Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera kwa Wokondedwa

Kalata Yochokera kwa Wokondedwa

Kalata Yochokera kwa Wokondedwa

Munthu wina wa ku New York ataŵerenga buku lakuti Yandikirani kwa Yehova analiyerekezera ndi kalata yochokera kwa munthu wina wokondedwa, n’kufotokoza kuti: “Mutu uliwonse umangokusiya mtima uli dyokodyoko kufuna kumva zambiri ndipo umangokuchititsa kuti um’konde kwambiri Yehova.” Ananenanso kuti: “Panopo poti ndamaliza kuliŵerenga lonse, sindichitira mwina koma ndiliŵerenganso kachiŵiri, ngati mmene mukanachitira mutalandira kalata yochokera kwa munthu amene mumam’konda kwambiri.” Taonani zimene anthu enanso ananena.

Munthu wina wa ku Kansas amene anaŵerenga bukuli anati: “Ndikuona kuti ndikuyandikiranadi kwambiri ndi Atate athu akumwamba. Chikondi chikuchita kusefukira mumtimamu . . . Tsiku lililonse kukamacha mtima umangokhala uli pa bukuli kuti ndizingoliŵerengabe, ndipo ndiliŵerengadi kambirimbiri.”

Mkazi wina wa ku Maine, analemba kuti: “Landithandiza kwambiri kuzindikira bwino umunthu wa Yehova! Mawu amene ali patsamba 74 akuti, ‘kwa amene akumwalira, malo okha osungika amene iwo angakhalemo ndi m’chikumbukiro cha Mulungu,’ ndi olimbikitsa kwambiri.” Munthu winanso wa ku Alaska amene amaonanso chimodzimodzi anati: “Bukuli linandifikapo, moti ndinafika mpaka pogwetsa misozi.” Iye ananenanso kuti: “Ndithudi ndizingoliŵerenga nthaŵi ndi nthaŵi n’kumapezamo mfundo zina ndi zina.”

Tikukhulupirira kuti inunso mukaŵerenga bukuli mungagwirizane nawo amene ananena zimenezi. Bukuli linayamba ndi mitu itatu, kenako linagaŵidwa m’zigawo zinayi, ndipo zigawozi zili ndi mitu yakuti “Wolimba Mphamvu,” “Wokonda Chilungamo,” “Wa Mtima Wanzeru,” ndiponso “Mulungu Ndiye Chikondi.” Mutu womaliza m’bukuli ndi wakuti “Yandikirani kwa Mulungu Ndipo Adzayandikira kwa Inu.”

Mukhoza kuitanitsa buku lofewa chikutoli lomwe lili ndi masamba 320 polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kutumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Nditumizireni buku lakuti Yandikirani kwa Yehova.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere