Kuthana ndi Khalidwe Lopezerera Ena
Kuthana ndi Khalidwe Lopezerera Ena
‘Munthu amachita kuphunzira kupezerera ena, ndipo chilichonse chimene munthu anachita kuphunzira akhoza kuchisiya.’—Anatero Dr. C. Sally Murphy.
WOPEZERERA anzake ndiponso wopezereredwayo, onse amafunika thandizo. Wopezerera anzake amafunika kuphunzira kuchita zinthu ndi anthu ena popanda kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika. Ndipo wopezereredwayo amafunika kudziŵa njira zimene zingamuthandize kulimbana ndi vutoli.
Nthaŵi zambiri, munthu wopezerera anzake sadziŵa kukhala bwino ndi anthu ndipo amalephera kuzindikira mmene anthu omwe amawaopsezawo amamvera. Iye amafunika kumuyang’anira ndiponso kumuphunzitsa kuchita zinthu bwino ndi anthu ena. Buku lakuti Take Action Against Bullying (Thanani ndi Khalidwe Lopezererana) limati: “Anthu opezerera anzawo akapanda kuphunzira makhalidwe ena atsopano, amapitirizabe kupezerera ena pamoyo wawo wonse. Amapezerera akazi kapena amuna awo, ana awo, ndipo mwinamwakenso anthu amene ali pansi pa udindo wawo kuntchito.”
Athandizeni Kusapezerera Ochepa Mphamvu
Kuphunzitsa ana adakali aang’ono kuti azimvera ena chisoni kungawathandize kuti asakhale ndi khalidwe lopezerera anzawo. Akuluakulu a zamaphunziro m’mayiko ena akugwiritsa ntchito njira yatsopano yophunzitsa ana kumvera anzawo chisoni. Cholinga chawo ndi kuphunzitsa ana a sukulu aang’ono a zaka ngakhale zisanu kuzindikira mmene anthu ena amamvera ndiponso kuti azikhala okoma mtima kwa anthu ena. Ngakhale kuti
padakalibe umboni wotsimikizirika woti zimenezi n’zothandiza kwanthaŵi yaitali motani, zotsatira zimene zaonekapo pakali pano zikusonyeza kuti amene aphunzitsidwa zimenezi sachita zamtopola kwambiri powayerekeza ndi amene sanaphunzitsidwepo.Makolo, simufunika kusiyira aphunzitsi okha kusukulu kuti ndiwo aziphunzitsa ana anu zimenezi. Ngati simukufuna kuti mwana wanu adzakhale ndi khalidwe limeneli, muyenera kumuphunzitsa polankhula naye ndi pomupatsa chitsanzo cha mmene angapatsire ulemu anthu ena ndi kuwalemekeza. Kodi chingakuthandizeni kuchita zimenezi n’chiyani? Mungagwiritse ntchito Mawu a Mulungu, Baibulo, lomwe n’zotheka kuti mumakhala nalo pafupi nthaŵi zonse ndipo n’lothandiza kwambiri pankhaniyi ngakhale kuti ambiri sadziŵa zimenezi. Kodi lingakuthandizeni motani?
Mwa zina, limaphunzitsa momveka bwino mmene Mulungu amaonera kupezerera ochepa mphamvu. Amanyansidwa nako kwambiri! Baibulo limanena kuti Mulungu ‘moyo wake umuda iye wakukonda chiwawa.’ (Salmo 11:5) Ndiponso, Mulungu amaona zonse zimene zikuchitika. Baibulo limafotokoza kuti iye anali kugwidwa chisoni pamene Aisrayeli anali kuvutika “chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.” (Oweruza 2:18) Nthaŵi zambiri Mulungu analanga anthu amene anagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwa popezerera ofooka ndi osatha kudziteteza.—Eksodo 22:22-24.
M’Baibulo mulinso malangizo amene tingati ndiwo malangizo otchuka kwambiri pa kusonyeza chifundo. Yesu anati: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Si chapafupi kuphunzitsa ana kukonda ndiponso kugwiritsa ntchito pamoyo wawo langizo limeneli lochitira ena zomwe timafuna kuti atichitire; pamafunika kuwapatsa chitsanzo chabwino, kulimbikira, ndiponso khama, makamaka chifukwa chakuti ana kaŵirikaŵiri amakhala odzikonda. Komatu kuchita khama lonselo n’kopindulitsa ndithu. Ngati ana anu aphunzira kukhala okoma mtima ndi achifundo, kupezerera ena adzadana nako kwambiri.
Kuthandiza Opezereredwa
Amene anzawo amawapezerera, makamaka ana, amakhala ndi vuto lalikulu lakuti amafunika kuganizabe bwinobwino pamene apanikizika. Winawake akamakupezerera, amafunitsitsa ndithu kuti usaganize bwino. Amafuna kuti ukalipe kwambiri kapena uchite mantha zedi. Ndiye iweyo ukakalipa kapena ukayamba kulira ndi kuonetsa kuti zakupweteka kapena kuti ukuopa, iye amaona kuti zimene amafuna zatheka. Choncho nthaŵi ndi nthaŵi angamafune kuti uzichita zomwezo.
Kodi mungatani? Taonani malingaliro aŵa. Tawalemba moganizira ana, komabe mfundo zake n’zoti ngakhale anthu akuluakulu amene akulimbana ndi khalidweli akhoza kuzigwiritsa ntchito.
▪ Khala wodekha nthaŵi zonse. Osakalipa. Mwanzeru Baibulo limalangiza kuti: “Leka kupsa Salmo 37:8) Ukakalipa umapatsa mphamvu amene akukupezererayo, ndiponso ukhoza kuchita zinthu zomwe pambuyo pake ungadandaule nazo.—Miyambo 25:28.
mtima, nutaye mkwiyo.” (▪ Osaganiza zobwezera. Ukabwezera kaŵirikaŵiri umavutikanso ndiweyo. Mulimonse mmene zingachitikire, kubwezera sikukhutiritsa. Mtsikana wina yemwe anamenyedwa ndi atsikana ena asanu pamene anali ndi zaka 16 anati: “Mumtima mwanga ndinati, ‘Ameneŵa n’dzathana nawo basi.’ Ndiye ndinamema anzanga n’kumenya atsikana aŵiri pagulu lawolo.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Mtsikanayu anati: “Ndinkangodziona kuti ndachita zopusa kwambiri.” Ndipotu pambuyo pake khalidwe la mtsikanayo linaipa kwambiri. Osaiwala mawu anzeru aŵa a m’Baibulo: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa.”—Aroma 12:17.
▪ Ngati zikufika popsetsana mitima, chokapo mwamsanga. Baibulo limati: “Kupikisana kusanayambe tasiya makani.” (Miyambo 17:14) Nthaŵi zonse uziyesetsa kutalikirana ndi amene amakonda kupezerera ena. Miyambo 22:3 imati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”
▪ Ngati akupitirizabe kukupezerera, ungafunikire kumuuza maganizo ako. Sankha nthaŵi imene mtima wako uli pansi bwinobwino, ndiye polankhula naye uzimuyang’ana kumaso, ndipo uzilankhula motsimikiza ndi mwachifatse. Muuze kuti zimene amachita sugwirizana nazo, si zosangalatsa ndiponso zimapweteka. Osalankhula zomunyoza kapena zomuderera.—Miyambo 15:1.
▪ Fotokozera nkhaniyo munthu wina wamkulu amene akhoza kuthandizapo. Tchula vutolo mosapita m’mbali, ndipo pempha kuti akuthandize zimene ungachite. 1 Atesalonika 5:17.
Chitanso chimodzimodzi popemphera kwa Mulungu, ndipotu zimenezi zikhoza kukuthandiza ndi kukulimbikitsa kwambiri.—▪ Kumbukira kuti ndiwe munthu wofunika. Amene akukupezererayo angafune kuti uziganiza kuti ndiwe munthu wopanda ntchito, kuti ndiwe woyenera kukuvutitsa. Komatu iye si woweruza wako. Mulungu ndiye woweruza, ndipo iye amayang’ana zabwino zimene aliyense amachita. Wopezerera anzakeyo ndiye amakhala wopanda phindu chifukwa cha khalidwe lakelo.
Makolo, Tetezani Ana Anu
Makolo nawonso akhoza kukonzekeretsa ana awo adakali aang’ono kuti adzathe kulimbana mwanzeru ndi opezerera anzawo. Mwachitsanzo, akhoza kuchita maseŵero ndi ana awo oyerekeza zimene zingachitike atakumana ndi ana a khalidweli pofuna kuwasonyeza mmene angaonetsere kuti sakuchita mantha.
Ngakhalenso kaimidwe ka munthu, monga kuimirira mowongoka bwino, kangasonyeze kuti sakuchita mantha moti opezerera anzawo ena sangam’pute. Zingakhalenso zothandiza kuyang’ana munthuyo kumaso, kukhala manja ali omasuka, ndiponso kulankhula motsimikiza ndi mosadodoma. Makolo akulimbikitsidwa kuphunzitsa ana awo kuti azichokapo pamalowo ena akayamba kuwapezerera, kuti azipeŵa ana a khalidwe lotereli, ndi kuti azipempha munthu wina wamkulu yemwe angamudalire kuti awathandize, mwachitsanzo angapemphe aphunzitsi.
Kuthetsa khalidweli kumayamba ndi kuphunzitsa banja. Makolo amene amacheza ndi ana awo, amene amawamvetsera modekha ndi kumvetsetsadi nkhaŵa zawo, amakhomereza mwa anawo maganizo akuti ndi ofunikira, kuti ali ndi owathandiza, ndiponso kuti amakondedwa. Akatswiri ambiri amene amalangiza za kaleredwe ka ana ndi mavuto amene ana amakumana nawo akakhala ndi anzawo, amalimbikitsa makolo kuthandiza ana awo kuti azidziona kuti ndi ofunikira. Pokhala ndi maganizo abwino oterowo saoneka kukhala osavuta kuwapezerera.
Komatu kulankhula kokha sikokwanira. Aliyense m’banjamo amafunika kuphunzira kupatsa ena ulemu ndi kuwalemekeza, komanso kumvera ena chisoni. Ndiye musalole kuti m’nyumba mwanu wina akhale ndi khalidwe lotereli. Panyumba panu pazikhala pabwino kukhalapo, anthu ake muzilemekezana ndi kukondana.
Kutha kwa Kupezerera Ochepa Mphamvu
“Wina apweteka mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Ndi mmene Baibulo limafotokozera zochitika m’mbiri ya anthu. Inde, anthu akhala akupezerera anzawo ochepa mphamvu kwa zaka zikwi zambiri. Wolemba Baibulo wina anati: “Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwoŵa analibe wakuwatonthoza.”—Mlaliki 4:1.
Komabe, Mulungu amaona ndithu anthu onse amene amapezereredwa m’dzikoli, ndipo amawamvera chifundo. Koma kodi iye adzachitapo kalikonse? Inde adzatero! Taonani lonjezo ili lomwe lili pa Mika 4:4: “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”
Ndiye taganizirani mmene dzikoli lidzakhalire lonjezolo likadzakwaniritsidwa. Palibe amene adzaopsa anzake. Inde, kudzakhala kulibe opezerera anzawo! Kodi zimenezi sizosangalatsa? Komatu Mulungu sanangolonjeza tsogolo labwino chomwechi basi. Pakali pano ntchito yothandiza kwambiri yophunzitsa anthu Baibulo ili m’kati padziko lonse. Ntchitoyi ikuthandiza kwambiri. Amene akugwira nawo ntchitoyi amaphunzitsidwa kusintha makhalidwe awo amtopola, kukhala mwamtendere ndi anzawo, ndi kuti azipatsa ulemu ena ndi kuwalemekeza. (Aefeso 4:22-24) Posachedwapa zotsatira zamaphunziro apamwamba ameneŵa zidzakhudza dziko lonse, ndipo vuto la kupezerera anthu ochepa mphamvu silidzakhalakonso. Malonjezo a Mulungu amene ali m’Baibulo adzakwaniritsidwa. Aliyense amene adzakhala ndi moyo panthaŵiyo adzasangalala kukhala m’dziko lopanda anthu opezerera anzawo!
[Chithunzi patsamba 16]
Kumuchokerapo munthu wopezerera anzake sikochititsa manyazi
[Chithunzi patsamba 17]
M’banja lochitira zinthu pamodzi, ana amaphunzitsidwa kulimbana ndi anthu owapezerera m’njira ina iliyonse
[Chithunzi patsamba 18]
Phunzitsani ana anu kufotokoza maganizo awo motsimikiza koma mwaluso