Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zithunzi Zolaula N’zowononga

Zithunzi Zolaula N’zowononga

Zithunzi Zolaula N’zowononga

N’ZOSAVUTA kuona pa TV, m’mafilimu, m’mavidiyo a nyimbo, ndiponso pa Intaneti anthu akugonana m’njira zosiyanasiyana. Kodi zithunzi zolaula zomwe amangozionetsazi, zilibedi vuto monga mmene ambiri amanenera pofuna kuti tiwakhulupirire? *

Mmene Zimakhudzira Anthu Akuluakulu

Kaya anthu anene zotani zokometsera zithunzizi, choti mudziŵe n’chakuti zithunzi zolaula zimasokoneza mmene anthu ayenera kuonera nkhani ya kugonana ndiponso mmene amaonera zochita za anthu ena pankhaniyi. Ochita kafukufuku a m’bungwe la National Foundation for Family Research and Education ananena kuti “kumangoona zithunzi zolaula kumatha kupangitsa anthu oonawo kuyamba kulakalaka kwambiri kugonana m’njira zachilendo.” Malinga ndi chikalata chimene analemba, akuti ‘amuna ambiri amene ali ndi chizoloŵezi choona zithunzi zolaula amakhulupirira kwambiri kuti akazi ndiwo amene amachititsa kuti azigwiriridwa komanso kuti amasangalala nako kugwiriridwako, ndiponso kuti ogwirirawo ndi anthu abwinobwino.’

Ofufuza ena amati kumangoonerera zithunzi zolaula kukhoza kuyambitsa anthu okwatirana kukhala ndi vuto pogonana. Dr. Victor Cline, yemwe ndi dokotala wothandiza anthu amene amangoganizira za kugonana, watulukira mmene munthu amafikira pokhala ndi vuto lomangoonerera zithunzi zolaula. Munthu akapanda kusamala, zithunzi zolaula zomwe angayambe kuziona mwangozi zingathe kumukopa kuti afike pomaona zina zambirimbiri zochititsa manyazi kwenikweni. Iye anati zimenezi zikhoza kuchititsa munthuyo kuyamba kugonana ndi ena m’njira zosiyanasiyana zachilendo. Asayansi odziŵa bwino za kakhalidwe ka anthu amavomereza zimenezi. Dr. Cline analemba kuti “munthu angayambe khalidwe lililonse la kugonana kwachilendo m’njira imeneyi . . . ndipo khalidweli silingatheke kulithetsa ngakhale chikumbumtima chake chitamamuvutitsa kwambiri kuti amachita zolakwika.” Mapeto ake woonayo akhoza kumayesa kuchita nawo zinthu za pachithunzipo, kumangoganizira zinthu zachabechabe, ndipo kaŵirikaŵiri zotsatira zake zimakhala zoopsa kwambiri.

Vutoli limayamba pang’onopang’ono ndipo nthaŵi zina silidziŵika kuti layamba, anatero Cline. Iye anati: “Monga mmene amachitira matenda a kansa, vutoli limangokulabe ndi kufalikira. Sizichitika kaŵirikaŵiri kuti lithe palokha, komanso ndi lovuta zedi kuchiza. Kaŵirikaŵiri mwamuna amene khalidweli linamuloŵerera kwambiri amakana kuti n’zimene amachita ndiponso amakana kulithetsa, ndipo zimenezi nthaŵi zambiri zimachititsa kuti iye ndi mkazi wake asamagwirizane, mwina mpaka kusudzulana, ndipo angathenso kudana ndi anthu ena amene anali kugwirizana nawo kwambiri.”

Zimawononga Achinyamata

Kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene amakonda kwambiri zithunzi zolaula ndi achinyamata azaka zoyambira 12 mpaka 17. Ndipotu kwa ambiri, nkhani zakugonana amazidziŵira makamaka m’njira imeneyi. Komatu zotsatira zake zimakhala zomvetsa chisoni kwambiri. Chikalata china chinati: “Akamaonetsa zithunzi zolaula, saonetsa achinyamata atatenga mimba zapathengo ndiponso matenda opatsirana kudzera m’chiwerewere monga Edzi, motero amawapusitsa kuti azikhulupirira kuti palibe vuto lililonse ndi makhalidwe amene amawaonetsa m’zithunzizi.”

Ofufuza ena amati mwana akamaonera zithunzi zolaula, ubongo wake sukula bwino. Dr. Judith Reisman, yemwe ndi mtsogoleri wa bungwe la Institute for Media Education, anafotokoza kuti: “Atafufuza zimene zimachitika mu ubongo, munthu akamaona kapenanso kumvetsera zinthu zolaula, anapeza kuti ubongowo umasokonezeka moti munthuyo amachita zinthu mosaganizira kaye ubwino ndi kuipa kwake, ndipotu zoterezi n’zoipa kwambiri kwa ana chifukwa ubongo wawo suchedwa kusokonezeka. Zoterezi zingachititse anawo kumangoganizira zinthu zoti sizichitikadi motero sangakhale anthu olongosoka m’maganizo kapenanso a thanzi labwino ndipo zingawalepheretse kukhala anthu abwinobwino komanso osangalala.”

Zimadanitsa Anthu

Zithunzi zolaula zimasinthitsa munthu maganizo ndiponso khalidwe lake. Uthenga wa zithunzizi umakopa anthu makamaka chifukwa ndi wokokomeza ndiponso umamveka wosangalatsa kuposa zimene zimachitikadi. (Onani kabokosi kakuti “Kodi Mudzavomereza Uthenga Uti?”) Lipoti lina linati: “Anthu amene amaonera zithunzizi amayamba kuyembekezera zinthu zosayenera zimene zimachititsa anthu kuti adane.”

Zithunzi zolaula zikhoza kupangitsa anthu kukhala osakhulupirirana ndiponso osanena chilungamo, zomwe sizifunika n’komwe m’banja. Chifukwa chakuti munthu amakonda kuonerera zithunzizi mwakabisira, nthaŵi zambiri zimamuchititsa kukhala wachinyengo ndiponso wonama. Okwatirana amaona kuti akulakwiridwa. Samvetsa chifukwa chake mwamuna kapena mkazi wawo sawaŵerengeranso.

Zimawononga Moyo Wauzimu

Kuonerera zithunzi zolaula kumawononga kwambiri moyo wauzimu. Zikhoza kupinga kwambiri munthu kuti asagwirizane ndi Mulungu. * Baibulo limati chilakolako cha kugonana, ndi chimodzimodzi kusirira koipa ndiponso kupembedza mafano. (Akolose 3:5) Munthu amene amasirira kwambiri chinthu chinachake amachilakalaka kwambiri moti nthaŵi zonse sagona nacho tulo, ndipo saonanso ngati pali chinthu china chofunika. Moti anthu oloŵerera kwambiri m’zithunzi zolaula amaona kuti Mulungu si wofunika kwambiri poyerekezera ndi chilakolako chawo cha kugonana. Motero amapanga zithunzizi kukhala fano lawo. Komano lamulo la Yehova Mulungu limati: “Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.”—Eksodo 20:3.

Zithunzi zolaula zimawononga ubwenzi. Mtumwi Petro, yemwe analinso munthu wokwatira, analimbikitsa amuna achikristu okwatira kuti azichitira ulemu akazi awo. Mwamuna wolephera kutero, mapemphero ake kwa Mulungu angaletsedwe. (1 Petro 3:7) Kodi kungakhale kupatsa mkazi wako ulemu ukamaonerera mwakabisira zithunzi zoipa za akazi ena? Kodi angamve bwanji atatulukira kuti n’zimene umachita? Ndipo kodi Mulungu yemwe “adzanena mlandu wa zochita zonse” ndiponso yemwe ‘amayesa mizimu’ angakuganizireni zotani? (Mlaliki 12:14; Miyambo 16:2) Monga tinene kuti munthu wokonda zithunzi zolaula ali nacho chifukwa chilichonse choti n’kuganizira kuti Mulungu angamve mapemphero ake?

Mtima wadyera wofuna kudzisangalatsa zivute zitani ndi umene amakhala nawo anthu okonda zithunzi zolaula. Choncho si chikondi kuonerera zithunzi zolaula. Kumalepheretsa Mkristu kuti akhalebe munthu wosachita dama ndiponso wosadetsedwa pamaso pa Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ichi ndi chifuniro cha Mulungu . . . kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziŵe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeretso ndi ulemu, kosati m’chiliro cha chilakolako chonyansa, . . . asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake [ndi kumusokonezera ufulu wake, NW] mmenemo.”—1 Atesalonika 4:3-7.

Zithunzi zolaula zimapeputsa makamaka akazi ndi ana. Zimawanyazitsa ndiponso kuwachotsera ulemu ndi ufulu wawo. Munthu amene amakonda zithunzizi amagwirizana nazo zopeputsa enazo. Steven Hill ndi Nina Silver, omwe amachita kafukufuku wa nkhaniyi, anafotokoza kuti: “Kaya munthu . . . amadziona kuti ndi wabwino bwanji, akamakonda zithunzi zolaula amasonyeza kuti saganizira kwambiri anthu ena, komanso kuti amadana kwambiri ndi mkazi yemwe iye amati amam’kondayo.”

Kusiya Chizoloŵezi Choonerera Zithunzi Zolaula

Bwanji ngati panopa khalidweli linakuloŵererani kwambiri? Kodi chilipo chimene mungachite kuti mulisiye? Baibulo limalimbitsa mtima! Akristu ena oyambirira asanafike podziŵa Kristu, anali adama, achigololo, ndiponso osirira. “Koma munasambitsidwa,” anatero Paulo. Kodi zimenezo zinatheka bwanji? Iye anayankha kuti: “Munayeretsedwa . . . ndi mzimu wa Mulungu wathu.”—1 Akorinto 6:9-11.

Musanyozere mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu. Baibulo limati: “Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza.” Ndithudi, iye angakuthandizeni kuti musiye zimenezo. (1 Akorinto 10:13) N’zothandiza kulimbikirabe kupemphera mochokera pansi pamtima, n’kumauza Mulungu vuto lanu. Mawu ake amatilimbikitsa kuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza.”—Salmo 55:22.

Inde, muyenera kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene mukupemphererazo. Muyenera kunyalanyaza dala chilakolako choti muonerere zinthu zolaula ndiponso kutsimikiza mtima kuti musiyane nazo. Mnzanu wapamtima kapena mbale wanu angakuthandizeni kwambiri pokulimbikitsani kuti muzichita zinthu mogwirizanadi ndi zimene mwatsimikiza mtima kuchita. (Onani kabokosi kakuti “Kulandira Thandizo.”) Mukamakumbukira kuti kuchita zimenezo n’kokondweretsadi Mulungu zikhoza kukuthandizani kuti musabwererenso m’mbuyo. (Miyambo 27:11) Kudziŵa kuti Mulungu amakhumudwa mukamaonerera zithunzi zolaula kungakuthandizeninso kuti musiyiretu khalidweli. (Genesis 6:5, 6) N’zovutirapo ndithu, koma sikuti n’zokanika kusiya. Ndithudi, khalidweli limatheka kusiya!

Zithunzi zolaula ndi zoopsadi. Zimawononga munthu. Zimasokoneza anthu amene amazijambula ndiponso amene amazionerera. N’zonyazitsa amuna ndi akazi, n’zowononga ana, ndipo si zoti n’kuzisekerera ayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Kuti muone nkhani yofotokoza bwinobwino za kuopsa kwa zithunzi zolaula za pa Intaneti, onani nkhani ya mutu wakuti “Zithunzi Zamaliseche za Pa Intaneti—Kodi Zingavulaze Motani?” mu Galamukani! ya June 8, 2000, masamba 3-10.

^ ndime 14 Kuti muone zimene Baibulo limanena pankhani ya zithunzi zolaula, onani Galamukani! ya July 8, 2002, masamba 19-21.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

Kulandira Thandizo

Musaganize kuti kulimbana n’kuti munthu asiye kukonda zithunzi zolaula ndi koti wina angakuchite lero ndi lero; n’kovuta ndithu. Dr. Victor Cline, yemwe wathandizapo anthu ambirimbiri amene khalidweli linawaloŵerera, ananena kuti: “Kulonjeza kuti musiya sikuthandiza ayi. Ndipo sikuti mungasiye chifukwa chongoti mukufunadi kutero. N’zosatheka n’komwe kuti [munthu amene khalidweli linam’loŵerera] asinthe payekha.” Malinga n’kunena kwa Cline, chinthu chofunika kuti munthu wotere asiyiretu khalidweli n’chakuti azithandizidwa ali pamodzi ndi mkazi kapena mwamuna wake ngati munthuyo ali pabanja. Iye anati: “Munthuyo amasiya msanga ngati mukuwathandizira pamodzi. Onse zimawakhudza, motero onse afunika thandizo.”

Ngati munthuyo sali pabanja, nthaŵi zambiri mnzake wapamtima kapena mbale wake akhoza kumam’limbikitsa kwambiri. Kaya amene akuthandizidwa nawo limodzi pavutoli ndani, mfundo ya Cline nthaŵi zonse ndi yakuti: Musabise kalikonse kokhudza vutoli ndiponso musabise ngati vutolo likuyambiranso. Iye anati: “Kusunga chinsinsi ‘n’kopweteketsa.’ . . . Zikaululika umachita manyazi ndipo umanong’oneza bondo.”

[Tchati patsamba 25]

Kodi Mudzavomereza Uthenga Uti?

Wa Zolaula Wa M’Baibulo

▪ Kugonana ndi wina aliyense, ▪ “Ukwati uchitidwe ulemu ndi

nthaŵi ina iliyonse, pena ndi onse; ndi pogona pakhale

paliponse, ndiponso mwanjira posadetsedwa; pakuti adama

ina iliyonse n’kwabwino ndi achigololo adzawaweruza

ndipo sikubweretsa Mulungu.”Ahebri 13:4.

vuto lililonse.

 

“Wachiwerewere achimwira

thupi lake la iye yekha.”

​—1 Akorinto 6:18; onaninso

Aroma 1:26, 27.

▪ Ukwati umapinga munthu kuti ▪ “Ukondwere ndi mkazi wokula

azisangalala pankhani naye. . . . Ukondwe ndi

yakugonana. chikondi chake osaleka.”

Miyambo 5:18, 19; onaninso

Genesis 1:28; 2:24;

​—1 Akorinto 7:3.

▪ Akazi ntchito yawo ndi ▪ [Ine Yehova Mulungu]

imodzi yokha, ndidzam’pangirawom’thangatira

yotiazisangalatsa iye.”Genesis 2:18;

amuna pogona nawo basi. onaninso Aefeso 5:28.

▪ Amuna ndi akazi sangathe ▪ “Chifukwa chake fetsani

kudziletsa akakhala ndi ziŵalozo zili padziko; dama,

chilakolako chofuna kugonana Chidetso, chifunitso cha

manyazi, chilakolako choipa,

ndichisiriro, chimene chili,

kupembedza mafano.”

Akolose 3:5.

 

“Yense wa inu adziŵe kukhala

nacho chotengera chake

m’chiyeretso ndi ulemu.”

​—1 Atesalonika 4:4.

 

Muziwaona “akazi aakulu ngati

amayi; akazi aang’ono ngati

alongo m’kuyera mtima konse.”

​—1 Timoteo 5:1, 2; onaninso

1 Akorinto 9:27.

[Chithunzi patsamba 23]

Ofufuza ena amati mwana akamangoona zithunzi zolaula, ubongo wake sukula bwino

[Chithunzi patsamba 24]

Zithunzi zolaula zikhoza kupangitsa anthu kukhala osakhulupirirana ndiponso osanena chilungamo m’banja

[Chithunzi patsamba 26]

Kupemphera mochokera pansi pa mtima kungathandize