Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimene Mkuntho Sunathe Kukokolola

Chimene Mkuntho Sunathe Kukokolola

Chimene Mkuntho Sunathe Kukokolola

YOLEMBEDWA NDI OLEMBA GALAMUKANI! A KU GERMANY, AUSTRIA, MEXICO, NDI KOREA

M’CHAKA cha 2002, m’mayiko ambiri munachitika masoka oopsa a zanyengo. Ku Ulaya madzi osefukira anavutitsa kwambiri. M’madera ena padziko lonse monga ku Mexico ndi ku Korea, chimphepo chinabweretsa mvula yamkuntho. Ngakhale kuti zimenezi zinali zosautsa, zinathandiza kwambiri polimbitsa chikondi cha Akristu oona.

Madzi atasefukira ku Ulaya m’chaka cha 2002, a Helmut Schmidt, amene kale anali mtsogoleri wa dziko la West Germany, anafunsidwa kuti anthu okhudzidwa ndi tsokali akufunikira chithandizo chotani. Iwo anayankha kuti: “Anthuŵa akufunikira chakudya, pogona ndi ndalama, ndipo akufunikiranso kuwasamalira mwauzimu.” Pothandiza anthuŵa ndi zinthu zofunikira ngakhalenso zauzimu, a Mboni za Yehova anachita ntchito yaikulu kwambiri. Taonani ntchito imene anachita ku Germany, Austria, Mexico, ndi ku Korea.

Anthu Anadzipereka ku Germany

Anthu atadziŵa kuti kukubwera madzi osefukira, a Mboni za Yehova ambiri ku Germany anagwirizana ndi anthu ena onse pantchito yoyesa kuteteza kuti vutoli lisakule kwambiri. Kathleen, yemwe ali ndi zaka 19, ndipo amakhala ku Dresden ananena kuti: “Sindikanatha kungokhala osachitapo kanthu. Nditangomva kuti anthu ena ali pavuto limene lingawonongetse zinthu zawo zonse, ndinaona kuti ndiyenera kukawathandiza basi.”

A Mboni a ku Germany anayamba kukonzekera kuti athandizepo mwamsanga. Pokhala Akristu, ankaona kuti ali ndi udindo wapadera wothandiza abale ndi alongo awo auzimu. Koma anasonyezanso chikondi kwa anansi awo. (Marko 12:31) Motero panali anthu ongodzipereka oposa 2,000 omwe anawaika m’magulu a anthu 8 kapena 12, ndipo gulu lililonse linapatsidwa ntchito yoti lichite kumene kunagwa tsokako. Pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Selters, ku Germany, matelefoni 13 anawaika kuti angokhala oyankhirapo mafoni ambirimbiri amene anthu ankaimba pofuna kudziŵa za tsokali komanso pofuna kuthandizapo.

Ronnie ndi Dina ndi atumiki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova, amene nthaŵi yawo yambiri imathera pothandiza anzawo ndi anansi awo kuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Atamva za madzi osefukirawo, poyamba anapita m’kati mwa mzinda wa Dresden kuti akathandize pa chintchito cha kalavula gaga chofuna kuteteza nyumba zamakedzana za m’tauniyi. Madziwo ataphwerako, Ronnie ndi Dina anakathandiza anzawo pokonza pa Nyumba ya Ufumu ya ku Freital, imene inali itadzaza ndi madzi oipa. Kenaka gululi linayamba kuthandiza anansi awo. Mwini lesitilanti ina yoyang’anizana ndi nyumbayi anaimba lokoma a Mboniwo atachotsa m’nyumba yakeyo zogumukagumuka komanso matope onse amene anali m’chipinda chapansi ndi chapamwamba pake.

Siegfried ndi Hannelore amakhala m’mudzi wa Colmnitz, umene uli pamtunda wa makilomita 40 kum’mwera cha kum’maŵa kwa Dresden. Kamtsinje kamene kamadutsa pamudziwu kanadzaziratu, n’kusefukira motero kanamiza nyumba yawo ndiponso malo onse ozungulira nyumba yawo. Madziŵa ataphwera, anansi awo anadabwa kwambiri kuona a Mboni 30, achilendo m’derali, atafika kudzathandiza kukonza nyumba ya Siegfried ndi Hannelore. Kenaka, gulu la a Mbonili linayamba kukonza pabwalo pa nyumba za anansi aja. Anthu angapo a m’mudzimo anafuna kudziŵa kuti n’chiyani chinawachititsa a Mboniŵa kuyenda chimtunda cha makilomita 100 kuti akathandize anthu omwe sanawaonepo n’komwe. Motero a Mboniwo analimbikitsa mwauzimu anthu amene anakhudzidwa ndi tsokali ku Colmnitz.

Madera ozungulira tauni ya Wittenberg anakhudzidwanso ndi kusefukira kwa madziku. Madziŵa asanasefukire, Frank ndi mkazi wake Elfriede, omwe ndi a Mboni, anathandizana ndi anansi awo kwa masiku angapo pa ntchito yoika mchenga m’matumba n’kumawasanjikiza kuti atchingire madzi a mtsinjewo. Madzi osefukirawo atachepako, Frank ndi Elfriede anapita kunyumba za anthu okhudzidwa ndi tsokali, kukawapatsa chakudya ndiponso kukawapepesa. Frank anati: “Mayi wina amene tinam’yendera sanakhulupirire kuti ifeyo, anthu oti sitinkam’dziŵa n’komwe, tingam’bweretsere chakudya chaulere. Iye anatiuza kuti palibe aliyense wa ku tchalitchi kwawo amene anabwera kudzamuona. Ndipo bungwe linalake limene linali kum’bweretsera chakudya linkachita kumugulitsa chakudyacho. Anthu anadabwa kwambiri kuona a Mboni za Yehova atanyamula chakudya chotentha, m’malo monyamula mabuku ofotokoza za Baibulo.”

Ku Austria Sanazengereze Kuthandizapo

Madzi osefukira anawononganso kwambiri dziko loyandikana nalo la Austria. Motero anakhazikitsako makomiti atatu kuti ayang’anire ntchito yothandiza anthu. Anayambira kukonza Nyumba za Ufumu zitatu zimene zinawonongeka kwambiri. Komanso pakati pa a Mboni, pafupifupi mabanja 100 anakhudzidwa ndi vutoli, ndipo m’nyumba zokwana 50 munadzaza madzi. Ena sanatsale ndi china chilichonse kupatulapo zovala zomwe zinali m’thupi basi. Ofesi ya nthambi ku Austria inadziŵitsa mipingo ya m’dzikolo za vutoli, ndipo anakhazikitsa thumba la chithandizo. Mmene unkafika mwezi wa September, n’kuti anthu atapereka ndalama zopitirira madola 34,000 ku thumbali.

Mayi wina anati: “Mwana wanga wa mwamuna, wa zaka zisanu ndi zitatu, ngodziŵa kusungira ndalama kwabasi moti anasunga ndalama zokwana pafupifupi madola 14. Komano atamva kuti pali abale athu ena amene katundu wawo yense wawonongeka, iyeyu analolera kupereka ndalama zonsezo ku thumba la chithandizoli.”

Makomiti Omanga Achigawo, omwe ntchito yawo yeniyeni n’kuyendetsa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova, anasonkhanitsa ndi kuyang’anira magulu a anthu amene anadzipereka pofuna kukathandiza kukonza nyumba zimene zinawonongedwa ndi madziwo. Munthu wina amene ankaona zimenezi anati: “M’pofunika kuti manyuzipepala alembe zimene mukuchita panozi.” Anthu ena amene m’mbuyomo sankaona bwino a Mboni za Yehova anafika mpaka posintha maganizo awowo. Mayi wina wa Mboni anati: “Ana anga si a Mboni, moti m’mbuyo monsemu akhala akukana kumvetsera ndikati ndiwauzeko zimene ndimakhulupirira. Koma kwa nthaŵi yoyamba, ayambano kumvetsera!”

Pantchitoyi anayesetsanso kuthandiza anthu ambiri omwe si a Mboni. Mwachitsanzo, mayi wina anagoma kwambiri wa Mboni wina atabwera kunyumba kwake hafu pasiti seveni m’maŵa n’kumufunsa ngati akufunikira thandizo lililonse. Mayiyo anafunika kusamutsidwa m’nyumbayo chifukwa madzi anali atayamba kale kuloŵamo. Ndiye panthaŵi ina atabwereranso kunyumbako, anapeza kakalata pa khomo loloŵera mumpanda wa nyumba yake kochokera kwa a Mboniwo. Kakalatako kanali ndi mawu akuti: “Mukafuna thandizo lililonse, musazengereze kutiuza.” A Mboni anam’thandiza kuchotsa matope ndi zinyalala m’nyumba mwake ndi kutsuka katundu wake.

Gulu la a Mboni 100 linapita m’dera lotchedwa Au kuti likathandize a Mboni a kumeneko komanso anansi awo. Atsogoleri a gululo ankayendera khomo ndi khomo kumafunsa anthu ngati akufunikira thandizo. Anthu anadabwa kwambiri kuona kuti a Mboniwo ankabwera ali chikwanekwane, atatenga zida zoumitsira madzi ndiponso zoyeretsera, monga makina opopera madzi, matsache, ndiponso mafosholo. Ntchito imene eni nyumbazo akanalimbana nayo kwa sabatha yathunthu inatha m’maola ochepa chabe. Anthu oonerera misozi inkachita kulengeza chifukwa chogoma nazo.

A Mboni pafupifupi 400 a kumeneku anachita nawo ntchito yothandiza anthuyi. Ndipo nthaŵi zambiri ntchitoyi ankaichita ndi usiku womwe. Kwa oonerera, uwu unali umboni wosatsutsika wosonyeza kuti Chikristu chenicheni si zocheza ayi.

Mphepo Yamkuntho Yotchedwa Isidore Inakantha Mexico

Mphepo yamkuntho yotchedwa Isidore inayambira kumpoto kwa dziko la Venezuela. Ndiye pa September 22, 2002, mphepoyi inakantha chigawo cha Yucatán Peninsula, ku Mexico ndipotu apa inali yamphamvu kwambiri. Liŵiro lake linali makilomita 190 pa ola ndipo inabwera ndi chimvula choopsa. Mphepoyi inawononga zinthu kwambiri kuposa china chilichonse chimene chinawonongapo zinthu m’maboma a ku Mexico a Yucatán ndi Campeche komanso inawononga m’boma la Quintana Roo. Ku Yucatán kokha, nyumba zokwana 95,000 zinawonongeka modetsa nkhaŵa, moti anthu pafupifupi 500,000 anakhudzidwa.

Mboni za Yehova zinathandiza kwambiri ku Yucatán moti nyuzipepala ina ya kumpoto kwa Mexico inali ndi nkhani ya mutu wakuti: “A Mboni za Yehova Apulumutsa Anthu.” Komiti yachithandizo inakhazikitsidwa mphepo ya mkunthoyi isanafike. Anakonzeratu malo kuti a Mboni ochuluka a kuderali adzapeze pogona. Mipingo yozungulira derali inapereka ndalama zothandizira patsoka. Anthu amene anapulumuka pa tsokali, omwe ena ambiri sanali a Mboni, anawagaŵira zovala, mankhwala, ndiponso zakudya zopitirira matani 22. Akulu a kumeneko anapatsidwa ntchito yoyendera ndi kulimbikitsa anthu okhudzidwa ndi mphepoyi.

Mphepoyi itapita, a Mboni a kumeneko anakonza makomiti achithandizo kuti athandize kufunafuna a Mboni anzawo amene anasoŵa. Ena anapezedwa ali kutchire ndiponso malo ena ndi ena, atakhala mwina kwa masiku atatu osadya kapena kumwa chilichonse. M’madera ena madzi anadzaza kwambiri moti mpaka anamiza mapolo a magetsi! Motero anapeza maboti a injini kuti azifufuzira anthu, kukawapatsira chakudya, kuwanyumula n’kukawatula kwina kumene kunali kwabwino.

Akuluakulu a boma a kumeneko anabwereketsa maboti ndi zida zawo zina kwa a Mboniwo pakuti anadzipereka kuti akathandiza ku madera amene anthu ambiri sankayerekeza n’komwe kupitako. Poyamba mkulu wina wa asilikali anakana zoti a Mboniwo akafunefune anthu m’madera oopsaŵa. Komano ataona khama lawo losaopa nalo kanthu, iye anati: “Sindikukayika n’komwe kuti anthu inu mungalolere ngakhale kuyenda pa ndege za helikopitala kuti mukapulumutse anthu anu. Mukhoza kugwiritsira ntchito magalimoto athu kuti mukatengere abale anu n’kupita nawo kulikonse kumene mukufuna.”

Mwini sitolo wina anafuna kudziŵa kuti kwachitika zotani ataona a Mboni ena akugula madzi ambirimbiri a m’mabotolo. Motero iwo anamufotokozera kuti abale awo auzimu komanso anthu ena akufunikira madziwo. Atamva zimenezi munthuyu anaganiza zongowapatsa kwaulere madzi onse a m’mabotolo amene iye anali nawo. Maŵa lake mkuluyu anaperekanso mabotolo ena a madzi ndipo anali ambiri ndithu. Pasitolo ina, munthu wodzagula zinthu anafunsa a Mboniwo kuti n’chifukwa chiyani akugula chakudya chambiri choncho. Atamva kuti akugulira anthu ovutika pa tsokalo, iye anawapatsa ndalama kuti awonjezere zakudyazo.

Ngakhale kuti katundu yense wa mabanja pafupifupi 3,500 a Mboni anawonongedwa chifukwa cha mphepo yamkuntho ya Isidore, panalibe wa Mboni za Yehova aliyense amene anasoŵa kapena kufa. Komabe panafunika ntchito yomanganso nyumba chifukwa nyumba 331 za a Mboni, zinali zitawonongeka pang’ono, kapena kugumukiratu. A Mboni odziŵa zomangamanga anayendera nyumba iliyonse kuphatikizaponso Nyumba za Ufumu kuti aone mmene zinawonongekera. Pakali pano nyumba 258 anazikonza ndipo anamanganso nyumba zina 172 zatsopano. Komanso Nyumba za Ufumu 19 zimene zinagumukiratu panopo zili m’kati momangidwanso.

Mkulu wina wa mumpingo winawake wa ku Yucatán ananena kuti: “Ndakhala ndikuŵerenga m’mabuku athu nkhani zofotokoza ntchito zosiyanasiyana zothandiza anthu zimene zakhala zikuchitika m’mayiko ena. Koma panopa, ndikutha kusiyanitsa chifukwa ineyo pandekha ndachita nawo ntchitoyi. Chikhulupiriro changa ndiponso cha abale ambiri chalimbikitsidwa poona changu ndiponso kuganizirana kumene gulu la Yehova ndiponso abale athu okondedwa asonyeza potithandiza.”

Mayi wina anati: “N’kanakonda tchalitchi changa chikanathandizapo ngati inuyo a Mboni.” Ndipo mayi winanso, amene anapulumutsidwa ndi a Mboni anati: “Chipanda a Mboni za Yehova bwenzi titafa. Anasonyeza chikondi chawo poika moyo wawo pachiswe kuti atipulumutse pamene nyumba yathu inamira ndi madzi.”

Chimvula Champhepo Chinakantha Dziko la Korea

Pa August 31 ndi September 1, 2002, chimvula champhepo chotchedwa Rusa chinakantha mbali yaikulu ya dziko la Korea. Song-pil Cho, yemwe ndi mkulu mumpingo wina anati: “Zinkangokhala ngati kuti madziwo akutuluka pa mpopi wa shawa. Ndipo chimvulachi chinali chamvumbi.” Pasanathe n’komwe maola 24 kunagwa chimvula chimene chinaloŵa pansi mamilimita 870 ndipo zoterezi sizinachitikepo kumeneku n’kale lonse.

Nyuzipepala yotchedwa Korea Herald, inati m’dziko lonselo, nyumba 28,100 ndiponso mafamu okwana maekala 210,000 anamira m’madzi. Moti anthu 70,000 anafunikira kusamuka. Chimvulachi chinapha ziŵeto 301,000, chinamiza sitima za pamadzi 126, ndipo chinagwetsa mapolo ambirimbiri a magetsi. Anthu opitirira 180 akuti anasoŵa kapena anafa ndipo aŵiri anali a Mboni za Yehova.

Mboni za Yehova zinathandizapo mwamsanga kwambiri monga mmene zinachitira ku Ulaya ndi ku Mexico kuja. Mboni za m’madera onse a dzikolo zinapereka thandizo la zinthu zosiyanasiyana. Zinthuzi zinali zovala, mabulangete ndi zinthu zina zofunikira. Komabe anthu ena a mumpingo anali kumadera omwe sizikanatheka kufikako mosavuta. Misewu ya m’maderawo inawonongeka, ndiponso milatho inapita ndi madzi. Kunalibe magetsi kapena mafoni. Motero anakonza timagulu toyenda wapansi kukapereka chithandizo kumeneku. Song-pil Cho, amene anagwira ntchito m’kagulu kena koteroko, analongosola mmene zinthu zinalili m’dera linalake limene anathandizapo. Iye anati: “Milatho isanu ndi iŵiri ndiponso mbali zazikulu za msewu zinali zitawonongekeratu ndi madziwo. Mmene ifeyo tinkafika m’deralo, nyumba zambirimbiri zinali zitawonongeka ndipo zina zitagumukiratu. Munali chifungo chosaneneka ndipo mitembo ya nyama zakufa inangoti mbwee. Koma tinasangalala kwambiri titakumana nawo abale ndi alongo athu achikristu asanu ndi mmodzi. Katundu wawo anali atawonongekeratu, koma onse anali moyo ndipo anali bwinobwino.”

Kwenikweni tingati a Mboni za Yehova tsoka limeneli analikonzekera. Pakuti zoterezi sizachilendo nthaŵi ya mvula, Komiti Yomanga Yachigawo ya m’dera la Seoul inali itayamba kale kukonzekera zodzathandiza ngati kutagwa tsoka lotereli. Kungoyambira mu 1997, chaka n’chaka komiti imeneyi yakhala ikuthandiza pophunzitsa anthu ongodzipereka kuti ngati patachitika tsoka lotere anthuwo adzakhale chikwanekwane.

Pa September 2, antchito othandiza a m’komiti imeneyi anafika mumzinda wa Kangnŭng womwe uli cha kum’maŵa, m’mphepete mwa nyanja, ndipo anakhazikitsa likulu lawo pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova ya m’deralo. Koma kodi ntchito yawo yoyamba inali yotani? Inali yopereka madzi abwino kwa anthu amene anapulumuka pa tsokali. Madzi akasefukira motere, nthaŵi zambiri mapaipi a madzi amawonongeka. Madzi osefukira amakhala oipa kwambiri. Komiti Yomanga Yachigawo inakonza zoti magalimoto akuluakulu a mathanki a madzi apite m’madera okhudzidwa ndi tsokali.

Madzi osefukira akaphwera, chilichonse chimakutidwa ndi chithope chonunkha. Koma anapanga njira yothandiza kwambiri yokonzera zinthu zotere. Pakuti pafupifupi nyumba zonse m’derali n’zopangidwa ndi simenti, n’kutheka kukonzamo m’nyumbazo pochotsamo zimene amamata m’makoma ndiponso pansi n’kutsukamo pothiramo madzi otuluka mwamphumvu kuchokera mu paipi.

Madzi osefukira amawononga zipangizo zambiri zamagetsi. Komano anthu odziŵa zamagetsi akazimasula pasanapite masiku ambiri n’kuzitsuka, kuziumika, ndiponso kuzibwezeretsa m’chimake, zipangizo monga mafiliji ndi zotenthetsera m’nyumba nthaŵi zambiri zimatha kuyambanso kugwira ntchito. Komiti Yomanga Yachigawo imakhala chikwanekwane kuchita ntchito imeneyi. Zipangizo zotenthetsera m’nyumba zimene sizinawonongeke amazigwiritsira ntchito poumika m’nyumbamo. Ntchito imeneyi imatenga milungu iŵiri kapena itatu.

Mabulangete ndiponso zovala zimene zawonongedwa ndi madzi osefukiraŵa amayeneranso kuzichapa bwinobwino pasanathe masiku ambiri kuti zisawonongekeretu. Anthu ongodzipereka ochokera mumpingo wina wa Mboni za Yehova m’deralo anathandiza kutolera zinthu zonse zoterezi za abale awo achikristu. Thope limene linaloŵa m’zovala ndi zofunda zimenezi linali lovuta kwambiri kulichapa. Komanso ankachapa pamanja, m’kamtsinje kozizira kwambiri. Mtolankhani wina atamva za ntchito yosonyeza chikondi yotereyi, m’nyuzipepala anajambulamo chithunzi chachikulu cha a Mboniŵa akugwira ntchitoyi.

Madzi osefukira ku Ulaya, North America, ndi ku Asia anakokolola nyumba, katundu, ndiponso anthu ambirimbiri opanda chifukwa. Ngakhale kuti izi n’zomvetsa chisoni, zafala kwambiri “masiku otsiriza” amene tikukhala ano, amene atchuka ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” (2 Timoteo 3:1) Koma masoka otereŵa angathenso kutithandiza kwambiri kukumbukira mfundo iyi yakuti: Akristu oona amakondana ndiponso amakonda anansi awo. Chikondi chopanda dyera chotere palibe mkuntho umene ungachikokolole.

[Chithunzi patsamba 10]

GERMANY—Nyumba iyi inawonongeka ndi chimvula

[Zithunzi patsamba 11]

GERMANY—Anthu ongodzipereka pafupifupi 2,000 anathandizapo mwamsanga

[Zithunzi patsamba 12]

AUSTRIA—Kukonza Nyumba yawo ya Ufumu ku Ottensheim

Kumanzere: Gulu la anthu ongodzipereka likubwerako ku Au, komwe limakathandiza a Mboni a kumeneko komanso anansi awo

[Zithunzi patsamba 13]

MEXICO—Kumanja: Komiti yachithandizo ikupereka madzi akumwa kwa anthu opulumuka pa mkuntho

Pamunsi: Kumanga nyumba yatsopano

[Zithunzi patsamba 15]

KOREA—Kuchoka kumanzere kupita kumanja: Mbali ya mzinda imene madzi anasefukira; kukonza malo powatsuka ndi madzi otuluka mwamphamvu kuchokera mu paipi; kuchapa zovala m’kamtsinje ka pafupi