Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Akristu Azichita Zogodomalitsa Maganizo?

Kodi Akristu Azichita Zogodomalitsa Maganizo?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Akristu Azichita Zogodomalitsa Maganizo?

“Asapezeke mwa inu munthu . . . wotsirika.”—DEUTERONOMO 18:10, 11.

ANTHU akhala akutsutsana kwambiri pankhani ya kugodomalitsa maganizo. * Ngakhale akatswiri ogodomalitsa munthu maganizo satha kufotokoza bwinobwino zomwe zimachitika. Nthaŵi zambiri anthu amati kugodomalitsa maganizoku n’kuchititsa munthu kuti asamadziŵe bwinobwino zimene zikuchitika kapena azichita ngati wagwa majini. Komabe anthu ambiri zimenezi alibe nazo ntchito, koma amachita chidwi ndi zimene zimachitika munthu akagodomala maganizo.

M’zaka zochepa zapitazi kakhala kachisimo ka madokotala m’mayiko ena kuuza odwala kuti alandire chithandizo chowagodomalitsa maganizo. Mwachitsanzo, magazini yotchedwa Psychology Today inati: “Kugodomalitsa maganizo kungachize litsipa, kungachepetse ululu amayi akamachira, kungakuthandizeni kusiya kusuta fodya, kungaloŵe m’malo mwa mankhwala ochititsa dzanzi pochita opaleshoni, komanso kungathandize kuti munthu aziphunzira bwino, ndipotu zonsezi zingachitike popanda kubweretsa vuto lililonse.” Komano anthu ambiri amaona kuti kugodomalitsa maganizo kumayenderana ndi zamizimu ndiponso zamatsenga.

Kodi Baibulo limati chiyani pankhaniyi? N’zoona kuti Baibulo si buku la zachipatala, ndipo silinena mwachindunji za kugodomalitsa maganizo. Komabe mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu zingatithandize kudziŵa mmene Mulungu amaonera nkhaniyi.

Kodi Zogodomalitsa Maganizo Zimayenderana ndi Zamatsenga?

Kodi anthu akamati kugodomalitsa maganizo kumayenderana ndi zamatsenga amakhala akungonena zam’mutu mwawo? Mwina chimawachititsa kuganiza choncho ndi mafilimu ndiponso mabuku a nkhani zongopeka, komabe zakuti kugodomalitsa maganizo kumayenderana ndi zamatsenga si zam’mutu chabe. Pofotokoza za kugodomalitsa maganizo, buku lotchedwa Encyclopedia of Occultism and Parapsychology limati: “Mbiri yake imagwirizana m’njira zambiri ndi zamatsenga.” Kugwidwa mizimu, komwe chiyambire kwakhala mbali ya zamatsenga, kaŵirikaŵiri kumaikidwa m’gulu la zogodomalitsa maganizo. Nawonso, ansembe akale ku Igupto ndi ku Girisi ankachita zina zom’godomalitsa munthu maganizo akafuna kum’chiza m’dzina la milungu yawo yonyenga.

Buku lomwe taligwira mawu pamwambapa limati: “Ngakhale masiku anonso zambiri zimene zimachititsa munthu kugodomala maganizo amati ndi ‘zamizimu.’” Ngakhale kuti n’zovuta kufotokoza mmene njira zosiyasiyana zogodomalitsira maganizo zimakhudzirana ndi zamatsenga, mfundo njakuti Mulungu amakaniratu chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. (Deuteronomo 18:9-12; Chivumbulutso 21:8) Motero Akristu sangachitire dala zinthu zokhudza kugodomalitsa maganizo zomwe n’zochita kuonekeratu kuti sizigwirizana ndi malemba.

Mmene Kumakhudzira Zochita za Munthu

Kodi zimenezi zimakhudza bwanji maganizo ndiponso zochita za munthu? Kodi zimabweretsa vuto lililonse? Chodetsa nkhaŵa kwambiri n’chakuti munthu akagodomala maganizo, nthaŵi zina sadziŵa n’komwe zomwe akuchita. Akatswiri ogodomalitsa anthu pa zionetsero amapezera mwayi pamenepo, n’kumachititsa anthu amene adzipereka kuti awagodomalitse, kuchita zinthu zomwe sangachite ali bwinobwino, mwinanso kuwachititsa kuti azioneka ngati aledzera.

Buku lotchedwa The Encyclopedia Americana limanena izi pankhani ya chionetsero cha kugodomalitsa maganizo: “N’kosavuta kuti amene wagodomalayo achite chilichonsecho chomwe angauzidwe. Iye angachite mosavuta zinthu zomwe nthaŵi zambiri sangachite pagulu ndipo angathe kumaona kuti palibe vuto kuchita chilichonse chochititsa manyazi pagulu.” Buku lotchedwa Collier’s Encyclopedia limati: “Maganizo ake onse amakhala pachinthu chimodzi, ndipo zimenezi zimam’pangitsa kuti akhale tcheru kwambiri kumvetsera munthu amene wam’godomalitsayo ndiponso kuti azichita zonse zomwe akumuuza kuchita.”

Kodi zimenezi sizikukuopsani? Kodi n’chanzeru kuti Mkristu alole anthu ena kulamulira maganizo ake pom’godomalitsa n’kumamuuza zochita? Zimenezi zingasiyane kwambiri ndi malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yoyera, yolandirika kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika ndi mphamvu yanu ya kulingalira. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”—Aroma 12:1, 2, NW.

Kodi Mkristu angakhale ndi “chikumbumtima chabwino,” ngati walola kuti munthu wina alamulire maganizo ake, kapena zofuna zake kapenanso zochita zake? (1 Petro 3:16) Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yense wa inu adziŵe kulamulira thupi lake m’chiyero ndi ulemu.” (1 Atesalonika 4:4 NW) N’zoonekeratu kuti kugodomalitsidwa maganizo kungalepheretse munthu kutsatira malangizo ameneŵa.

Chiyembekezo Chodzakhaliratu Athanzi

Malinga ndi mfundo za m’Baibulo zomwe tatchulazi, Mboni za Yehova zimapeŵa chilichonse chokhudza kuti munthu wina, kapena iwowo paokha adzigodomalitse maganizo. Amatsatira lamulo la pa Deuteronomo 18:10, 11, lakuti: “Asapezeke mwa inu . . . wotsirika.” Kwa anthu amene akudwala, pali njira zina zambiri zachithandizo zomwe siziloŵetsapo zamatsenga kapena kulola kuti ena akuseŵeretse maganizo.

Mwa kupeŵa zinthu zomwe sizigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, Akristu angathe kuyembekezera kudzakhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Mulungu lomwe lidzakhale lolungama. Nthaŵi imeneyo anthu adzakhala ndi thanzi ndiponso maganizo abwino popanda kuwagodomalitsa maganizo.—Chivumbulutso 21:3, 4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Kugodomala maganizo kumene tikunena m’nkhani ino kumam’chititsa munthu kukhala ngati ali mtulo ndipo nthaŵi zambiri ndi munthu wina amam’chititsa kutero. Ndipo zikatero wogodomalayo amatha kukumbukira zinthu zomwe anaziiwala kalekale, kuona zideruderu, ndipo amatha kuchita chilichonse chomwe munthu wam’godomalitsayo wamuuza kuchita.