Analemba Nkhani Yochititsadi Chidwi
Analemba Nkhani Yochititsadi Chidwi
Ginny, mtsikana wa Mboni za Yehova yemwe amakhala ku United States, anali ndi mpata wabwino kwambiri wolankhula za chipembedzo chake m’chaka chomaliza cha sukulu yake. “Aphunzitsi athu anatiuza kuti, kuti timalize bwino maphunziro athu, tifunika kulemba nkhani yokhudza zina zimene tinaphunzira,” iye anatero. “Ndinawauza kuti ndikufuna kulemba za Mboni za Yehova m’ndende za a Nazi.”
Aphunzitsiwo anavomera kuti Ginny alembe zimene ankafunazo. “Ndinkanjenjemera itakwana nthaŵi yoti ndichongetse nkhani yanga komanso kuti ndifotokozere anzanga a m’kalasi zimene ndinalemba,” anatero Ginny. “Sindinadziŵe kuti anzanga ati chiyani kayanso ngati azindiseka.”
Ginny anayamba kufotokoza nkhani yake ndi funso lakuti: “Ndani akudziŵa amene ankavala chizindikiro cha Nyenyezi ya Davide m’ndende za a Nazi?” Aliyense anayankha kuti, “Ayuda.” Kenako anafunsa ngati alipo amene akudziŵa omwe ankavala kansalu kofiirira ka makona atatu. Palibe anayankha. “Ndinawauza kuti Mboni za Yehova ndizo zinkavala chizindikiro chimenechi,” anatero Ginny.
Aphunzitsi ndi ana a sukulu anzakewo anachita chidwi kwambiri ndi zimene Ginny anafotokoza. “Anadabwa kwambiri ndi mfundo yakuti Mboni za Yehova zikanakhala zaufulu mwa kungosayina pepala linalake losonyeza kuti asiya chikhulupiriro chawo,” anatero Ginny. “Pambuyo pake anzanga ena a m’kalasimo anandiuza kuti m’mbuyomo anali kuseka a Mboni za Yehova koma nthaŵi yotsatira imene wina anafika pakhomo pawo anacheza naye.”
Ginny analandira ma A folo chifukwa cha nkhani analembayo komanso zimene anafotokozazo. Iye anati: “Inde ndinakhoza bwino, komansotu ndinali ndi mpata wabwino zedi wolankhula za chikhulupiriro changa!”
[Chithunzi patsamba 22]
A Mboni za Yehova ambiri anauzidwa kuti angakhale aufulu mwa kusayina chikalata ichi chosonyeza kusiya chikhulupiriro chawo
[Mawu a Chithunzi]
Mololezedwa ndi a Holocaust Memorial Museum ku United States