Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kamtengo Kamene Kamayeretsa Mano

Kamtengo Kamene Kamayeretsa Mano

Kamtengo Kamene Kamayeretsa Mano

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU ZAMBIA

KU AFRICA anthu ake ali ndi mano okongola komatu kuli misuwachi ya kusitolo yochepa! Zimatheka bwanji? Kwa anthu ambiri, chinsinsi chokhala ndi mano owala chagona pa kutafuna timitengo.

Panthaŵi inayake Ababulo nawo ankatafuna timitengo, kenakonso Aigupto, Agiriki, ndi Aroma ankachita chimodzimodzi. “Misuwachi” ing’onoing’ono ya mitengo imeneyi inalinso kugwiritsidwa ntchito ndi anthu ambiri m’dziko la Arabia lisanakhale la Chisilamu. Anthu ambiri a ku Ulaya anasiya kutafuna timitengo zaka pafupifupi 300 zapitazo, komatu zimenezi zikuchitikabe m’madera ena ku Africa, ku Asia, ndi ku Middle East.

Ku Middle East, nthaŵi zambiri amatafuna tinthambi ta mtengo womwe amautcha kuti mtengo wamsuwachi. Ku West Africa amagwiritsa ntchito mitengo ya malalanje ndi ina yokhala ngati ya mandimu, pamene ku India amagwiritsa ntchito mitengo ya nimu. Ku East Africa amagwiritsa ntchito pafupifupi mitundu 300 ya mitengo ndi zitsamba zosiyanasiyana. Koma kodi kamtengoko kamayeretsa mano motani?

Akamatafuna, nsalensale za kamtengoko ku mbali imene akutafunayo zimalekanalekana n’kukhala ngati cheyo. Akapitiriza kutafuna, nsalensalezo zimaloŵa m’mano ndipo zimachititsa kuti magazi aziyenda bwino mu usinini. Kutafuna timitengoti kumadzetsanso malovu ambiri m’kamwa, omwe amakhala ngati madzi otsukira m’kamwamo kuchotsa mabakiteriya ndipo simukhala mwabwino kuswaniramo mabakiteriyawo. *

Komatu mitengo imene amatafunayi simangokhala ngati misuwachi basi. Nthambi ndi mizu ya mitengo ina ili ndi mankhwala amene amachepetsa zinthu zokangamira m’mano zoyambitsa chiseyeye. M’mitengo ina munapezeka kuti muli mankhwala opha mabakiteriya ndi tizirombo tina. Nthambi za mtengo wamsuwachi tinatchula uja zingathandize kuteteza zilonda za m’mimba. Ku Namibia, timitengo timene amathyola ku mtengo wotchedwa muthala timateteza tizirombo towoletsa mano, toyambitsa matenda a usinini, ndi zilonda zapakhosi. Zoyeretsera mano zachilengedwe zimenezi zingateteze mano kuti asabooke ndiponso zingalimbitse mizu ya manowo ndi usinini. Masiku ano mafakitale ena amapanga mankhwala otsukira mano omwe amaikamo mankhwala ochokera ku mitengo imeneyi.

Inde, ena amakonda kugwiritsa ntchito msuwachi wa kusitolo. Kaya musankha kugwiritsa ntchito msuwachi woterowo kapena kutafuna kamtengo, monga ankachitira anthu akale, sitingatsutse mfundo imodzi iyi: Kusamalira mano ndi mbali yofunika kwambiri ya kusamalira thupi lathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 N’zoona kuti mtundu wa chakudya nawonso ndi wofunikira. Anthu a kumidzi mu Africa kaŵirikaŵiri amadya kwambiri zakudya za m’gulu la chimanga ndi ndiwo zamasamba kuposa anthu a m’tauni. Ndiponso nthaŵi zambiri amadya shuga wochepa, zakudya zochepa zokonzedwa ku fakitale, komanso amamwa zakumwa zoziziritsa kukhosi zochepa; zonsezitu zimawoletsa mano.

[Chithunzi patsamba 21]

Mtengo wa nimu ndi mtengo umodzi umene amatengako timitengo totafuna

[Mawu a Chithunzi]

William M. Ciesla, Forest Health Management International, www.forestryimages.org