Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Akusiyana Maganizo pa Zithunzi Zolaula

Anthu Akusiyana Maganizo pa Zithunzi Zolaula

Anthu Akusiyana Maganizo pa Zithunzi Zolaula

“Zimachititsa munthu kulakalaka zimene sayenera kulakalaka ndiponso zimamuchititsa kukhala ndi chikhumbo chochita zimene sayenera kuchita.”—Anatero wolemba nkhani Tony Parsons.

JOHN sanali kuganiza kuti ‘nkhani ndiponso zithunzi zogonana za pa Intaneti’ zingamulowerere kwambiri. * Mofanana ndi anthu ambiri amene amapezeka kuti mwangozi akuona zithunzi zolaula kapena atsegula malo okambiranapo zogonana pa Intaneti, iye tsiku lina mosayembekezera anatsegula malo oterowo pa kompyuta yake. Sipanapite nthaŵi, iye anayamba kukonda kwambiri nkhani zogonana pa Intaneti. “Ndinali kudikira kuti mkazi wanga apite kuntchito,” anatero pokumbukira zimene anali kuchita, “ndiyeno ndimadzuka msangamsanga pabedi ndi kupita pa kompyuta pomwe ndinali kukhalapo maola ambiri.” Panthaŵi zimene anali kukhalitsapo kwambiri, sanali kulekeza n’komwe kuti adye kapena kumwa kanthu kalikonse. Iye anati: “Njala sinali kuŵaŵa ngakhale pang’ono.” Anayamba kunamiza mkazi wake zomwe anali kuchita m’seri. Kuntchito, maganizo ake anali kungoyendayenda osakhazikika bwino pantchitoyo, ndipo anayamba kumadzikayikira akakhala ndi anthu ena. Banja lake linayamba kuvuta. Atafika pokonza zokakumana pamaso m’pamaso ndi mmodzi mwa anthu omwe anali kukambirana nawo zogonana pa Intaneti paja, mkazi wake anaitulukira nkhaniyi. Lero John akulandira thandizo kuti athetse vuto lake lokonda zolaula.

Anthu amene amalimbikitsa kudana ndi zolaula amati nkhani ngati imeneyi ndi umboni wakuti zithunzi zolaula zimachotsa ulemu anthu. Iwo amati zithunzi zimenezi zimathetsa ubwenzi wa anthu, zimanyozetsa akazi, zimachititsa kuti ana azivutika, ndiponso zimapangitsa anthu kukhala ndi maganizo opotoka ndi ovulaza pankhani ya kugonana. Koma okonda zithunzi zolaula amati zithunzizi zimaonetsa ufulu wa anthu wonena kapena kuchita zimene amafuna, ndipo amati amene amadana nazo ndi anthu amene sachedwa kukhumudwa ndi zolaula. “Anthu sayenera kuchita manyazi kuonetsa zimene amafuna pogonana,” analemba motero munthu wina amene saona vuto ndi zithunzi zimenezi. “Poona zithunzi zolaula anthu angayambe kukambirana momasuka za kugonana.” Ena amati kuchuluka kwa zithunzizi kukusonyeza kuti anthu ndi omasuka ndiponso ndi a maganizo abwino. “Anthu ozindikira amene sadzidzimuka nazo zoona zithunzi zoonetsa poyera anthu akuluakulu akugonana mochita kufuna ndiwo amene sangadandaule kuti anthu azigonana m’njira zachilendo ndiponso kuti akazi azikhala ndi ufulu wofanana ndi amuna,” anatero wolemba nkhani wina dzina lake Brian McNair.

Popeza kuti anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana, kodi ndiye kuti zithunzi zolaula ndi zabwinobwino? N’chifukwa chiyani zatenga malo kwambiri? Kodi zithunzizi ndi zoopsadi? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Tasintha mayina.