Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amavomereza Makhalidwe a Kugonana Kwachilendo?

Kodi Mulungu Amavomereza Makhalidwe a Kugonana Kwachilendo?

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Amavomereza Makhalidwe a Kugonana Kwachilendo?

“KODI ndidzadziŵa liti mtundu wakugonana umene ndimakonda?” Analemba motero msungwana wina wazaka 13 padanga la malangizo m’magazini inayake. Funso la msungwanayu likutikumbutsa kuganiza kwa anthu ena amene amaona ngati kuti ali ndi ufulu kugonana m’njira ina iliyonse imene angafune.

Anthu ena amasokonezekadi akamaganiza za kugonana kumene angakonde. Ena sabisa kuti amakonda kugonana kwachilendo monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Pamene ena mopanda manyazi n’komwe amachita zinthu ndiponso amavala ngati akazi kapena amuna. Ena amachita opaleshoni yoti akhale akazi kapena amuna. Palinso anthu amene amati anthu akuluakulu aziloledwa kugona ndi ana aang’ono.

Kodi munthu ali ndi ufulu wosankha mtundu wina uliwonse wa kugonana kapena wosankha kukhala mwamuna kapena mkazi? Kodi Mawu a Mulungu amanenanji pankhani zimenezi?

“Anawalenga Iwo Mwamuna ndi Mkazi”

Malinga ndi buku la m’Baibulo la Genesis, Mulungu iyemwini analenga amuna ndi akazi mowasiyanitsa. Nkhaniyo imati: “Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake . . . Adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.”—Genesis 1:27, 28.

Mulungu analenga anthu kukhala aufulu wosankha ndipo anawapatsa mwayi wosangalala ndi ufuluwo. (Salmo 115:16) Munthu anapatsidwa udindo wosamalira zinthu zonse zamoyo zapadziko lapansi, ndi kuzitcha mayina oziyenerera. (Genesis 2:19) Komano pankhani yakugonana, Mulungu anapereka malangizo osapita m’mbali.—Genesis 2:24.

Chifukwa cha kusamvera kwa Adamu, tonsefe tinakhala opanda ungwiro. Chotero tiyenera kulimbana ndi zofooka zathupi ndi zikhumbo zamphamvu zimene sizigwirizana konse ndi cholinga cha Mulungu choyambirira. M’chilamulo chimene chinaperekedwa kwa Mose, Mulungu ananenamo kuti amanyansidwa ndi zochitika za kugonana kwina monga chigololo, kugonana pachibale, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, ndi kugonana kwa munthu ndi nyama. (Levitiko 18:6-23) Mulungu analetsanso kuti munthu asadzionetsere iye yekha ngati wamkazi kapena wamwamuna n’cholinga chokhala ndi makhalidwe oipa. (Deuteronomo 22:5) Baibulo nthaŵi zonse limaphunzitsa kuti kugonana kovomerezeka ndi Mulungu ndi kwa pakati pa mwamuna ndi mkazi okwatirana. (Genesis 20:1-5, 14; 39:7-9; Miyambo 5:15-19; Ahebri 13:4) Kodi kutsatira miyezo imeneyi n’kwanzeru?

Kodi ndi Ndani Ayenera Kusankha?

Baibulo limayerekezera zochita za munthu kwa Mlengi kukhala zofanana ndi dothi lomwe lili m’manja mwa woumba. Baibulolo limati: “Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mawu? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?”(Aroma 9:20) N’zosachita kufunsa konse kuti njira imene Mulungu anaipanga yolenga amuna ndi akazi ndiyo yoyenera pankhani ya kugonana. Motero kugonana kwa anthu ofanana ziwalo, kugonana ndi nyama, kapena kugona ana si chilengedwe cha anthu.—Aroma 1:26, 27, 32.

Chifukwa cha chimenechi, anthu amene amachita kugonana kwachilendoku, amadziika paudani ndi Mulungu. Baibulo lili ndi chenjezo ili lakuti: “Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wake! phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga chiyani?” (Yesaya 45:9) N’zomveka kuti Wopanga anthuyo ndiye woyeneradi kupereka malangizo a kugonana. Kodi si zomvekanso kuti anthu atsatire malangizo ameneŵa?

Kudziŵa Kukhala Nacho Chotengera Chanu

Wolemba Baibulo Paulo anagwiritsa ntchito fanizo lofananalo panthaŵi imene anali kupereka malangizo kwa Akristu pankhani ya kugonana. Iye anati: “Yense wa inu adziŵe kukhala nacho chotengera chake m’chiyeneretso ndi ulemu, kosati m’chiliro cha chilakolako chonyansa.” (1 Atesalonika 4:4, 5) Paulo anayerekezera thupi la munthu ndi chotengeramo zinthu. Kudziŵa kukhala nacho chotengera chako kumatanthauza kuchititsa maganizo, ndi zokhumba za munthuwe kukhala zogwirizana ndi malamulo a Mulungu a khalidwe labwino.

Kunena zoona, kuchita zimenezi sikungakhale kwapafupi. Zingakhale zovuta ndithu kwa munthu amene anagwiriridwapo paubwana, kaya amene anali ndi makolo kapena anthu ena omulera omwe anaonetsa chitsanzo cholakwika cha umuna ndi ukazi wawo, kapenanso kuti anali kuonerera zolaula akadali mwana. Chibadwa cha munthu, mahomoni a m’thupi lake, ndi mavuto amaganizo zingapangitse munthu kuganiza molakwa pankhani ya kugonana. Komabe, n’kotonthoza kudziŵa kuti Mlengi wathu angapereke thandizo ndi chilimbikitso kwa iwo ofuna.—Salmo 33:20; Ahebri 4:16.

Lolani Woumba Wamkulu Kuti Akuumbeni

Dongo limaikidwa pakati pa phale loumbira mbiya, woumbayo asanayambe ntchito yake. Ndipo phale loumbiralo likamazungulira, woumbayo amadinikiza dongolo mwaluso ndi zala zake n’kukhala mbiya. Mofananamo ifeyo tisanaumbidwe kuti tikhale ofunika kwambiri m’maso mwa Mulungu, tifunika kuika maganizo athu pa malangizo ndi malamulo osasintha a Mulungu. Ifeyo tikayamba kuchita khama, Mulungu amatiumba mwachikondi kudzera m’Baibulo, mzimu wake, ndi abale achikristu. Zikatere munthu amayamba kuona chisamaliro cha Mulungu m’moyo wake.

Ndithudi, tifunika kuyamba kudalira kwambiri nzeru za Mlengi, kukhulupirira kuti ndiye amadziŵa zimene zingatithandizedi. Chikhulupiriro choterocho chimakula mwapemphero ndi kuphunzira Baibulo mwakhama. Munthu akakhala ndi maganizo otere polingalira nkhani ya kugonana kosayenera, amatha kuumbika m’manja mwa Mlengi. Pa 1 Petro 5:6, 7 pamanena kuti: “Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthaŵi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.”

Kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku kumatidziŵitsa za atumiki okhulupirika ambirimbiri a Mulungu omwe analimbana ndi zikhumbo zathupi koma osagonja. Ndi zitsanzotu zolimbikitsa kwambiri! Tingaone kukhumudwa kwa mtumwi Paulo panthaŵi inayake pamene anafuula kuti: “Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m’thupi la imfa iyi?” Komabe, iye anatilozeranso kumene tingapeze thandizo lenileni pamene anadziyankhira funso lakelo kuti: “Ndiyamika Mulungu mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.”—Aroma 7:24, 25.

Zimene Zingakuthandizeni Kusintha

Tingathenso kugwiritsa ntchito mzimu woyera wa Mulungu. Mzimuwu ndi mphamvu yothandiza kwambiri kuti munthu asinthe. Umatithandiza ‘kuvula makhalidwe oyamba’ ndi ‘kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa monga mwa chifuniro cha Mulungu m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ (Aefeso 4:22-24) Atate wathu wachikondi wakumwamba salephera kutiyankha tikam’pempha mzimu woyera mochokera pansi pamtima kuti utithandize kusintha moteremu. Yesu anatitsimikizira kuti Atate “adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akupempha Iye.” (Luka 11:13) Kulimbikira kupemphera n’kofunika, monga mmene mawu a Yesu amasonyezera kuti: “Pemphani ndipo chidzapatsidwa kwa inu.” (Mateyu 7:7) Zimenezi zingatheke makamaka pamene tikuthetsa zikhumbo zamphamvu zakugonana.

Mulungu amatithandizanso kudzera mu ubale weniweni wachikristu, womwe wapangidwa ndi anthu osiyanasiyana. Akristu ena a ku Korinto a m’zaka 100 zoyambirira analinso ‘olobodoka ndi zoipa’ ndi ‘akudziipsa ndi amuna.’ Komabe anasintha. Mwazi wa Kristu unawayeretsa, ndipo analandiridwa pamaso pa Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Anthu ena masiku ano afunika kusintha koteroko. Ndipo anthu oterowo angalandire thandizo mu mpingo wachikristu lolimbana ndi zikhumbo zoipa.

Kodi zikutanthauza kuti kukhala Mkristu kungapangitse munthu kuthetsa zikhumbo zonse zolakwika kapena kusasokonezeka maganizo ndi nkhani yakuti ndi mwamuna kapena ndi mkazi? Osati kwenikweni. Inde, kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo kumathandiza ena kukhala ndi moyo wabwino. Koma ngakhale zili choncho, Akristu ameneŵa afunika kulimbana ndi zikhumbo zoipa za tsiku ndi tsiku. Kuchita tero kumawathandiza kutumikira Mulungu ngakhale ali ndi “munga m’thupi” wophiphiritsira. (2 Akorinto 12:7) Malinga ngati angapitirize kulimbana ndi zizoloŵezi zoipa ndi kukhalabe ndi khalidwe lolungama, Mulungu angawaone monga atumiki okhulupirika ndiponso opanda banga m’maso mwake. Angapitirizebe kuyembekezera nthaŵi imene mtundu wonse wa anthu ‘udzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’—Aroma 8:21.

Pakalipano, anthu onse ofuna kukondweretsa Mulungu ayenera kutsatira miyezo yake yolungama. Akristu oona amasankha kutumikira Mulungu, osati kutsatira zizoloŵezi zawo. Anthu amene modzichepetsa amagonjera chifuno cha Mulungu m’njira zonse za moyo wawo adzafupidwa ndi chimwemwe chosatha.—Salmo 128:1; Yohane 17:3.

Ngati mukufuna kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani Mboni za Yehova, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5.

[Mawu Otsindika patsamba 30]

Pankhani yakugonana, Mulungu anapereka malangizo osapita m’mbali

[Mawu Otsindika patsamba 31]

Akristu ena a ku Korinto a m’zaka 100 zoyambirira poyamba anali ‘olobodoka ndi zoipa’ ndi ‘akudziipsa ndi amuna.’ Komabe anasintha

[Chithunzi patsamba 32]

Kuphunzira Baibulo kumatithandiza kukhala ndi makhalidwe apamwamba