Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Njira Yeniyeni Yothetsera Vutoli Ingapezekedi?

Kodi Njira Yeniyeni Yothetsera Vutoli Ingapezekedi?

Kodi Njira Yeniyeni Yothetsera Vutoli Ingapezekedi?

CHIWAWA chikuoneka kuti chatenga malo kulikonse masiku ano. Ngakhale kuti pali anthu amene akuyesetsa kugwira ntchito zothandiza anzawo ovutika, apolisi, ndiponso odziŵa kuthandiza anthu achiwawa kuti asinthe, zochitika za m’dzikoli zayamba kuopsa kwambiri. Kodi njira yothetsera zimenezi ilipo?

Baibulo limasonyeza kuti nthaŵi ikubwera yakuti zinthu zisinthe kwambiri. Zimenezi sizidzachitika chifukwa cha khama limene maboma a anthu angachite. Anthu onse amene amalamulira, kaya zolinga zawo zikhale zabwino bwanji, penapake iwo amalepherabe ndithu. Vuto n’lakuti iwo alibe mphamvu zoti n’kuthetseratu chimene chimapangitsa anthu kukhala achiwawa kapena kuti sangathe kukhazikitsa chitetezo kwa muyaya.

Kusintha kwa zinthu kumene Baibulo limatchula kudzachitika chifukwa cha Mlengi wathu. Iye monga wopanga chilengedwe chonse, ali ndi mphamvu ndiponso ufulu wonse wochita zinthu zimene anthu sangakwanitse. Baibulo limam’fotokoza kuti ndiye ‘amene asandutsa akalonga kuti akhale achabe, nasandutsa oweruza a dziko lapansi akhale opanda pake . . . , ndiponso ali wolimba mphamvu.’ (Yesaya 40:23-26) Kodi ndi zinthu ziti zimene Mulungu amalonjeza kuti zidzasintha, ndipo ndi motani mmene zinthuzi zimatilimbitsira mtima kuti dzikoli lidzakhala labwinopo?

Lemba la Salmo 37:10 limatiuza zimene Mulungu analonjeza kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.” Mulungu akufuna kuchotseratu anthu onse oipa okanika kusintha amenenso sakufuna n’komwe kusintha. Koma sadzawononga anthu ena onse ayi. Wamasalmo akulonjeza anthu onse amene akufunitsitsa kukhala ofatsa, odzichepetsa, ndiponso amtendere kuti: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko: Pakudulidwa oipa udzapenya.” Oipa onse akadzatha, anthu onse otsala adzakhala nawo “mtendere wochuluka,” popandanso chiwawa chamtundu wina uliwonse.—Salmo 37:11, 34.

M’pofunika Kuti Anthu Asinthe Maganizo ndi Mtima

Si kuti kungowononga anthu oipa ndi kupulumutsa abwino n’kokwanira kuti vutoli litheretu. Kaŵirikaŵiri anthu amakhala achiwawa chifukwa chakuti sanaphunzitsidwe bwino kuugwira mtima wawo. Choncho, pamenepa m’pamene boma la Mulungu lingapambanire maboma ena onse. Anthu adzalangizidwa ndiponso kuphunzitsidwa bwino pofuna kuti adzakhale okonda chilungamo. Yesaya 54:13 amati: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.”

Zikadzatero, ndithudi zinthu zidzakhala bwino kwambiri! Mochitira chitsanzo, Baibulo limafotokoza kusintha kumene adzachite anthu amene mwina anali ndi makhalidwe auchinyama. Limati: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi.” N’chifukwa chiyani zidzakhale choncho? “Chifukwa chakuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:6, 9) Komano si zoti inu ndi am’banja mwanu muchite kudikira nthaŵi imeneyi kuti mudzaone zoterezi. Bwanji tikutero?

Mungapindule Panopo

Pali anthu amene panopo akusintha pokonzekera dziko lopanda chiwawa. Avala kale umunthu watsopano umene Mulungu amafuna kuti anthu odzakhala m’dziko lake latsopano akhale nawo. (2 Petro 3:13) Anthuwo amachita zimenezi potsatira mfundo za m’Baibulo m’moyo mwawo. Taonani izi zochititsa chidwi zimene Baibulo limanena: “Mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.”—Aefeso 4:23, 24.

Akolose 3:12-14 amapitiriza kufotokoza za makhalidwe abwino amene anthu ambiri okhulupirika akuwasonyeza panopo. Amati: “Valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”

Kodi mukufuna kuti muthandizidwe kuvala umunthu watsopano wachikristu? Anthu ambirimbiri padziko lonse anayamba kale kuchita zimenezo pothandizidwa ndi Mboni za Yehova. Ngakhale anthu amene poyamba ankachita ziwawa zoopsa aphunzira kukhala anthu amtendere pamisonkhano imene imachitika nthaŵi zonse m’Nyumba za Ufumu, ndiponso pamisonkhano inanso ikuluikulu. * Ngati nanunso mukufuna kuti mupindule chifukwa cha ntchito yabwino kwambiriyi yophunzitsa anthu Baibulo, musazengereze kuwafotokozera amene amafalitsa magazini ino. Iwo adzakondwa kukuthandizani kuti mukhale m’gulu la anthu amene panopo akukonzekera kudzakhala m’dziko la Mulungu lopanda chiwawa.

[Mawu a M’munsi]

[Chithunzi patsamba 10]

Anthu ambirimbiri akuphunzitsidwa kuti adzathe kukhala m’dziko lopanda chiwawa