Kufuna Kuoneka Bwino Kuli M’poipira Pake
Kufuna Kuoneka Bwino Kuli M’poipira Pake
N’ZOSACHITA kukayika kuti, utawatsata mosamala, mafashoni angakuthandize kuti uzioneka bwino ndiponso kuti usamadzikayikire. Kuvala zovala zoyenerera kungathe kubisa zinthu zina zosaoneka bwino pathupi pako mwinanso kungakuchititse kuoneka mokongola kwambiri. Kungathenso kuchititsa kuti anthu ena azikuona m’njira inayake.
Koma mafashoni ali m’poipira pake, pamene sitiyenera kupanyalanyaza. Anthu ofuna kugula zovala za m’fasho angathe kumangokhalira kugula zovala zatsopano. Ndipotu mafashoni atsopano sati abwera liti. Izitu si kuti zimangochitika mwangozi ayi chifukwa okonza mafasho amapanga ndalama ngati zovala zikutha fasho msanga. Monga mmene ananenera Gabrielle Chanel, yemwe amakonza masitayelo a zovala, “mafashoni amapangidwa n’cholinga choti adzathe fasho.” Moti anthu osadziŵa zimenezi amaganiza kuti ayenera kugula zovala zilizonse zongotuluka kumene poopa kutsalira.
M’posavutanso kutengeka ndi zonenerera malonda. Makampani opanga zovala za m’fasho amawononga ndalama zochuluka zedi pokopa anthu kuti azigula zovala zawo ndipo nthaŵi zambiri anthu amene amavala zovalazi potsatsa malondaŵa amawaonetsa ngati anthu oti sakhala ndi nkhaŵa ina iliyonse. Zimenezi zimatha kukopa anthu kwambiri. Mphunzitsi wina ku Spain ananena kuti: “Palibe chinthu chimene chimavutitsa kwambiri achinyamata kuposa kukhala opanda nsapato zinazake ‘zotsogola’.”
Kutengeka ndi Zovala Zosachedwa Kutha Fasho
Pali magulu ena amene amakhala ndi zovala zoti azidziŵika nazo. Zimene amavalazo zingasonyeze kuti saŵerengera za anthu ena onse, ali ndi ufulu wotsatira mfundo zimene akufuna, mwinanso kuti ndi okonda zachiwawa kapena zatsankho. Ngakhale kuti masitayelo ena a zovalazi amachita kukhala onyanyira, ambiri m’gulumo amavalabe zovala zotero. Ngakhale anthu ena amene satsatira mfundo za gululo angathe kukopeka nawo masitayeloŵa. Anthu amene amatsanzira mavalidwe ameneŵa amachititsa anthu owaona kuganiza kuti nawonso amavomereza ndiponso kulimbikitsa mfundo za maguluwo.
Nthaŵi zambiri mafasho otchukitsidwa ndi magulu ena ake sachedwa kutha, ena amangokhalapo miyezi yochepa chabe. Amatha kuyambitsidwa ndi woimba nyimbo winawake wotchuka kapena munthu wina woyambitsa mafasho. Koma mafasho ochepa otere masitayelo ake amatha kukhalitsa ndithu. Mwachitsanzo jinzi za buluu zinali zotchuka kwambiri pakati pa magulu a achinyamata ochita zionetsero zotsutsa mfundo zosiyanasiyana m’zaka za m’ma 1950 ndi m’ma 1960. Komano masiku ano anthu amisinkhu yosiyanasiyana amavala jinzi pa nthaŵi zosiyanasiyananso.
Kulakalaka Kukhala ndi Thupi Looneka Bwino Kwambiri
Anthu amene amaganizira kwambiri za mafasho amatha kuvutika kwambiri m’maganizo ndi nkhani ya kaonekedwe kawo. Anthu ovala zovala za pa zionetsero za mafashoni amakonda kukhala aatali ndiponso ochepa thupi, ndipo zithunzi zawo zimaoneka nthaŵi ndi nthaŵi. * Akamanenerera china chilichonse, kaya ndi magalimoto ngakhale maswiti amene, amasankha anthu amene amati ngooneka bwino kuti anenerere malondawo. Bungwe loona za chikhalidwe la ku Britain la Social Issues Research Centre linati, n’kutheka kuti “masiku ano patsiku limodzi lokha atsikana amaona ziphadzuŵa zambiri kuposa ziphadzuŵa zonse zimene amayi athu anaonapo pa utsikana wawo wonse.”
* Nieves Álvarez, mtsikana wovala zovala pa zionetsero za mafashoni wa ku Spain, yemwe anakhalapo ndi vutoli, ananena kuti: “Ndinkaopa kunenepa kuposa kufa.”
Kuona zithunzi zochuluka motere kungathe kusokoneza munthu. Mwachitsanzo ku United States, kafukufuku amene analembedwa m’magazini ya Newsweek ananena kuti achinyamata 90 pa 100 alionse achizungu ankadziona kuti ngosakongola. Ambiri mwa achinyamataŵa angalolere kuchita china chilichonse kuti angokhala ndi thupi limene amati n’looneka bwinolo. Koma bungwe la Social Issues Research Centre linati ndi atsikana osakwana n’komwe 5 pa atsikana 100 alionse amene angafikepo pokhala ndi thupi longa la akazi otchuka m’zofalitsidwawo. Ngakhale zili choncho, kukhumbira kwambiri kathupi kochepa kwachititsa kuti atsikana ambiri akhale pa ukapolo. Kwachititsa atsikana ena kukhala ndi vuto losala zakudya lomwe limatchedwa kuti anorexia nervosa.N’zoona kuti mavuto okhudza kudya angati anorexia kapena bulimia amatha kuyamba pa zifukwa zinanso zambirimbiri. Komabe Dr. Anne Guillemot ndi Dr. Michel Laxenaire anati: “Kufunitsitsa kukhala wochepa thupi kukuwonjezeranso vutoli.”
N’zoonekeratu kuti mafashoni ali m’pabwino komanso m’poipira pake. Amakwaniritsa chikhumbo chimene anthu onse ali nacho chofuna kuoneka bwino ndiponso kuvala zovala zatsopano. Koma kutengeka kwambiri ndi mafasho kungatichititse kuvala zovala zopatsa ena maganizo olakwika. Ndipo tikamaona ngati kuti maonekedwe athu ngofunika kwambiri zedi, tingathe kuyamba kukhulupirira mfundo yabodza yakuti chimatipangitsa kukhaladi munthumunthu n’kaonekedwe kathu osati mtima wathu ayi. Álvalez, yemwe tam’tchulapo kale uja, anati: “Tiyenera kuyamba kuona kufunika kwa munthu malingana ndi luso lake ndiponso mtima wake, osati zovala zake chabe ayi.” Koma zoti anthu angasinthe motero sikuti zingachitike posachedwa. Nanga kodi tingatani kuti tisamatengeke ndi mafasho?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Nthaŵi zambiri anthu ovala zovala za pa zionetsero za mafashoni amafunika kukhala “aatali mosachepera mamita 1.74, ochepa thupi kwambiri, okhuthala milomo, a masaya otukuka, a maso aakulu bwino, a miyendo yaitali ndiponso a mphuno yowongoka koma osati yaikulu kwambiri,” inatero magazini ya Time.
^ ndime 10 Bungwe la ku United States loona za mavuto otere lotchedwa National Association of Anorexia Nervosa and Associated Disorders linati anthu pafupifupi 8 miliyoni ali ndi vutoli ku United States kokha ndipo linati ambiri ndithu amafa nalo kumene. Ambiri mwa ameneŵa (86 pa 100 alionse) anayamba kukhala ndi mavuto okhudza kudya asanakwanitse zaka 21.
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 8, 9]
Kodi Alipo Angavaledi Chimenechi?
Nyumba zochitirako zionetsero za mafashoni ku New York, ku Paris, ndi ku Milan, chaka chilichonse zimaonetsa anthu ovala zovala za m’fasho atavala zovala zochititsa kaso zokonzedwa ndi akatswiri. Kuwonjezera kuti zovalazi zimakhala zokwera mtengo kwambiri, zambiri zimaoneka kuti n’zosati pangapezekedi nthaŵi inayake yoti munthu ungazivale mwinanso zimakhala zoti sungayende nazo kwina kulikonse. Juan Duyos, wokonza masitayelo a zovala wa ku Spain anati: “Zovala zoimitsa mutu zimene mumaona zija sikuti amazipanga n’cholinga choti anthu akavaledi ayi. Cholinga cha zionetsero zotere mwina chimangokhala chotchukitsa okonza zovalawo kapena zinthu za kampani yawo koma sikuti amakhala akufuna kugulitsa zovala zimene akusonyezazo ayi. Mwachitsanzo zovala zinazake zatsopano zodolola zimene azitchukitsa kwambiri zingathandize kuti perefyumu winawake wa kampani yokonza zovalazo ayambe kuyenda malonda.”
[Chithunzi patsamba 7]
Kufuna kukhala ndi chilichonse chimene chaloŵa m’fasho kumawonongetsa ndalama
[Chithunzi patsamba 7]
Kutengera kavalidwe kenakake kotchuka kungachititse anthu kuganiza kuti muli m’kagulu kenakake
[Chithunzi patsamba 7]
Ena zawapangitsa kukhala ndi vuto losala zakudya lotchedwa anorexia