Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mumasankha Zimakhudza Thanzi Lanu

Zimene Mumasankha Zimakhudza Thanzi Lanu

Zimene Mumasankha Zimakhudza Thanzi Lanu

NTHAŴI zambiri anthu amavutika kudya moyenerera ndiponso kukhala athanzi. Chifukwa cha moyo wopanikiza wa masiku anowu, zikuoneka kuti n’kwapafupi kungodya zakudya zosavuta kukonza kusiyana ndi zakudya zofunika kukonza bwinobwino ndipo zikuonekanso kuti munthu ukapeza nthaŵi yopuma n’zophweka kumaona zinazake pa TV kapena pa kompyuta kusiyana n’kumachita zinthu zothamangitsa magazi. Komatu zinthu zimenezi n’kutheka kuti zikupereka matenda oopsa kwa achikulire ambiri ndi achinyamata omwe.

Magazini ya ku Asia yotchedwa Asiaweek inati, “kudya zakudya zamafuta ambiri ndiponso khalidwe lokonda kumangokhala likuchititsa kuti matenda a shuga achuluke kwambiri.” N’zodandaulitsa kuti matendaŵa ayambanso kumagwira achinyamata. Ndipo ku Canada “ofufuza anapeza kuti ndi wachinyamata m’modzi yekha pa achinyamata asanu ndi aŵiri amene amadya zipatso ndi ndiwo zamasamba [ndipo] anapeza kuti achinyamata ongoposa pang’ono pa theka la achinyamata ameneŵa ndi amene amachita maseŵera oti n’kutuluka thukuta,” inatero magazini yotchedwa The Globe and Mail. Moyo woterewu umachititsa kuti achinyamataŵa “adzayambe kudwala matenda a mtima adakali zaka za m’ma 30,” inatero nkhaniyo.

Akatswiri a za kugona nawonso amati munthu wamkulu amafunikira kugona mwina maola eyiti tsiku lililonse ndipo achinyamata angafunikire kugona maola oposa pamenepa. Ndipotu a ku yunivesite ya Chicago atachita kafukufuku, anapeza kuti anyamata athanzi lawo amene anagona maola anayi okha kwa masiku sikisi otsatizana, anayamba kukhala ndi zizindikiro za matenda amene makamaka amagwira anthu okalamba. Ngakhale kuti anthu ambiri amalolera kusagona n’cholinga choti agwire ntchito, achite za kusukulu kapena asangalale, kuteroko sikuŵapindulira pamapeto pake. James Maas, katswiri wofufuza nkhani zokhudza kugona pa yunivesite ya Cornell ku New York anati: “Munthu angathe kuchita zinthu ali ndi tulo koma sizitanthauza kuti zinthuzo akuzichitadi mwatcheru ndi mwaluso ndipo sizitanthauza kuti sangayambe kusinza atati ayendetse galimoto.”

N’zoona kuti pali zinthu zinanso zimene zimakhudza thanzi lathu. Mwachitsanzo kusadandauladandaula kungatithandize kukhala athanzi. Ndipo kukhala n’cholinga chenicheni m’moyo wathu kungatilimbikitse kusankha kuchita zinthu zimene zingatithandize kukhala athanzi.