Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndingatani Kuti Ndisiye Kufuna Kumangochita Zinthu Mosalakwitsa?

Ndingatani Kuti Ndisiye Kufuna Kumangochita Zinthu Mosalakwitsa?

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Ndingatani Kuti Ndisiye Kufuna Kumangochita Zinthu Mosalakwitsa?

“Pamoyo wanga ndimangofuna kuchita zinthu mosalakwitsako.”—Anatero Carly.

ACHINYAMATA ambiri amavutika ndi chikhumbo chofuna kuchita chilichonse mosalakwitsako ngakhale pang’ono.

Buku lakuti Perfectionism—What’s Bad About Being Too Good? linati: “Kufuna kuchita zinthu mwambambande n’kosiyana kwambiri ndi kufuna kuchita zinthu zoti sizingatheke. Inde anthu amene amafuna kuchita zinthu mwambambande amafunitsitsa kuchita zinthu mwadongosolo ndipo safuna kuchita zinthu mwamwambo chabe, komano anthu otere amalolera kulakwitsa kwawo ndipo amadziŵa njira zabwino zochitira zinthu akalakwitsa. . . . Komatu anthu amene amafuna kuchita zinthu mosalakwitsa n’komwe, nthaŵi zonse akamachita chinachake, mtima umakhala m’mwamba poopa kulakwitsa. Amafuna kukwanitsa kuchita zinthu zovuta kwambiri.”

Kodi inuyo ndinu munthu wotero? Ngati mumafuna kuchita zinthu mwapamwamba kwambiri mungamalephere kuchita zinthu zina. Mungathe kumapeŵa kuchita china chilichonse chimene simunachichitepo. Kapenanso mungathe kumazengereza kuchita zinthu zinazake zofunika chifukwa choopa kulakwitsa. N’kuthekanso kuti simungamafune munthu aliyense amene sakwanitsa kuchita zinthu mmene inuyo mumafunira, ndipo mapeto ake mungasoŵe anzanu omagwirizana nawo.

Ngati inuyo muli ngati munthu amene tam’longosolayu, ganizirani mawu a m’Baibulo a pa Mlaliki 7:16, omwe amati: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?” Inde, munthu wofuna kuchita zinthu mosalakwitsa ngakhale pang’ono angathe “kudziwononga” yekha! Ndipotu khalidwe lotere akuti limachititsa anthu ena kukhala ndi mavuto okhudza kudya otchedwa anorexia nervosa ndi bulimia. *

Motero mwina mungadzifunse kuti ‘Nangano ndingatani kuti ndisiye kufuna kumangochita zinthu mosalakwitsa?’ N’zoona kuti kusiya kuganiza motere n’kovuta. Koma Mulungu angathe kukuthandizani. Motero tiyeni tione mmene Mulungu amaonera nkhani imeneyi.

Kodi N’zotheka Kumangochita Zinthu Mosalakwitsa?

Poyamba tiyeni tifunse kuti kodi zingatheke kuti inuyo muzichita zinthu mwangwiro? Baibulo limasonyeza kuti n’zosatheka, chifukwa limati: “Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi . . . Onseŵa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino.” (Aroma 3:10-12) Aŵatu ndi mawu ogwira mtima kwambiri, si choncho? Akusonyeza kuti munthu aliyense amene amafuna kuchita zinthu mosalakwitsako amangodzivuta.

Taganizirani za mtumwi Paulo yemwe anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kukonda zinthu zauzimu. Koma ngakhale Paulo amene analephera kutumikira Mulungu popanda kulakwitsako. Iye anaulula kuti: “Pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. Pakuti monga mwa munthu wa m’kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lili kulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.” (Aroma 7:21-23) Ndi Mulungu yekha basi amene anathandiza Paulo kuti akhale Mkristu wokhulupirika.

Ubwino wake ngwakuti, Mulungu safuna kapenanso kuganiza kuti ifeyo tizichita zinthu mosalakwitsako. “Popeza adziŵa mapangidwe athu; akumbukila kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Ndi m’dziko latsopanso la Mulungu mokha mmene anthu adzakhale angwiro.

Sinthani Maganizo Anu

Motero, pakali pano si chinthu chanzeru kumaganiza kuti mungakwanitse kumachita zinthu mosalakwitsako. Ndipotu muyenera kuyembekezekera kuti nthaŵi ndi nthaŵi mungachite zinthu zina molakwitsa. (Aroma 3:23) Inde, nthaŵi zina sitidziŵa n’komwe kuti talakwitsa! Lemba la Salmo 19:12 limati: “Palibe amene angathe kuona zolakwa zake zomwe.” (Today’s English Version) Mnyamata wina wotchedwa Matthew anati: “Inuyo si munthu wangwiro ayi ndipo padziko lapansi palibe munthu wangwiro. Mukamafuna kuti muzichita zinthu mwangwiro, simudzaumva kukoma moyo. . . . Kumeneko n’kuganiza mobwerera chifukwa n’zosatheka.”

Bwanji muiganizire bwinobwino mfundo yatchulidwayi n’kusintha maganizo anu? Mwachitsanzo kodi mukudzivutitsa kwambiri pofuna kukhala katswiri woposa wina aliyense pa chinthu chinachake? Baibulo limanena kuti kudzivutitsa motere kungathe kukhala kwa “chabe ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:4) Kwenikweni, ndi anthu ochepa chabe amene amakwanitsa kukhala akatswiri oposa wina aliyense. Ndipo ngakhale munthu wina atakwanitsa kutero, nthaŵi zambiri pamadzabwera winanso amene amadzam’posa.

Mtumwi Paulo anapereka malangizo akuti: “Ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha.” (Aroma 12:3) Osafuna kuchita zinthu zosatheka! Ganizani mofatsa kuti muone ngati zimene mumafuna kuchita zili zoti mungazikwanitse. Muzifuna kuchita zinthu mwambambande, koma osati mwangwiro. Inde, muzikhala ndi cholinga chinachake koma chizikhala choti mungachikwanitse.

Mwachitsanzo, Paulo analimbikitsa Timoteo kuti akhale “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Inde Paulo ankalimbikitsa kuchita zinthu mwambambande, koma osati mwangwiro. Moteronso khalani ndi zolinga zimene mungathedi kuzikwanitsa. Ndipo ngati simukudziŵa kuti ndi zinthu zotani zimene mungathe kuzikwanitsa, kambiranani ndi makolo anu kapena munthu wina wachikulire amene mumam’khulupirira.

Ena mpaka amanena kuti ndi bwino kuchitira dala zinthu zina zimene simutha, monga kuyamba kuphunzira maseŵera enaake kapena kuyamba kuphunzira kuimba nyimbo mogwiritsira ntchito chida chinachake. N’zoona kuti mukayamba kuphunzira chinthu chinachake chatsopano muzilakwitsa zambiri. Koma zimenezi sizodandaulitsa ayi. Chifukwa mwina n’zimene zingakuthandizeni kuona kuti kulakwitsa ndiko kuphunzira.

Chilichonse chimene mukufuna kuchita, kaya n’kulemba nkhani yokachongetsa kusukulu, kaya n’kuphunzira kuimba mwaluso nyimbo inayake pa piyano, ganiziraninso malangizo ena aŵa a mtumwi Paulo akuti: “Musakhale aulesi m’machitidwe anu.” (Aroma 12:11) Inde musazengereze kuchita zinthu chifukwa choopa kulakwitsa.

Mtsikana wina ankakonda kuzengereza kulemba ntchito ya kusukulu ponamizira kuti “anali kukonzekera kaye.” Ngakhale kuti ndi bwino kukonzekera pochita zinthu, samalani kuti zimenezi zisakhale pobisalira mukamazengereza kuchita zinthu. Mtsikanayu anadzazindikira kuti “utati usankhepo pakati pa kuchongetsa ntchito imene siinakufike pamtima ndi kusachongetsa n’komwe, chinthu chabwino ndi kungochongetsa.”

Lekani Kuganiza Zinthu Zosathandiza!

N’zoona kuti zingakuvuteni maganizo kuchita ntchito inayake molakwitsa pena ndi pena. Maganizo ofooketsa ndi osathandiza angamakufikirenibe. Kodi zitatero mungatani? Dziŵani kuti kumangoganizira zinthu zosathandiza kumangosokoneza munthu basi. Choncho yesetsani kungowakankhira kunkhongo maganizo otero. Muzitha kumadziseka nokha pa zolakwa zanu. Chifukwatu ilipo “mphindi yakuseka.” (Mlaliki 3:4) Kumbukiraninso kuti Yehova sasangalala ndi mawu onyoza ngakhale atakhala mawu odzinyoza wekha munthu.—Aefeso 4:31.

M’malo momangodzinyoza nthaŵi zonse, tsatirani mawu a pa Miyambo 11:17 akuti: “Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake.” Choncho ganizirani funso ili lakuti, Kodi khalidwe lofuna kuchita zinthu zovuta kwambiri kuzikwanitsa lakuthandizani kupeza anzanu mosavuta? N’kutheka kuti silinakuthandizeni kutero. Mwinanso alipo anthu enaake amene simuwafuna n’komwe chifukwa choti satha kuchita zinthu mosalakwitsako. Nanga ndiye mungatani?

Tsatirani lamulo la m’Baibulo lakuti anthu ayenera “kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake.” (Akolose 3:13) Inde, simudzavutika kukhala ndi anzanu ngati mumalolera kuti azichita zimene iwo angakwanitse!

Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi anzanga angandithaŵirenji ngati nditakhala ndi khalidwe lofuna kuti ndisamalakwitse ngakhale pang’ono?’ Tangoganizirani mmene anzanu amamvera mukamanena zinthu zosonyeza kuti simufuna kuchita chinthu molakwitsako penapake. Buku lakuti When Perfect Isn’t Good Enough linalongosola kuti: “Kukonda kudandaula pa mayeso mukapanda kupeza A, kunganyozetse anzanu ena amene amachita kuvutikira kuti angopeza B kapena C amene.” Choncho yesetsani kuchepetsa madandaulo ndiponso kumangoganiza za inu nokha. Mukatero anthu azisangalala kwambiri kucheza nanu.

Mtsikana wotchedwa Carly anangonena mwachidule kuti: “Ineyo ndimangodziuza kuti ndiiwaleko za khalidwe langa losafuna kulakwitsali.” Kodi inuyo mungachite bwanji zimenezi? Sinkhasinkhani za mmene Mulungu amaionera nkhaniyi. Ngati mukuvutikabe kusintha maganizo anu pankhaniyi, kambiranani ndi makolo anu kapena ndi Mkristu wina wokhwima maganizo m’mpingo mwanu. Pempherani kwa Mulungu kuti akuthandizeni kusintha maganizo anu. Pemphero lingathandize kwambiri pothana ndi khalidweli.—Salmo 55:22; Afilipi 4:6, 7.

Nthaŵi zonse kumbukirani kuti Yehova safuna kuti tizichita zinthu mwangwiro; amangofuna kuti tizikhala okhulupirika kwa iye. (1 Akorinto 4:2) Ngati mukuyesetsa kukhala okhulupirika, mungasangalale ndi moyo wanu ngakhale kuti si inu wangwiro.

Ngati mukufuna kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani Mboni za Yehova, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5.

[Mawu a M’munsi]

[Chithunzi patsamba 30]

Kuopa kulakwitsa kungakulepheretseni kuchita zinthu

[Chithunzi patsamba 31]

Kuyesa kuphunzira zinthu zatsopano kungakuthandizeni kuzoloŵera kuti zinthu zimatha kulakwika