Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sikudzakhalanso Masoka Chifukwa cha Nyengo!

Sikudzakhalanso Masoka Chifukwa cha Nyengo!

Sikudzakhalanso Masoka Chifukwa cha Nyengo!

“MASIKU ANO anthu asiya kusamalira dziko pofunitsitsa moyo wapamwamba, kuyenda msanga, ndiponso ndalama,” anatero mawu a pachikuto cha buku lonena zoteteza dzikoli lotchedwa 5000 Days to Save the Planet. Dyera la anthu ndi limene likutipweteketsa. Ndipo kaya zimene akatswiri ena amanena pa nkhani ya kutentha kwa dziko n’zoonadi kapena ayi, mfundo njakuti anthu akuwononga dziko lathu lokongolali. Chinthu chimodzi chokha chotilimbitsa mtima ndicho lonjezo la Baibulo lakuti Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18.

Mulungu adzachotsa ulamuliro wa anthu wopanda pakewu n’kubweretsa ulamuliro watsopano wosiyana kwambiri ndi umenewu. Musafulumire kuganiza kuti izi n’zikhulupiriro zachipembedzo zopanda mutu, chifukwa tangoganizani: Kodi ndani angadziŵe bwino zimene dziko lathuli limafunikira kuposa Mlengi wake? Kodi iyeyo poti ndiye mwiniwake wa dzikoli, tingati sizim’khudza zimene zikuchitika padziko pano? Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti zimam’khudza. Pa Yesaya 45:18 Baibulo limanena kuti Yehova “ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.” Mulungu angathe kuchitapo kanthu pofuna kukwaniritsa cholinga chimenechi ndipo adzaterodi.

Mulungu adzachita zimenezi pobweretsa boma latsopano, kapena kuti ufumu woti udzayendetse dzikoli. Akristu akamapemphera pemphero lomwe ena amalitcha Pemphero la Ambuye n’kumati: “Ufumu wanu udze,” amakhala akupempha kuti boma limeneli ndilo liloŵe m’bwalo. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu kapena kuti boma la Mulungu, lizidzachita zinthu mozindikira kufunika kwa zinthu zosamvetsetseka zachilengedwe za padziko lapansi. Motero lidzatha kukonzanso madera ena a dzikoli amene aipitsidwa chifukwa cha kuwonongedwa kwa dziko. Lemba la Yesaya 35:1, 6 limati: ‘Dziko loti se . . . lidzaphuka ngati duwa. . . . Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.’

Pokhapokha Mulungu Atachitapo Kanthu

Madzi atasefukira m’chaka cha 2002, Helmut Schmidt, yemwe kale anali mtsogoleri wa dziko la West Germany, analemba kuti: “Palibe munthu amene angatchingire madzi osefukira. Masoka amachitika basi.” Zimenezi n’zoonadi. Ndipotu nyengo ikasokonekera mowononga chonchi, anthu amangochitapo zinthu zokha zimene angakwanitse. Ngakhale kuti masoka otere amabweretsa mavuto ambirimbiri, amathanso kuthandiza m’njira zina. Amatha kuchititsa anthu kusonyeza chikondi ndi kuganizira anansi awo. (Marko 12:31) Mwachitsanzo, zikuoneka kuti kusefukira kwa madzi ku Ulaya kunathandiza anthu ena m’njira imeneyi. Nyuzipepala ina inati: “Kwabwera anthu amene angodzipereka mwa mtima wonse, kuchokera m’madera osiyanasiyana a dziko la Germany kuti adzagwire ntchito [yothandiza anthu okhudzidwa ndi tsokali]. Anthu sanadziperekepo chonchi chichitikireni nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse.”

Pagulu la anthu ongodziperekaŵa panalinso a Mboni za Yehova ambirimbiri. Nkhani yotsatira ilongosola ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi masokaŵa imene Mboni za Yehova zinachita m’zigawo zinayi zimene zinakhudzidwa ndi mkuntho. Zochitika za Akristu ameneŵa zimasonyeza mmene anthu azidzakhalira mu Ufumu wa Mulungu umene ukubwerawo, umene anthu okhalamo adzakhale okondana ndiponso oganizirana koma osati anthu odzikonda ndiponso osaganizira ena.—Yesaya 11:9. *

Akristu angalimbe mtima poganizira lonjezo limene Mulungu anauza mtundu wakale wa Aisrayeli, lakuti: “Ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m’nyengo yake, ya myundo ndi ya masika.” (Deuteronomo 11:14) Lonjezo limenelo lidzakwaniritsidwanso kwa anthu amene adzakhale ndi mwayi wokhala m’dziko latsopano la Mulungu, limene silidzakhala ndi masoka a kusokonekera kwa nyengo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Ngati mukufuna kudziŵa bwino za lonjezo la m’Baibulo lonena za boma lolamulidwa ndi Mfumu limeneli, pezani a Mboni za Yehova kumene mumakhalako kapena lembani kalata kwa ofalitsa magazini ino.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Kulamulira Nyengo Bwinobwino

M’dziko latsopano la Mulungu, anthu sadzaopa kuti nyumba kapena mbewu zawo zipita ndi madzi osefukira mwadzidzidzi. (2 Petro 3:13) Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, angathe kulamulira nyengoyi bwinobwino. Taganizirani malemba otsatiraŵa.

Genesis 7:4: “Pakuti akapita masiku asanu ndi aŵiri Ine ndidzavumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anayi usana ndi usiku.”

Eksodo 14:21: “Ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum’maŵa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagaŵikana.”

1 Samueli 12:18: “Momwemo Samueli anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.”

Yona 1:4: “Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.”

Marko 4:39: “Ndipo anauka [Yesu, atapatsidwa mphamvu ndi Mulungu] nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.”

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

M’dziko latsopano la Mulungu, sitidzaopanso kuti nyengo isokonekera