndiponso amijedu. (Yakobo 3:2) Komabe, Akristu oona sayenera kuona kuti kuyankhula kotero si nkhani yaikulu. Baibulo silibisa n’komwe kuti Yehova Mulungu sagwirizana nawo mawu onse opweteka.

Mwachitsanzo, m’buku la m’Baibulo la 2 Mafumu, timaŵerengamo za gulu la anyamata amene ananyoza mneneri Elisa. Nkhani yake imati anyamatawo anayamba kum’seka n’kumati: “Takwera wadazi, takwera wadazi!” Yehova anaona kuti zimene zinali mumtima mwa ana ameneŵa zinali zoipa motero sanalekerere mawu awo achipongwewo. Nkhaniyi imati Mulungu anachititsa kuti anyamata okwana 42 aang’onoŵa afe chifukwa cha kuyankhula mwachipongweko.—2 Mafumu 2:23, 24.

Aisrayeli “ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.” (2 Mbiri 36:16) Ngakhale kuti chimene chinam’kwiyitsa kwambiri Mulungu n’chakuti anthu ake ankalambira mafano ndiponso sankamvera, palinso mfundo yofunika kuiganizira yakuti Baibulo limatchulanso mwapadera kuti iwo ankayankhulira zachipongwe aneneri a Mulungu. Zimenezi zikusonyezeratu kuti khalidwe lotere Mulungu sagwirizana nalo m’pang’ono pomwe.

Motero, Baibulo limalimbikitsa Akristu kuti: “Mkulu usam’dzudzule.” (1 Timoteo 5:1) Tingathe kugwiritsira ntchito mfundo imeneyi pankhani zokhudza munthu wina aliyense. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tisachitire mwano munthu aliyense, tisakhale andewu, tikhale aulere, ndi kuonetsera chifatso chonse pa anthu onse.’—Tito 3:2.

Kumayankhula Bwino

Nthaŵi zina zimavuta kuti munthu usayankhule zopweteketsa mtima. Munthu akalakwiridwa amatha kuona kuti palibe vuto kum’nenera munthu wam’lakwirayo mawu okhadzula, kaya pamaso pake kapena momujeda. Komabe, Akristu amapeŵa zimenezo. Miyambo 10:19 amati: “Pochuluka mawu zolakwa sizisoŵeka; koma wokhala chete achita mwanzeru.”

Angelo a Mulungu amapereka chitsanzo chabwino pankhaniyi. Iwo amadziŵa zoipa zonse zimene anthu onse amachita. Ngakhale kuti angelo ali ndi mphamvu zochuluka kuposa anthu, iwo sayankhula monyoza anthu ndipo amatero pofuna kulemekeza Yehova. (2 Petro 2:11) Angelowo amatero podziŵa kuti Mulungu amadziŵa kwambiri zoipa zimene aliyense amachita ndiponso kuti Mulunguyo atafuna angathe kuchitapo kanthu. Mikayeli, mkulu wa angelo onse, sanafune kuyankhula monyoza ngakhale kwa Mdyerekezi weniweniyo.—Yuda 9.

Akristu amayesetsa kutsanzira angeloŵa. Amatsatira zimene Baibulo limalangiza zakuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.”—Aroma 12:17-19.

N’zochititsatu chidwi kudziŵa kuti ngakhale mmene mawu athu akumvekera ndiponso mphamvu yake zingathe kum’pweteka wina. Sizachilendo kwa amuna ndi akazi awo kupweteketsana mitima akamabwezerana mawu. Kaŵirikaŵiri makolo ambiri amawayankhula ana awo mokalipa. Koma palibe chifukwa choti tizikalipa tikafuna kunena za kukhosi kwathu. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu.” (Aefeso 4:31) Baibulolo limanenanso kuti “kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndewu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse.”—2 Timoteo 2:24.

Mawu Olimbikitsa

Chifukwa chakuti masiku ano anthu oyankhula zachipongwe ndiponso zotukwana achuluka, Akristu ayenera kupeza njira yowathandiza kupeŵa kutengera zoipazi. Baibulo limatisonyeza njira yabwino yopeŵera zimenezi, yomwe ndi kukonda mnansi wathu. (Mateyu 7:12; Luka 10:27) Kuganizira ndiponso kukonda kwambiri anansi athu kungatithandize kuti nthaŵi zonse tiziyankhula mawu olimbikitsa. Baibulo limati: “Nkhani yonse yovunda isatuluke m’kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.”—Aefeso 4:29.

Komanso tikamayesetsa kuti Mawu a Mulungu akhazikike m’maganizo mwathu tingathe kupeŵa kuyankhula mawu opweteka. Kuŵerenga Malemba Oyera ndi kuwasinkhasinkha kungatithandize ‘kuvula chinyanso chonse.’ (Yakobo 1:21) Indedi, Mawu a Mulungu angatilimbikitse.