Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndizitani Tsoka Likandigwera?

Kodi Ndizitani Tsoka Likandigwera?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndizitani Tsoka Likandigwera?

“N’chifukwa chiyani zigaŵenga zinapha amayi anga?”—Anafunsa motero Kevin. *

“[Pasanafike pa September 11], ndinkakonda kuyenda m’misewu ya pansi panthaka. Panopo ndimatha kuona ndikufera mu msewu ngati umenewu anthu atauphulitsa.”—Anatero Peter.

AMAYI a Kevin anafa pa zauchigaŵenga zimene zinachitika pa September 11, 2001, zophwasula Likulu la Zamalonda Padziko Lonse mu mzinda wa New York City. Peter sanaone nawo zoopsa ngati zimenezo, komabe anachita mantha kwambiri ndi zauchigaŵengazo.

Nyuzipepala ina inati: “Ana ambiri a ku New York asokonezeka maganizo malinga ndi [zauchigaŵenga] zomwe zinachitika pa September 11, ndipo ambiri mwa anaŵa akula ali ndi vutoli.” N’zodetsa nkhaŵa kuti ‘nawonso ana oti panalibe n’komwe pamalo pomwe panachitikira zauchigaŵengazi akusonyeza zizindikiro zakuti anasokonezeka maganizo monga momwe anachitira ana amene anadzionera okha zauchigaŵengazo zikuchitika.’ *

Zingachitikenso chimodzimodzi ndi masoka ena monga kuphulitsidwa kwa mabomba komwe kukuchitika m’dziko la Israel ndiponso kuwombera anthu mwachisawawa m’dera lina lililonse. Pofotokoza za kuwomberana koteroko, katswiri wina woona za vuto la kusokonezeka maganizo anati: ‘Ngakhale anawo atati amakhala makilomita oposa 3,000 kuchokera pamene anthu awomberanapo, zochitika zimenezi zingathe kumawadetsa nkhaŵa kwambiri anawo.’

Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kukagwa tsoka linalake, ana amaona zithunzi zambiri zosonyeza zomwe zachitikazo. Zithunzi zochititsa mantha zosonyeza malo ataphulitsidwa ndi zigaŵenga, kusukulu atawomberana ndi mfuti, ndiponso masoka achilengedwe amazisonyeza mobwerezabwereza, ndipo zimenezi zimachititsa kuti zithunzizo zikhazikike m’maganizo mwa ana ambiri. Ndiye n’zosadabwitsa kuti kafukufuku wina amene anachititsa a bungwe la zamaphunziro ku New York City anasonyeza kuti: “Miyezi isanu ndi umodzi chigwereni Likulu la Zamalonda Padziko Lonse, ana 6,282 pa ana 8,266 a m’sukulu za boma ankaganizirabe mobwerezabwereza zauchigaŵengazo.”

Tikukhala m’masiku amene Baibulo limati “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Kodi mungatani kukagwa masoka oopsa zedi? *

Chomwe Chimachititsa Kuti Pakhale Zopweteka

Imodzi mwa njira zomwe mungathetsere maganizo okulefulani ndiyo kuyamba kulingalira zinthu moona mtima. (2 Petro 3:1) Musapupulume, yesetsani kuganiza bwinobwino kuti muone zinthu monga mmene Mulungu amaonera. Mwachitsanzo, mungafunike kukumbukira kuti masoka ambiri amangotigwera chifukwa cha “nthaŵi ndi zochitika zamwadzidzidzi.” (Mlaliki 9:11, NW) Yesu Kristu anapereka chitsanzo cha zimenezi pamene ananena za kugwa kwa nsanja inayake ya ku Siloamu. Anthu 18 anafa pangozi imeneyo. Komabe, Yesu anafotokoza bwinobwino kuti anthu omwe anafawo sikuti anali kulangidwa ndi Mulungu. Kungoti anali pamalo olakwika ndiponso panthaŵi yolakwika. (Luka 13:1-5) Kuganizira za mfundoyi kungakuthandizeni kukhala ndi maganizo oyenerera pankhani ya masoka.

Kulingalira zinthu moona mtima kungakuthandizeninso kuti musakwiyire Yehova n’kumamuimba mlandu chifukwa cha ngoziyo. (Miyambo 19:3) Yehova satibweretsera mavuto, iye ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Kukagwa masoka, timafunika kuyandikana naye kwambiri osati kutalikirana naye chifukwa cha mkwiyo. Sinkhasinkhani mawu a m’Baibulo a pa Yakobo 1:13, omwe amati: “Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” *

Chitsanzo pa mfundo imeneyi ndi tsoka lina lomwe linagwa ku Middle East zaka zambiri zapitazo. Baibulo limatiuza kuti munthu mmodzi yekha amene anapulumuka tsokalo anabwera ndi uthenga wakuti: “Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa.” (Yobu 1:16) Zinali zoopsatu zimenezi! Ndipo n’zoonekeratu kuti munthu ameneyu, yemwe anali ndi mantha kwambiri, ankaganiza kuti Mulungu ndiye wabweretsa tsokalo. Koma sanali Mulungu, ayi. Yobu 1:7-12 amasonyeza kuti motowo sunatumizidwe ndi Mulungu, koma unatumizidwa ndi Mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi!

Izi n’zosachitikachitika: Yehova analoleza Satana mwapadera kuti ayese kukhulupirika kwa Yobu. Ndiyetu apa osaganiza kuti Satana ndiye amachititsa mwachindunji masoka achilengedwe monga mphepo zamkuntho ndi kusefukira kwa madzi. * Ngakhale kuti zili choncho, Baibulo limanena kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Motero, iye angathe kugwiritsira ntchito anthu kuti awononge zinthu.

Komabe, sitikufunika kutaya mtima. Taganizirani zinanso zimene zinachitika, zomwe zinalembedwa m’Baibulo pa 1 Samueli 22:12-23. Pamenepa timamva za kuphedwa mwankhanza kwa gulu la ansembe okhulupirika limodzi ndi mabanja awo. Mosakayikira Satana anathandizira nawo kuti Mfumu yoipa Sauli ichite zankhanzazi. Komabe, Davide yemwe anali wokhulupirika, amenenso pambuyo pake anadzakhala mfumu, analemba Salmo 52, momwe anafotokozamo chiyembekezo chake choti Mulungu adzawononga anthu oipa omwe anachita zankhanzazo.—Salmo 52:5.

N’chimodzimodzinso ndi masiku ano, dziŵani kuti Mulungu salekerera kuti kuphana ndiponso ziwawa zomwe zikusonkhezeredwa ndi Mdyerekezi zipitirize mpaka kalekale. Onani kuti, Baibulo limatilonjeza kuti posachedwapa Mulungu adzagwiritsira ntchito Mwana wake, Yesu, ‘kuwononga ntchito za Mdyerekezi’! (1 Yohane 3:8) Mkupita kwa nthaŵi sipadzakhalanso chilichonse chosonyeza zoipa zomwe Satana wachita. Mwa kuukitsa anthu kwa akufa, Mulungu angathe kuukitsa anthu, ngakhale amene anafa m’masoka a ziwawa kapena zauchigaŵenga.—Machitidwe 24:15.

Zimene Zingakuthandizeni Kupirira

Kukhulupirira zinthu za m’Baibulozi kungakuthandizeni kuti musalefulidwe ndi mantha. Koma palinso zinthu zina zothandiza zomwe mungachite. Mwachitsanzo, taonani mfundo ya m’Baibulo ya pa Miyambo 12:25. Kufotokozera ena maganizo anu, ndi njira yokhayo yomwe mungalandirire “mawu abwino” oti n’kukulimbikitsani. Kutero kungakuthandizeninso kuzindikira kuti simuli nokha pamavuto anuwo. Motero ngati mukuvutika maganizo, takambiranani zimenezo ndi makolo anu kapena ndi munthu wina wachikulire mu mpingo wachikristu. *

Naŵa malingaliro ena: Chepetsani kuona zithunzi zosonyeza masoka. Kuziona mopitirira muyeso kumangopangitsa kuti muzingokumbukira zomwezo basi.—Salmo 119:37.

Kodi ndinu Mkristu? Ndiyetu pitirizani kuchita zinthu zosiyanasiyana zachikristu. (Afilipi 3:16) Zina mwa zinthuzi ndi monga kusonkhana pamodzi ndi Akristu anzanu ndi kuuza ena za chikhulupiriro chanu. (Ahebri 10:23-25) Kuchita zimenezo kudzakuthandizani kuti maganizo anu asangokhala pa zinthu zofooketsa. Kudzipatula pakati pa anzanu kungathe kungokusokonezani maganizo ndiponso kungawononge moyo wanu wauzimu.—Miyambo 18:1.

Kupitiriza kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kungathandize kwambiri nthaŵi zonse pamene mutu wathu sukugwira bwinobwino. Mayi wa mtsikana wina dzina lake Loraine ankadwala matenda a kansa mwakayakaya. Taonani mmene Loraine anapiririra vutoli. Iye anati: “Ndikukumbukira kuti ndinaŵerenga buku la Yobu maulendo angapo nthaŵi ya zothetsa nzeruzi. Buku la Masalmo nalonso linkandilimbikitsa kwambiri. Ndinkati ndikamaŵerenga mawu olimbikitsa a m’Malemba, ndinkamva ngati kuti Yehova akundikumbatira.” Nayenso mng’ono wake, dzina lake Mishael, anati: “Sindinkamva bwino tsiku lina likangodutsa osaŵerenga Baibulo. Zikatero, m’maganizo mwanga munkangokhala zinthu zofooketsa zokhazokha. Kuŵerenga Baibulo kunkandipatsa nyonga zauzimu zomwe zinkandithandiza kupirira tsiku ndi tsiku.”

Ngati mwaonekedwa zovuta, makamaka imfa ya munthu amene mumam’konda, mungalimbikitsidwe kwambiri poŵerenga kabuku ka Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. * Pezani nthaŵi yoŵerenga ndi kusinkhasinkha za malemba onse omwe sanagwidwe mawu. Komanso, sinkhasinkhani za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. Loraine anati: “Nthaŵi zina zimangokhala ngati ndikuwaona amayi akubwera, ataukitsidwa kwa akufa. Ndimayerekezera ndikuwamva akunena kuti: ‘Ndabwera. Mwaphika chiyani tsopano choti tidye?’ Ndikatero ndimamwetulira.”

Kudalira Yehova m’pemphero kungakupatseninso mphamvu kuti mupirire masoka akuluakulu kwambiri. Loraine anati: “Pamene amayi anga ankatsirizika, ndinali m’chipinda momwemo. Zitangotero, ndinapempha Yehova kuti andipatse mphamvu kuti ndipirire zimenezo. Nthaŵi yomweyo, ndinakhala ndi mtendere wa Mulungu.” Popemphera kwa Yehova, tchulani mosapita m’mbali zinthu zomwe mukufuna. M’fotokozereni mmene mukumvera. “Tsanulirani mitima yanu pamaso pake,” amalimbikitsa motero wamasalmo.—Salmo 62:8.

N’zosakayikitsa kuti mtsogolomu zinthu zosautsa mtima ziziwonjezeka padziko pano. (2 Timoteo 3:13) Koma Baibulo limatilonjeza kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:9-11, 29) Kukhulupirira kwambiri lonjezo limeneli kudzakuthandizani kupirira kukagwa masoka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha maina ena.

^ ndime 6 Malinga n’kunena kwa akatswiri a za maganizo, zina mwa zizindikirozi ndi kusakhudzidwa mtima, kulota zoopsa, kudzipatula, kusachita zinthu mwachizoloŵezi, komanso kudziimba mlandu ndiponso kukhala waukali.

^ ndime 9 Ngakhale kuti nkhani ino ikunena makamaka za masoka akuluakulu, malangizo ake angagwirenso ntchito tsoka likagwera munthu payekha, monga kuferedwa munthu amene amamukonda.

^ ndime 12 Kuti mumve tsatanetsatane wa chifukwa chimene Mulungu walolera kuipa, onani mutu 7 wa buku la Lambirani Mulungu Woona Yekha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 14 Onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya December 1, 1974.

^ ndime 18 Mwina pangafunike kupita kuchipatala ngati kuvutika maganizoko kwafika poipa kwambiri.

^ ndime 22 Kabukuka n’kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 18]

Ndi bwino kuchepetsa kuona zithunzi zosonyeza zinthu zosokoneza maganizo