Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusatengeka ndi Mafasho

Kusatengeka ndi Mafasho

Kusatengeka ndi Mafasho

BAIBULO limanena kuti, “chilichonse [Mulungu] anachikongoletsa pa mphindi yake.” (Mlaliki 3:11) Zinthu zokongola timaziona kwina kulikonse ngakhalenso pakati pa anthu.

Okonza masitayelo a zovala amafuna kuti zovala zathu zizitikongoletsa. Koma mmene taonera m’nkhani yam’mbuyoyi, kukongola kumene iwoŵa amanena n’kwinakwina. Pulofesa wina wa zamaganizo a anthu, Ruth Striegel-Moore anati: “Tazoloŵera kuona akazi ochepa thupi kwambiri moti tayamba kuganiza kuti kumeneko ndiko kukongola.”

N’zoonekeratu kuti n’kupanda nzeru kulola kuti titengeke n’zimene masiku ano anthu m’dzikoli amati n’kukongola. M’buku lake lakuti Always in Style, Doris Pooser anatchula mfundo yakuti “masiku ano mkazi sayenera kusintha kapena kubisa thupi lake akaona kuti maonekedwe enaake a thupi aloŵa m’fasho.” Izi n’zoonadi chifukwatu si zomveka ayi kuti munthu azingotsanzira maonekedwe amene akuchemereredwa m’nkhani zofalitsidwa. Pooser anati: “Kuli bwino kungokhala mmene munthuwe ulili kusiyana ndi kumangolimbana n’kusinthasintha maonekedwe ako.”

Kukongola Kosatha

Kudzipatsa ulemu ndiponso kukhala wokhutira pamoyo wako sikulira kuoneka bwino kokha ayi. Judy Sargent, yemwe anakhalapo ndi vuto losala kudya la anorexia analemba kuti: “Chimwemwe chenicheni chimachokera mumtima. Simungachipeze chifukwa chongochepa thupi.” Mfundo imeneyi Baibulo limaifotokoza mozama. Mtumwi Petro analemba kuti: “Kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wa m’katimo, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.”—1 Petro 3:4, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.

Kukongola kosatha kumene Petro akunena n’koposa maonekedwe okoma a munthu chifukwa kumakhalitsa ndiponso Mulungu amakuona kuti n’kofunika kwambiri. Kalekale mfumu ina yanzeru inanena kuti: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.”—Miyambo 31:30.

Ngakhale kuti masiku ano kukongola kumakopa kwambiri anthu, pali anthu ambiri amene amalemekeza munthu wokhala ndi makhalidwe achikristu. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kuti: “[Valani umunthu] watsopano . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.”—Akolose 3:10, 12.

Mafasho sakhalira kusintha chifukwa ndiko kukhala kwawo. Ngakhale zitakhala zokongola bwanji, zovala za m’fasho yatsopano zingatikongoletse kwa kanthaŵi kochepa chabe. Moti ngakhale anthu atamatitayira kamtengo chifukwa cha mmene timavalira, posapita nthaŵi anthuwo angaiwaleko zonsezi ngati khalidwe lathu silikugwirizana ndi maonekedwe athuwo. Kumbukirani kuti “chipatso cha mzimu” chomwe chili ndi makhalidwe monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ndiponso chiletso, sichitha fasho ayi.—Agalatiya 5:22, 23; 1 Timoteo 2:9, 10.

Koma n’zoona kuti tiyenera kuganizira kavalidwe kathu. Aline, wa ku France anavomereza kuti zinkamuvuta kwambiri kuchita zinthu mosamala pankhani imeneyi. Iye anati, “Ndili mtsikana ndinkaganizira kwambiri nkhani ya zovala. Ndinkafuna kutsanzira sitayelo iliyonse imene yangotuluka kumene chifukwa potero ndinkayenda ndi mgugu. Ndipo ndinkasangalala kwambiri ndikagula chovala chokonzedwa ndi makampani otchuka okonza zovala.”

Aline anapitiriza kunena kuti: “Koma nditakula ndinafunika kuphunzira kudzisamalira ndekha, ndiponso nthaŵi yanga yambiri ndinkaithera pochita utumiki wachikristu. Pamenepa m’pamene ndinazindikira kuti ngati ndikufunadi kuti ndalama zimene ndimapeza zizindikwanira, ndinayenera kusiya kukhala kapolo wa mafasho. Motero ndinayamba kugula zovala zanga kukakhala selo, apo ayi ndinkapita kumasitolo otchipa. Ndinaona kuti ndinkakhala ndi zovala zabwino koma ndinkangowononga ndalama zochepa chabe. Chinsinsi chake n’kudziŵa kugula zovala zokukhala, zimene ungamavaledi, zogwirizana ndi zovala zina zimene uli nazo, komanso zimene sizingachoke msanga m’fasho. M’malo mogula zovala potengera zimene zili m’fasho, panopo ndimayesetsa kuganizira kwambiri za mmene chovala chimene ndikufuna kugula chikundikhalira. Sikuti ndikunena kuti panopo nkhani ya zovala siindikhudzanso ayi. Koma ndazindikira kuti kukhala munthumunthu si maonekedwe okha.”

Nthaŵi zambiri masiku ano anthu amaona kuti maonekedwe ndiwo ofunika koposa khalidwe la munthu, motero ndi bwino kuti Akristu azikumbukira malangizo a m’Baibulo aŵa: “Pakuti zonse za pansi pano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma kumkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lilikupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu amene amachita zimene Mulungu afuna, adzakhala kwamuyaya.—1 Yohane 2:16, 17, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.

[Chithunzi patsamba 9]

Kukongola kwenikweni kumachokera mumtima osati m’zovala

[Chithunzi patsamba 10]

Sankhani zovala zimene mungamavaledi komanso zogwirizana ndi zovala zina zimene muli nazo