Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiwawa Choopsa Chikungoipiraipira Chifukwa Chiyani?

Chiwawa Choopsa Chikungoipiraipira Chifukwa Chiyani?

Chiwawa Choopsa Chikungoipiraipira Chifukwa Chiyani?

FRANK ndi Gabriella ankangodziyendera m’maŵa powongola miyendo m’mphepete mwa nyanja ku Oregon m’dziko la America, kwinaku akuyang’ana dzuŵa likutuluka. Sankadziŵa n’komwe kuti kunja kugwanji. Patangopita mphindi zoŵerengeka chabe, iwo anapezeka atamwalira munthu wina atawawombera ali nawo pafupi kwambiri. Kodi munthuyo anachita zimenezo pobwezera chinachake? Kapena anawaphera njiru? Ayi ndithu. Munthuyu sankadziŵana nawo n’komwe, kungoti anachita zimenezo ati pofuna kulaŵako mmene zimakhalira ukapha munthu.

“Lamlungu pa 28 April, 1996, Martin Bryant anadabwitsa anthu kumayiko a azungu ndi zimene ankachita ati posangalala. Iyeyu ankayendayenda m’tauni ya Port Arthur, pachilumba cha Tasmania, n’kumawombera munthu aliyenseyo amene wakumana naye, ndipo potero ankamva bwino kumtima kwake n’kumadziona kuti ndi amunamuna.” (Linatero buku la Philip Atkinson lotchedwa A Study of Our Decline) Munthuyu anapha anthu 35!

Monga mwa nthaŵi zonse, munthu wina wopuma pantchito wazaka 65 ku Canada anachoka m’maŵa panjinga yake kuti angothamangitsa magazi. Ali m’kati mopalasa njinga yakeyo, dalaivala wina anam’gunda kumbuyo ndi galimoto n’kungom’siya akuchita kudziŵa kuti akuthatha ndi imfa. Njinga yakeyo inakhwekhwerezeka mumsewu kamtunda ndithu pafupifupi mamita 700. Poyamba anthu ankaganiza kuti dalaivalayo anagunda munthuyu mwangozi kungoti sanaime, koma atafufuza bwinobwino zinadziŵika kuti dalaivalayo anachita kuba galimotoyo ndipo apa ankangoseŵera nayo moti sankasamala zapamsewu pofuna kuimva kukoma. Zikuonekanso kuti pogunda wanjingayo, inali mbali yachisangalalo chokhachokhacho.

Kodi Umenewu ndi Mtundu Winanso wa Chiwawa?

Ziwawa zakhala zikuchitika kwa zaka zambirimbiri, koma mitundu ya chiwawa imene tatchula pamwambapa ikuchititsa anthu kudzuma n’kumangoti: “Koma n’chifukwa chiyani anthu akuchita nkhanza zotere? Ndithu munthu wamoyo angachite zoterezi?” Mwina zinthu zina zachiwawa zomwe n’zodziŵika kale, monga umbava kapena chinyengo, sizingachite kuimitsa anthu ambiri mitu, koma pali zinthu zambiri zimene anthu akuchita zomwe zikukopa atolankhani ambiri ndipo anthu akamva zinthu zotere akumangoti, ‘Izinso ndiye n’zinazina! Kodi chikuchitika n’chiyani padzikoli?’

Ziwawa zoterezi n’zinazina. Nthaŵi zambiri zikumakhala zochititsa nthumanzi kwambiri komanso zauchinyama. Monga taonera zitsanzo zili pamwambazo, kaŵirikaŵiri anthu ochitidwa ziwawa zotere amakhala opanda chifukwa chilichonse ndi anthu achiwawawo ndipo sadziŵana nawo n’komwe. Komanso, nthaŵi zambiri zimaoneka kuti anthu achiwawawo sakhala ndi chifukwa chenicheni chochitira zimenezi. Mitundu ya ziwawa zochita popanda cholinga chenicheni njosaŵerengeka.

M’mwezi wa April mu 1999, ku Colorado, m’dziko la America, ana aŵiri asukulu pasukulu ina anapha ana anzawo 12 ndi mphunzitsi kenaka iwo n’kudziphanso. Munthu wina anamwalira ku California m’chaka cha 1982 atamwa mankhwala ochita kugula omwe munthu wina anali atawathira poizoni. Mu 1993, anyamata aŵiri a zaka 10 ananyengerera kamwana ka zaka ziŵiri, dzina lake James Bulger kuti kasiyane ndi amayi ake omwe anali kubutchala mumsika wina wa m’tauni ya Bootle, m’dera la Merseyside, ku England. Anapita nako kumene kuli njanji n’kukakamenya zolimba mpaka anakapha.

Zochita zina tingaziike m’gulu la zauchigaŵenga, monga zomwe zinachitika ku Tokyo mu 1995 zopopera mpweya wapoizoni m’sitima zoyenda pansi panthaka. Anthu a ku Japan anachita nthumanzi kwambiri pamene anthu a m’kagulu kena kachipembedzo anapopera mpweya wapoizoni m’sitima zoyenda pansi ku Tokyo, anthu 12 n’kufa ndipo enanso ambirimbiri n’kuvulala. Ndi anthu ochepa okha amene angaiwale kugwa kwa nyumba zimene zinali Likulu la Zamalonda Padziko Lonse mumzinda wa New York ndiponso za chiwembu cha kulikulu la asilikali a America, la Pentagon mumzinda wa Washington D.C., zomwe zinaphetsa anthu pafupifupi 3,000. Komanso za mabomba amene anaphulitsidwa ku Bali, m’dziko la Indonesia n’kupha anthu okwana 200.

Zonsezi zikuonetseratu kuti chiwawa choopsa chawanda tsopano. Vutoli lafalikira padziko lonse ndipo likusautsa mayiko ambiri ndi anthu osiyanasiyana.

Pankhani zina zoterezi zimangokhala ngati kuti anthu achiwawawo anali pampikisano woti aone kuti ndani amene angapose anzake pochita zinthu zachiwawa zochititsa nthumanzi kwambiri. Komanso, ziwawa za magulu okhalirana pachidani chifukwa cha kusiyana mtundu ndi zina zotere zikuchuluka kwambiri. Ochita ziwawawo akumachitira nkhanza zoopsa kwambiri anthu amene sanalakwe chilichonse chifukwa chongosiyana nawo mtundu, chipembedzo kapena fuko basi ndipo zimenezi n’zimene zinachitika mu 1994 pamene anthu a mtundu wachitutsi pafupifupi 800,000 anaphedwa ku Rwanda.

Zonsezi zikuchititsa anthu kuti chamumtima azingoti: ‘Kodi zinthu zatani masiku ano? Kodi zinali chonchi kumbuyo konseku? Kodi chikuchititsa ziwawa zoopsa chonchi n’chiyani makamaka? Nanga chilipo chotilimbitsa mtima kuti ziwawa zoterezi zidzachepako kapena kutheratu?’ Nkhani zotsatira ziyankha mafunsoŵa ndi enanso.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Anthu amene amachita ziwawa zotere kaŵirikaŵiri amangochitira anthu osalakwa ndiponso popanda chifukwa chenicheni