Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Ndinaphera Ludzu la Mawu a Mulungu

Mmene Ndinaphera Ludzu la Mawu a Mulungu

Mmene Ndinaphera Ludzu la Mawu a Mulungu

YOSIMBIDWA NDI LUCIA MOUSSANETT

KUMPOTO chakumadzulo kwa dziko la Italy, kuli chigawo china chotchedwa Valle d’Aosta ndipo chigawochi chili kufupi ndi mapiri a Alps a m’dziko la Switzerland komanso phiri lotchuka kwambiri la ku France la Mont Blanc. Kumeneku n’komwe ndinabadwira mu 1941, m’kadera kotchedwa Challant St. Anselme.

Ndinali mwana wachisamba m’banja la ana asanu, ndipo azing’ono anga onse anayi anali aamuna. Amayi anga anali munthu wakhama pantchito ndiponso anali Mkatolika wolimbikira kwambiri kupembedza. Nawonso abambo anga ankachokera kubanja lopembedza. Azilongo awo aŵiri anali masisitere. Makolo anga analolera kumakhala moyo wozunzika n’cholinga choti ndikule bwino kuphatikizaponso kuti ndiphunzire sukulu. Masiku amenewo m’dera lathulo munalibe sukulu, motero nditakwanitsa zaka 11, makolo anga ananditumiza kusukulu ina yogonera komweko yomwe inkayendetsedwa ndi masisitere.

Kusukulu imeneyo, ndinaphunzirako Chilatini ndi Chifalansa, komanso maphunziro ena. Kenako, nditakwanitsa zaka 15, ndinayamba kuganizira mwakuya za mmene ndingatumikirire Mulungu. Ndinaona kuti njira yabwino kwambiri yotumikirira Mulungu ndi yokakhala ku nyumba ya masisitere. Koma makolo anga sanagwirizane nawo maganizoŵa chifukwa chakuti kutero kukanapangitsa kuti amayi azisamalira okha azichimwene anga aja. Makolo angawo ankaŵerengera kuti maphunziro anga adzandithandiza kukhala pantchito yabwino ndiponso kuti ndizidzapezera banjalo chithandizo.

Ngakhale kuti sindinasangalale ndi maganizo awowo pankhaniyi, ndinkafunabe kukhala ndi moyo waphindu ndipo ndinkafuna kuti Mulungu azikhala woyamba m’moyo wanga. Motero, mu 1961, ndinapita kukakhala ku nyumba ya masisitere a Roma Katolika.

Usisitere Wanga

M’miyezi yoyambirira, ndinkaphunzira mwambo ndi malamulo a tchalitchi chathu ndipo ndinkagwira ntchito zina zongothandiza kusamalira panyumbapo. Mu August 1961, ndinayamba maphunziro ausisitere ndipo ndinayamba kuvala zausisitere. Ndinasankhanso kukhala ndi dzina latsopano, lakuti Ines, lomwe linali dzina la amayi anga. Atalivomera dzinali, ndinayamba kutchedwa Sisitere Ines.

Ngakhale kuti anthu ambiri omwe ankachita maphunziro ausisitere ankagwira ntchito zina zongothandiza kusamalira panyumbapo, ndinali ndi maphunziro okwanira kuti ndikhale mphunzitsi wa pulayimale. Patatha zaka ziŵiri, mu August 1963, anandilumbiritsa kuti ndiloŵe chipani cha Masisitere a San Giuseppe ku Aosta, m’dziko la Italy. Kenako, oyang’anira nyumba ya masisitere ija anandithandiza kukapitiriza maphunziro ponditumiza ku yunivesite ya Maria Santissima Assunta mumzinda wa Rome.

Nditatsiriza maphunziro anga ku Rome ndi kubwerera ku Aosta mu 1967, ndinayamba kuphunzitsa pa sukulu ya sekondale. Mu 1976, anandiika kukhala mkulu wapasukulupo. Ngakhale kuti ndinkaphunzitsabe maphunziro ena, ndinapatsidwa ntchito yoyang’anira sukuluyo ndipo ndinakhala membala wa bungwe la zamaphunziro la ku Valle d’Aosta.

Ndinkalakalaka kwambiri kuthandiza anthu osauka. Ankandimvetsa chifundo kwambiri. Motero ndinayambitsa ntchito zosiyanasiyana zachifundo, ndipo ina inali yothandiza anthu omwe adwala mwakayakaya oti alibe achibale. Ndinayambitsanso ntchito ina yophunzitsa ana omwe makolo awo achokera kunja kwa dziko lathu. Kuwonjezera pamenepo, anthu osauka ndinkawapezera ntchito ndiponso malo okhala komanso anthu ovutika akadwala ndinkawathandiza kupeza chithandizo. Ndinkayesetsa kuti moyo wanga ukhale wogwirizana ndi malamulo a kapembedzedwe ka tchalitchi chathu.

Panthaŵiyi, ndinkakhulupirira zinthu zomwe Akatolika amaphunzitsa, monga za Utatu, zoti moyo sufa, ndiponso zonse zokhudza nkhani ya tsogolo losatha la munthu. Panthaŵiyo, m’chipembedzo cha Chikatolika ankalola kupempherera pamodzi ndi zipembedzo zina.

Zinthu Zimene Zinayamba Kundisoŵetsa Mtendere

Komabe sindinkasangalala ndi zinthu zina zomwe zinkachitika m’tchalitchi cha Akatolika. Mwachitsanzo, munthu asanabatizidwe ndi kulandira ulimbitso, makolo ndiponso ana ankafunika kuphunzira tanthauzo la zimenezi. Koma ambiri sankabwera ku maphunziro ake, ndipo ena sankayesa n’komwe kuphunzira zimenezi. Komanso, ena akalephera kubatizidwa ndi kulandira ulimbitso pa parishi ina ankangopita ku parishi ina n’kukabatizidwa kapena kulandira ulimbitso kumeneko. Ine ndinkaona kuti zimenezo zinali zachiphamaso chabe.

Nthaŵi zina ndinkasinkhasinkha ndiponso kumafunsa masisitere anzanga kuti, “Kodi anzanga, sitiyenera kumalalikira Uthenga Wabwino m’malo mongolimbana ndi ntchito zina zosiyanasiyana?” Yankho lomwe ndinkalandira linali loti, “Timalalikira kudzera m’ntchito zathu zabwino.”

Kuwonjezera pamenepo, sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani ndifunika kupita kwa wansembe kukalapa machimo. Ndinkaona kuti ndiyenera kumuuza ndekha Mulungu nkhani zodziŵa mwini ngati zimenezi. Komanso, sindinkagwirizana ndi zoloŵeza ndi kumangolakatula mapemphero. Zinkandivutanso kukhulupirira kuti apapa salakwa. M’kupita kwa nthaŵi, ndinaona kuti ndi bwino kukhala ndi chikhulupiriro changachanga pankhani zimenezi n’kungopitiriza kupembedza.

Kulakalaka Nditalidziŵa Bwino Baibulo

Nthaŵi zonse ndinkalilemekeza kwambiri Baibulo komanso ndinkalakalaka n’talidziŵa bwino. Ndikafuna kuchita zinazake kapena ndikafuna kuti Mulungu andithandize, ndinkaŵerenga Baibulo. Ngakhale kuti kunyumba ya masisitere kuja sitinkaliphunzira, ndinkaliŵerenga ndekha. Nthaŵi zonse ndinkachita chidwi kwambiri ndi nkhani ya pa Yesaya 43:10-12, pomwe Yehova Mulungu ananena kuti, “Inu ndinu mboni zanga.” Koma panthaŵiyo, sindinkazindikira bwinobwino tanthauzo la mawu ameneŵa.

Panthaŵi ija yomwe ndinali ku yunivesite ku Rome, chamkatikati mwa m’ma 1960, ndinachita maphunziro apamwamba a zaumulungu omwe anakonzedwa ndi a ku Vatican. Koma pamabuku omwe tinkaphunzira panalibepo Baibulo. Nditabwerera ku Aosta, ndinachita nawo misonkhano yambirimbiri yolimbikitsa mgwirizano pakati pa zipembedzo zachikristu, ngakhalenso ina yomwe inakonzedwa ndi mabungwe a zipembedzo zosiyanasiyana ndiponso mabungwe omwe si a Tchalitchi cha Katolika. Zimenezo zinakulitsa kwambiri njala yanga yofuna kudziŵa zimene Baibulo limaphunzitsa. Panali chisokonezo chachikulu pakati pa magulu amene ankati zimene amaphunzitsa n’zochokera m’buku limodzimodzi lomwelo!

Kuphunzira Baibulo Mokwanira

M’chaka cha 1982, mayi wina wa Mboni za Yehova anabwera pamalo omwe ndinkagwira ntchito zachifundo n’kuyamba kukambirana nane za m’Baibulo. Ngakhale kuti ndinali wotanganidwa kwambiri, ndinasangalala kwambiri ndi mfundo yoti ndiphunzire Baibulo. Motero ndinamuuza kuti, “Chonde, muzibwera kusukulu kwathu, ndipo tikhoza kumakambirana ndikapeza mpata.”

Ngakhale kuti mayiyo ankabweradi, mpata womwe ndinkati ukhoza kumapezekawo sunkapezeka. Kenako amayi anga anawapeza ndi matenda a kansa, motero patapita kanthaŵi ndinapempha tchuthi kuti ndizikawathandiza. Atamwalira mu April 1983, ndinabwerera kuntchito, komano panthaŵiyo a Mboni aja sankadziŵa kuti ndili kuti. Koma patangotha nthaŵi pang’ono, mtsikana wina wa Mboni, wa zaka za m’ma 25, anabwera kudzacheza nane za Baibulo. Nthaŵiyi n’kuti n’taŵerenga pandekha buku la m’Baibulo la Chivumbulutso. Motero ndinam’funsa kuti, “Kodi anthu 144,000 otchulidwa pa Chivumbulutso chaputala 14, ndani?”

Ineyo ndinali nditaphunzitsidwa kuti anthu onse abwino amapita kumwamba, ndiye sindinkamvetsa chifukwa choti kumwambako anthu 144,000 ameneŵa akasiyanitsidwe ndi anzawo. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi anthu 144,000 ameneŵa ndani? Amakachita chiyani?’ Ndinakhala ndikusinkhasinkha za mafunso ameneŵa. Wa Mboni uja anapitiriza kumabwera, koma nthaŵi zonse sankandipeza chifukwa choti sindinkakhala pansi.

Patapita nthaŵi, wa Mboni uja anapereka adiresi yanga kwa Marco, mkulu wa mumpingo wake. Ndiyeno mkulu uja anadzandipeza mu February 1985. Chifukwa choti ndinali wotanganidwa, tinayankhulana kwa mphindi zochepa chabe, koma tinagwirizana kudzakumananso. Kenaka, iye ndi mkazi wake, Lina, anayamba kumandichezera nthaŵi ndi nthaŵi, n’kumandithandiza kuti ndilimvetsetse Baibulo. M’nthaŵi yochepa chabe, ndinayamba kuona kuti Baibulo siliphunzitsa m’pang’ono pomwe za Utatu, zoti moyo sufa, ndiponso za moto wa helo ndipotu izi n’ziphunzitso zikuluzikulu za Akatolika.

Kusonkhana ndi a Mboni

Ndikapita kumsonkhano wa Mboni za Yehova ku Nyumba yawo ya Ufumu, ndinkaoneratu kuti ankachita zinthu mosiyana kwambiri ndi ku tchalitchi cha Akatolika. Aliyense ankaimba nawo nyimbo osati kwaya yokha. Kenaka onse ankakhala ndi mwayi woti n’kuyankhulapo pa msonkhanowo. Ndinayambanso kuona kuti gulu lonse la a Mboni linali la “abale” ndi “alongo.” Anali anthu oganizirana kwambiri. Ndinachita nazo chidwi kwambiri zinthu zimenezi.

Nthaŵi imeneyo, ndinkapita kumisonkhano nditavala zausisitere. Anthu ena ankachita kuoneka kuti akuchita chidwi kwambiri kuona sisitere pa Nyumba ya Ufumu. Ndinkasangalala komanso mtima unkakhala m’malo chifukwa cha chikondi cha banja lalikululi. Komanso, pophunzira, ndinayamba kuzindikira kuti zinthu zambiri zomwe ndinkatsatira pa moyo wanga sizinkagwirizana ndi Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, Baibulo silinena kuti atumiki a Mulungu azivala zovala zapadera. Mmene anthu m’matchalitchi amakokomezera maudindo komanso miyambo yodzionetsera zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa ponena za akulu odzichepetsa otsogolera mpingo.

Ndinkangoona kuti ndinali n’tatayikiratu. Zinali zovuta kwambiri kukhulupirira kuti ndinali wosochera chonchi kwa zaka 24. Komabe, zinali zoonekeratu kuti zomwe ndinayamba kuphunzirazi ndiye choonadi cha m’Baibulo. Zinkandiopsa kwambiri kuganizira kuti munthu wa zaka 44 ngati ine ndikufunika kuyamba moyo wina. Komano, kodi ndikananyalanyaza bwanji kuchita zimenezo nditaona zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa?

Chichitike Chichitike Basi

Ndinkadziŵa kuti ndikhala paumphaŵi wadzaoneni ndikachoka kunyumba ya masisitere kuja. Koma ndinakumbukira mawu a Davide onena za anthu olungama kuti ‘sangasiyidwe, kapena mbumba yawo singapemphetse chakudya.’ (Salmo 37:25) Ndinkadziŵa kuti ndikhala moyo wozunzika, koma ndinadalira Mulungu, n’kumadzilimbitsa mtima kuti, ‘Chochitiranso mantha n’chiyani?’

Achibale anga ankaganiza kuti ndayamba misala. Ngakhale kuti sindinasangalale ndi zimenezo, ndinakumbukira mawu a Yesu akuti: ‘Anthu okonda atate awo kapena amayi awo koposa Ine, sayenera Ine.’ (Mateyu 10:37) Komanso zina n’zina zimene a Mboni ankachita zosonyeza kuti amandikonda zinkandilimbikitsa kwambiri. Ndikamayenda mu msewu nditavala zausisitere, iwo ankayesetsa kundipatsa moni. Zimenezi zinandipangitsa kukondana kwambiri ndi abale ndi alongo ndiponso kumamva kuti ndine mnansi wawo.

Kenako ndinapita kwa Sisitere Wamkulu, n’kumufotokozera chifukwa chomwe ndaganizira zosamuka panyumbayo. Ngakhale kuti ndinamuuza kuti ndingathe kum’sonyeza m’Baibulo zomwe zandiganizitsa zimenezo, iye anakana, n’kunena kuti: “Ineyo n’tafuna kumvetsa chilichonse cha m’Baibulo, ndingakafunse kwa katswiri wa Baibulo!”

Tchalitchi cha Katolika chinakhumudwa ndi zimene ndinachitazi. Anandinena kuti ndayamba kufuna amuna ndiponso kuti ndayamba misala. Koma ondidziŵa bwino ankadziŵa kuti zimenezo zinali zabodza. Nkhaniyi inawakhudza mosiyanasiyana anthu omwe ndinkagwira nawo ntchito. Ena ankati kumeneko kunali kulimba mtima. Ena zinawapweteka kwambiri poganiza kuti ndayamba kutayika. Ena ndiye ankachita kundimvera chisoni kumene.

Pa July 4, 1985 ndinasiya Chikatolika. Podziŵa zimene anthu ena ankawachita akapanga zotere, a Mboni ankachita mantha kuti mwina andichita chipongwe, motero anakhala akundibisa pafupifupi mwezi wathunthu. Ankanditenga pagalimoto kupita nane kumisonkhano kenako n’kukanditula komwe ndinkakhala. Ndinakhala ndikubisala mpaka pamene zinthu zinazizirako. Kenako pa August 1, 1985, ndinayamba kulalikira pamodzi ndi Mboni za Yehova.

Nditapita ku Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova chakumapeto kwa mwezi umenewo wa August, atolankhani a manyuzipepala, mawailesi, ndiponso a TV anadziŵa zoti ndasiya Chikatolika ndipo anafalitsa nkhaniyo. Nditabatizidwa pa December 14, 1985, a TV yakwathuko komanso a nyuzipepala anaona kuti zinali zamanyazi kwambiri moti anafalitsanso nkhani imeneyi, kuti aliyense amve zomwe ndachitazo.

Kunyumba ya masisitere kuja ndinangochokako chimanjamanja. Ndinali lova, ndinalibe nyumba, ndiponso sindinkalandira ndalama iliyonse ya munthu wopuma ntchito. Motero pafupifupi kwa chaka chathunthu, ndinkagwira ntchito yosamalira munthu wina wolumala. Mu July 1986, ndinakhala mpainiya, lomwe ndi dzina la mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Ndinasamukira ku dera lina komwe kunali mpingo waung’ono wongokhazikitsidwa kumene. Kumeneko ndinayamba kuphunzitsa pandekha chinenero komanso maphunziro ena, motero ndinapeza mwayi wogwiritsira ntchito maphunziro anga. Zimenezi zinkandipatsa mpata wotha kuchita zinthu zina ndi zina.

Kutumikira M’dziko Lina

Popeza tsopano ndinali nditaphunzira choonadi cha m’Baibulo, ndinkafuna kuyesetsa kuti ndiuzekonso anthu ena ochuluka za choonadichi. Poti ndimayankhula Chifalansa, ndinaganiza zokatumikira kudziko lina loyankhula Chifalansa la mu Africa. Koma kenaka mu 1992, Mboni za Yehova zinavomerezedwa m’dziko la Albania lomwe lili kufupi ndi kwathu. Kumapeto kwa chaka chimenecho, kagulu ka apainiya a ku Italy kanatumizidwa kumeneko. M’kagulumo munali Mario ndi Cristina Fazio a mu mpingo wathu. Anthu aŵiriŵa anandiitana kuti ndikawachezere ndiponso anandipempha kuti ndiganizire zokatumikira ku Albania. Motero, n’taiganizira mofatsa komanso kuipempherera nkhaniyi, ndili ndi zaka 52, ndinasiyanso malo abwino ndithu n’kupita kumalo achilendo kwambiri.

Umu munali m’March 1993. Nditangofika, ndinaoneratu kuti ngakhale kuti sindili kutali kwenikweni ndi dziko lakwathu, ndili m’dziko lachilendo kwambiri. Anthu ankayenda pansi akamapita kulikonse komwe akufuna, ndipo chinenero chawo chomwe ankayankhula sindinkamvako n’chimodzi chomwe. Dzikolo linkangosinthasintha ndale zake. Komabe, anthu anali ndi ludzu la choonadi cha m’Baibulo, ndipo ankakonda kuŵerenga ndi kuphunzira. Anthu omwe tinkaphunzira nawo Baibulo ankachita bwino kwambiri pa zauzimu, izi zinkandisangalatsa ndipo zinandithandiza kuti dziko lachilendoli ndilizoloŵere.

Pamene ndinkafika ku Tiranë, likulu la dziko la Albania, mu 1993, mu Albania munali mpingo umodzi wokha ndipo munali Mboni zongopitirira 100, zomwe zinangobalalika m’dziko monsemo. Mwezi umenewo, pa tsiku la msonkhano wapadera woyamba womwe unachitikira ku Tiranë, panasonkhana anthu 585 ndipo anthu 42 anabatizidwa. Ngakhale kuti pamsonkhanowo sindinkamvapo chilichonse, zinali zochititsa chidwi kumva Mboni zikuimba ndiponso kuona kuti zinali zatcheru kwambiri. Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu chinachitika mu April, ndipo panafika anthu 1,318! Kungoyambira pamenepo, ntchito za Akristu a Mboni zapita patsogolo kwambiri ku Albania.

Panthaŵiyo ndinkati ndikaima m’khonde mwa nsanjika yachinayi pa nyumba yomwe ndinkakhala n’kumayang’ana mzinda wa Tiranë ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi tidzatha liti kuwafikira anthu onseŵa?’ Yehova Mulungu anachitapo kanthu. Tsopano mu Tiranë muli mipingo 23 ya Mboni za Yehova. M’dziko lonse la Albania, muli mipingo 68 ndiponso magulu 22 omwe sanafike pokhala mipingo, ndipo Mboni zonse zilipo 2,846. Zonsezi zachitika m’zaka zochepa zomwezi! Ndipo pa Chikumbutso cha chaka cha 2002, panafika anthu 12,795!

M’zaka khumi zomwe ndakhala mu Albania, ndakhala ndi mwayi waukulu kwambiri wothandiza anthu pafupifupi 40 mpaka kufika pobatizidwa. Ena mwa iwo tsopano ndi apainiya ndiponso akuchita mautumiki ena a nthaŵi zonse. M’zaka zonsezi, magulu asanu ndi limodzi a apainiya ochoka ku Italy atumizidwa ku Albania kuti akathandizeko. Gulu lililonse linkaphunzira chinenero cha m’dzikoli kwa miyezi itatu, ndipo ndinaitanidwa kukaphunzitsa makalasi anayi omalizira.

M’mbuyo muja, anzanga atangomva zoti ndikusiya tchalitchi, sanamve bwino ngakhale pang’ono. Komano patatha zaka zonsezi, iwo asinthako maganizo awo poona kuti ndikungodzikhalira bwinobwino. N’zosangalatsa kuti achibale anga, kuphatikizapo azakhali anga omwe ali ndi zaka 93 ndipo adakali sisitere, nawonso anayamba kundimvetsa.

Kuchokera pamene ndinadziŵa Yehova, Iye wakhala akundisamalira pa zinthu zosiyanasiyana! Wanditsogolera kubwera m’gulu lake. Ndikamaganizira za m’mbuyo, ndimakumbukira chikhumbo changa chofuna kuthandiza osauka, ndi ovutika ndipo ndimakumbukiranso cholinga changa chofuna kutumikira Mulungu ndi moyo wanga wonse. Ndiye n’chifukwa chake ndimam’thokoza Yehova poonetsetsa kuti ludzu langa la mawu ake latha.

Ngati mukufuna kudziŵa zambiri kapena ngati mukufuna kuti wina azibwera kudzachita nanu phunziro la Baibulo la panyumba kwaulere, tumizani dzina lanu ndi adiresi ya kumene mumakhala kwa Mboni za Yehova, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5.

[Chithunzi patsamba 31]

Banja la ku Albania lomwe ndinaphunzira nalo Baibulo. Anthu khumi ndi mmodzi m’banjali anabatizidwa

[Chithunzi patsamba 31]

Ambiri mwa azimayi aŵa omwe ndinaphunzira nawo Baibulo ku Albania tsopano akuchita utumiki wa nthaŵi zonse